Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 25

“Mtima Wachifundo wa Mulungu Wathu”

“Mtima Wachifundo wa Mulungu Wathu”

1, 2. (a) Kodi mwachibadwa mayi amachita bwanji mwana wake akamalira? (b) Kodi ndi khalidwe lachikondi liti limene limaposa chifundo cha mayi?

KHANDA likulira pakati pa usiku. Mayi ake akudzuka mofulumira. Kungochokera pamene mwana wake anabadwa, mayiyu sagona kwambiri monga mmene ankagonera kale. Waphunzira kusiyanitsa maliridwe osiyanasiyana a mwana wakeyo. Motero nthaŵi zambiri amadziŵa ngati khandalo likufuna kuyamwa, kufukatidwa, kapena kulisamalira m’njira zina. Koma kaya mwanayo akulira chiyani, mayi akewo amachitapo kanthu. Mtima wake umakhala pa mwana wakeyo moti sanganyalanyaze zimene mwanayo akufuna.

2 Chifundo cha mayi pa mwana wake chili khalidwe limodzi mwa makhalidwe achikondi chakuya kwambiri amene anthu amawadziŵa bwino. Komabe, pali khalidwe lina lachikondi limene limaposa pamenepo, ndilo mtima wachifundo wa Mulungu wathu, Yehova. Kuphunzira khalidwe labwino limeneli kungatithandize kuyandikira kwambiri kwa Yehova. Choncho tiyeni tikambirane zimene chifundo chimatanthauza ndiponso mmene Mulungu wathu alili wachifundo.

Kodi Chifundo N’chiyani?

3. Kodi mawu achihebri otembenuzidwa kuti “kuchitira chifundo” kapena “kuchitira chisoni” amatanthauzanji?

3 M’Baibulo, mawu akuti chifundo amafanana kwambiri ndi akuti kuchitira munthu chisoni. Mawu angapo a Chihebri ndi Chigiriki ali ndi lingaliro la kukhala ndi mtima wachifundo. Mwachitsanzo, talingalirani mawu achihebri akuti ra·cham′, omwe kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa kuti “kuchitira chifundo” kapena “kuchitira chisoni.” Buku lina limafotokoza kuti mawu akuti ra·cham′ “amalongosola mmene munthu amamvera chifundo kwambiri ndiponso mwachikondi,  monga mmene zimakhalira tikaona munthu yemwe timamukonda kapena yemwe tifunika kumuthandiza wafooka kapena wavutika.” Mawu achihebri ameneŵa, omwe Yehova amawagwiritsa ntchito ponena za iye mwini, amafanana ndi mawu otanthauza “chiberekero” ndipo tikhoza kuwafotokoza kuti ndi “chifundo cha mayi.” *Eksodo 33:19; Yeremiya 33:26.

“Kodi mkazi angaiwale . . . mwana womubala iye?”

4, 5. Kodi Baibulo limagwiritsa ntchito motani mmene mayi amamvera ndi mwana wake wakhanda kuti litiphunzitse chifundo cha Yehova?

4 Baibulo limagwiritsa ntchito mmene mayi amamvera ndi mwana wake kuti litiphunzitse tanthauzo la chifundo cha Yehova. Pa Yesaya 49:15 timaŵerenga kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana womubala iye? Inde aŵa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” Mafotokozedwe ogwira mtima ameneŵa akutsindika mfundo yakuti Yehova amamvera chifundo kwambiri anthu ake. Motani?

5 N’zovuta kulingalira kuti mayi akhoza kuiwala kuyamwitsa ndi kusamalira mwana wake wakhanda. Ndi iko komwe, khanda silingadzithandize; khanda limafuna chisamaliro ndiponso chikondi cha mayi ake usana ndi usiku. Koma mwachisoni timamva nthaŵi ndi nthaŵi kuti mayi wina wathaŵa mwana wake, makamaka mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino zimene zikudziŵika ndi kupanda “chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1, 3) “Koma Ine sindingaiwale iwe,” akutero Yehova. Yehova sangaleke kukhala ndi mtima wachifundo pa atumiki ake. Chifundo chake n’chachikulu kwambiri kuposa mmene mayi mwachibadwa amamvera chifundo ndi mwana wake wakhanda. N’zosadabwitsa kuti munthu wina pothirira ndemanga pa Yesaya 49:15 anati: “Ameneŵa ndi amodzi mwa mawu amphamvu kwambiri, mwinanso ndiwo amphamvu kwambiri pa onse onena za chikondi cha Mulungu mu Chipangano Chakale.”

6. Kodi anthu opanda ungwiro ambiri amakuona motani kukhala ndi mtima wachifundo, koma kodi Yehova amatitsimikiziranji?

 6 Kodi munthu wa mtima wachifundo ndiye kuti ndi wofooka? Anthu opanda ungwiro ambiri amatero. Mwachitsanzo, Seneca, wafilosofi wina wa ku Roma yemwe anakhalako m’masiku a Yesu komanso anali munthu wophunzira kwambiri ku Romako, anali kuphunzitsa kuti “kumvera ena chisoni ndiko kufooka maganizo.” Seneca anali kulimbikitsa chiphunzitso cha Chistoiki, filosofi imene inali kunena kuti munthu azikhala wodekha koma wosamvera anthu chisoni. Seneca anati munthu wanzeru akhoza kuthandiza ovutika, koma sayenera kuwamvera chisoni chifukwa zimenezi zikhoza kumuchititsa kukhala wosadekha. Malingaliro okhala ndi moyo wodzikonda amenewo sanapereke mpata uliwonse wosonyeza chifundo kuchokera pansi pamtima. Koma Yehova sali choncho! M’Mawu ake, Yehova amatitsimikizira kuti “ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Monga mmene tionere, kukhala wachifundo si kufooka, koma ndi khalidwe losonyeza mphamvu ndiponso lofunika kwambiri. Tiyeni tipende mmene Yehova, monga kholo lachikondi, amasonyezera khalidweli.

Yehova Anachitira Chifundo Mtundu Winawake

7, 8. Kodi Aisrayeli anavutika motani ku Igupto wakale, ndipo Yehova anachitapo chiyani pa kuvutika kwawoko?

7 Chifundo cha Yehova chimaoneka mosavuta m’zimene anali kuchitira mtundu wa Israyeli. Kumbukirani nthaŵi ija pamene Aisrayeli miyandamiyanda anali akapolo ku Igupto wakale, komwe anali kuponderezedwa kwambiri. Aigupto ‘anaŵaŵitsa moyo wawo ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa.’ (Eksodo 1:11, 14) Ali m’kati movutika choncho, Aisrayeli ankachonderera Yehova kuti awathandize. Kodi Mulungu wa mtima wachifundo anachitanji?

8 Yehova anakhudzika mtima. Ananena kuti: “Ndapenyetsetsa  mazunzo a anthu anga ali m’Igupto, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziŵa zoŵaŵitsa zawo.” (Eksodo 3:7) Yehova sakanatha kungoona anthu ake akuvutika kapena kungomva akufuula iye wosamva chisoni. Monga taonera m’Mutu 24 wa buku lino, Yehova ndi Mulungu amene amamvera ena chisoni. Ndipotu kumvera munthu wina chisoni, kukhudzidwa ndi ululu umene munthu wina akumva, n’kogwirizana ndi kukhala munthu wachifundo. Komatu Yehova sanangomvera chisoni anthu ake; analimbikitsidwa kuchitapo kanthu kuti awathandize. Yesaya 63:9 amati: “M’kukonda kwake ndi m’chisoni chake Iye anawawombola.” Yehova analanditsa Aisrayeli ku Igupto ndi “dzanja lamphamvu.” (Deuteronomo 4:34) Ndiyeno, iye anawapatsa chakudya mozizwitsa ndiponso dziko lawolawo lachonde kwambiri.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anali kulanditsa Aisrayeli mobwerezabwereza atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa? (b) M’masiku a Yefita, kodi Yehova analanditsa Aisrayeli pamene anali kuponderezedwa ndi ndani, ndipo n’chiyani chinamuchititsa zimenezi?

9 Chifundo cha Yehova sichinathere pamenepa. Atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa, nthaŵi ndi nthaŵi Aisrayeli anali kuchita zinthu mosakhulupirika ndipo ankavutika pamapeto pake. Zikatero anthuwo ankazindikira kulakwa kwawo ndi kufuulira Yehova kuti awathandize. Mobwerezabwereza iye anali kuwalanditsa. Chifukwa chiyani? “Chifukwa anamvera chifundo anthu ake.”—2 Mbiri 36:15; Oweruza 2:11-16.

10 Talingalirani zimene zinachitika m’masiku a Yefita. Popeza kuti Aisrayeli anali atayamba kutumikira milungu yonyenga, Yehova analola Aamoni kuwapondereza kwa zaka 18. Pamapeto pake Aisrayeli analapa. Baibulo limatiuza kuti: “Anachotsa milungu yachilendo pakati pawo, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israyeli.” (Oweruza 10:6-16) Anthu ake atalapa moona mtima, Yehova sanathe kumangowaona akuvutika. Motero Mulungu wa mtima wachifundoyu anapatsa mphamvu  Yefita kuti alanditse Aisrayeli m’manja mwa adani awo.—Oweruza 11:30-33.

11. Kodi tikuphunziranji za kukhala wachifundo kuchokera pa zimene Yehova anachitira Aisrayeli?

11 Kodi zimene Yehova ankachitira mtundu wa Israyeli zikutiphunzitsanji za kukhala ndi mtima wachifundo? Chinthu chimodzi n’chakuti, chifundo cha Yehova sindicho kungozindikira momva chisoni mavuto amene anthu akukumana nawo. Kumbukirani chitsanzo chija cha mayi amene mwana wake akamalira amachitapo kanthu chifukwa chomumvera chifundo. Mofananamo, Yehova sanyalanyaza madandaulo a anthu ake. Mtima wake wachifundo umamuchititsa kuwathandiza mavuto awo. Chinanso n’chakuti, mmene Yehova anachitira zinthu ndi Aisrayeli zimatiphunzitsa kuti kukhala wachifundo si kukhala wofooka. Khalidwe lachikondi limeneli linachititsa Yehova kuchita zinthu zamphamvu ndiponso zotsimikizika pothandiza anthu ake. Koma kodi Yehova amachitira chifundo atumiki ake monga gulu basi?

Yehova Amachitira Chifundo Munthu Aliyense Payekha

12. Kodi Chilamulo chinasonyeza motani kuti Yehova amachitira chifundo munthu aliyense payekha?

12 Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Israyeli chinasonyeza kuti iye amachitira chifundo munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, talingalirani mmene iye anali kudera nkhaŵa anthu aumphaŵi. Yehova anadziŵa kuti pakhoza kubuka zochitika zadzidzidzi zimene zikanachititsa Mwisrayeli kukhala waumphaŵi. Kodi anthu osauka anafunika kuwaona motani? Yehova analamula Aisrayeli kuti: “[Musakakala] mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphaŵi; muzimupatsa ndithu, osaŵaŵa mtima wanu pomupatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse.” (Deuteronomo 15:7, 10) Yehova analamulanso Aisrayeli kuti asamakolole zonse za m’mphepete mwa minda yawo  kapenanso kukunkha khunkha. Anthu ovutika ndiwo anafunika kukunkha zimenezi. (Levitiko 23:22; Rute 2:2-7) Pamene mtunduwo unachita zimene linanena lamulo limeneli loganizira aumphaŵi amene anali nawo, anthu osauka mu Israyeli sanali kupemphetsa chakudya. Kodi zimenezi sizinaonetse kuti Yehova ndi wa mtima wachifundo?

13, 14. (a) Kodi mawu a Davide amatitsimikizira motani kuti Yehova amadera nkhaŵa kwambiri aliyense wa ife monga munthu payekha? (b) Kodi tingachitire chitsanzo motani kuti Yehova ali pafupi ndi amene ali ndi “mtima wosweka” kapena “mzimu wolapadi”?

13 Lerolinonso, Mulungu wathu wachikondi amadera nkhaŵa kwambiri munthu aliyense payekha. Tingakhale otsimikiza kuti amadziŵa bwino kwambiri chilichonse chimene tikuvutika nacho. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:15, 18) Munthu wina wothirira ndemanga pa Baibulo ananena za anthu amene akufotokozedwa m’mavesiŵa kuti: “Iwo ali ndi mtima wosweka ndi mzimu wolapa, ndiko kuti, uchimo wawanyazitsa ndipo sakudziona monga ofunika; amadziona monga anthu achabechabe, ndipo amakhala alibe chidaliro chilichonse m’zochita zawo.” Anthu otereŵa angaone ngati Yehova ali nawo kutali kwambiri. Angaonenso kuti ndi opanda ntchito m’pang’ono pomwe moti iye sangawasamalire. Koma sichoncho. Mawu a Davide akutitsimikizira kuti Yehova sasiya anthu amene “amadziona monga anthu achabechabe.” Mulungu wathu wachifundo amadziŵa kuti panthaŵi zoterozo timamufuna kuposa nthaŵi zina zilizonse, ndipo iye amakhala pafupi nafe.

14 Talingalirani izi zimene zinachitika ku United States. Mayi wina anathamangira ku chipatala ndi mwana wake wazaka ziŵiri yemwe anali kubanika ndi kutsokomola kwambiri. Atamupima, madokotala anauza mayi akewo kuti mwanayo afunika kuti agone m’chipatalamo. Kodi usiku umenewo mayiyo anagona kuti? Anali pa mpando pafupi ndi bedi la mwana  wakeyo m’chipatala momwemo! Mwana wake anali kudwala ndipo iye anafunika kukhala naye pafupi. Ndithudi tingayembekeze zoposa pamenepa kwa Atate wathu wachikondi wakumwamba. Ndi iko komwe, tinapangidwa m’chifanizo chake. (Genesis 1:26) Mawu ogwira mtima a pa Salmo 34:18 amatiuza kuti pamene tili ndi “mtima wosweka” kapena tili ndi “mzimu wolapadi,” Yehova, monga kholo lachikondi, amakhala “ali pafupi,” ndiko kuti nthaŵi zonse amakhala wachifundo ndi wokonzeka kutithandiza.

15. Kodi Yehova amathandiza aliyense payekha m’njira zotani?

15 Ndiyeno, kodi Yehova amathandiza motani aliyense wa ife payekha? Si kuti amachotsa chimene chikutivutitsacho. Koma anthu amene amachonderera kwa iye kuti awathandize, Yehova wawapatsa zinthu zambiri zowathandiza. Mawu ake, Baibulo, ali ndi uphungu wothandiza womwe ungasinthe zinthu. Mu mpingo, Yehova amapereka oyang’anira oyenerera mwauzimu omwe amayesetsa kusonyeza chifundo chake pothandiza olambira anzawo. (Yakobo 5:14, 15) Pokhala “Wakumva pemphero,” amapereka “Mzimu Woyera kwa iwo akumupempha Iye.” (Salmo 65:2; Luka 11:13) Mzimu umenewo ungatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tithe kupirira mpaka Ufumu wa Mulungu utachotsa mavuto onse. (2 Akorinto 4:7) Kodi sitingathokoze kuti amatipatsa zonsezi kuti zitithandize? Tisaiwale kuti zimatisonyeza kuti Yehova ndi wa mtima wachifundo.

16. Kodi chitsanzo chachikulu kwambiri cha chifundo cha Yehova n’chiti, ndipo munthu aliyense payekha chimamukhudza motani?

16 Zoonadi, chitsanzo chachikulu cha chifundo cha Yehova n’chakuti anapereka Munthu yemwe amamukonda kwambiri kuti akhale dipo lathu. Yehova anadzipereka mwachikondi pochita zimenezi, ndipo zinatipatsa njira yopulumukira. Kumbukirani kuti dipo limenelo linaperekedwa m’malo mwa ife, aliyense payekha. Mpake kuti Zakariya, atate wake wa Yohane Mbatizi, ananeneratu kuti mphatso imeneyi inaonetsa bwino kwambiri “mtima wachifundo wa Mulungu wathu.”—Luka 1:78.

 Pamene Yehova Sasonyeza Chifundo

17-19. (a) Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti Yehova amafika poleka kuchitira anthu chifundo? (b) Kodi n’chiyani chinachititsa Yehova kuleka kuchitira chifundo anthu ake?

17 Kodi tiyenera kulingalira kuti Yehova amangosonyezabe mtima wachifundo mpaka kalekale? Ayi, chifukwa Baibulo limanena momveka bwino kuti kwa anthu amene amatsutsa njira zake zolungama, moyenerera Yehova sawachitira chifundo. (Ahebri 10:28) Kuti timvetse chifukwa chimene amachitira zimenezi, kumbukirani chitsanzo cha mtundu wa Israyeli chija.

18 Ngakhale kuti Yehova analanditsa Aisrayeli mobwerezabwereza kwa adani awo, m’kupita kwanthaŵi analeka kuwachitira chifundo. Anthu aliuma ameneŵa ankalambira mafano, ndipo ankaika mafano awo onyansawo ngakhale m’kachisi wa Yehova weniweniyo! (Ezekieli 5:11; 8:17, 18) Ndiponso timamva kuti: ‘Ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe chowalanditsa.’ (2 Mbiri 36:16) Aisrayeli anafika pakuti panalibe chifukwa chomveka chowachitira chifundo, ndipo molungama Yehova anawakwiyira. Kodi n’chiyani chinatsatirapo?

19 Yehova sanapitirize kuchitira chifundo anthu ake. Analengeza kuti: “Sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawawononge.” (Yeremiya 13:14) Motero Yerusalemu ndi kachisi wake zinawonongedwa, ndipo Aisrayeli anatengedwa ukapolo ku Babulo. Imakhalatu ngozi yaikulu kwambiri pamene anthu ochimwa apandukiratu kwakuti Mulungu sangawamverenso chisoni!—Maliro 2:21.

20, 21. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani pamene Mulungu wafika poleka kuchitira anthu chifundo m’masiku athu ano? (b) Kodi ndi mphatso yachifundo iti ya Yehova imene tikambirane m’mutu wotsatira?

20 Nanga bwanji lerolino? Yehova sanasinthe. Chifukwa cha chifundo chake, watuma Mboni zake kuti zilalikire ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14)  Pamene anthu a mitima yabwino alabadira, Yehova amawathandiza kumvetsetsa uthenga wa Ufumuwo. (Machitidwe 16:14) Koma ntchitoyi sikuti idzagwiridwa mpaka kalekale. Kungakhale kupanda chifundo ngati Yehova atalola dziko loipali limodzi ndi mavuto ake onse kukhalapobe mpaka kalekale. Yehova akadzafika poti sangachitirenso anthu chifundo, adzaweruza dziko lilipoli. Ngakhale panthaŵi imeneyo, adzapereka chiweruzo chifukwa cha chifundo, adzachitira chifundo ‘dzina lake loyera’ ndiponso atumiki ake odzipereka. (Ezekieli 36:20-23) Yehova adzachotsa kuipa ndipo adzabweretsa dziko latsopano lachilungamo. Yehova analengeza izi zokhudza oipa: “Diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yawo pamutu pawo.”—Ezekieli 9:10.

21 Mpaka nthaŵi imeneyo itakwana, Yehova akuchitirabe anthu chifundo, ngakhale amene adzawonongedwa. Anthu ochimwa amene amalapadi moona mtima angapindule ndi imodzi mwa mphatso zachifundo kwambiri za Yehova—angawakhululukire machimo awo. M’mutu wotsatira, tikambirana mawu ena a m’Baibulo amene amapereka chithunzi chabwino kwambiri cha mmene Yehova amakhululukira anthu kotheratu.

^ ndime 3 N’zochititsatu chidwi kuti pa Salmo 103:13, mawu achihebri akuti ra·cham′ akunena za chifundo chimene atate amakhala nacho pa ana ake.

Mafunso Owasinkhasinkha