Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 24

Palibe ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’

Palibe ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’

1. Kodi ndi maganizo ogwetsa mphwayi ati amene anthu ambiri, kuphatikizapo Akristu ena oona, amavutika nawo?

KODI Yehova Mulungu amakukondani inuyo monga munthu panokha? Ena amavomereza kuti Mulungu amakonda anthu onse, monga mmene Yohane 3:16 amanenera. Komano amati: ‘Mulungu sangandikonde ine monga munthu pandekha.’ Ngakhale Akristu oona nthaŵi zina angakayikire zimenezi. Mwamuna wina atagwa mphwayi anati: “N’zovuta kwambiri kukhulupirira kuti Mulungu amandisamalira pa chinachake.” Kodi inunso mumakayikira chomwechi nthaŵi zina?

2, 3. Kodi ndani amafuna kuti tizikhulupirira kuti m’maso mwa Yehova ndife achabechabe kapenanso kuti palibe yemwe akhoza kutikonda, nanga malingaliroŵa tingawathetse motani?

2 Satana amafunitsitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova Mulungu satikonda ndiponso sationa ngati ofunika. N’zoona kuti Satana kaŵirikaŵiri amanyenga anthu powachititsa kukhala odzikuza ndi onyada. (2 Akorinto 11:3) Komanso amasangalala pochititsa anthu ofooka kudziona kuti ndi osanunkha kanthu. (Yohane 7:47-49; 8:13, 44) Akuchita zimenezi makamaka mu “masiku otsiriza” ano. Lerolino anthu ambiri amaleredwa m’mabanja “opanda chikondi chachibadwidwe.” Ena amakumana kaŵirikaŵiri ndi anthu amene ali aukali, odzikonda, ndi aliuma. (2 Timoteo 3:1-5) Chifukwa chokhala zaka zambiri akuvutitsidwa, kusankhidwa mtundu, kapena kudedwa, anthu oterowo angafike pokhulupirira kuti ndi achabechabe kapena kuti palibe yemwe akhoza kuwakonda.

3 Ngati muli ndi maganizo olefula otereŵa, musataye mtima. Ambiri a ife timadziweruza mosayenerera nthaŵi zina. Koma kumbukirani kuti Mawu a Mulungu analinganizidwa kuti ‘azikonza zolakwa’ ndi ‘kuzula zinthu zozikika mwamphamvu.’ (2 Timoteo 3:16, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono; 2 Akorinto 10:4, NW) Baibulo limati: “Tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, mmene monse mtima wathu  utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Tiyeni tione njira zinayi zimene Malemba amatithandizira ‘kukhazikitsa mtima wathu’ pa chikondi cha Yehova.

Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Wofunika

4, 5. Kodi fanizo la Yesu la mpheta limasonyeza motani kuti ndife ofunika kwa Yehova?

4 Choyamba, Baibulo limaphunzitsa mosapita m’mbali kuti Mulungu amaona mtumiki wake aliyense kukhala wofunika. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW]: komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu aŵerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Talingalirani zimene mawu ameneŵa anatanthauza kwa anthu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino amene anamva Yesu akulankhula.

“Inu mupambana mpheta zambiri”

5 Tingadabwe kuti munthu angagule mpheta chifukwa chiyani. Eya, m’masiku a Yesu mpheta ndiyo inali mbalame yotsika mtengo kwambiri imene anali kugulitsa anthu kuti adye. Taonani kuti munthu anali kugula mpheta ziŵiri ndi kakobiri kamodzi. Koma panthaŵi ina Yesu anati ngati munthu anali ndi timakobiri tiŵiri anali kugula, osati mpheta zinayi, koma zisanu. Mbalame inayo anali kumuikirapo ngati kuti inalibe mtengo uliwonse. Mwinamwake zolengedwa zoterozo zinali zachabechabe m’maso mwa anthu, koma kodi Mlengi anali kuziona motani? Yesu anati: “Palibe imodzi ya izo [ngakhale yoikirirayo] iiwalika pamaso pa Mulungu.” (Luka 12:6, 7) Tsopano tingayambe kumvetsa mfundo ya Yesu. Ngati Yehova amaona mpheta imodzi kukhala yofunika kwambiri moteromo, ndiye kuti munthu ndi wofunika kwambiri zedi! Monga anafotokozera Yesu, Yehova amadziŵa chilichonse chokhudza ife. Inde, tsitsi lonse la kumutu kwathu amaliŵerenga.

6. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza kuti Yesu anali kunena zinthu zoti zikhoza kuchitika pamene ananena za kuŵerenga tsitsi la kumutu kwathu?

6 Kuŵerenga tsitsi lathu? Ena angaganize kuti pamfundoyi Yesu anali kunena zinthu zosatheka. Komabe, tangoganizirani za chiyembekezo cha chiukiriro. Yehova akuyeneratu kutidziŵa bwino  kwambiri kuti adzakhoze kutilenganso! Amationa kukhala ofunika kwambiri moti amakumbukira kalikonse kokhudza ifeyo, kuphatikizapo dongosolo lathu la majini ndiponso zokumbukira zathu zonse limodzi ndi zimene takumana nazo m’zaka zathu zonse. * Kuŵerenga tsitsi lathu, limene limakhalapo pafupifupi 100,000 ku mitu ya anthu ambiri, ingakhale ntchito yosavuta poyerekezera ndi zinazo.

Kodi Yehova Amaonanji mwa Ife?

7, 8. (a) Kodi ndi makhalidwe ena ati amene Yehova amasangalala nawo akawapeza pamene akusanthula mitima ya anthu? (b) Kodi ndi ntchito zina ziti zomwe timachita zimene Yehova amayamikira?

7 Chachiŵiri, Baibulo limatiphunzitsa zimene Yehova amaona kukhala zofunikira mwa atumiki ake. Kunena mosachulukitsa gaga m’diŵa, iye amasangalatsidwa ndi makhalidwe athu abwino ndiponso khama lathu. Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Pamene Mulungu akusanthula mitima ya anthu mabiliyoni ambirimbiri m’dziko lodzala chiwawa komanso chidanili, iye amasangalalatu kwambiri akapeza mtima wokonda mtendere, choonadi, ndi chilungamo! Kodi chimachitika n’chiyani pamene Mulungu wapeza mtima umene ukusefukira ndi chikondi kwa iye, mtima umene ukufunafuna kuphunzira za iye ndi kuuza ena zimene waphunzirazo? Yehova amatiuza kuti amawaona anthu omwe amauza ena za iye. Alinso ndi “buku la chikumbutso” kaamba ka “iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Makhalidwe otereŵa ndi amtengo wapatali kwa iye.

8 Kodi zina mwa ntchito zabwino zimene Yehova amayamikira ndi ziti? Ndithudi amayamikira khama limene timachita potsanzira Mwana wake, Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Ntchito ina yofunika kwambiri imene Mulungu amayamikira ndiyo kufalitsa  uthenga wabwino wa Ufumu wake. Pa Aroma 10:15, timaŵerenga kuti: “Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Kaŵirikaŵiri sitingaganizire kuti mapazi athu ndi “okometsetsa,” kapena kuti okongola. Koma m’lembali akuimira khama limene atumiki a Yehova amachita polalikira uthenga wabwino. Khama lonselo n’lokongola ndiponso n’lamtengo wapatali m’maso mwake.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova amayamikira kupirira kwathu pamene tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana? (b) Yehova saona atumiki ake okhulupirika m’njira yosalimbikitsa iti?

9 Yehova amayamikiranso kupirira kwathu. (Mateyu 24:13) Kumbukirani kuti Satana amafuna mutam’kana Yehova. Tsiku lililonse limene mumakhulupirikabe kwa Yehova mumathandiza kuyankha zotonza za Satana. (Miyambo 27:11) Nthaŵi zina kupirira kumakhala kovuta zedi. Matenda, mavuto azachuma, kuvutika maganizo, ndiponso mavuto ena zingakhale ziyeso za tsiku ndi tsiku. Tingagwenso mphwayi chifukwa chakuti zimene tikuyembekezera zikuchedwa kuchitika. (Miyambo 13:12) Kupirira pamene tikumana ndi mavuto oterowo n’kwamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova. Ndicho chifukwa  chake Mfumu Davide anapempha Yehova kuti amusungire misozi yake “m’nsupa.” Mwachidaliro anawonjezera kuti: “Kodi siikhala m’buku mwanu?” (Salmo 56:8) Inde, Yehova amasunga ndiponso amakumbukira misozi yonse ndi kuvutika konse kumene timapirira nako pokhalabe okhulupirika kwa iye. Misoziyo limodzi ndi kuvutikako ndi zamtengo wapatali m’maso mwake.

Yehova amayamikira kupirira kwathu pamene tikumana ndi ziyeso

10 Komano mtima wathu wokonda kudzitsutsa ungakane umboni umenewu wakuti ndife ofunika kwa Mulungu. Ungamanong’one mosalekeza kuti: ‘Komatu pali anthu ambirimbiri a chitsanzo chabwino kuposa ineyo. Yehova ayeneratu kuti amakhumudwa kwambiri akandiyerekezera ndi amenewo!’ Yehova satiyerekezera ndi ena; ndiponso saumirira pachinthu chimodzimodzi kaya kuganiza mwankhanza. (Agalatiya 6:4) Amaona mosamala kwambiri zimene zili m’mitima mwathu, ndipo amayamikira zabwino zimene waziona, ngakhale zili zochepa.

Yehova Amasefa Zabwino pa Zoipa

11. Kodi nkhani ya Abiya ingatiphunzitsenji za Yehova?

11 Chachitatu, pamene Yehova akutisanthula, amasefa zinthu mosamalitsa kuti apeze zabwino. Mwachitsanzo, pamene Yehova analamula kuti banja lonse lampatuko la Mfumu Yerobiamu liphedwe, analamula kuti mwana mmodzi wa mfumuyo, Abiya, aikidwe m’manda mwa mwambo wake. Chifukwa chiyani? “Mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israyeli.” (1 Mafumu 14:1, 10-13) Tinganene kuti Yehova anasefa zimene zinali mumtima mwa mnyamatayo n’kupezamo “chokoma.” Mosasamala kanthu kuti chokoma chimenecho chinali chochepa motani, Yehova anaona kuti chinali choyenera kuchitchula m’Mawu ake. Ndiponso iye anafupa chokomacho, mwa kusonyeza chifundo moyenerera kwa munthu mmodzi ameneyo wa m’banja lampatuko.

12, 13. (a) Kodi nkhani ya Mfumu Yehosafati imasonyeza motani kuti Yehova amafunafuna zabwino zimene timachita ngakhale pamene tachimwa? (b) Ponena za ntchito zathu zabwino ndi makhalidwe athu, kodi Yehova amachita motani monga Kholo lachikondi?

12 Tingaone chitsanzo chabwino kwambiri m’nkhani ya mfumu yabwino Yehosafati. Mfumuyi itachita zinthu zopanda nzeru, mneneri wa Yehova anaiuza kuti: “Chifukwa cha ichi ukugwerani  mkwiyo wochokera kwa Yehova.” Ameneŵa ndi mawu oopsa bwanji! Komatu uthenga wa Yehova sunathere pomwepo. Unapitirira kunena kuti: “Koma zapezeka zokoma mwa inu.” (2 Mbiri 19:1-3) Motero mkwiyo wolungama wa Yehova sunamupangitse kuti asaone zokoma zimene Yehosafati anachita. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi anthu opanda ungwiro. Anthu ena akatikhumudwitsa, tingalephere kuona zabwino zimene amachita. Ndipo tikachimwa, tingalephere kuona zabwino zimene timachita; chifukwa chokhumudwa, kuchita manyazi, ndiponso kumva kuti ndife olakwa. Komabe kumbukirani kuti ngati tilapa machimo athu ndi kuyesetsa kuti tisabwerezenso kuchimwa, Yehova amatikhululukira.

13 Pamene Yehova akukusanthulani, machimo oterowo amawataya, mofanana kwambiri ndi mmene munthu wofufuza golide amatayira miyala yosafunika. Kodi makhalidwe anu ndiponso ntchito zanu zabwino amatani nazo? Eya, zimenezi ndizo “timiyala tamtengo wapatali” timene amasunga! Kodi munaona mmene makolo ena amasungira mwachikondi zojambula za ana awo kapena zochita zina za kusukulu, nthaŵi zina mpaka zaka zambirimbiri anawo ataiwala? Yehova ndi Kholo lokonda ana ake kwambiri zedi. Malinga ngati tikukhalabe okhulupirika kwa iye, saiwala ntchito zabwino ndiponso makhalidwe abwino amene tili nawo. Ndipo iye angaone kuti ndi  kusalungama kuiwala zimenezi, komatu sali wosalungama. (Ahebri 6:10) Amatisefanso m’njira ina.

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani kupanda ungwiro kwathu sikulepheretsa Yehova kuona zinthu zabwino zimene timachita? Perekani chitsanzo. (b) Kodi Yehova amachitanji ndi zinthu zabwino zimene amapeza mwa ife, nanga anthu ake okhulupirika amawaona motani?

14 Yehova amayang’ana mopitirira pa kupanda ungwiro kwathu n’kuona zimene tingathe kuchita. Tifanizire motere: Anthu amene amakonda ntchito zaluso amayesetsa mwa mtima bii kukonzanso zojambula kaya zinthu zina zimene zawonongeka kwambiri. Mwachitsanzo, pamene m’nyumba yosungiramo zinthu zaluso ya National Gallery mu mzinda wa London, ku England, munthu wina anawonongamo ndi mfuti chithunzi cha ndalama pafupifupi madola 30 miliyoni chomwe anajambula Leonardo da Vinci, palibe yemwe ananenapo kuti popeza chithunzicho chawonongeka ndiye angochitaya. Mosakhalitsa ntchito inayambika yokonzanso chithunzi chojambulidwa mwalusocho chomwe chakhalapo kwa zaka pafupifupi 500. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu okonda zojambulajambula anali kuchikonda zedi. Kodi inu sindinu wofunika kwambiri kuposa chithunzi chojambulidwa ndi choko ndi makala? Ndithudi ndinu wamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu, ngakhale mutawonongeka chotani ndi kupanda ungwiro kumene munabadwa nako. (Salmo 72:12-14) Yehova Mulungu, yemwe analenga anthu mwaluso, adzachita zimene zikufunika kuti onse amene akulabadira chisamaliro chake chachikondi adzakhalenso angwiro.—Machitidwe 3:21; Aroma 8:20-22.

15 Inde, Yehova amaona zinthu zabwino mwa ife zomwe ife enife sitingazione. Ndipo pamene tikumutumikira, zinthu zabwinozo adzazikulitsa mpaka titafika pokhala angwiro. Mosasamala zimene latichita dziko la Satana, Yehova amaona atumiki ake okhulupirika kukhala ofunika.—Hagai 2:7.

Yehova Amasonyeza Chikondi Chake Pochitapo Kanthu

16. Kodi ndi uti umene uli umboni waukulu kwambiri wakuti Yehova amatikonda, ndipo timadziŵa bwanji kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa aliyense wa ife?

16 Chachinayi, Yehova amachita zambiri potsimikizira kuti  amatikonda. Ndithudi, nsembe ya dipo ya Kristu ili yankho logwira mtima kwambiri la bodza la Satana lakuti ndife achabechabe kapenanso lakuti palibe yemwe angatikonde. Tisaiwaletu kuti kufa mozunzika kwa Yesu pa mtengo wozunzirapo, ndipo ngakhalenso kuzunzika kwakukulu kumene Yehova anapirira nako poonerera Mwana wake wokondedwa akufa, ndi umboni wakuti iwo amatikonda. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amalephera kukhulupirira kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa iwowo pawokha. Amadziona kukhala achabechabe. Koma kumbukirani kuti mtumwi Paulo anali kupha otsatira a Kristu. Komatu iye analemba kuti: ‘Mwana wa Mulungu . . . anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’Agalatiya 1:13; 2:20.

17. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani kuti atikokere kwa iye mwini ndi kwa Mwana wake?

17 Yehova amatitsimikizira kuti amatikonda mwa kutithandiza aliyense payekha kugwiritsa ntchito mapindu a nsembe ya Kristu. Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amukoka iye.” (Yohane 6:44) Inde, Yehova mwiniyo amatikokera kwa Mwana wake ndi kutinso tikhale n’chiyembekezo cha moyo wamuyaya. Motani? Kupyolera m’ntchito yolalikira imene imafikira aliyense. Ndiponso kupyolera mwa mzimu wake woyera umene Yehova amagwiritsa ntchito potithandiza kumvetsetsa ndi kugwiritsa ntchito choonadi chauzimu ngakhale kuti tili ndi zolepheretsa komanso ndife opanda ungwiro. Motero Yehova akhoza kunena mawu aŵa kwa ife monga ananenera kwa Aisrayeli: “Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.”—Yeremiya 31:3.

18, 19. (a) Kodi ndi m’njira iti imene Yehova amasonyezera kwambiri chikondi chake kwa ife, ndipo n’chiyani chikuonetsa kuti nkhani imeneyi amaisamalira yekha? (b) Kodi Mawu a Mulungu amatitsimikizira motani kuti Yehova amamvera anthu chisoni?

18 Mwinamwake timamva kwambiri chikondi cha Yehova pamene tigwiritsa ntchito mwayi wa pemphero. Baibulo limauza aliyense wa ife ‘kupemphera kosaleka’ kwa Mulungu. (1 Atesalonika 5:17) Iye amamvetsera. Ndipotu amatchedwa kuti “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Udindo umenewu sanaupereke kwa wina aliyense, ngakhale kwa Mwana wake. Talingalirani izi: Mlengi wa chilengedwe chonse amatilimbikitsa kulankhula naye  momasuka m’pemphero. Ndipo kodi iye ndi womvetsera wotani? Wopanda nsangala, wosasamala za ena, kapena wopanda chifundo? Ayi sali choncho.

19 Yehova amamvera anthu chisoni. Kodi kumvera munthu chisoni n’kutani? Mkristu wina wokalamba ndiponso wokhulupirika anati: “Kumvera munthu chisoni ndiko kumva ululu wake mumtima mwanga.” Kodi ululu umene ife timamva umamukhudzadi Yehova? Timaŵerenga mawu aŵa onena za kuvutika kwa anthu ake Aisrayeli: “M’mazunzo awo onse Iye anazunzidwa.” (Yesaya 63:9) Yehova sanangoona anthuwo akuvutika; anawamvera chisoni. Timazindikira kuti Yehova amamva chisoni kwambiri m’mawu aŵa amene anauza atumiki ake: “Iye wokhudza inu akukhudza mwana wa m’diso langa.” * (Zekariya 2:8, NW) Zimenezi n’zopwetekatu kwambiri! Inde, Yehova amatimvera chisoni. Pamene tikumva kupweteka, iyenso amamva kupweteka.

20. Kodi tiyenera kupeŵa kulingalira kosayenera kotani kuti timvere uphungu womwe uli pa Aroma 12:3?

20 Palibe Mkristu aliyense wolingalira bwino yemwe angakhale wodzikuza kapena wodzitukumula chifukwa cha umboni umenewu wosonyeza kuti Mulungu amakonda atumiki ake ndipo amawaona kukhala ofunika kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.” (Aroma 12:3) Baibulo lina limati pa lembali: “Ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese akulu koposa mmene mulili.” (Chipangano Chatsopano) Motero pamene tikusangalala ndi chikondi cha Atate wathu wakumwamba, tiyeni tiziganiza bwino ndi kumakumbuka kuti sitikondedwa ndi Mulungu monga ngati ndi mphoto kapena malipiro a zochita zathu.—Luka 17:10.

21. Kodi ndi mabodza a Satana otani amene tifunika kuwakana nthaŵi zonse, ndipo kodi tingapitirize kukhazikitsa mitima yathu pa choonadi cha m’Baibulo chiti?

 21 Tiyeni tonse tichitetu zonse zimene tingathe kuti tikane mabodza a Satana, kuphatikizapo bodza lakuti ndife achabechabe kapenanso kuti palibe amene angatikonde. Ngati zimene zakhala zikukuchitikirani zakuphunzitsani kuti muzidziona monga chokhumudwitsa chovutitsa kwambiri choti sichingathe ngakhale n’chikondi chosefukira cha Mulungu, kapena kuti ntchito zanu zabwino n’zosanunkha kanthu m’pang’ono pomwe moti maso ake omwe amaona chilichonse sangazione, kapena kuti machimo anu ndi ochuluka kwambiri moti imfa ya Mwana wake wokondedwayo singathe kuwaphimba, ndiye kuti mwaphunzitsidwa bodza. Kanani mabodza oterowo ndi mtima wanu wonse! Tiyeni tipitirize kukhazikitsa mitima yathu pa choonadi chimene chili m’mawu ouziridwa a Paulo akuti: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 8:38, 39.

^ ndime 6 Mobwerezabwereza Baibulo limagwirizanitsa chiyembekezo cha chiukiriro ndi kukumbukira zinthu kwa Yehova. Munthu wokhulupirikayo Yobu anauza Yehova kuti: ‘Ha! . . . Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira.’ (Yobu 14:13) Yesu anatchula za chiukiriro cha “onse amene ali m’manda achikumbukiro.” Izi zinali zoyenera chifukwa Yehova amawakumbukira bwino kwambiri akufa amene akufuna kudzawaukitsa.—Yohane 5:28, 29, NW.

^ ndime 19 Palembali mabaibulo ena amasonyeza kuti munthu amene akukhudza anthu a Mulungu ndiye kuti munthuyo amadzikhudza yekha m’diso lake kapena la Israyeli, osati la Mulungu. Kulakwitsa kumeneku anakuyambitsa ndi alembi ena amene anali kuona kuti ndimeyi ndi yosayenerera ndipo anaikonza. Zoyesayesa zawo zophonyazo zinabisa mmene Yehova alili wachifundo kwambiri.