Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 30

“Yendani M’chikondi”

“Yendani M’chikondi”

1-3. Kodi chimachitika n’chiyani tikatengera chitsanzo cha Yehova chokhala achikondi?

“KUPATSA kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mawu a Yesu ameneŵa amaphera mphongo mfundo iyi ya choonadi chofunika zedi: Chikondi chopanda dyera chimapindulitsa. Ngakhale kuti kulandira chikondi kumasangalatsa, timakhala achimwemwe kwambiri popatsa, kapena posonyeza, ena chikondicho.

2 Atate wathu wakumwamba amazidziŵa bwino kwambiri zimenezi kuposa wina aliyense. Monga taonera m’mitu yapitayi ya chigawo chino, Yehova ndiye chitsanzo chapamwamba kwambiri cha chikondi. Palibe amene wasonyezapo chikondi m’njira zikuluzikulu kapenanso kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene iye wachitira. N’zosadabwitsa kuti Yehova akutchedwa “Mulungu wachimwemwe”!—1 Timoteo 1:11, NW.

3 Mulungu wathu wachikondi amafuna titayesetsa kukhala ngati iye, makamaka pankhani yokhala achikondi. Aefeso 5:1, 2 amatiuza kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.” Pamene titengera chitsanzo cha Yehova chokhala achikondi, timakhala achimwemwe kwambiri chimene chimabwera ndi kupatsa. Timakhalanso okondwa podziŵa kuti tikukondweretsa Yehova, chifukwa Mawu ake amatilangiza kuti tiyenera “kukondana.” (Aroma 13:8) Komabe palinso zifukwa zina zimene tiyenera ‘kuyendera m’chikondi.’

Chifukwa Chake Chikondi N’chofunika Kwambiri

4, 5. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuti tizikonda okhulupirira anzathu ndi chikondi chodzimana?

4 Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti tizikonda okhulupirira anzathu? Mwachidule, chikondi ndicho Chikristu choona. Popanda chikondi sitingagwirizane kwambiri ndi Akristu anzathu, ndipo, kuposa pamenepo, tingakhale opanda phindu  kwa Yehova. Taonani zimene Mawu a Mulungu amanena pa mfundo za choonadi zimenezi.

5 Usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) “Monga ndakonda inu”—inde, tikulamulidwa kukhala ndi chikondi chonga chimene Yesu anali nacho. Taona m’Mutu 29 kuti Yesu anapereka chitsanzo chapamwamba cha kukhala ndi chikondi chodzimana; kusamalira choyamba zimene ena akusoŵeka ndiponso zofuna zawo. Ifenso tifunika kukhala ndi chikondi chopanda dyera, ndipo tiyenera kuchisonyeza mooneka bwino moti ngakhale anthu amene sali mu mpingo wachikristu azitha kuona chikondi chathucho. Ndithudi, chikondi chodzimana cha paabale ndicho chizindikiro chimene timadziŵika nacho monga otsatira oona a Kristu.

6, 7. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti Mawu a Yehova amanena motsindika kwambiri za kufunika kwa chikondi? (b) Kodi mawu a Paulo olembedwa pa 1 Akorinto 13:4-8 amanena za mbali iti ya chikondi?

6 Bwanji nanga titakhala kuti tilibe chikondi? Mtumwi Paulo anati, ngati “ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.” (1 Akorinto 13:1, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Chinganga chosokosera chimachita phokoso kwambiri. Nanga bwanji chitsulo chongolira? Mabaibulo ena pamenepa amati “belu laphokoso” kapena “belu lolira kwambiri.” Zimenezi ndi zitsanzo zoyenerera kwambiri. Munthu wopanda chikondi amafanana ndi chida choimbira chimene chimasokosera ndipo sichisangalatsa m’malo moti chizikondweretsa. Kodi munthu wotereyu angasangalale bwanji ndi anthu ena? Paulo anatinso: “Ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.” (1 Akorinto 13:2) Tangoganizirani, munthu wopanda chikondi ndi munthu ‘wachabechabe,’ ngakhale angachite ntchito zotani! Kodi sizikuonekeratu kuti Mawu a Yehova amati kukhala achikondi n’kofunika zedi?

 7 Komabe, kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife achikondi pa zochita zathu ndi ena? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tipende mawu a Paulo opezeka pa 1 Akorinto 13:4-8. Mavesiŵa sakunena za mmene Mulungu amatikondera kapenanso mmene timakondera Mulungu. M’malo mwake, Paulo anali kunena za mmene tiyenera kusonyezerana chikondi. Anafotokoza zinthu zina zimene chikondi chimachita ndiponso zina zimene sichichita.

Zimene Chikondi Chimachita

8. Kodi kuleza mtima kungatithandize motani pochita zinthu ndi ena?

8 “Chikondi chikhala chilezere.” Kukhala woleza kumatanthauza kulolerana ndi ena moleza mtima. (Akolose 3:13) Timafunikadi kuleza mtima kotereku, kodi sichoncho? Popeza ndife opanda ungwiro ndiponso tikutumikira pamodzi, si kulakwa kuganizira kuti nthaŵi zina abale athu achikristu adzatikwiyitsa, ndiponso kuti nafenso tikhoza kuwakwiyitsa. Koma kuleza mtima  ndi kudziletsa kungatithandize kupirira zokhumudwitsa zazing’ono zimene zimakhalapo tikamachita zinthu ndi ena—popanda kusokoneza mtendere wa mpingo.

9. Kodi tingakhale okoma mtima kwa ena m’njira zotani?

9 “Chikondi . . . chili chokoma mtima.” Timasonyeza kuti ndife okoma mtima mwa kuchita zinthu zothandiza ndi kulankhula mawu odera nkhaŵa ena. Chikondi chimatichititsa kufunafuna njira zoti tikhale okoma mtima kwa ena, makamaka kwa amene akuvutika kwambiri. Mwachitsanzo, wokhulupirira mnzathu wokalamba angamasungulumwe ndipo angamalakalake wina atakamuchezera ndi kumulimbikitsa. Mayi yemwe akulera yekha ana kapena mlongo amene mwamuna wake ndi wachipembedzo china angafunike kumuthandiza zinthu zina. Munthu wodwala kapena amene ali ndi mavuto ena ake angafune kumva mawu abwino a bwenzi lokhulupirika. (Miyambo 12:25; 17:17) Pamene tiyamba ndife kuchitapo kanthu kuti tisonyeze kukoma mtima m’zinthu zoterozo, timaonetsa kuti chikondi chathu n’choona.—2 Akorinto 8:8.

10. Kodi chikondi chimatithandiza motani kuchirikiza ndi kulankhula choonadi ngakhale pamene kuli kovuta kuchita zimenezi?

10 “Chikondi . . . chikondwera ndi choonadi.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . chimakondwera ndi kukhalira kumbuyo choonadi.” Chikondi chimatichititsa kuchirikiza choonadi ndi ‘kunena choonadi yense ndi mnzake.’ (Zekariya 8:16) Mwachitsanzo, ngati munthu yemwe timamukonda wachita tchimo lalikulu, kukonda Yehova—ndiponso wolakwayo—kudzatithandiza kumamatira miyezo ya Mulungu m’malo moyesa kubisa tchimolo, kapena kupeza zifukwa zolichepetsera, kapenanso ngakhale kunena zabodza za tchimolo. N’zoona kuti kungakhale kovuta kuvomereza zimene zachitikazo. Koma ngati timamufunira zabwino munthu yemwe timamukondayo, tidzafuna kuti alandire ndi kulabadira chilango chachikondi cha Mulungu. (Miyambo 3:11, 12) Pokhala Akristu achikondi, timafunanso “kukhala nawo makhalidwe abwino [mu zinthu zonse, NW].”—Ahebri 13:18.

11. Popeza kuti chikondi ‘chimakwirira zinthu zonse,’ kodi tiyenera kuyesetsa kuchitanji ndi zolephera za okhulupirira anzathu?

11 “Chikondi . . . chikwirira zinthu zonse.” Lemba la 1 Petro 4:8  limati: “Chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” Inde, Mkristu amene amachita zinthu mwachikondi salakalaka kuti azikamba za zonse zimene abale ake achikristu amaphonya kapenanso amalephera kuchita. Nthaŵi zambiri, zolakwa za okhulupirira anzathu zimakhala zazing’ono moti tikhoza kuzikwirira ndi chikondi.—Miyambo 10:12; 17:9.

Chikondi chimatichititsa kukhala ndi chidaliro mwa abale athu

 

12. Kodi mtumwi Paulo anaonetsa motani kuti anali kukhulupirira kuti Filemoni achita zabwino kwambiri, nanga chitsanzo cha Paulo chingatiphunzitse chiyani?

12 “Chikondi . . . chikhulupirira zinthu zonse.” Baibulo limene anatembenuza Moffatt limati chikondi chimakhala “chofunitsitsa nthaŵi zonse kukhulupirira zabwino kwambiri.” Okhulupirira anzathu sitiwakayikira mosayenera, kukayikira zolinga zawo pa chilichonse chimene akuchita. Chikondi chimatithandiza kudalira abale athu ndi kukhulupirira kuti amachita “zabwino kwambiri.” * Taonani chitsanzo ichi mu kalata imene Paulo analembera Filemoni. Paulo analemba kalatayi kuti alimbikitse Filemoni kuti amulandire bwino kapolo wake Onesimo amene anathaŵa, yemwe tsopano anali Mkristu. M’malo mokakamiza Filemoni, Paulo anamuchonderera mwachikondi. Anali n’chidaliro chakuti Filemoni adzachita zoyenera. Anati: “Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziŵa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.” (Vesi 21) Pamene tikhulupirira abale athu moteremu chifukwa chowakonda, timawathandiza kuchita zinthu zabwino kwambiri.

13. Kodi tingaonetse motani kuti timayembekezera zabwino kwa abale athu?

13 “Chikondi . . . chiyembekeza zinthu zonse.” Monga mmene munthu wachikondi amakhulupirira ena, amayembekezeranso zabwino. Chikondi chimatichititsa kuyembekezera zabwino kwa abale athu. Mwachitsanzo, ngati mbale “agwidwa nako kulakwa kwakuti,” timayembekezera kuti adzalabadira zoyesayesa zachikondi zofuna kumubweza. (Agalatiya 6:1) Timayembekezeranso kuti amene ali ndi chikhulupiriro chofooka adzakhalanso olimba. Timaleza mtima ndi anthu otero, ndipo timachita zimene  tingathe kuti tiwathandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 15:1; 1 Atesalonika 5:14) Ngakhale pamene wokondedwa wathu waloŵerera, sitileka kuyembekezera kuti tsiku lina adzakumbukira mu mtima mwake ndi kubwereranso kwa Yehova, mofanana ndi mwana woloŵerera wa m’fanizo la Yesu.—Luka 15:17, 18.

14. Kodi kupirira kwathu kungayesedwe m’njira zotani mu mpingo, nanga chikondi chidzatithandiza kuchita motani?

14 “Chikondi . . . chipirira zinthu zonse.” Kupirira kumatithandiza kuimabe nji pamene ena atikhumudwitsa kapenanso pamene takumana ndi mavuto. Sikuti ziyeso za kupirira zimachokera kunja kwa mpingo kokha. Nthaŵi zina tingayesedwe ndi anzathu a mu mpingo momwemo. Chifukwa cha kupanda ungwiro, nthaŵi zina abale athu akhoza kutikhumudwitsa. Kulankhula kosalingalira bwino kukhoza kutipweteka mumtima. (Miyambo 12:18) Mwinamwake nkhani ina mu mpingo sinasamaliridwe monga mmene ife tinali kuganizira. Zochita za mbale wina amene anthu amamupatsa ulemu zikhoza kukhala zokhumudwitsa, moti tingamaganize kuti, ‘Kodi Mkristu angachite bwanji zoterezi?’ Pamene tiona zinthu zimenezi, kodi tidzachoka mu mpingo ndi kusiya kutumikira Yehova? Sitidzatero ngati tili ndi chikondi. Inde, chikondi chimatithandiza kuti zophonya za mbale zisatitseke m’maso n’kumalephera kuona zabwino zimene iye amachita kapenanso zabwino zimene zili mu mpingo. Chikondi chimatithandiza kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ndi kuchirikiza mpingo mosasamala kanthu za zimene munthu wina wopanda ungwiro anganene kapena kuchita.—Salmo 119:165.

Zimene Chikondi Sichichita

15. Kodi kaduka n’chiyani, nanga chikondi chimatithandiza motani kupeŵa malingaliro owononga ameneŵa?

15 “Chikondi sichidukidwa.” Ngati tili n’kaduka tingamachite nsanje ndi zimene ena ali nazo, kaya ndi katundu wawo, maudindo awo, kapenanso maluso awo. Nsanje yoteroyo ndiwo malingaliro adyera ndi owononga amene, ngati atati asatetezedwe, angasokoneze mtendere wa mpingo. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupeŵa ‘kukhumbitsa kuchita nsanje’? (Yakobo 4:5) Chikondi. Khalidwe labwino limeneli lingatithandize  kukondwera nawo limodzi amene akuoneka kuti ali ndi zinthu zina zabwino zomwe ife tilibe. (Aroma 12:15) Chikondi chimatithandiza kuti tisaone ngati kuti ifeyo tikunyozedwa pamene winawake watamandidwa chifukwa cha luso lapadera limene ali nalo kapena chifukwa cha zimene wachita bwino kwambiri.

16. Ngati abale athu timawakondadi, n’chifukwa chiyani tidzapeŵa kudzitamanda chifukwa cha zimene tikuchita mu utumiki wa Yehova?

16 “Chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” Chikondi chimatiletsa kuonetsera maluso athu kapena zimene tachita n’cholinga choti ena asirire. Ngati abale athu timawakondadi, kodi tingamadzitamande nthaŵi zonse ndi zimene tachita mu utumiki kapena chifukwa cha maudindo athu mu mpingo? Kudzitama koteroko kungalefule ena, ndi kuwachititsa kudziona kuti ndi opanda pake poyerekezera ndi ena. Chikondi chimatiletsa kudzitamanda chifukwa cha zimene Mulungu amatipatsa kuti tichite mu utumiki wake. (1 Akorinto 3:5-9) Ndiponso, chikondi “sichidzikuza,” kapena malinga n’kunena kwa Baibulo lina, “sichisangalala ndi maganizo okokomeza amene paokha amaoneka ofunika.” Chikondi chimatiteteza kuti tisadzione monga apamwamba kwambiri.—Aroma 12:3.

17. Kodi chikondi chimatichititsa kulingalira ena motani, ndipo ndi zinthu zotani zimene tidzapewa kuchita?

17 “Chikondi . . . sichichita zosayenera.” Munthu amene amachita zosayenera amachita zinthu m’njira yolakwika kwambiri kapena yokhumudwitsa ena. Kuchita zinthu motero ndi kupanda chikondi, chifukwa kumasonyeza kuti munthuyo amanyalanyaza kwabasi maganizo a anthu ena limodzi ndi ubwino wawo. Koma timakhala okoma mtima pamene tilingalira ena mwachikondi. Chikondi chimatichititsa kukhala ndi makhalidwe abwino, kuchita zinthu zimene Mulungu amavomereza, ndiponso kulemekeza okhulupirira anzathu. Motero sitidzachita zonyansa ngati tili ndi chikondi—inde, sitidzakhala ndi khalidwe lililonse limene lingadabwitse kapena kukhumudwitsa abale athu achikristu.—Aefeso 5:3, 4.

18. N’chifukwa chiyani munthu wachikondi salamula kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira?

18 “Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha.” Baibulo lina limati: “Chikondi sichiumirira njira yakeyake.” Munthu wachikondi salamula  kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira, ndiye ngati kuti malingaliro ake ndiwo amakhala olondola nthaŵi zonse. Sanyengerera ena pogwiritsa ntchito luso lake lokopa ena kuti afoole amene ali ndi malingaliro osiyana ndi ake. Liuma lotero limaonetsa kuti munthuyo ndi wonyada, ndipo Baibulo limati: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka.” (Miyambo 16:18) Ngati abale athu timawakondadi, tidzalemekeza malingaliro awo, ndipo pamene kuli koyenera, tidzavomereza mofunitsitsa zonena zawo. Kukhala ndi mtima wovomereza zinthu moteromo n’kogwirizana ndi mawu a Paulo akuti: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”—1 Akorinto 10:24.

19. Kodi chikondi chimatithandiza kuchita motani ena akatilakwira?

19 “Chikondi . . . sichipsa mtima, sichilingirira zoipa.” Munthu wachikondi sapsa mtima msanga ndi zimene ena amanena kapena kuchita. N’zoona kuti n’chibadwa kukhumudwa ena akatilakwira. Koma ngakhale titakwiya pazifukwa zomveka, chikondi chimatiletsa kumangokhalabe opsa mtima. (Aefeso 4:26, 27) Sitilemba mawu oŵaŵa kapena zochita zopweteka, monga ngati tikulemba ndalama m’buku loŵerengetseramo ndalama kuti tisaziiwale. M’malo mwake, chikondi chimatichititsa kutsanzira Mulungu wathu wachikondi. Monga taonera m’Mutu 26, Yehova amatikhululukira pakakhala zifukwa zomveka zotikhululukirira. Pamene wakhululuka, amaiwala, ndiko kuti, panthaŵi ina m’tsogolo sationanso kuti ndife ochimwa ndi machimo omwe anatikhululukirawo. Timayamikiratu kwambiri kuti Yehova salingalira zoipa!

20. Kodi tiyenera kutani ngati wokhulupirira mnzathu wakodwa ndi zolakwa n’kuvutika pambuyo pake?

20 “Chikondi . . . sichikondwera ndi chinyengo.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . sichinyadira machimo a anthu ena.” Baibulo limene anatembenuza Moffatt limati: “Chikondi sichikondwera ena akalakwa.” Chikondi sichikondwera ndi zinthu zosalungama, motero khalidwe lonyansa lililonse timaliona kukhala loipa kwambiri. Kodi timatani wokhulupirira mnzathu akagwa m’tchimo ndiyeno n’kuvutika? Chikondi chimatiletsa kusangalala, monga ngati kunena kuti ‘Zakhala bwino! Anafunika kuona zimenezi.’ (Miyambo 17:5) Komabe timasangalala  pamene mbale yemwe wachita cholakwa akuyesa kuchita zabwino kuti akhalenso ndi moyo wauzimu wabwino.

“Njira Yokoma Yoposatu”

21-23. (a) Kodi Paulo anatanthauzanji ponena kuti “chikondi sichitha nthaŵi zonse?” (b) N’chiyani chimene tikambirane m’mutu wotsiriza?

21 “Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” Kodi Paulo anatanthauzanji ndi mawu amenewo? Malinga ndi nkhani imene anali kukamba, anali kulongosola mphatso za mzimu zimene Akristu oyambirira anali nazo. Mphatso zimenezo zinali zizindikiro zakuti Mulungu anali kuyanja mpingo wopangidwa chatsopanowo. Koma si Akristu onse amene anali kuchiritsa, kunenera, kapena kulankhula m’malilime. Komabe zimenezi zinalibe kanthu, chifukwa mphatso zochita zozizwitsa m’kupita kwanthaŵi zinali kudzatha. Koma panali kudzatsala chinachake chimene Mkristu aliyense akanayesetsa kukhala nacho. Chinali chapadera  kwambiri ndiponso chokhalitsa zedi kuposa mphatso iliyonse yochita zozizwitsa. Ndipotu Paulo anachitcha kuti “njira yokoma yoposatu.” (1 Akorinto 12:31) Kodi “njira yokoma yoposatu” imeneyi inali iti? Inali njira yachikondi.

Anthu a Yehova amadziŵika ndi kukondana

22 Indedi, chikondi chachikristu chimene Paulo anafotokoza “sichitha nthaŵi zonse,” ndiko kuti, sichidzatha mpaka kalekale. Mpaka lerolino, otsatira oona a Yesu akudziŵika ndi chikondi chodzimana pa abale awo. Umboni wa chikondi choterocho umaoneka bwino m’mipingo ya olambira a Yehova padziko lonse lapansi. Chikondi chimenecho sichidzatha, chifukwa Yehova akulonjeza kupatsa atumiki ake okhulupirika moyo wosatha. (Salmo 37:9-11, 29) Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tipitirize ‘kuyenda m’chikondi.’ Mwa kuchita zimenezi, tingakhale n’chimwemwe chimene chimabwera chifukwa cha kupatsa. Kuposa pamenepo, tingapitirize kukhalabe ndi moyo—inde, tingapitirize kukhala achikondi—kwa umuyaya wonse potsanzira Mulungu wathu wachikondi Yehova.

23 M’mutu uno womaliza wa chigawo chonena za chikondi, tafotokoza mmene tingakondere ena. Koma polingalira kuti timapindula m’njira zochuluka ndi chikondi cha Yehova—ndiponso ndi mphamvu zake, chilungamo chake, komanso nzeru zake—ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova ndingamusonyeze bwanji kuti ndimamukondadi?’ Tikambirana funso limeneli m’mutu wathu wotsiriza.

^ ndime 12 Inde, sikuti chikondi chachikristu chimanyengeka mosavuta. Baibulo limatichenjeza kuti: “Yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa . . . ndipo potolokani pa iwo.”—Aroma 16:17.