Pa makhalidwe onse a Yehova, khalidwe lake lalikulu kwambiri ndi chikondi. Ndilonso khalidwe lokondweretsa kwambiri. Pamene tikuphunzira mbali zina zosangalatsa za khalidwe lochititsa kaso limeneli, tiona chifukwa chake Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.