Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

Zimene Mungachite Kuti Mupindule ndi Kabukuka

Zimene Mungachite Kuti Mupindule ndi Kabukuka

Kabuku kano kakuthandizani kuti muzisangalala mukamaphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo. Kumapeto kwa ndime iliyonse kuli malemba a m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa yankho la funso limene lalembedwa ndi mawu akuda kwambiri lomwe lili pamwamba pa ndimeyo.

Pamene mukuwerenga malemba a m’Baibulo, ganizirani mmene malembawo akuyankhira mafunsowo. Aliyense wa Mboni za Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kumvetsa bwino Malembawo. Werengani Luka 24:32, 45.

Dziwani izi: Mabuku omwe atchulidwa m’kabuku kano ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Onaninso

PHUNZIRO LA BAIBULO

Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?

A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi amadziwika bwino chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa anthu Baibulo kwaulere. Onani mmene amaphunzitsira.