Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 5

Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?

Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?

1. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi?

Yehova analenga dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. Choncho anthufe kwathu ndi padzikoli. Cholinga cha Mulungu polenga anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, sichinali chakuti iwo akakhale kumwamba, chifukwa iye anali atalenga kale angelo n’kuwaika kumwambako. (Yobu 38:4, 7) M’malomwake, Mulungu anaika munthu woyambirirayo m’paradaiso wokongola kwambiri, wotchedwa munda wa Edeni. (Genesis 2:15-17) Cholinga cha Yehova chinali chakuti munthuyo, pamodzi ndi ana amene akanabereka, akhale ndi moyo wosatha padziko lapansili.​—Werengani Salimo 37:29; 115:16.

Poyamba, munda wa Edeni wokha ndi womwe unali paradaiso. Koma Mulungu ankafuna kuti banja loyambiriralo libereke ana, n’kuchuluka padziko lonse lapansi. M’kupita kwa nthawi, iwo akanadzaza dziko lonse lapansi, ndipo dziko lonseli likanakhala paradaiso. (Genesis 1:28) Choncho dziko lapansili silidzawonongedwa, ndipo anthu adzapitiriza kukhalamo.​—Werengani Salimo 104:5.

2. N’chifukwa chiyani dziko lapansili silili paradaiso panopa?

Adamu ndi Hava sanamvere Yehova Mulungu, ndipo iye anawatulutsa m’munda wa Edeni. Chifukwa cha zimenezi, iwo anataya mwayi wokhala m’paradaiso, ndipo palibe munthu amene angakwanitse kubweretsanso paradaiso. Baibulo limati: “Dziko lapansi laperekedwa m’manja mwa woipa.”—Yobu 9:24.​—Werengani Genesis 3:23, 24.

Kodi Yehova wasintha cholinga chimene analengera anthu? Ayi, sanasinthe. Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo sangalephere kuchita zimene akufuna. (Yesaya 45:18) Yehova adzathandiza anthu kuti akhale ndi moyo wosatha komanso wosangalala ngati mmene iyeyo anafunira poyamba.​—Werengani Salimo 37:11, 34.

3. Kodi chidzachitike n’chiyani kuti dzikoli likhalenso Paradaiso?

Yesu Khristu akulamulira monga Mfumu yoikidwa ndi Mulungu ndipo posachedwapa dzikoli likhalanso paradaiso. Pa  nkhondo yotchedwa Aramagedo, Yesu adzatsogolera angelo a Mulungu powononga onse amene amatsutsana ndi Mulungu. Kenako Yesu adzatsekera Satana m’ndende kwa zaka 1,000. Oipa akamadzawonongedwa, anthu a Mulungu adzapulumuka chifukwa Yesu adzawatsogolera ndiponso kuwateteza. Iwo adzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.​—Werengani Chivumbulutso 20:1-3; 21:3, 4.

4. Kodi mavuto a anthu adzatha liti?

Kodi Mulungu adzathetsa liti mavuto onse padziko lapansili? Yesu anapereka “chizindikiro” chimene chidzasonyeze kuti mapeto a dzikoli atsala pang’ono kufika. Zinthu zimene zikuchitika padzikoli masiku ano n’zoopsa kwambiri ndipo zikuika moyo wa anthu pangozi. Koma zonsezi zikungosonyeza kuti tsopano tikukhala m’nyengo ya “mapeto a nthawi ino.”​—Werengani Mateyu 24:3, 7-14, 21, 22.

Yesu adzathetsa mavuto onse mu ulamuliro wake wa zaka 1,000 pamene azidzalamulira dziko lapansili ali kumwamba. (Yesaya 9:6, 7; 11:9) Kuwonjezera pa udindo wake monga Mfumu, Yesu adzatumikiranso monga Mkulu wa Ansembe ndipo adzafafaniza machimo a anthu omwe amakonda Mulungu. Choncho kudzera mwa Yesu, Mulungu adzathetsa matenda, ukalamba ndiponso imfa.​—Werengani Yesaya 25:8; 33:24.

5. Kodi ndani amene adzakhale m’Paradaiso m’tsogolo muno?

Mukapita ku Nyumba ya Ufumu, mukapeza anthu amene amakonda Mulungu komanso amene amafunitsitsa kuphunzira zimene angachite kuti azimukondweretsa

Anthu omvera Mulungu ndi omwe adzakhale m’Paradaiso. (1 Yohane 2:17) Yesu anatumiza otsatira ake kuti akafufuze anthu ofatsa ndi kuwaphunzitsa zimene angachite kuti Mulungu aziwakonda. Masiku ano, Yehova akuthandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti adzakhale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) Ku Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, anthu amaphunzira zimene angachite kuti akhale amuna ndi abambo abwino, kapenanso kuti akhale akazi ndi amayi abwino. Ana ndi makolo amalambira Mulungu pamodzi ndipo amaphunzira zimene angachite kuti apeze madalitso chifukwa cha uthenga wabwino.​—Werengani Mika 4:1-4.