Paulo anayenda maulendo apanyanja ndi pamtunda popita kukalalikira

PAULO atakhala Mkhristu, ankalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Chifukwa cha ntchito imeneyi, Paulo amene kale ankazunza Akhristu, nayenso anayamba kuzunzidwa kwambiri. Mtumwi wakhama ameneyu anayenda maulendo ambirimbiri opita kukalalikira ndipo anapita m’madera a kutali kukafalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, umene udzakwaniritsa cholinga choyambirira cha Mulungu chokhudza anthu.

Pa ulendo wake woyamba wokalalikira, Paulo anafika mumzinda wa Lusitara ndipo anachiritsa munthu amene anabadwa ali wolumala. Khamu la anthu linayamba kufuula kuti Paulo ndi Baranaba, mnzake amene ankayenda naye, ndi milungu. Amuna awiriwa anayesetsa kuletsa anthu amene ankafuna kupereka nsembe kwa iwo kuti asachite zimenezo. Kenako molimbikitsidwa ndi adani a Paulo, khamu la anthu lomwelo linamuponya miyala ndipo anamusiya poganiza kuti wafa. Paulo anapulumuka chiwembucho ndipo patapita nthawi anabwerera kumzinda womwewo kukalimbikitsa ophunzira a kumeneko.

Akhristu ena achiyuda ankanena kuti Akhristu amene sanali Ayuda ayenera kumatsatira mfundo zina za m’Chilamulo cha Mose. Choncho, Paulo anapita kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu kukawauza nkhani imeneyi. Atumwi ndi akuluwo ataona bwino nkhaniyi pogwiritsa ntchito Malemba komanso motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, analemba makalata kumipingo ndipo anawauza kuti azipewa kulambira mafano, kudya magazi komanso nyama yosakhetsa magazi ndiponso azipewa dama. N’zoona kuti malamulo amenewa anali ‘ofunika’ koma kuti munthu awatsatire, samachita kufunikira kutsatira Chilamulo cha Mose.—Machitidwe 15:28, 29.

Pa ulendo wake wachiwiri wokalalikira, Paulo anafika kumzinda wa Bereya, umene unali m’dziko limene masiku ano limatchedwa Greece. Ayuda amene ankakhala kumeneko anasangalala kwambiri ndi uthenga wake ndipo ankafufuza m’Malemba tsiku ndi tsiku kuti atsimikize zimene iye ankaphunzitsazo. Kenako Paulo anakakamizika kuchoka n’kupita ku Atene chifukwa chotsutsidwa. Iye analankhula mfundo zogwira mtima pamaso pa anthu ophunzira kwambiri a ku Atene, ndipo zimene ananena pa nthawiyi zimatipatsa chitsanzo cha mmene tingalankhulire mosamala, mozindikira komanso momveka bwino.

Atamaliza kuyenda ulendo wake wachitatu wokalalikira, Paulo anapita ku Yerusalemu. Atafika kukachisi, Ayuda ena anayambitsa chipolowe ndipo ankafuna kumupha. Koma asilikali achiroma anamutenga ndi kuyamba kumufunsa mafunso. Popeza kuti iye anali nzika ya dziko la Roma, anakaonekera pamaso pa bwanamkubwa wachiroma dzina lake Felike. Komabe, Ayuda analibe umboni wokwanira pa milandu imene ankamuneneza. Patapita nthawi, iye anakaonekera pamaso pa bwanamkubwa wina wachiroma dzina lake Fesito. Kumeneko Paulo anakana kuti akaweruzidwe ndi Ayuda ndipo anati: “Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!” Ndipo Fesito anamuyankha kuti: “Udzapitadi kwa Kaisara.”—Machitidwe 25:11, 12.

Kenako Paulo anapita naye ku Italiya pa ngalawa kuti akaweruzidwe. Pa ulendowu ngalawa yawo inasweka ndipo anaima pachilumba cha Melita poyembekezera kuti nyengo yachisanu ithe. Atafika ku Roma, anakhala zaka ziwiri m’nyumba ya lenti. Ngakhale kuti asilikali ankamulondera, mtumwi wachangu ameneyu, anapitiriza kulalikira za Ufumu wa Mulungu kwa anthu onse amene ankabwera kudzamuona.

—Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 11:22–28:31.