Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

 GAWO 10

Solomo Anali Mfumu Yanzeru

Solomo Anali Mfumu Yanzeru

Yehova anapatsa Mfumu Solomo mtima wanzeru, ndipo pa nthawi yonse imene ankalamulira, Aisiraeli anali pamtendere waukulu ndipo zinthu zinkawayendera bwino

KODI moyo ungakhale wotani ngati anthu m’dziko lonse komanso wolamulira dzikolo atamatsatira Yehova monga Wolamulira wawo wamkulu ndiponso kumvera malamulo ake? Zimene zinachitika mu ulamuliro wa zaka 40 wa Mfumu Solomo zingatithandize kuyankha funso limeneli.

Davide asanamwalire, anasankha mwana wake Solomo kuti alowe m’malo mwake monga mfumu. Ndiyeno m’maloto, Mulungu anauza Solomo kuti amupemphe chilichonse chimene angafune. Choncho Solomo anapempha kuti amupatse nzeru komanso kuti akhale wozindikira kuti azitha kuweruza anthu mwachilungamo komanso mwanzeru. Yehova anasangalala kwambiri ndipo anam’patsadi mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu. Komanso Yehova anamulonjeza kuti akapitiriza kukhala womvera, adzam’patsa chuma, ulemerero ndiponso moyo wautali.

Solomo anatchuka kwambiri chifukwa chakuti ankaweruza milandu mwanzeru. Mwachitsanzo, azimayi awiri ankakanganirana mwana wamwamuna moti aliyense ankanena kuti mwanayo ndi wake. Choncho Solomo analamula kuti mwanayo adulidwe pakati kuti mayi aliyense atenge mbali imodzi. Mayi mmodzi anavomereza, koma nthawi yomweyo mayi amene anali mwini wake weniweni wa mwanayo anapempha kuti angomupereka kwa mayi winayo. Pamenepa Solomo anaona kuti mayi wachifundoyo ndiye anali mwini wake wa mwanayo ndipo anam’patsa mwana wakeyo. Posapita nthawi Aisiraeli onse anamva za chiweruzo chimenechi, ndipo anthu anazindikira kuti nzeru zimene Solomo anali nazo zinali zochokera kwa Mulungu.

Chimodzi mwa zinthu zazikuluzikulu zimene Solomo anachita chinali kumanga kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Kachisi ameneyu anali malo ofunika kwambiri olambiriramo Mulungu m’dziko lonse la Isiraeli. Potsegulira kachisiyo, Solomo anapemphera kuti: “Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko. Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?”—1 Mafumu 8:27.

Solomo anatchuka ngakhale m’madera akutali monga ku Sheba, m’dziko la Arabia. Mfumukazi ya ku Sheba inabwera kudzaona ulemerero ndi chuma cha Solomo komanso kudzamuyesa kuti ione kuchuluka kwa nzeru zakezo. Mfumukaziyo inagoma ndi nzeru za Solomo komanso kutukuka kwa dziko la Isiraeli moti inatamanda Yehova chifukwa anapereka ufumu kwa munthu wanzeru zotero. Zoonadi, Yehova anadalitsa Solomo ndipo chifukwa cha zimenezi, ulamuliro wake unali wotchuka kwambiri ndiponso wamtendere kuposa maulamuliro onse amene anakhalapo mu Isiraeli.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti Solomo sanapitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi nzeru zimene Yehova anam’patsa. Iye ananyalanyaza lamulo la Mulungu n’kukwatira akazi ambirimbiri ndipo ambiri mwa iwo ankalambira milungu yonyenga. Pang’onopang’ono akazi akewo anamukopa n’kusiya kulambira Yehova ndipo anayamba kulambira mafano. Yehova anauza Solomo kuti adzamulanda gawo lina la ufumu wake n’kulipereka kwa munthu wina. Koma Mulungu anamuuzanso kuti adzamusiyira gawo lochepa la ufumuwo chifukwa cha pangano limene anachita ndi bambo ake, Davide. Yehova anakhalabe wokhulupirika ku pangano la Ufumu limene anachita ndi Davide, ngakhale kuti Solomo anasiya kumutumikira.

—Nkhaniyi yachokera pa 1 Mafumu chaputala 1 mpaka 11, 2 Mbiri chaputala 1 mpaka 9 komanso pa Deuteronomo 17:17.