Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika

Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika
 1. “Pa chiyambi . . .”

 2. 4026 B.C.E. Adamu analengedwa

 3.  3096 B.C.E. Adamu anafa

 4.  2370 B.C.E. Chigumula chinayamba

 5.  2018 B.C.E. Abulahamu anabadwa

 6. 1943 B.C.E. Pangano la Abulahamu

 7.  1750 B.C.E. Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo

 8.  chaka cha 1613 B.C.E. chisanafike Mayesero a Yobu

 9.  1513 B.C.E. Ulendo wochoka ku Iguputo

 10.  1473 B.C.E. Aisiraeli analowa m’dziko la Kanani motsogoleredwa ndi Yoswa

 11. 1467 B.C.E. Anagonjetsa mbali yaikulu ya dziko la Kanani

 12.  1117 B.C.E. Sauli anadzozedwa kukhala mfumu

 13.  1070 B.C.E. Mulungu analonjeza Davide kuti adzam’patsa ufumu

 14. 1037 B.C.E. Solomo anakhala mfumu

 15. 1027 B.C.E. Anamaliza kumanga kachisi ku Yerusalemu

 16. cha m’ma 1020 B.C.E. Anamaliza kulemba Nyimbo ya Solomo

 17.  997 B.C.E. Ufumu wa Isiraeli unagawanika

 18.  cha m’ma 717 B.C.E. Ntchito yolemba buku la Miyambo inatha

 19.  mu 607 B.C.E. Yerusalemu anawonongedwa; Aisiraeli anapita ku ukapolo ku Babulo

 20.  539 B.C.E. Babulo anagonjetsedwa ndi Koresi

 21. 537 B.C.E. Ayuda amene anali ku ukapolo anabwerera ku Yerusalemu

 22. 455 B.C.E. Anamanganso mpanda wa Yerusalemu; kuyambika kwa masabata 69 a zaka

 23.  443 B.C.E. itadutsa Malaki anamaliza kulemba buku lake la ulosi

 24.  Yesu anabadwa cha m’ma 2 B.C.E.

 25. 29 C.E. Yesu anabatizidwa ndipo  anayamba kulalikira za Ufumu wa Mulungu

 26. 31 C.E. Yesu anasankha atumwi 12; analalikira paphiri

 27.  32 C.E. Yesu anaukitsa Lazaro

 28.  Nisan 14, 33 C.E. Yesu anapachikidwa (Mwezi wa Nisani umayamba mkatikati mwa March ndipo umathera mkatikati mwa April)

 29. Nisan 16, 33 C.E. Yesu anaukitsidwa

 30.  Sivani 6, 33 C.E. Pentekosite; kulandira mzimu woyera (Mwezi wa Sivani umayamba mkatikati mwa May ndipo umathera mkatikati mwa June)

 31. 36 C.E. Koneliyo akhala Mkhristu

 32.  cha m’ma 47-48 C.E. Ulendo woyamba wa Paulo wopita kukalalikira

 33. cha m’ma 49-52 C.E. Ulendo wachiwiri wa Paulo wopita kukalalikira

 34. cha m’ma 52-56 C.E. Ulendo wachitatu wa Paulo wopita kukalalikira

 35.  60-61 C.E. Paulo analemba makalata ali m’ndende ku Roma

 36.  chaka cha 62 C.E. chisanafike Yakobo, m’bale wake wa Yesu, analemba kalata

 37.  66 C.E. Ayuda anagalukira Aroma

 38. 70 C.E. Aroma anawononga Yerusalemu ndi kachisi

 39.  cha m’ma 96 C.E. Yohane analemba buku la Chivumbulutso

 40. cha m’ma 100 C.E. Yohane, mtumwi womalizira anamwalira