Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 3

Anthu Anapulumuka Chigumula

Anthu Anapulumuka Chigumula

Mulungu anawononga anthu oipa koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake

ANTHU atayamba kuchuluka, uchimo ndiponso makhalidwe oipa zinafalikira kwambiri padziko lapansi. Koma Inoki, yemwe anali mneneri yekhayo pa nthawiyo, anachenjeza anthu kuti tsiku lina Mulungu adzawononga anthu oipawo. Koma anthuwo anapitirizabe kuchita zinthu zoipa kwambiri. Angelo ena anagalukira Yehova ndipo anasiya malo awo amene Mulungu anawapatsa kumwamba, ndipo chifukwa cha dyera, anabwera padziko lapansi n’kuvala matupi ngati a anthu ndipo anakwatira akazi. Iwo anabereka ana achilendo otchedwa Anefili, omwe anali ziphona zankhanza kwambiri. Ana amenewa anachititsa kuti chiwawa komanso kuphana zichuluke kwambiri padziko lapansi ndipo Mulungu anamva chisoni kwambiri ataona kuti dzikoli likuwonongedwa.

Inoki atamwalira, panali munthu wina amene zochita zake zinali zosiyana ndi za anthu oipawo ndipo dzina lake anali Nowa. Iye ndi banja lake ankayesetsa kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Mulungu ataganiza kuti awononge anthu onse oipa padziko lapansi, anafuna kuti apulumutse Nowa ndi nyama zina. Choncho, Mulungu anamuuza kuti amange chingalawa chachikulu chooneka ngati bokosi. Cholinga cha Mulungu chinali chakuti Nowa ndi banja lake pamodzi ndi nyama za mitundu yosiyanasiyana, adzalowe m’chingalawacho kuti asafe, pa nthawi ya chigumula. Nowa anamvera zimene Mulungu anamuuzazo ndipo kwa zaka pafupifupi 40 kapena 50, iye anagwira ntchito yomanga chingalawa komanso anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petulo 2:5) Iye ankachenjeza anthu kuti Chigumula chikubwera, koma iwo sankalabadira. Kenako nthawi inakwana yakuti Nowa ndi banja lake pamodzi ndi nyama alowe m’chingalawacho. Atalowa, Mulungu anatseka chitseko ndipo mvula inayamba kugwa.

Mvula yoopsa inapitiriza kugwa kwa masiku 40, usana ndi usiku. Zimenezi zinachititsa kuti dziko lonse lapansi likwiririke ndi madzi ndipo anthu onse oipa anafa. Patapita miyezi ingapo, madzi anayamba kuphwera ndipo chingalawacho chinakaima paphiri linalake. Pa nthawi imene Nowa ndi banja lake ankatuluka m’chingalawacho, anali atakhalamo kwa chaka chathunthu. Posonyeza kuyamikira, Nowa anapereka nsembe kwa Yehova. Mulungu analandira nsembeyo ndipo anatsimikizira Nowa ndi banja lake kuti sadzawononganso zamoyo padziko lapansi ndi chigumula. Ndipo Yehova anaika utawaleza, monga chizindikiro cha lonjezo lotonthoza limenelo.

Patapita nthawi Chigumula chitachitika, Mulungu anapatsa anthu malamulo ena atsopano. Iye anawalola kudya nyama koma anawaletsa kudya magazi. Analamulanso anthu onse obadwa kuchokera mwa Nowa kuti afalikire padziko lonse, koma ena sanamvere. Motsogoleredwa ndi Nimurodi, anthu anagwirizana ndipo anayamba kumanga nsanja yaikulu kwambiri mumzinda wa Babele, umene kenako unadzatchedwa Babulo. Cholinga chawo chinali kutsutsana ndi lamulo la Mulungu loti afalikire padziko lonse. Koma Mulungu analepheretsa zimene anthu osamverawo ankafuna kuchita, posokoneza chinenero chawo ndi kuwapangitsa kuyamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Popeza kuti iwo sankamvana, anasiya ntchito yomangayo ndipo anamwazikana.

—Nkhaniyi yachokera pa Genesis chaputala 6 mpaka 11 ndi pa Yuda 14, 15.