Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

 GAWO 7

Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli

Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli

Yehova anabweretsa miliri m’dziko la Iguputo, ndipo Mose anatsogolera ana a Isiraeli potuluka m’dzikomo. Mulungu anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose

ANA a Isiraeli anakhala ku Iguputo kwa zaka zambiri ndipo zinthu zinkawayendera bwino ndiponso anachulukana. Komabe, Farao watsopano anayamba kulamulira dzikolo ndipo iye sankadziwa Yosefe. Farao ameneyu anali wankhanza kwambiri ndipo anasandutsa Aisiraeli kukhala akapolo komanso analamula kuti ana awo onse aamuna akhanda aziwaponya mumtsinje wa Nailo. Iye anachita zimenezi chifukwa ankaopa Aisiraeli omwe ankachuluka kwambiri. Koma mayi wina wolimba mtima anateteza mwana wake wamwamuna wakhanda pomuika mukabokosi, ndipo anakabisa kabokosiko m’mabango. Kenako mwana wamkazi wa Farao atapeza mwanayo, anam’tenga n’kumupatsa dzina lakuti Mose, ndipo anamulera m’banja lachifumu ku Iguputo komweko.

Mose atafika zaka 40, analowa m’mavuto chifukwa anayesa kuteteza kapolo wachiisiraeli amene ankazunzidwa ndi woyang’anira ntchito wa ku Iguputo. Chifukwa cha zimenezi, Mose anathawa n’kukakhala kudziko lina lakutali kwambiri. Koma Mose ali ndi zaka 80, Yehova anamuuza kuti abwerere ku Iguputo kukauza Farao kuti amasule anthu a Mulungu mu ukapolo.

Farao anakanitsitsa kwa mtu wagalu ndipo Mulungu anabweretsa miliri 10 m’dziko la Iguputo. Nthawi iliyonse imene Mose anapita kukaonekera kwa Farao kukam’pempha kuti amasule Aisiraeli, zomwe zikanamuthandiza kupewa mliri wina, Farao ankakana mwamwano kumvera Mose ndi Mulungu wake Yehova. Kenako, mliri womaliza unapha ana onse oyamba kubadwa m’dzikolo, kupatulapo ana a m’mabanja amene anapaka magazi a nkhosa pafelemu pomvera lamulo la Yehova. Mngelo wa Mulungu amene ankapha ana onse oyamba kubadwa, anapitirira nyumba zimenezi. Kenako Aisiraeli anayamba kuchita chikondwerero cha Pasika chaka ndi chaka pokumbukira kupulumutsidwa kodabwitsa kumeneku.

Mwana wa Farao wamwamuna woyamba kubadwa ataphedwa pa mliriwo, iye analamula Mose ndi ana onse a Isiraeli kuti achoke m’dziko la Iguputo. Nthawi yomweyo Mose anasonkhanitsa khamu la anthu n’kuyamba ulendo wotuluka m’dzikolo. Koma kenako Farao anasintha maganizo ndipo anayamba kuwatsatira ali ndi asilikali ndiponso magaleta ambiri. Aisiraeli atafika pamalo ena m’mbali mwa Nyanja Yofiira, ankaoneka ngati alibe kothawira. Kenako Yehova analekanitsa Nyanja Yofiira kuti Aisiraeli adutse pouma, pakati pa makoma awiri a madzi. Koma nawonso Aiguputo atalowa m’nyanjayo potsatira Aisiraeli, Mulungu anachititsa kuti madzi aja abwerere ngati mmene analili poyamba ndipo Farao pamodzi ndi asilikali ake anamira.

Kenako Aisiraeli anasonkhana m’mbali mwa phiri la Sinai ndipo Yehova anachita nawo pangano. Kudzera mwa Mose, Mulungu anapereka malamulo kwa Aisiraeli kuti aziwatsogolera komanso kuwateteza pa moyo wawo watsiku ndi tsiku. Ngati Aisiraeli akanapitiriza kuvomereza mokhulupirika ulamuliro wa Yehova Mulungu, iye akanapitiriza kukhala nawo ndiponso akanadalitsa anthu ena kudzera mumtunduwo.

Komabe, Aisiraeli ambiri anakhumudwitsa Mulungu chifukwa chosamukhulupirira. Motero, Yehova anachititsa kuti anthu a m’badwo umenewo azingoyenda m’chipululu mpaka zaka 40. Ndiyeno Mose anasankha Yoswa, yemwe anali wolungama, kuti apitirize kutsogolera Aisiraeli. Kenako nthawi inakwana yakuti Aisiraeli alowe m’dziko limene Mulungu analonjeza Abulahamu.

—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Ekisodo, Levitiko, Numeri, Deuteronomo komanso pa Salimo 136:10-15 ndi pa Machitidwe 7:17-36.