Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 11

Nyimbo Zouziridwa Zomwe Ndi Zolimbikitsa Komanso Zamalangizo

Nyimbo Zouziridwa Zomwe Ndi Zolimbikitsa Komanso Zamalangizo

Davide ndi anthu ena anapeka nyimbo zomwe ankaziimba polambira Mulungu, ndipo ena mwa mawu a nyimbo zimenezo ali m’buku la Masalimo. M’buku limeneli muli mawu a nyimbo zokwana 150

BUKU la Masalimo, lomwe ndi lalikulu kwambiri m’Baibulo, ndi buku la nyimbo zopatulika. Buku lonseli linalembedwa pa nthawi ya zaka pafupifupi 1,000. Pa mfundo zonse zokhudza chikhulupiriro zimene zinalembedwapo, buku la Masalimo lili ndi mfundo zambiri zosangalatsa komanso zogwira mtima kwambiri. Buku limeneli likusonyeza m’njira zosiyanasiyana mmene anthu ankamvera mumtima mwawo. Mwachitsanzo, muli mawu osonyeza kusangalala, kutamanda ndi kuyamikira Mulungu, kulira, kumva chisoni komanso osonyeza kulapa. N’zoonekeratu kuti anthu amene analemba Masalimo ankakonda kwambiri Mulungu ndiponso ankamukhulupirira. Tiyeni tione zina mwa mfundo zikuluzikulu zimene zili m’nyimbo zimenezi.

Yehova ndiye woyenera kulamulira komanso woyenera kumulambira ndi kumutamanda. Pa lemba la Salimo 83:18 pali mawu akuti: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Masalimo ambiri amatamanda Yehova chifukwa cha zinthu zimene analenga, monga nyenyezi zakumwamba, zinthu zamoyo zapadziko zomwe ndi zochititsa chidwi komanso thupi la munthu lomwe ndi lodabwitsa. (Masalimo 8, 19, 139, 148) Masalimo ena amalemekeza Yehova chifukwa ndi Mulungu amene amateteza ndi kupulumutsa anthu ake okhulupirika. (Masalimo 18, 97, 138) Ndipo masalimo ena amatamanda Yehova chifukwa ndi Mulungu wachilungamo, amene amathandiza anthu oponderezedwa ndi kupereka chilango kwa anthu oipa.—Masalimo 11, 68, 146.

Yehova amathandiza ndiponso kulimbikitsa amene amamukonda. Mwina Salimo 23 ndi lotchuka kwambiri pa masalimo onse chifukwa musalimo limeneli, Davide anafotokoza kuti Yehova ndi M’busa amene amatsogolera, kuteteza ndiponso kusamalira nkhosa zake. Salimo 65:2 limakumbutsa anthu onse amene amalambira Mulungu kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero.” Anthu ambiri amene anachitapo machimo akuluakulu amalimbikitsidwa akawerenga Masalimo 39 ndi 51 amene Davide analemba atachita machimo akuluakulu. M’masalimo amenewa, iye anafotokoza mawu ochokera pansi pa mtima osonyeza kulapa ndiponso osonyeza kuti amakhulupirira kuti Yehova amakhululuka. Salimo 55:22 lili ndi mfundo zotilimbikitsa kuti tizidalira Yehova ndiponso tizimutulira nkhawa zathu.

Yehova adzasintha zinthu padzikoli pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Ndime zambiri m’buku la Masalimo zimanena za Mesiya, amene ndi Mfumu yolonjezedwa. Mwachitsanzo, Salimo 2 linalosera kuti Wolamulira ameneyu adzawononga mitundu ya anthu oipa amene akutsutsana naye. Salimo 72 limasonyeza kuti Mfumu imeneyi idzathetsa njala, kupanda chilungamo ndi kuponderezana. Malinga ndi Salimo 46:9, Mulungu adzathetsa nkhondo ndiponso adzawononga zida zonse zankhondo kudzera mu Ufumu wa Mesiya. Pa Salimo 37 timawerenga kuti anthu oipa adzawonongedwa, koma anthu olungama adzakhala padziko lapansi kwamuyaya, mwamtendere komanso mogwirizana.

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Masalimo.