Yehova ananena kuti Yesu wa ku Nazareti ndi Mesiya amene analonjezedwa kalekale

KODI Yehova anathandiza anthu kuti adziwe Mesiya wolonjezedwayo? Inde, ndipo onani zimene Mulungu anachita. Panali patadutsa zaka pafupifupi 400 Malemba Achiheberi atamalizidwa kulembedwa. Namwali wina dzina lake Mariya amene ankakhala mumzinda wa Nazareti m’chigawo chakumpoto m’dera la Galileya, analandira mlendo wodabwitsa. Mngelo wotchedwa Gabirieli anaonekera kwa iye ndipo anamuuza kuti ngakhale iye anali asanagonepo ndi mwamuna, Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu yake ya mzimu woyera ndipo adzakhala ndi pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. Mwana ameneyu adzakhala Mfumu imene inalonjezedwa kalekale ndipo idzalamulira kosatha. Mwana ameneyu ndi Mwana wa Mulungu, ndipo Mulungu anasamutsa moyo wake kuchokera kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya.

Mariya anavomereza ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Yosefe anali pa chibwenzi ndi Mariya ndipo anali kalipentala. Iye anakwatira Mariya, Mulungu atatumiza mngelo kukamutsimikizira za mmene iye anakhalira ndi pakati. Nanga bwanji za ulosi wakuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu? (Mika 5:2) Mzinda waung’ono umenewo unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 140 kuchokera ku Nazareti.

Wolamulira wachiroma analamula kuti pachitike kalembera ndipo munthu aliyense ankafunika kuti akalembetse mumzinda umene anabadwira. Zikuoneka kuti Yosefe ndi Mariya anali ochokera ku Betelehemu, choncho Yosefe anatengana ndi mkazi wake amene anali ndi pakati n’kupita kwawo. (Luka 2:3) Mariya anaberekera m’khola ndipo anagoneka mwana wake modyera ziweto. Kenako Mulungu anatumiza angelo ambirimbiri kukauza gulu la abusa amene anali mphepete mwa phiri kuti kwabadwa mwana amene ndi Mesiya kapena kuti Khristu wolonjezedwa.

Patapita nthawi, anthu enanso anavomereza kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. Mneneri Yesaya analosera kuti munthu wina adzakonza msewu pokonzekera kuti Mesiya adzagwire ntchito yake yofunika kwambiri. (Yesaya 40:3) Munthu ameneyo anali Yohane M’batizi. Iye ataona Yesu anafuula kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!” Ena mwa ophunzira a Yohane anayamba kutsatira Yesu nthawi yomweyo. Ndipo mmodzi mwa ophunzirawo anati: “Ifetu tapeza Mesiya.”—Yohane 1:29, 36, 41.

Panali umboni winanso wotsimikizira kuti Yesu anali Mesiya. Pamene Yohane ankabatiza Yesu, Yehova analankhula kuchokera kumwamba. Iye anagwiritsa ntchito mzimu woyera podzoza Yesu kuti akhale Mesiya, ndipo anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mateyu 3:16, 17) Pa nthawiyi Mesiya amene analonjezedwa kale kwambiri anali atafika.

Kodi zimenezi zinachitika liti? Zinachitika mu 29 C.E., nthawi yeniyeni imene zaka 483, zimene Danieli analosera zinatha. N’zoonadi, imeneyi ndi mbali ya umboni wamphamvu wakuti Yesu ndi Mesiya kapena kuti Khristu. Nanga kodi Yesu ankalengeza uthenga wotani ali padziko lapansi?

—Nkhaniyi yachokera pa Mateyu chaputala 1 mpaka 3, Maliko chaputala 1, Luka chaputala 2 ndi pa Yohane chaputala 1.