Sauli amene anali mfumu yoyamba ya Isiraeli sanamvere Yehova. Atachoka pa udindowu, Davide ndi amene analowa m’malo mwake ndipo Mulungu anachita naye pangano kuti ufumu wake sudzatha

SAMISONI atamwalira, kunabwera Samueli amene anali mneneri komanso woweruza mu Isiraeli. Aisiraeli ankauza Samueli mobwerezabwereza kuti awasankhire munthu kuti akhale mfumu yawo ngati mmene zinalili ndi mitundu ina. Ngakhale kuti zimenezi zinaipira Yehova, iye anauza Samueli kuti achite zimene anthuwo akufuna. Choncho Mulungu anasankha Sauli amene anali munthu wodzichepetsa kuti akhale mfumu. Koma patapita nthawi, Mfumu Sauli anayamba kudzikuza ndiponso kusamvera. Yehova sanafunenso kuti iye akhale mfumu, ndipo anauza Samueli kuti asankhe Davide amene anali mnyamata, kuti akhale pa udindowu. Komabe, panapita zaka zambiri Davide asanakhale mfumu.

Davide adakali mwana, anapita kukaona abale ake amene anali m’gulu la asilikali a Sauli. Gulu lonse la asilikalilo linkaopa kwambiri mdani mmodzi wotchedwa Goliyati amene anali chiphona ndipo ankawanyoza pamodzi ndi Mulungu wawo. Choncho Davide anakwiya ndipo anavomera kuti akamenyane ndi munthu ameneyu. Ngakhale kuti anali ndi miyala yochepa chabe ndiponso choponyera chake, mnyamatayu anapita kukamenyana ndi Goliyati, amene anali wamtali pafupifupi mamita atatu. Goliyati atanyoza Davide, iye anayankha kuti ali ndi zida zamphamvu kuposa za chiphonacho chifukwa chakuti ankamenya nkhondoyo m’dzina la Yehova Mulungu. Davide anaphadi Goliyati ndi mwala umodzi wokha ndipo kenako anamudula mutu ndi lupanga lake lomwe. Zitatero gulu lankhondo la Afilisiti linathawa chifukwa cha mantha.

Poyamba Sauli anachita chidwi ndi kulimba mtima kwa Davide ndipo anamusankha kuti aziyang’anira gulu lake lankhondo. Koma zinthu zitayamba kumuyendera bwino Davide, Sauli anayamba kumuchitira nsanje. Choncho Davide anathawa kuti apulumutse moyo wake ndipo anakhala kudziko lina kwa zaka zambiri. Koma Davide anakhalabe wokhulupirika kwa Mfumu Sauli amene ankafuna kumupha uja, chifukwa chakuti anaikidwa ndi Yehova Mulungu. Kenako, Sauli anaphedwa kunkhondo, ndipo posakhalitsa Davide anakhala mfumu, monga mmene Yehova analonjezera.

“Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.”—2 Samueli 7:13

Monga mfumu, Davide ankafunitsitsa kumangira Yehova kachisi. Koma Yehova anamuuza kuti mmodzi mwa ana ake ndi amene adzamange kachisiyo. Choncho Solomo, mwana wa Davide, ndi amene anamanga kachisi. Komabe, Mulungu anadalitsa Davide ndipo anachita naye pangano losangalatsa kwambiri lonena kuti: Banja lake lachifumu lidzakhala lalikulu kuposa mabanja onse achifumu. Kenako m’banja lachifumu limeneli mudzatuluka Mpulumutsi, kapena kuti Mbewu imene Mulungu analonjeza m’munda wa Edeni. Mpulumutsi ameneyu adzakhala Mesiya, kutanthauza “Wodzozedwa,” woikidwa ndi Mulungu. Yehova analonjeza kuti Mesiya adzakhala Wolamulira wa boma kapena kuti Ufumu umene sudzatha.

Poyamikira Mulungu, Davide anasonkhanitsa zipangizo zambiri ndiponso zitsulo zamtengo wapatali zoti azigwiritse ntchito pomanga kachisi. Iye anapekanso masalimo ambiri mouziridwa ndi Mulungu. Cha kumapeto kwa moyo wake, Davide ananena kuti: “Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa, ndipo mawu ake anali palilime langa.”—2 Samueli 23:2.

—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a 1 Samueli; 2 Samueli; 1 Mbiri; komanso pa Yesaya 9:7, Mateyu 21:9, Luka 1:32 ndi pa Yohane 7:42.