CHOLINGA CHA MUTUWU

Chifukwa chimene Yesu anayengera ndiponso kuyeretsa anthu ake mwauzimu komanso mmene anachitira zimenezi

1-3. Kodi Yesu anatani atapeza anthu akudetsa kachisi?

YESU ankalemekeza kwambiri kachisi wa ku Yerusalemu chifukwa ankadziwa kuti kachisiyo ankaimira kulambira koona padziko lapansi. Komatu kulambira kumeneku kuyenera kukhala koyera chifukwa Mulungu amene timamulambira ndi woyera. Ndiyeno taganizirani mmene Yesu anamvera pa Nisani 10, mu 33 C.E., atafika kukachisi n’kupeza anthu akuchita zinthu zodetsa kachisi. Kodi ankamudetsa bwanji?​—Werengani Mateyu 21:12, 13.

2 Yesu atafika m’bwalo la anthu a mitundu ina anapeza amalonda amene ankachita zinthu mwadyera komanso osintha ndalama akubera anthu amene ankabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. * Yesu ‘anathamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama.’ (Yerekezani ndi Nehemiya 13:7-9.) Kenako anawadzudzula chifukwa chosandutsa nyumba ya Atate ake kukhala “phanga la achifwamba.” Pochita zimenezi Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza kwambiri kachisi chifukwa ankadziwa kuti ankaimira kulambira koona. Anaonetsetsa kuti malo amene anthu amalambirirapo Atate ake azikhala oyera.

3 Patapita zaka zambiri, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ndipo anagwiranso ntchito yoyeretsa kachisi. Kachisi ameneyu amakhudza munthu aliyense amene akufuna kulambira Yehova m’njira yovomerezeka. Kodi kachisi ameneyu ndi uti?

Kuyeretsa “Ana a Levi”

4, 5. (a) Kodi otsatira a Yesu odzozedwa anayengedwa komanso kuyeretsedwa bwanji kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa 1919? (b) Kodi kumeneku kunali kuyengedwa komanso kuyeretsedwa kwa anthu a Mulungu komaliza? Fotokozani.

4 Monga mmene tinaonera m’Mutu 2 m’bukuli, Yesu ataikidwa kukhala Mfumu mu 1914 anabwera ndi Atate ake kudzayendera kachisi wauzimu, yomwe ndi njira yovomerezeka yolambirira Mulungu. * Pambuyo poyendera kachisiyu, Mfumu inaona kuti Akhristu odzozedwa, omwe ndi “ana a Levi,” ankafunika kuyengedwa ndiponso kuyeretsedwa. (Mal. 3:1-3) Kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka chakumayambiriro kwa chaka cha 1919, Yehova, yemwe ndi Woyenga, analola kuti anthu ake akumane ndi mayesero komanso mavuto osiyanasiyana kuti awayenge ndiponso kuwayeretsa. N’zosangalatsa kuti odzozedwawa anatuluka m’moto wa woyenga ali oyera komanso ali okonzeka kugwira ntchito yothandiza Mfumu yomwenso ndi Mesiya.

5 Kodi kameneka kanali komaliza kuti anthu a Mulungu ayengedwe komanso kuyeretsedwa? Ayi. M’masiku onse otsirizawa, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito Mfumu yomwenso ndi  Mesiya pothandiza otsatira ake kuti akhale oyera n’cholinga choti apitirizebe kukhala m’kachisi wauzimu. M’mitu iwiri yotsatirayi tiona mmene Yehova wayengera anthu ake kuti akhale ndi makhalidwe abwino komanso mmene wayengera gulu lonse. Koma choyamba, tiyeni tikambirane za kuyeretsa mwauzimu. N’zolimbitsa chikhulupiriro kuona zimene Yesu wachita pothandiza otsatira ake kuti akhale oyera mwauzimu. Zina mwa zinthu zimene Yesu wachita n’zoonekera kwambiri pomwe zina n’zosaonekera.

“Khalani Oyera”

6. Kodi malangizo amene Yehova anapereka kwa Ayuda amene anali ku ukapolo amatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la kukhala woyera mwauzimu?

6 Kodi kuyera mwauzimu kumatanthauza chiyani? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione mawu amene Yehova ananena kwa Ayuda amene anali atatsala pang’ono kutuluka ku ukapolo ku Babulo m’zaka za m’ma 500 B.C.E. (Werengani Yesaya 52:11.) Ayudawo ankabwerera kwawo ku Yerusalemu n’cholinga choti akamange kachisi kuti abwezeretse kulambira koona. (Ezara 1:2-4) Yehova ankafuna kuti anthu ake asakachite china chilichonse chokhudzana ndi kulambira konyenga komwe kunkachitika ku Babulo. Taonani ena mwa malangizo amene anawapatsa: “Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa,” “chokani pakati pake” komanso “khalani oyera.” Yehova safuna kuti kulambira koyera kuzisakanikirana ndi kulambira konyenga. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo imeneyi? Tikuphunzira kuti kukhala oyera mwauzimu kumatanthauza kupewa ziphunzitso komanso miyambo ya chipembedzo chonyenga.

7. Kodi Yesu wakhala akugwiritsa ntchito njira iti pothandiza otsatira ake kukhala oyera mwauzimu?

7 Atangoikidwa kumene kukhala Mfumu, Yesu anakonzeratu njira yooneka bwino imene wakhala akugwiritsa ntchito pothandiza otsatira ake kukhala oyera mwauzimu. Khristu wakhala akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene anamusankha mu 1919. (Mat. 24:45) Pofika m’chaka chimenechi, Ophunzira Baibulo anali atadziyeretsa kale posiya ziphunzitso zambiri za chipembedzo chonyenga. Koma ankafunika kuyeretsedwabe mwauzimu. Kudzera mwa kapolo wokhulupirika, Khristu wakhala akuthandiza pang’onopang’ono otsatira ake kudziwa miyambo komanso zinthu zina zimene ayenera kusiya. (Miy. 4:18) Tiyeni tikambirane zina mwa zinthu zimene anayenera kusiya.

Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Khirisimasi?

8. Kodi Ophunzira Baibulo anali akudziwa kale chiyani zokhudza mwambo wa Khirisimasi, koma sankamvetsa mfundo iti?

8 Ophunzira Baibulo anali akudziwa kale kuti mwambo wa Khirisimasi unachokera ku zikondwerero zachikunja komanso kuti Yesu sanabadwe pa December 25. Magazini ya Zion’s Watch Tower ya December 1881 inanena kuti: “Anthu ambiri amene anali achikunja analowa m’matchalitchi ndipo anangosintha dzina. Ansembe achikunja anayamba kudziwika kuti ansembe achikhristu ndipo miyambo yawo anaipatsa mayina achikhristu. Khirisimasi ndi umodzi mwa miyambo imeneyi.” Mu 1883, nkhani ya mutu wakuti “Kodi Yesu Anabadwa Liti?” yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda, inafotokoza mfundo zosonyeza kuti Yesu  anabadwa chakumayambiriro kwa mwezi wa October. * Koma pa nthawi imeneyo Ophunzira Baibulo sankaona chifukwa chosiyira kukondwerera Khirisimasi moti ngakhale anthu a m’banja la Beteli ku Brooklyn ankachitabe mwambo wa Khirisimasi. Koma pambuyo pa chaka cha 1926, zinthu zinayamba kusintha. Kodi zinthu zinayamba kusintha chifukwa chiyani?

9. Kodi Ophunzira Baibulo anazindikira chiyani pa nkhani ya Khirisimasi?

9 Chifukwa chofufuza nkhaniyi mosamala kwambiri, Ophunzira Baibulo anazindikira kuti kumene mwambowu unachokera komanso zimene zimachitika pamwambowo sizisangalatsa Mulungu. Nkhani ya mutu wakuti, “Kumene Khirisimasi Inachokera” yomwe inatuluka m’magazini ya The Golden Age ya December 14, 1927, inanena kuti Khirisimasi ndi mwambo wachikunja womwe cholinga chake ndi kungofuna kusangalala ndipo pamwambowu pamakhala kulambira mafano. Nkhaniyi inanena momveka bwino kuti Khristu sanatilamule kuchita mwambo umenewu ndipo inanenanso mosapita m’mbali kuti: “Popeza kuti dziko, anthu osakonda Mulungu, komanso Mdyerekezi amakonda mwambowu ndipo amafuna kuti usathe . . . umenewu ndi umboni wooneka bwino wosonyeza kuti anthu amene anadzipereka ndi mtima wonse kuti atumikire Yehova sayenera kuchita nawo mwambo umenewu.” Choncho n’zosadabwitsa kuti kungoyambira nthawi imeneyo banja la Beteli linasiyiratu kukondwerera Khirisimasi.

10. (a) Kodi mu December 1928, Ophunzira Baibulo anaphunzira mfundo zina ziti zosonyeza kuti Khirisimasi ndi mwambo wachikunja? (Onaninso bokosi lakuti, “ Chiyambi cha Khirisimasi ndi Cholinga Chake.”) (b) Kodi anthu a Mulungu anachenjezedwa bwanji za maholide komanso zikondwerero zimene ayenera kuzipewa? (Onani bokosi lakuti, “ Maholide ndi Zikondwerero Zachikunja.”)

10 Chaka chotsatira, Ophunzira Baibulo anaphunziranso mfundo zina zosonyeza kuti Khirisimasi ndi mwambo wachikunja. Pa December 12, 1928, M’bale Richard H. Barber yemwe ankatumikira kulikulu lathu anakamba nkhani yomwe inaulutsidwa pa wailesi ndipo anafotokoza miyambo yoipa yachikunja imene  inachititsa kuti pakhale mwambo wa Khirisimasi. Kodi anthu a Mulungu anatani atalandira malangizo omveka bwino amenewa ochokera kulikulu lawo? M’bale Charles Brandlein anafotokoza za nthawi imene iye ndi banja lake anasiya kukondwerera Khirisimasi. Iye anati: “Sizinativute kusiya miyambo yachikunja imeneyo. Zinangokhala ngati tavula zovala zakuda n’kuzitaya.” M’bale Henry A. Cantwell, yemwe nthawi ina anatumikirapo ngati woyang’anira woyendayenda, anafotokozanso mfundo yofanana ndi yomweyi. Iye anati: “Tinali osangalala kusiya zinthu zimenezi kuti tisonyeze kuti timakonda Yehova.” Otsatira a Khristu okhulupirika anali okonzeka kusintha chilichonse komanso kusiya kuchita nawo mwambo umene unachokera ku chipembedzo chonyenga. *​—Yoh. 15:19; 17:14.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya Mfumu yomwenso ndi Mesiya?

11 Zimene Ophunzira Baibulowa anachita ndi chitsanzo chabwino kwa ifenso masiku ano. Tikaganizira zimene anachitazo tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimatani tikalandira malangizo ochokera kulikulu lathu? Kodi ndimasangalala kutsatira malangizowo komanso kugwiritsa ntchito zimene ndaphunzira?’ Tikamafunitsitsa kutsatira malangizo amene timalandira, timasonyeza kuti ndife okonzeka kugwira ntchito yothandiza Mfumu yomwenso ndi Mesiya, amene akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika popereka chakudya chauzimu.​—Mac. 16:4, 5.

Kodi Akhristu Ayenera Kugwiritsa Ntchito Mtanda?

Baji yokhala ndi chizindikiro cha mtanda ndiponso cha chisoti chachifumu (Onani ndime 12 ndi 13)

12. Kodi kwa zaka zambiri Ophunzira Baibulo ankaona bwanji mtanda?

12 Kwa zaka zambiri, Ophunzira Baibulo ankaona kuti mtanda ndi chizindikiro chofunika cha Akhristu. Sikuti ankaulambira, chifukwa ankadziwa kuti kulambira mafano n’kulakwa. (1 Akor. 10:14; 1 Yoh. 5:21) Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka  m’chaka cha 1883, inanena mosapita m’mbali kuti “Mulungu amadana ndi kulambira mafano kwa mtundu uliwonse.” Poyamba, Ophunzira Baibulowa ankaonabe kuti palibe vuto kugwiritsa ntchito mtanda m’njira zoyenerera. Mwachitsanzo, pofuna kudzidziwikitsa kwa anthu, ankavala kabaji kokhala ndi chizindikiro cha mtanda ndi chisoti chachifumu. Kwa iwowo kabajika kankatanthauza kuti ngati atakhala okhulupirika mpaka imfa adzalandira mphoto ya moyo. Kuyambira m’chaka cha 1891, kabajika kankakhala pachikuto cha Nsanja ya Olonda.

13. Kodi otsatira a Khristu analandira malangizo otani pa nkhani yogwiritsa ntchito mtanda? (Onaninso bokosi lakuti, “ Anathandizidwa Pang’onopang’ono Kuti Asiye Kugwiritsa Ntchito Mtanda.”)

13 Ophunzira Baibulo ankakonda kwambiri kabaji kokhala ndi zizindikiro za mtanda ndi chisoti chachifumu. Koma kuyambira m’zaka za m’ma 1920, otsatira a Khristu anayamba kuthandizidwa pang’onopang’ono kudziwa kuti sayenera kugwiritsa ntchito mtanda. Ponena za msonkhano umene unachitika m’chaka cha 1928 ku Detroit, Michigan, m’dziko la America, M’bale Grant Suiter, yemwe patapita nthawi anatumikira m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti: “Nkhani zomwe zinakambidwa pamsonkhanowu zinasonyeza kuti Akhristu sayenera kungopewa kuvala kabajika koma ayeneranso kupewa kukagwiritsa ntchito.” Patangodutsa zaka zochepa, analandiranso malangizo ena othandiza. Malangizowa anathandiza Akhristu kuzindikira kuti mtanda suyenera kugwiritsidwa ntchito pa kulambira koyera.

14. Kodi anthu a Mulungu anatani atathandizidwa kudziwa zoona pa nkhani yogwiritsa ntchito mtanda?

14 Kodi anthu a Mulungu anatani atathandizidwa pang’onopang’ono kudziwa zoona pa nkhani yogwiritsa ntchito mtanda? Popeza ankakonda kwambiri kugwiritsa ntchito baji yokhala ndi chizindikiro cha mtanda ndi cha chisoti chachifumu, kodi anapitirizabe kugwiritsa ntchito bajiyi? Mlongo wina yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri, dzina lake Lela Roberts, anati: “Titangozindikira zimene zinthuzi zimaimira, sizinativute kusiya kuzigwiritsa ntchito.” Mlongo winanso wokhulupirika, dzina lake Ursula Serenco, anafotokoza maganizo amene anthu ambiri anali nawo. Iye anati: “Tinazindikira kuti chizindikiro chimene tinkachikonda kwambiri poganiza kuti chikuimira imfa ya Ambuye wathu ndiponso kuti ndife Akhristu odzipereka, chinali chizindikiro chachikunja. Malinga ndi zimene lemba la Miyambo 4:18 limanena, tinayamikira kwambiri kudziwa kuti kuwala kwa njira yathu kwawonjezereka.” Otsatira a Khristu okhulupirika sankafuna kuchita nawo miyambo ya chipembedzo chonyenga.

15, 16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufunitsitsa kusunga bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu wa Yehova kuti likhalebe loyera?

15 Ifenso masiku ano sitifuna kuchita nawo miyambo ya chipembedzo chonyenga. Timazindikira kuti Khristu wakhala akugwiritsa ntchito njira yooneka bwino pothandiza anthu ake kukhala oyera mwauzimu. Njira imeneyi ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Choncho, akatipatsa malangizo otichenjeza kuti miyambo inayake kapena maphwando enaake ndi ogwirizana ndi chipembedzo chonyenga timamvera nthawi yomweyo. Mofanana ndi abale ndi alongo amenewa, tiyeni nafenso tiyesetse kuti bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu wa Yehova likhalebe loyera.

16 M’masiku otsiriza ano, Khristu wakhala akuchita zinthu zosiyanasiyana zosaonekera pofuna kuteteza mipingo ya anthu a  Yehova kuti anthu ena asaisokoneze mwauzimu. Kodi akuchita bwanji zimenezi? Tiyeni tione.

‘Kuchotsa Oipa Pakati pa Olungama’

17, 18. M’fanizo la khoka, kodi zinthu zotsatirazi zikutanthauza chiyani (a) kuponya “khoka . . . m’nyanja,” (b) ‘kusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu,’ (c) kusankha “zabwino ndi kuziika m’mitanga,” (d) kutaya “zosafunika”?

17 Nthawi zonse Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu amayang’anira mipingo ya padziko lonse lapansi ya anthu a Mulungu. Khristu ndi angelo akhala akugwira ntchito yosiyanitsa anthu abwino ndi oipa ndipo akhala akuchita zimenezi m’njira yomwe ifeyo sitingathe kuimvetsa. Yesu anafotokoza za ntchito imeneyi mu fanizo lake la khoka. (Werengani Mateyu 13:47-50.) Kodi fanizo limeneli limatanthauza chiyani?

Khoka likuimira ntchito yolalikira za Ufumu imene ikuchitika padziko lonse lapansi (Onani ndime 18)

18 Kuponya “khoka . . . m’nyanja.” Khoka likuimira ntchito yolalikira za Ufumu imene ikuchitika padziko lonse lapansi. ‘Kusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.’ Uthenga wabwino umakopa anthu a mitundu yonse. Ena mwa anthu amenewa amadzakhala Akhristu oona pomwe ena amangokhala ndi chidwi chofuna kuphunzira zambiri koma samayamba kulambira koona. * Kusankha “zabwino ndi kuziika m’mitanga.” Anthu amene ali ndi mtima wofunadi kuphunzira choonadi amasonkhanitsidwa m’mipingo yomwe ili ngati mitanga n’cholinga choti azitha kulambira Yehova m’njira yoyenera. Kutaya “zosafunika.” M’masiku otsiriza ano, Khristu ndi angelo akhala akusiyanitsa anthu “oipa pakati pa olungama.” * Zimenezi zathandiza kuti anthu amene safuna kuphunzira choonadi, omwenso safuna kusiya miyambo kapena zikondwerero zogwirizana ndi chipembedzo chonyenga, asasokoneze mipingo yachikhristu. *

19. Kodi mumamva bwanji kudziwa kuti Khristu wakhala akuchita zinthu zosiyanasiyana potetezera anthu a Mulungu ndiponso potetezera kuti kulambira koona kusadetsedwe?

19 Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti Mfumu yathu, Yesu Khristu, imatetezera anthu ake? Ndi zolimbikitsanso kudziwa kuti akuyesetsa kuyeretsa komanso kuteteza kulambira koona ndiponso atumiki a Mulungu ngati mmene anachitira poyeretsa kachisi ali padziko lapansi. Timayamikira kwambiri kudziwa kuti Khristu wakhala akuchita zinthu zosiyanasiyana potetezera mwauzimu anthu a Mulungu ndiponso potetezera kuti kulambira koona kusadetsedwe. Choncho tiyenera kupewa kuchita zinthu zogwirizana ndi kulambira konyenga kuti tisonyeze zoti tili kumbali ya Mfumuyi limodzi ndi Ufumu wake.

^ ndime 2 Ayuda ochokera m’madera ena ankafunika kugwiritsa ntchito ndalama zovomerezeka popereka msonkho wapachaka wapakachisi ndipo anthu osintha ndalama ankawalipiritsa akafuna kusintha ndalama zawo kuti apeze ndalama zovomerezekazo. Anthu a m’madera enawa ankafunikanso kugula nyama zoti apereke nsembe. Yesu anatchula amalondawa kuti ndi “achifwamba,” ndipo n’kutheka kuti anawatchula choncho chifukwa choti ankalipiritsa anthu mitengo yokwera kwambiri.

^ ndime 4 Anthu a Yehova apadziko lapansi amamutumikira m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wamkulu wauzimu.

^ ndime 8 Nkhani imeneyi inanena kuti sizomveka kuti Yesu anabadwa nyengo ya dzinja chifukwa “sizikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti pa nthawi imene Yesu amabadwa n’kuti abusa akugonera kubusa ndi nkhosa zawo.”​—Luka 2:8.

^ ndime 10 M’kalata imene M’bale  Frederick W. Franz analemba pa November 14, 1927, anati: “Chaka chino sitikhala ndi Khirisimasi. Banja la Beteli lagwirizana kuti tisadzapangenso mwambo wa Khirisimasi mpaka kalekale.” Patangopita miyezi yochepa, pa February 6, 1928, M’bale Franz analembanso kuti: “Ambuye akutiyeretsa pang’onopang’ono kuti tisakhalenso ndi zinthu zochokera ku Babulo yemwe akutsogoleredwa ndi Mdyerekezi.”

^ ndime 18 Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika m’chaka cha 2013. Chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa chinali 7,965,954, koma anthu amene anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Khristu analipo 19,241,252.

^ ndime 18 Kusiyanitsa nsomba zabwino ndi zosafunika n’kosiyana ndi kusiyanitsa nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:31-46) Kusiyanitsa nkhosa ndi mbuzi, kapena kuti chiweruzo chomaliza, kudzachitika m’tsogolo pa nthawi ya chisautso chachikulu. Pakali pano anthu amene ali ngati nsomba zosafunika adakali ndi mwayi wobwerera kwa Yehova ndipo akhoza kusonkhanitsidwa m’mipingo yomwe ili ngati mosungira nsomba.​—Mal. 3:7.

^ ndime 18 Pomaliza, anthu amene ali ngati nsomba zosafunika adzawonongedwa, zomwe zili ngati kuponyedwa m’ng’anjo ya moto.