CHOLINGA CHA MUTUWU

Yehova wakhala akukonza gulu loti lizimutumikira

1, 2. N’chiyani chinasintha pamagazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895, ndipo kodi abale ena ananena chiyani chifukwa cha kusinthaku?

WOPHUNZIRA Baibulo wina wakhama, dzina lake John A. Bohnet, anasangalala kwambiri ndi zimene anaona pamagazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895. Pachikuto cha magaziniyi panali chithunzi cha nsanja yomwe imathandiza anthu oyenda panyanja ndipo m’munsi mwake munali mafunde amphamvu. M’mbali mwa nsanjayo munali mdima ndipo kuwala kochokera pamwamba pa nsanjayo kunkaonekera bwinobwino. Chilengezo chonena za kaonekedwe katsopanoko chimene chinali m’magaziniyi chinali ndi mutu wakuti “Mmene Magazini Yathu Izionekera.”

2 Atasangalala ndi mmene magaziniyi inkaonekera, M’bale Bohnet analembera kalata M’bale Russell. Iye analemba kuti: “Ndasangalala kuona kuti NSANJA imene ili pa magaziniyi ikuoneka bwino kwambiri.” Pofotokoza za mmene chikuto cha magaziniyi chinkaonekera, wophunzira Baibulo wina wokhulupirika dzina lake John H. Brown, analemba kuti: “N’zochititsa chidwi kwambiri kuona kuti mafunde amphamvu akuomba nsanja yomwe ili pamaziko olimba.” Kusintha kumeneku kunali chiyambi chabe chifukwa m’mwezi wa November abale anaonanso kusintha kwina kwakukulu.

3, 4. Kodi Nsanja ya Olonda ya November 15, 1895 inafotokoza vuto liti lomwe linalipo, ndipo magaziniyi inalengeza chiyani komwe kunali kusintha kwakukulu?

3 Nkhani ina imene inatuluka m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya November 15, 1895, inafotokoza za vuto lomwe linali m’gulu la Yehova. Ophunzira Baibulo ankakumana ndi mavuto omwe anali ngati mafunde ndipo ankasokoneza mtendere pakati pawo. Pa nthawiyi abale ankakangana kuti ndi ndani amene ayenera kutsogolera mumpingo. Pofuna kuthandiza abale kudziwa zimene ankayenera kuchita kuti athetse kusagwirizana kumeneku komwe kunkayambitsa mzimu wampikisano, nkhaniyo inayerekeza gulu la Yehova ndi ngalawa. Nkhaniyo inanena mosapita m’mbali kuti abale amene ankatsogolera gulu analephera kukonzekeretsa gululi, lomwe linali ngati ngalawa, kuti lithe kulimbana ndi mavuto omwe anali ngati mafunde. Kodi vuto limeneli likanathetsedwa bwanji?

4 Nkhaniyo inanena kuti woyendetsa ngalawa amaonetsetsa kuti watenga zipangizo zopulumutsira anthu pangozi ndipo anthu ogwira ntchito m’ngalawayo akudziwa zoyenera kuchita ngati mafunde amphamvu atayamba. Mofanana ndi zimenezi, amene ankatsogolera  gulu anafunika kuonetsetsa kuti mipingo yonse ndi yokonzeka kulimbana ndi mavuto amene angabwere. Kuti zimenezi zitheke, m’nkhaniyo analengeza za kusintha kwakukulu. Ananena kuti kungoyambira nthawi imeneyo, “mumpingo uliwonse muyenera kusankhidwa akulu” oti “‘akhale oyang’anira’ gulu la nkhosa.”​—Mac. 20:28.

5. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti dongosolo loti mumpingo muzikhala akulu linali la pa nthawi yake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Kusintha kumeneku kunali kwa pa nthawi yake ndipo inali njira imodzi yothandizira mipingo kuti ikhale yolimba. Kunathandiza abale athu kuti apirire mavuto amene anabwera chifukwa cha nkhondo yoyamba yapadziko lonse. M’zaka zotsatira, zinthu zinanso zinasintha m’gulu ndipo zinathandiza anthu a Mulungu kutumikira Yehova m’njira yoyenera. Kodi ndi ulosi uti wa m’Baibulo womwe unanena za kusintha kumeneku? Kodi inuyo mwaona zinthu ziti zikusintha m’gululi? Nanga kusintha kumeneku kwakuthandizani bwanji?

“Ndidzaika Mtendere Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anira”

6, 7. (a) Fotokozani zimene lemba la Yesaya 60:17 limatanthauza. (b) Kodi mawu akuti “wokuyang’anira” komanso “wokupatsa ntchito” akusonyeza chiyani?

6 Monga taonera m’Mutu 9, Yehova analosera kudzera mwa Yesaya kuti adzadalitsa anthu ake powonjezera chiwerengero chawo. (Yes. 60:22) Koma Yehova analonjeza kuti adzachitanso zinthu zina zambiri chifukwa ulosiwu umanena kuti: “M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide. M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira, ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito,” (Yes. 60:17) Kodi ulosi umenewu umatanthauza chiyani? Nanga ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

Zinthu zimene zikulowa m’malozo ndi zabwino kwambiri kuposa zoyambazo

7 Ulosi wa Yesaya unanena kuti zinthu zina zidzalowedwa m’malo ndi zinthu zina. Onani kuti zinthu zimene zikulowa m’malozo ndi zabwino kwambiri kuposa zoyambazo. Mwachitsanzo, ulosiwu ukunena kuti golide akulowa m’malo mwa mkuwa ndipo kumeneku ndi kusintha kwabwino kwambiri. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ananeneratu kuti gulu la atumiki ake lizidzasintha pang’onopang’ono ndipo kusinthako kudzachititsa kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino kwambiri. Kodi ulosiwu unkanena kuti n’chiyani chidzasinthe? Ponena kuti “wokuyang’anira” komanso “wokupatsa ntchito,” Yehova anasonyeza kuti padzakhala kusintha pa kayendetsedwe ka gulu komanso mmene ankasamalira anthu ake.

8. (a) Kodi ndani amene akuchititsa kuti zinthu zimene zikutchulidwa m’buku la Yesaya zisinthe? (b) Kodi kusintha kumeneku kwatithandiza bwanji? (Onaninso bokosi lakuti, “ Anathandizidwa Chifukwa Anali Wodzichepetsa.”)

8 Kodi ndani amene akanachititsa kuti zinthu ziziyenda bwino m’gululi? Yehova ananena kuti: “Ndidzabweretsa golide, . . . ndidzabweretsa siliva” komanso “ndidzaika mtendere.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova, osati munthu wina aliyense, ndi amene wakhala akuchititsa kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo. Ndipo kungoyambira pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito Mwana wakeyu kuti asinthe kayendetsedwe ka zinthu mumpingo. Kodi kusintha kumeneku kwatithandiza bwanji? Lemba lija limanenanso kuti kusintha kumeneku kudzabweretsa “mtendere” komanso “chilungamo.” Tikamalola kuti Mulungu azititsogolera n’kumayendera limodzi ndi  gulu zinthu zikasintha, timakhala ndi mtendere ndipo kukonda chilungamo kumatichititsa kutumikira Yehova, yemwe mtumwi Paulo anamufotokoza kuti ndi “Mulungu wamtendere.”​—Afil. 4:9.

9. N’chiyani chimathandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti pakhale mgwirizano mumpingo ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Ponena za Yehova, Paulo analembanso kuti: “Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.” (1 Akor. 14:33) Onani kuti Paulo sanasiyanitse chisokonezo ndi kuchita zinthu mwadongosolo, koma anasiyanitsa chisokonezo ndi mtendere. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Taganizirani izi: Kuchita zinthu mwadongosolo pakokha sikubweretsa mtendere. Mwachitsanzo, gulu la asilikali likhoza kupita kunkhondo likuyenda mwadongosolo. Koma cholinga chawo poyenda mwadongosolo ndi kukamenya nkhondo, osati kubweretsa mtendere. Choncho, ifeyo monga Akhristu, tiyenera kukumbukira mfundo yofunika iyi: Ngati gulu la anthu likuchita zinthu mwadongosolo koma cholinga chawo sikubweretsa mtendere, ngakhale patapita nthawi yaitali bwanji lidzalephera. Koma mosiyana ndi zimenezi, mtendere wa Mulungu umachititsa kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti gulu lathu likhalepobe. Ndife osangalala kwambiri kudziwa kuti “Mulungu amene amapatsa mtendere” ndi amene akutsogolera komanso kuyenga gulu lathu. (Aroma 15:33) Mtendere umene Mulungu amapereka umachititsa kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti tizisangalala ndi kuyamikira mgwirizano womwe ulipo m’mipingo yathu padziko lonse.​—Sal. 29:11.

10. (a) M’zaka zoyambirira, kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha m’gulu lathu? (Onani bokosi lakuti, “ Mmene Zinthu Zasinthira pa Kayendetsedwe ka Mpingo.”) (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

10 Bokosi lakuti, “ Mmene Zinthu Zasinthira pa Kayendetsedwe ka Mpingo,” likufotokoza zinthu zina zimene zinasintha m’gulu lathu m’zaka zoyambirira. Koma kodi Yehova wagwiritsa ntchito Mfumu kusintha zinthu ziti posachedwapa, zomwe tingaziyerekezere kuti ndi mkuwa womwe walowedwa m’malo ndi golide? Kodi kusintha pa nkhani ya kayendetsedwe ka mpingo kwathandiza bwanji kuti mipingo ikhale mwamtendere komanso yogwirizana padziko lonse? Kodi kusintha kumeneku kukukuthandizani bwanji inuyo kutumikira “Mulungu wamtendere”?

Zimene Khristu Akuchita Potsogolera Mpingo

11. (a) Ndi zinthu ziti zimene zinasintha chifukwa chomvetsa bwino nkhani zina za m’Baibulo? (b) Kodi abale a m’bungwe lolamulira anali okonzeka kuchita chiyani?

11 Kuyambira m’chaka cha 1964 mpaka mu 1971, Bungwe Lolamulira linatsogolera ntchito yaikulu yofufuza nkhani zina za m’Baibulo imene abale anagwira. Nkhani ina imene anafufuza ndi yokhudza mmene mpingo wachikhristu unkayendetsera zinthu m’nthawi ya atumwi. * Pa kafukufukuyu anapeza kuti, m’nthawi ya atumwi mipingo inkatsogoleredwa ndi bungwe la akulu osati ndi mkulu m’modzi. (Werengani Afilipi 1:1; 1 Timoteyo 4:14.) Atamvetsa mfundo imeneyi, abale a m’bungwe lolamulira anazindikira kuti Yesu, yemwe ndi Mfumu yawo, ankawatsogolera kuti asinthe zinthu pa kayendetsedwe ka zinthu m’gulu la anthu a Mulungu. Abale a m’bungwe lolamulirawa anali okonzeka kutsatira malangizo a Mfumu. Nthawi yomweyo anasintha zinthu kuti atsatire zimene Baibulo limanena posankha akulu mumpingo. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zinasintha chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970?

12. (a) Kodi n’chiyani chinasintha m’bungwe lolamulira? (b) Fotokozani mmene Bungwe Lolamulira limayendetsera zinthu. (Onani bokosi lakuti, “ Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Zinthu Zaufumu,” patsamba 130.)

 12 Kusintha koyamba kunakhudza bungwe lolamulira lenilenilo. Pa nthawi imeneyo, abale amene anali m’bungwe lolamulira analipo okwana 7 ndipo analinso madailekitala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Koma mu 1971, chiwerengero cha abale a m’bungwe lolamulira chinawonjezeka kuchoka pa 7 kufika 11, ndipo anasiya kudziwika monga madailekitala. Abale a m’bungwe lolamulirawa anayamba kudziona kuti ndi ofanana ndi wina aliyense ndipo chaka chilichonse anayamba kusintha tcheyamani wa bungweli. Ankasinthana udindowu potsatira chilembo choyamba cha dzina la munthu aliyense.

13. (a) Kodi mpingo unkayendetsedwa bwanji kuyambira mu 1932 mpaka mu 1972? (b) Kodi Bungwe Lolamulira linachita chiyani mu 1972?

13 Kusintha kwina kunakhudza mpingo uliwonse. Kuyambira m’chaka cha 1932 mpaka 1972, mpingo uliwonse unali ndi m’bale m’modzi amene ankauyang’anira. M’bale amene ankatsogolera mpingo ankadziwika kuti wotsogolera utumiki ndipo zimenezi zinasintha pofika mu 1936. Dzina la m’baleyu linasintha n’kukhala mtumiki wa gulu, kenako linasintha n’kukhala mtumiki wa mpingo. Patapita nthawi linasinthanso n’kukhala woyang’anira mpingo. Abalewa ankachita khama kwambiri posamalira nkhosa mwauzimu. Nthawi zambiri woyang’anira mpingo ankapanga zosankha zokhudza mpingo wonse popanda kufunsa aliyense. Koma m’chaka cha 1972, Bungwe Lolamulira linasintha zinthu zomwe zinakhudza kwambiri kayendetsedwe ka gulu. Kodi kusintha kumeneku kunali kotani?

14. (a) Kodi ndi kusintha kotani komwe kunayamba kugwira ntchito pa October 1, 1972? (b) Kodi wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu amatsatira bwanji mfundo ya pa Afilipi 2:3?

 14 M’malo mokhala ndi m’bale m’modzi monga woyang’anira mpingo, abale ena amene akwaniritsa zimene Malemba amanena anayamba kuikidwa pa udindo monga akulu. Akulu amenewa ankapanga bungwe la akulu loti liziyang’anira mpingo. Kusintha kumeneku kunayamba kugwira ntchito pa October 1, 1972. Masiku ano, wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu sadziona kuti ndi wofunikira kwambiri kuposa akulu onse, koma amadziona kuti ndi “wamng’ono.” (Luka 9:48) Kukhala ndi abale oterewa ndi dalitso lalikulu m’mipingo ya padziko lonse.​—Afil. 2:3.

N’zoonekeratu kuti Mfumu yathu yomwe ndi yanzeru yasankha abusa pa nthawi yake oti aziyang’anira otsatira ake

15. (a) Kodi timapindula bwanji chifukwa chokhala ndi bungwe la akulu m’mipingo? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Mfumu yathu inachita zinthu mwanzeru?

15 Abale amene ali m’bungwe la akulu amagawana zochita pampingo ndipo zimenezi zathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino kwambiri. Taonani mfundo zitatu izi: Choyamba komanso chofunika kwambiri n’chakuti kusintha kumeneku kumachititsa mkulu aliyense, kaya ali ndi udindo waukulu bwanji, kukumbukira kuti Yesu Khristu ndiye Mutu wa mpingo. (Aef. 5:23) Chachiwiri, lemba la Miyambo 11:14 limati: “Pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.” Akulu akamakambirana nkhani zimene zimakhudza moyo wauzimu wa abale mumpingo komanso akamamvetsera pamene m’bale wina akufotokoza maganizo ake, amasankha zinthu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Miy. 27:17) Yehova amadalitsa zimene abalewa amasankha ndipo zinthu zimayenda bwino. Chachitatu, chifukwa chokhala ndi abale omwe akuyenera kutumikira monga akulu, gulu lakwanitsa kuyang’anira komanso kutsogolera mipingo imene yakhala ikuwonjezeka. (Yes. 60:3-5) Tangoganizani, m’chaka cha 1971, chiwerengero cha mipingo  padziko lonse chinali 27,000 koma pofika mu 2013 chinapitirira 113,000. Pamenepa n’zoonekeratu kuti Mfumu yathu yomwe ndi yanzeru yasankha abusa pa nthawi yake oti aziyang’anira otsatira ake.​—Mika 5:5.

“Mukhale Zitsanzo Kwa Gulu la Nkhosa”

16. (a) Kodi akulu ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Ophunzira Baibulo ankaona bwanji langizo la Yesu lakuti: “Weta ana a nkhosa”?

16 Ngakhale m’nthawi ya Ophunzira Baibulo, akulu ankadziwa kuti ali ndi udindo wothandiza okhulupirira anzawo kuti akhale okhulupirika kwa Mulungu. (Werengani Agalatiya 6:10.) Mu 1908, nkhani ina yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda inafotokoza mawu amene Yesu ananena akuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Nkhaniyo inauza akulu kuti: “M’pofunika kuti tizikumbukira mfundo imene Mbuye wathu anatilamula yokhudza nkhosa zake ndipo izikhala pa malo oyamba mumtima mwathu. Zimenezi zingatithandize kuti tiziona kuti tili ndi udindo waukulu wodyetsa komanso kusamalira otsatira a Ambuye.” Mu 1925, nkhani ina imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda inakumbutsa akulu udindo umene ali nawo. Nkhaniyi inati: “Mpingo ndi wa Mulungu, . . .  ndipo adzaimba mlandu aliyense chifukwa cha mmene akuchitira zinthu potumikira abale.”

17. Kodi akulu athandizidwa bwanji kuti ayenerere kukhala abusa?

17 Kodi gulu la Yehova lathandiza bwanji akulu kuti awonjezere luso lawo pa ntchito yoweta, zomwe zili ngati kuchoka pa ‘chitsulo kufika pa siliva’? Gululi lakhala likuphunzitsa akulu. Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yoyamba yomwe inakonzedwa n’cholinga chofuna kuthandiza akulu inachitika mu 1959. Mutu wa nkhani ina imene anaphunzira unali wakuti, “Kuthandiza Munthu Aliyense Payekha.” Abalewa analimbikitsidwa kuti “akonze ndandanda yowathandiza kuti aziyendera ofalitsa kunyumba zawo.” Nkhaniyi inafotokoza njira zosiyanasiyana zimene abusa angatsatire kuti azilimbikitsa abale omwe akuwayenderawo. M’chaka cha 1966, anasinthanso zinthu zina ndi zina mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Mu sukuluyi anakambirana nkhani ya mutu wakuti “Kufunika Kochita Ubusa.” Kodi mfundo yaikulu mu nkhaniyi inali yotani? Inali  yakuti amene ali ndi udindo wotsogolera mumpingo “ayenera kuthandizana posamalira nkhosa za Mulungu. Pamene akuchita zimenezi ayenera kusamaliranso mabanja awo komanso kugwira nawo ntchito yolalikira.” Pa zaka zaposachedwapa akulu ambiri alowa mu sukulu imeneyi. Kodi chachitika n’chiyani chifukwa cha maphunziro amene gulu la Yehova lakhala likupereka kwa akulu? Masiku ano, abale ambirimbiri oyenerera akutumikira m’mipingo yachikhristu ngati abusa auzimu.

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yomwe inachitika ku Philippines, m’chaka cha 1966

18. (a) Kodi akulu anapatsidwa udindo waukulu uti? (b) N’chifukwa chiyani Yehova komanso Yesu amakonda kwambiri akulu amene amagwira ntchito mwakhama?

18 Yehova, kudzera mwa Mfumu yathu Yesu, ndi amene anakonza zoti mumpingo muzikhala akulu kuti azigwira ntchito yofunika kwambiri. Ntchito yake ndi yotsogolera nkhosa za Mulungu mu nthawi yovuta komanso yamapeto ino. (Aef. 4:11, 12; 2 Tim. 3:1) Yehova komanso Yesu amakonda kwambiri akulu amene amagwira ntchito mwakhama chifukwa abale amenewa amamvera langizo la m’Malemba lakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, . . . mofunitsitsa . . . [komanso] ndi mtima wonse . . . . Mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2, 3) Pali njira zambiri zimene abusa achikhristu amasonyezera kuti ndi zitsanzo zabwino kwa nkhosa, koma m’nkhani ino tikambirana njira ziwiri zokha. Njira zimenezi zimathandiza kuti akulu alimbikitse mtendere komanso kuti abale ndi alongo azikhala osangalala mumpingo.

Zimene Akulu Amachita Poweta Nkhosa za Mulungu Masiku Ano

19. Fotokozani mmene mumamvera mukalowa muutumiki ndi mkulu.

19 Njira yoyamba ndi yakuti, akulu amagwira ntchito yolalikira ndi ofalitsa mumpingo. Pofotokoza za Yesu, Luka yemwe analemba Uthenga Wabwino wodziwika ndi dzina lake, anati: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.” (Luka 8:1) Potengera chitsanzo cha Yesu yemwe ankalalikira ndi atumwi ake, masiku ano akulu achitsanzo chabwino amagwira ntchito yolalikira pamodzi ndi okhulupirira  anzawo. Amadziwa kuti kuchita zimenezi kumathandiza kuti mpingo ukhale wolimba. Kodi abale ndi alongo amawaona bwanji akulu oterewa? Mlongo wina wazaka za m’ma 80, dzina lake Jeannine, anati: “Ndikamalalikira ndi mkulu ndimakhala ndi mwayi wocheza naye komanso womudziwa bwino.” M’bale wina wazaka za m’ma 30, dzina lake Steven, ananena kuti: “Ndikamalalikira khomo ndi khomo ndi mkulu ndimaona kuti akufuna kundithandiza. Kuthandizidwa mwa njira imeneyi kumandichititsa kukhala wosangalala.”

Akulu amayesetsa kufufuza anthu amene asiya kusonkhana ndi mpingo ngati mmene m’busa amafufuzira nkhosa yotayika

20, 21. Kodi akulu angatsanzire bwanji m’busa wa m’fanizo la Yesu? Perekani chitsanzo. (Onaninso bokosi lakuti, “ Kuwayendera Mlungu Uliwonse Kunathandiza Kwambiri.”)

20 Njira yachiwiri ndi yakuti gulu la Yehova lakhala likuphunzitsa akulu kuti azithandiza anthu amene anasiya kusonkhana. (Aheb. 12:12) Koma n’chifukwa chiyani akulu ayenera kuthandiza anthu amene anafooka mwauzimu ndipo ayenera kuchita chiyani pothandiza anthu amenewa? Fanizo limene Yesu anafotokoza lonena za m’busa ndi nkhosa yotayika lingatithandize kuyankha mafunso amenewa. (Werengani Luka 15:4-7.) M’busa wa m’fanizoli ataona kuti nkhosa imodzi yasowa, anayamba kuifufuza ngati kuti anali ndi nkhosa imodzi yokhayo. Kodi masiku ano akulu achikhristu amatsanzira bwanji m’busa ameneyu? M’busa wa m’fanizoli ankaona kuti nkhosa yotayikayo ndi yofunika kwambiri. Mofanana ndi m’busa ameneyu, akulu amaona kuti munthu amene wasiya kusonkhana ndi anthu a Mulungu ndi wofunikabe kwambiri. Akuluwa amaona kuti munthu amene wafooka mwauzimu ali ngati nkhosa yotayika ndipo akamathandiza munthu ameneyu saona ngati akungotaya nthawi. Komanso m’busa uja ndi amene ananyamuka “n’kupita kukafunafuna [nkhosa] imodzi yotayikayo kufikira ataipeza.” Masiku anonso akulu amachita zofanana ndi zimenezi pofufuza ndiponso kuthandiza anthu amene afooka mwauzimu.

21 Kodi m’busa wa m’fanizoli amachita chiyani akapeza nkhosa yotayikayo? “Amainyamula paphewa pake” n’kupita nayo kumene kuli nkhosa zina. Mofanana ndi zimenezi, mawu olimbikitsa amene mkulu amanena amakhala ngati akunyamula komanso kuthandiza munthu amene wafookayo kuti ayambirenso kusonkhana ndi mpingo. Zimenezi n’zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Africa, dzina lake Victor, yemwe anasiya kusonkhana ndi mpingo. Iye anati: “Pa zaka 8 zonse zimene sindinkasonkhana, akulu ankayesetsa kundithandiza.” Kodi n’chiyani kwenikweni chimene chinamulimbikitsa? Iye ananena kuti: “Tsiku lina, John, yemwe ndi mkulu amene ndinachita naye Sukulu ya Utumiki Waupainiya, anabwera kudzacheza nane ndipo anandionetsa zithunzi zina zimene anajambula nthawi imene tinkachita sukuluyi. Nditaona zithunzi zimenezi ndinakumbukira zinthu zambiri zosangalatsa moti ndinkafuna kuyambiranso kukhala wosangalala ngati mmene ndinkakhalira pamene ndinkatumikira Yehova.” Patangopita nthawi yochepa Victor anayambiranso kusonkhana. Panopa akutumikiranso ngati mpainiya. Pamenepatu n’zoonekera kuti akulu achikhristu amene amasamalira bwino nkhosa amatithandiza kuti tizikhala osangalala.​—2 Akor. 1:24. *

 Kusintha Kwathandiza Kuti Anthu a Mulungu Akhale Ogwirizana

22. Kodi chilungamo komanso mtendere zimathandiza bwanji kuti anthu akhale ogwirizana mumpingo wachikhristu? (Onaninso bokosi lakuti, “ Tinadabwa Kwambiri.”)

22 Monga taonera m’mutu umenewu, Yehova ananeneratu kuti zinthu zizidzasintha pang’onopang’ono pakati pa anthu ake ndipo padzakhala chilungamo komanso anthuwa azidzakhala mwamtendere. (Yes. 60:17) Makhalidwe awiri onsewa amachititsa kuti abale ndi alongo akhale ogwirizana mumpingo. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Pa nkhani ya chilungamo, Malemba amati: “Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” (Deut. 6:4) Mfundo zimene mipingo yachikhristu imatsatira sizisiyana chifukwa chakuti mipingoyi ili m’mayiko osiyanasiyana. Mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa sizisintha “m’mipingo yonse ya oyerawo.” (1 Akor. 14:33) Choncho, mpingo umayenda bwino ngati ukutsatira mfundo za Mulungu. Pa nkhani ya mtendere, Mfumu yathu imafuna kuti tizikhala mwamtendere komanso kuti tikhale “anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mat. 5:9) Ndipotu timayesetsa ‘kutsatira zinthu zobweretsa mtendere.’ Tikasemphana maganizo ndi okhulupirira anzathu timachita zonse zomwe tingathe kuti tithetse kusemphana maganizoko. (Aroma 14:19) Tikamatsatira mfundo imeneyi timalimbikitsa mtendere ndiponso timakhala ogwirizana m’mipingo yathu.​—Yes. 60:18.

23. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ndi osangalala masiku ano?

23 Mu November 1895, Nsanja ya Olonda itangolengeza kumene kuti mumpingo muzikhala akulu, abale ena amene anali pa udindowu anasonyeza mmene anamvera ndi kusintha kumeneku. Iwo anasonyeza kuti ankafuna komanso ankapemphera kuti kusintha kumeneku kuthandize anthu a Mulungu kuti “ayambe kukhala ogwirizana m’chikhulupiriro.” Tikaona zimene zakhala zikuchitika m’zaka za m’mbuyomu, ndife osangalala chifukwa cha kusintha komwe kwakhala kukuchitika pang’onopang’ono pa nkhani yokhudza oyang’anira mumpingo. Yehova ndi amene wachititsa kusintha kumeneku kudzera mwa Mfumu yathu ndipo zimenezi zatilimbikitsa ndiponso kutithandiza kukhala ogwirizana polambira Mulungu. (Sal. 99:4) Chifukwa cha zimenezi, masiku ano anthu a Yehova padziko lonse lapansi akusangalala pamene akuyenda “mumzimu umodzi,” kutsatira “mapazi amodzimodzi,” ndiponso kutumikira “Mulungu wamtendere” “mogwirizana.”​—2 Akor. 12:18; werengani Zefaniya 3:9.

^ ndime 11 Anatulutsa zotsatira za kafukufuku ameneyu m’buku lakuti Aid to Bible Understanding.