Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 21

Ufumu wa Mulungu Udzachotsa Adani Ake

Ufumu wa Mulungu Udzachotsa Adani Ake

CHOLINGA CHA MUTUWU

Zochitika zosiyanasiyana zimene zidzachititse kuti nkhondo ya Aramagedo iyambe

1, 2. (a) Kodi pali umboni wanji wosonyeza kuti Mfumu yathu yakhala ikulamulira kuyambira mu 1914? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu umenewu?

N’ZOLIMBITSA kwambiri chikhulupiriro kuona zimene Ufumu wa Mulungu wakwanitsa kuchita pakati pa adani ake. (Sal. 110:2) Mwachitsanzo, Mfumu yathu yasonkhanitsa gulu la anthu omwe akulalikira modzipereka. Mfumuyi yayeretsa komanso kuyenga otsatira ake mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Komanso tikusangalala ndi ubale wapadziko lonse ngakhale kuti adani a Ufumuwu ayesetsa kuti atigawanitse. Zinthu zimenezi komanso zinthu zina zimene takambirana m’bukuli ndi umboni wosatsutsika woti kuyambira mu 1914, Mfumu yathu yakhala ikulamulira pakati pa adani a Ufumu.

2 Ufumuwu uchita zinthu zambiri zodabwitsa posachedwapa. ‘Ubwera’ kuti ‘udzaphwanye ndi kuthetsa’ adani ake. (Mat. 6:10; Dan. 2:44) Koma nthawi imeneyo isanafike, padzachitika zinthu zina zapadera. Kodi kudzachitika zotani? Maulosi angapo a m’Baibulo amayankha funso limeneli. Tiyeni tikambirane ena mwa maulosi amenewa kuti tione zinthu zimene zichitike kutsogoloku.

Zimene Zidzachitike “Chiwonongeko Chodzidzimutsa” Chisanachitike

3. Kodi ndi chinthu choyamba chiti chimene tikuyembekezera kuchitika posachedwapa?

3 Kulengeza za mtendere. M’kalata imene mtumwi Paulo analembera Atesalonika anafotokoza chinthu choyamba chimene tikuyembekezera kuti chichitike. (Werengani 1 Atesalonika 5:2, 3.) M’kalatayi Paulo ananena za “tsiku la Yehova,” lomwe lidzayambe ndi kuukiridwa kwa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:5) Komabe, tsiku la Yehova lisanayambe mitundu ya anthu idzakhala ikunena kuti, “Bata ndi mtendere.” Mwina mawuwa adzanenedwa kamodzi kapena maulendo angapo. Kodi atsogoleri achipembedzo adzalengeza nawo zimenezi? Popeza iwo ali mbali yadziko, n’kutheka kuti adzanena nawo kuti: “Kuli mtendere!” (Yer. 6:14; 23:16, 17; Chiv. 17:1, 2) Kulengezedwa kwa bata ndi mtendere kudzasonyeza kuti tsiku la Yehova latsala pang’ono kuyamba. Ndipo adani onse a Ufumu wa Mulungu “sadzapulumuka.”

4. Kodi kumvetsa kufunika kwa ulosi umene Paulo ananena wa kulengezedwa kwa bata ndi mtendere n’kothandiza bwanji kwa ife?

 4 Kodi kumvetsa kufunika kwa ulosi umenewu n’kothandiza bwanji kwa ife? Paulo ananena kuti: “Simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.” (1 Ates. 5:3, 4) Mosiyana ndi anthu ena onse, ifeyo tikudziwa tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika masiku ano. Koma kodi ulosi wonena za bata ndi mtenderewu udzakwaniritsidwa bwanji kwenikweni? Tiyeni tingodikira kuti tidzaone zimene zidzachitike. Choncho, “tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.”1 Ates. 5:6; Zef. 3:8.

Kuyamba Kwa Chisautso Chachikulu

5. Kodi chiyambi cha “chisautso chachikulu” chidzakhala chiyani?

5 Kuukira chipembedzo. Kumbukirani kuti Paulo analemba kuti: “Pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Akadzangonena kuti “Bata ndi mtendere!” nthawi yomweyo “chiwonongeko chodzidzimutsa” chidzafika. Zidzakhala ngati mmene mabingu amamvekera mphezi ikangong’anima. Kodi n’chiyani chidzawonongedwe? Choyamba, “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo amadziwikanso kuti “hule.” (Chiv. 17:5, 6, 15) Kuwonongedwa kumeneku kwa matchalitchi amene amati ndi achikhristu ndiponso zipembedzo zina zonse zonyenga kudzakhala chiyambi cha “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; 2 Ates. 2:8) Kwa anthu ambiri, zimenezi zidzakhala zodabwitsa kwambiri. Tikutero chifukwa pa nthawi imeneyi hule lija lidzakhala likudzionabe ngati “mfumukazi” yomwe ‘sidzalira ngakhale pang’ono.’ Koma mosayembekezereka lidzazindikira kuti lakhala likudzinamiza. Lidzachotsedwa mofulumira kwambiri ngati kuti lachotsedwa ‘tsiku limodzi.’Chiv. 18:7, 8.

6. Kodi ndani adzaukire “Babulo Wamkulu”?

6 Koma kodi ndani adzaukire “Babulo Wamkulu”? Adzaukiridwa ndi “chilombo” chokhala ndi “nyanga 10.” Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti chilombo chimenechi chikuimira bungwe la United Nations (UN). Nyanga 10 zikuimira maulamuliro onse andale a masiku ano omwe amathandiza ‘chilombo chofiira kwambirichi.’ (Chiv. 17:3, 5, 11, 12) Kodi Babulo Wamkulu adzamuchita chiyani? Mayiko amene ali m’bungwe la United Nations adzawononga chuma chake, kumudya kenako ‘n’kumunyeketsa ndi moto.’Werengani Chivumbulutso 17:16. *

7. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 24:21, 22 anakwaniritsidwa bwanji m’nthawi ya atumwi, nanga adzakwaniritsidwa bwanji m’tsogolo?

7 Kufupikitsa masiku. Mfumu yathu inanena zimene zidzachitike pa nthawi imeneyi. Yesu ananena kuti: “Chifukwa cha osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.” (Werengani Mateyu 24:21, 22.) Mawu a Yesu anakwaniritsidwa koyamba mu 66 C.E. pamene Yehova ‘anafupikitsa’ nthawi imene asilikali a Roma anaukira Yerusalemu. (Maliko 13:20) Zimenezi zinapereka mwayi kwa Akhristu a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya kuti apulumutsidwe. Koma kodi mawu amenewa adzakwaniritsidwa bwanji padziko lonse pa nthawi ya chisautso chachikulu? Yehova, pogwiritsa ntchito Mfumu yathu, ‘adzafupikitsa’ nthawi imene bungwe la United Nations lidzaukire chipembedzo pofuna  kuteteza kuti chipembedzo choona chisawonongedwere limodzi ndi chipembedzo chonyenga. Choncho, ngakhale kuti zipembedzo zonse zonyenga zidzawonongedwa, chipembedzo choona chidzapulumuka. (Sal. 96:5) Tsopano tiyeni tikambirane zimene zidzachitike pambuyo poti mbali imeneyi ya chisautso chachikulu yatha.

Zimene Zidzachitike Aramagedo Isanayambe

8, 9. Kodi n’kutheka kuti Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena za zizindikiro zodabwitsa zakumwamba, nanga anthu adzatani akadzaona zizindikirozi?

8 Ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza umasonyeza kuti padzachitika zinthu zingapo Aramagedo isanachitike. Zinthu ziwiri zoyambirira zimene tikambirane m’nkhaniyi zinatchulidwa m’Mauthenga Abwino a Mateyu, Maliko ndi Luka.Werengani Mateyu 24:29-31; Maliko 13:23-27; Luka 21:25-28.

9 Zizindikiro zodabwitsa zakumwamba. Yesu analosera kuti: “Dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba.” Anthu sadzayembekezeranso kulandira kuwala kuchokera kwa atsogoleri achipembedzo, kutanthauza kuti sadzawaonanso kuti angawathandize. Kodi Yesu ankatanthauza kuti kumwamba kudzaonekanso zizindikiro zenizeni zodabwitsa? N’kutheka. (Yes. 13:9-11; Yow. 2:1, 30, 31) Kodi anthu adzatani akadzaona zimenezi zikuchitika? Anthu “adzazunzika” chifukwa ‘chothedwa nzeru.’ (Luka 21:25; Zef. 1:17) Adani onse a Ufumu wa Mulungu, kuyambira ‘mafumu mpaka akapolo,’ ‘adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitike.’ Iwo adzathawa kukabisala koma sadzapeza malo abwino oti n’kubisala mkwiyo wa Mfumu yathu.Luka 21:26; 23:30; Chiv. 6:15-17.

10. Kodi Yesu adzalengeza chiweruzo chotani, nanga atumiki a Mulungu komanso anthu amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu adzatani Yesu akadzalengeza zimenezi?

10 Kulengezedwa kwa chiweruzo. Kenako adani onse a Ufumu wa Mulungu adzaona zinthu zimene zidzawawonjezere mantha. Yesu ananena kuti: “Adzaona Mwana wa munthu akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.” (Maliko 13:26) Mphamvu zodabwitsa zimenezi zidzasonyeza kuti Yesu wabwera kudzalengeza za chiweruzo. Mu ulosi winanso wonena za masiku otsiriza, Yesu anafotokoza mwatsatanetsatane za chiweruzo chimene chidzalengezedwe pa nthawiyi. Mfundo zimene anafotokozazo timazipeza m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Werengani Mateyu 25:31-33, 46.) Anthu onse amene akutumikira Ufumu wa Mulungu mokhulupirika adzaweruzidwa kuti ndi “nkhosa” ndipo ‘adzatukula mitu yawo,’ pozindikira kuti ‘chipulumutso chawo chikuyandikira.’ (Luka 21:28) Koma adani a Ufumu adzaweruzidwa kuti ndi “mbuzi” ndipo “adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni,” pozindikira kuti atsala pang’ono kulandira “chiwonongeko chotheratu.”Mat. 24:30; Chiv. 1:7.

11. Kodi sitiyenera kuiwala mfundo iti tikamakambirana za zinthu zimene zichitike kutsogoloku?

11 Pambuyo poti Yesu walengeza za chiweruzo chake pa “mitundu yonse ya anthu,” padzachitikanso zinthu zina zapadera nkhondo ya Aramagedo isanayambe. (Mat. 25:32) Tikambirana ziwiri mwa zinthu zimenezi, zomwe ndi kuukira kwa Gogi ndi kusonkhanitsidwa kwa odzozedwa. Pamene tikukambirana zinthu  ziwiri zimenezi, tisaiwale kuti Mawu a Mulungu samafotokoza bwinobwino kutalika kwa nthawi imene zinthuzi zidzachitike. Koma zimaoneka kuti china chidzayamba chinzake chisanathe.

12. Kodi nkhondo yoopsa imene Satana adzachite yolimbana ndi Ufumu idzakhala yotani?

12 Kuukira koopsa. Gogi wa kudziko la Magogi adzaukira otsalira odzozedwa komanso anzawo a nkhosa zina. (Werengani Ezekieli 38:2, 11.) Zimene Satana adzachite pamenepa, poukira ulamuliro wa Ufumu, kudzakhala kuukira kwake komaliza pa nkhondo yonse imene wakhala akulimbana ndi otsalira odzozedwa kungoyambira pa nthawi imene anathamangitsidwa kumwamba. (Chiv. 12:7-9, 17) Makamaka kungoyambira pamene odzozedwa anayamba kusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu, Satana wakhala akuyesetsa kuti awasokoneze mwauzimu koma walephera. (Mat. 13:30) Komabe, zipembedzo zonse zonyenga zikadzawonongedwa, anthu a Mulungu adzaoneka ngati akukhala malo opanda “mipanda ndipo alibe zotsekera ndiponso zitseko,” choncho Satana adzaona kuti umenewu ndi mwayi umene wakhala akuuyembekezera. Adzatsogolera otsatira ake kuti aukire atumiki a Ufumu ndipo kuukira kumeneku kudzakhala koopsa kwambiri.

13. Kodi Yehova adzatani pofuna kuteteza anthu ake?

13 Ezekieli anafotokoza zimene zidzachitike pa nthawiyi. Ponena za Gogi, ulosi wake unanena kuti: “Udzabwera kuchokera kumalo ako, kumadera akutali a kumpoto. Udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala chigulu chachikulu chankhondo. Onsewo adzabwera atakwera pamahatchi. Ndithu iwe udzabwera ngati mitambo kudzaphimba dzikolo ndi kudzaukira anthu anga.” (Ezek. 38:15, 16) Kodi Yehova adzatani adani ake akadzatsala pang’ono kuwonongeratu atumiki onse a Mulungu? Yehova ananena kuti: “Mkwiyo wanga udzatulukira” ndipo “ndidzamubweretsera lupanga.” (Ezek. 38:18, 21; werengani Zekariya 2:8.) Yehova adzalowelera kuti ateteze atumiki ake padziko lapansi. Kulowelera kumeneku ndi kumene kumatchulidwa kuti nkhondo ya Aramagedo.

14, 15. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zomwe zidzachitike pambuyo poti Satana waukira atumiki a Mulungu?

14 Tisanapitirize kukambirana mmene Yehova adzatetezere anthu ake pa nkhondo ya Aramagedo, tiyeni tikambirane kaye za zinthu zina zapadera. Zinthu zimenezi zidzachitika pakati poti Satana wayamba kuukira mwamphamvu atumiki a Mulungu ndi nthawi imene Yehova adzalowelere n’kuyambitsa nkhondo ya Aramagedo. Malinga ndi zimene tafotokoza mu ndime 11, zinthu zimene zidzachitikezo ndi kusonkhanitsidwa kwa otsalira odzozedwa.

15 Kusonkhanitsa otsalira odzozedwa. Mateyu ndi Maliko analemba mawu a Yesu onena za “osankhidwa,” omwe ndi Akhristu odzozedwa ndi mzimu, ndipo analemba mawuwa m’gulu la zinthu zimene zidzachitike nkhondo ya Aramagedo isanayambe. (Onani ndime 7.) Pamene ankafotokoza zoti ndi Mfumu, Yesu analosera kuti: “Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira  kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.” (Maliko 13:27; Mat. 24:31) Kodi ndi kusonkhanitsa anthu kotani kumene Yesu ankafotokoza pamenepa? Iye sankanena za kudinda chidindo komaliza pamphumi pa otsalira odzozedwa, chifukwa kudinda kumeneku kudzachitika chisautso chachikulu chisanayambe. (Chiv. 7:1-3) M’malomwake, Yesu ankafotokoza za zinthu zimene zidzachitike pa nthawi ya chisautso chachikulu chimene chikubwera. Choncho, n’kutheka kuti pa nthawi ina pambuyo poti Satana wayamba kuukira anthu a Mulungu, odzozedwa omwe adzakhalebe padziko lapansi adzatengedwa kupita kumwamba.

16. Kodi odzozedwa adzachita chiyani pa nthawi ya nkhondo ya Aramagedo?

16 Kodi kusonkhanitsidwa kwa otsalira odzozedwa kumeneku kukugwirizana bwanji ndi nkhondo ya Aramagedo yomwe idzachitike pambuyo pake? Popeza kusonkhanitsidwaku kudzachitika Aramagedo isanayambe, zikusonyeza kuti odzozedwa onse adzakhala ali kumwamba pamene nkhondo ya Mulungu imeneyi izidzayamba. Kumwambako, olamulira anzake a Khristu okwana 144,000 amenewa adzapatsidwa mphamvu kuti athandizane ndi Yesu kuwononga adani a Ufumu wa Mulungu pogwiritsa ntchito “ndodo yachitsulo.” (Chiv. 2:26, 27) Kenako, odzozedwa limodzi ndi angelo amphamvu adzatsatira Khristu, Mfumu ya Nkhondo, pamene azidzapita kukamenyana ndi “chigulu chachikulu chankhondo” cha adani ake omwe atsala pang’ono kuukira anthu a Yehova. (Ezek. 38:15) Magulu amenewa akadzangokumana ndiye kuti nkhondo ya Aramagedo yayamba.Chiv. 16:16.

Pachimake pa Chisautso Chachikulu

Kuyamba kwa nkhondo ya Aramagedo

17. Kodi n’chiyani chidzachitikire “mbuzi” pa nthawi ya Aramagedo?

17 Kupereka chilango. Nkhondo ya Aramagedo idzakhala pachimake pa chisautso chachikulu. Pa nthawi imeneyi, Yesu adzakhalanso ndi udindo wina. Kuwonjezera pa kukhala Woweruza wa “mitundu yonse ya anthu,” adzakhalanso Wakupha ndipo adzapha mitundu ya anthu. Mitundu imeneyi ndi anthu omwe adzakhale atawaweruza kuti ndi “mbuzi.” (Mat. 25:32, 33) Pogwiritsa ntchito “lupanga lalitali lakuthwa,” Mfumu yathu ‘idzapha mitundu ya anthu.’ Choncho, anthu onse omwe ali ngati mbuzi, kuyambira “mafumu” mpaka “akapolo,” “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu.”Chiv. 19:15, 18; Mat. 25:46.

18. (a) Kodi zinthu zidzasintha bwanji kwa “nkhosa”? (b) Kodi Yesu adzamaliza bwanji ntchito yogonjetsa adani ake?

18 Kusintha kumeneku kudzakhala kosangalatsa kwambiri kwa anthu amene Yesu adzawaweruze kuti ndi “nkhosa.” M’malo mophedwa ndi gulu lalikulu la asilikali a Satana omwe ndi “mbuzi,” “khamu lalikulu” la “nkhosa” zooneka ngati zopanda chitetezo lidzapulumuka kwa adani awo ndipo ‘lidzatuluka m’chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Kenako, pambuyo poti Yesu wagonjetsa adani ake komanso wachotsa anthu onse omwe amadana ndi Ufumu wa Mulungu, adzaponya Satana  ndi ziwanda zake m’phompho. Iwo sadzatha kuchita chilichonse ndipo adzangokhala ngati akufa kwa zaka 1,000.Werengani Chivumbulutso 6:2; 20:1-3.

Mmene Tingakonzekerere

19, 20. Kodi tingatsatire bwanji mfundo ya pa Yesaya 26:20 ndi pa 30:21?

19 Kodi tingakonzekere bwanji zinthu zochititsa mantha zomwe zichitike kutsogoloku? Nsanja ya Olonda ina ya m’mbuyomu inanena kuti: “Tidzapulumuka pokhapokha ngati tili omvera.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Mawu ochenjeza amene Yehova anauza Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo akuyankha funso limeneli. Yehova ananeneratu kuti Babulo adzagonjetsedwa. Koma kodi anthu a Mulungu anayenera kuchita chiyani kuti akonzekere zimenezi? Yehova ananena kuti: “Pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Taonani mawu akuti “pitani,” “mukalowe,” “mukatseke,” ndiponso akuti “mukabisale” omwe ali mu vesili. Mawu onsewa akusonyeza kuti akuwauza zochita, kapena kuti kuwalamula. Ayuda amene anatsatira mawu amenewa ayenera kuti anakhala m’nyumba zawo ndipo sanapite m’misewu momwe munali asilikali amene akanawapha. Choncho, kuti Ayudawa apulumuke anafunika kumvera malangizo a Yehova. *

20 Kodi ifeyo tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Mofanana ndi atumiki a Mulungu akalewa, ifenso tiyenera kumvera malangizo a Yehova kuti tidzapulumuke zinthu zimene zichitike kutsogoloku. (Yes. 30:21) Malangizo amenewa timawalandira kudzera kumpingo. Choncho, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi mtima womvera malangizo amene timalandira. (1 Yoh. 5:3) Ngati timamvera panopa sizidzakhala zovuta kuti tidzamverenso m’tsogolo, zomwe zidzachititse kuti titetezedwe ndi Atate wathu, Yehova, ndiponso Mfumu yathu, Yesu. (Zef. 2:3) Chitetezo chimenechi chidzatipatsa mwayi woona ndi maso athu mmene Ufumu wa Mulungu udzachotsere adani ake onse. Zimenezitu zidzakhala zinthu zosaiwalika.

^ ndime 6 N’zomveka kunena kuti kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu” kwenikweni kukutanthauza kuwonongedwa kwa mabungwe a chipembedzo, osati kuphedwa kwa anthu onse omwe ali m’chipembedzo chonyenga. Choncho, anthu ambiri amene poyamba anali m’Babulo Wamkulu adzapulumuka kuwonongedwa kumeneku ndipo n’kutheka kuti adzayamba kulankhula zosonyeza kuti asiya zachipembedzo ngati mmene lemba la Zekariya 13:4-6 limafotokozera.

^ ndime 19 Kuti mumve zambiri, onani Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1, patsamba 282-283.