Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ufumu wa Mulungu Ukulamulira

 MUTU 15

Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka

Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka

CHOLINGA CHA MUTUWU

Mmene Khristu wathandizira otsatira ake kumenyera ufulu woti avomerezedwe ndi maboma komanso kuti akhale ndi ufulu wotsatira malamulo a Mulungu

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti ndinudi nzika ya Ufumu wa Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zina a Mboni za Yehova amafunika kumenyera ufulu wawo wolambira Mulungu?

NGATI ndinu wa Mboni za Yehova, ndiye kuti ndinu nzika ya Ufumu wa Mulungu. Koma kodi munthu angadziwe bwanji kuti ndife nzika ya Ufumuwu? Sikuti tili ndi mapasipoti kapena mapepala ena ake a boma omwe amasonyeza zimenezi, koma zimene timachita polambira Yehova Mulungu zimasonyeza kuti ndifedi nzika za Ufumuwu. Kulambira Mulungu sikumangokhudza zimene timakhulupirira, koma kumaphatikizaponso kutsatira malamulo a Ufumu wa Mulungu. Chilichonse chomwe timachita pa moyo wathu chimagwirizana kwambiri ndi kulambira kwathu, kuphatikizapo mmene timalerera ana komanso chithandizo cha mankhwala chimene timasankha kulandira tikadwala.

2 Koma nthawi zina anthu a m’dzikoli samvetsa zinthu zimene ifeyo, monga nzika za Ufumuwu, timaona kuti n’zofunika kwambiri pa moyo wathu. Maboma ena ayesa kuletsa kapena kuthetsa kulambira koona. Nthawi zina otsatira a Khristu amamenyera ufulu wawo kuti azitha kutsatira malamulo a Mfumu yomwenso ndi Mesiya. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa kuyambira kalekale, anthu a Yehova akhala akumenyera ufulu wolambira.

3. Kodi anthu a Mulungu a nthawi ya Mfumukazi Esitere anafunika kumenyera chiyani?

3 Mwachitsanzo, m’masiku a Mfumukazi Esitere, anthu a Mulungu ankafunika kumenyera ufulu wawo kuti akhale ndi moyo. Kodi chinachitika n’chiyani? Munthu wina woipa mtima, dzina lake Hamani yemwe anali Nduna Yaikulu, anauza Mfumu Ahasiwero ya ku Perisiya kuti Ayuda onse omwe anali mu ufumu wake aphedwe chifukwa ‘malamulo awo anali osiyana ndi malamulo a anthu ena onse.’ (Esitere 3:8, 9, 13) Kodi Yehova anathandiza atumiki ake? Inde, chifukwa anadalitsa zimene Esitere ndi Moredekai anachita pa nthawi imene ankakonzekera kukapempha Mfumu ya Perisiya kuti iteteze anthu a Mulungu.Esitere 9:20-22.

4. Kodi tikambirana chiyani mu nkhaniyi?

4 Kodi masiku ano Akhristu amamenyera ufulu wawo wa kulambira? Monga taonera m’mutu wapitawu, nthawi zina olamulira amatsutsa Mboni za Yehova. M’mutu uno, tikambirana zinthu zina zimene maboma akhala akuchita n’cholinga chofuna kutilepheretsa kulambira momasuka. Tikambirana mfundo zitatu izi: (1) ufulu wodziwika monga gulu lovomerezeka komanso wolambira mmene tikufunira, (2) ufulu wosankha chithandizo cha mankhwala mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo komanso (3) ufulu umene makolo ali nawo wolera ana mogwirizana ndi mfundo  za Yehova. Pokambirana mfundo iliyonse, tiona zimene nzika zokhulupirika za Ufumu zayesetsa kuchita pofuna kuteteza ufulu wawo monga nzika ndiponso tiona mmene Mulungu wawadalitsira.

Kuyesetsa Kuti Gulu Lathu Likhale Lovomerezeka Ndi Boma Komanso Kuti Tikhale Ndi Ufulu Ngati Ena Onse

5. Kodi kuvomerezedwa ndi boma n’kothandiza bwanji kwa Akhristu oona?

5 Kodi timafunika kuvomerezedwa ndi boma kuti tizilambira Yehova? Ayi, kungoti tikavomerezedwa ndi boma, timalambira momasuka. Mwachitsanzo, timatha kusonkhana momasuka mu Nyumba za Ufumu komanso Malo a Misonkhano, timatha kusindikiza ndi kutumiza mabuku m’mayiko ena komanso kulalikira uthenga wabwino popanda kusokonezedwa. M’mayiko ambiri, a Mboni za Yehova ndi ovomerezedwa ndi boma ndipo ali ndi ufulu wolambira wofanana ndi zipembedzo zina zonse zovomerezedwa ndi boma. Koma kodi chimachitika n’chiyani boma likakana kulemba Mboni za Yehova m’kaundula wa zipembedzo zovomerezeka kapena likamatiphwanyira ufulu wathu?

6. Kodi Mboni za Yehova za ku Australia zinakumana ndi mavuto otani kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940?

6 Australia. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940, mtsogoleri wa dziko la Australia ankaona kuti zomwe timakhulupirira zingasokoneze mapulani a nkhondo omwe anali nawo. Zimenezi zinachititsa kuti achotse Mboni za Yehova m’kaundula wa zipembedzo komanso kuwalanda ufulu wawo. A Mboni sankathanso kusonkhana kapena kulalikira poyera, ofesi ya nthambi inatsekedwa ndipo Nyumba za Ufumu zinalandidwa. Ndipo ngakhale kukhala ndi mabuku athu ofotokoza Baibulo kunali koletsedwa. A Mboni a ku Australia ankachita zinthu zawo mobisa kwa zaka zambiri mpaka pa June 14, 1943, pamene Khoti Lalikulu la m’dzikolo linaperekanso ufulu kwa Mboni za Yehova.

7, 8. Fotokozani zimene abale athu a ku Russia achita pomenyera ufulu wawo m’zaka zapitazi.

7 Russia. Pa nthawi ya ulamuliro wa chikomyunizimu, a Mboni za Yehova analibe ufulu wolambira kwa zaka zambiri koma kenako analoledwa kulembetsa m’kaundula wa zipembedzo zovomerezeka mu 1991. Ulamuliro wa Soviet Union utatha, mu 1992 boma la Russia linayamba kutiona ngati chipembedzo chovomerezeka. Koma pasanapite nthawi yaitali, anthu ena otsutsa, makamaka a m’tchalitchi cha Orthodox, anayamba kukwiya poona mmene chiwerengero cha Mboni za Yehova chinkakulira. Pakati pa chaka cha 1995 ndi 1998, otsutsa anakasuma kukhoti milandu 5 yosonyeza kuti a Mboni za Yehova akuphwanya malamulo a dzikolo. Koma pa milandu yonseyi, woweruza sanapeze umboni uliwonse wosonyeza kuti a Mboni ankaphwanyadi malamulo. Otsutsawo sanagonje ndipo mu 1998 anakasumanso mlandu wina. Poyamba a Mboni anawina mlanduwu koma otsutsawo sanagwirizane ndi chigamulochi ndipo anapanga apilo. A Mboni analuza pa mlandu wa apilowo mu May, 2001. Mlanduwu unayamba kuunikidwanso mu October chaka chomwecho ndipo mu 2004 anagamula kuti Mboni za Yehova si chipembedzo chovomerezeka ndi boma komanso analetsa ntchito zonse za gululi.

8 Chigamulo chimenechi chinachititsa kuti a Mboni ayambe kuzunzidwa kwambiri komanso kuchitidwa chipongwe. (Werengani 2 Timoteyo 3:12.) Ankalandidwa mabuku awo komanso  sankaloledwa kumanga kapena kuchita lendi nyumba zoti azisonkhanamo. Taganizirani mmene abale ndi alongo athu ankamvera pamene ankakumana ndi mavuto amenewa. Mu 2001 anapititsa nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya ndipo anatumizanso mfundo zina zofunika pa nkhaniyi m’chaka cha 2004. Khotili linagamula nkhaniyi m’chaka cha 2010. A khoti anaona kuti anthu a zipembedzo zina ndi amene anachititsa kuti Mboni za Yehova zichotsedwe m’kaundula wa boma, ndipo anagamula kuti panalibe chifukwa chomveka chogwirizana ndi chigamulo chimene makhoti aang’ono anapanga chifukwa panalibe umboni wosonyeza kuti a Mboni ankaphwanya malamulo. Khotilo linaonanso kuti makhotiwo anachotsa a Mboni za Yehova m’kaundula pofuna kuti asakhalenso ndi ufulu wolambira. Khoti Lalikululo linagamula kuti a Mboni za Yehova apatsidwenso ufulu umene zipembedzo zonse zili nawo. Ngakhale kuti akuluakulu ambiri a m’dzikolo sakutsatira zimene khotili linagamula, kupambana pa milanduyi kwathandiza anthu a Mulungu kuti azichita zinthu molimba mtima.

Titos Manoussakis (Onani ndime 9)

9-11. Kodi anthu a Yehova ku Greece anavutika motani kuti akhale ndi ufulu wosonkhana, nanga nkhaniyi inatha bwanji?

9 Greece. Mu 1983, Titos Manoussakis anachita lendi chipinda china ku Heraklion, mumzinda wa Crete, n’cholinga choti kagulu ka Mboni za Yehova kazisonkhanamo. (Aheb. 10:24, 25) Koma pasanapite nthawi, wansembe wa tchalitchi cha Orthodox analemba kalata ku boma yosonyeza kusakondwa ndi zoti a Mboni azigwiritsa ntchito chipindacho polambira. Iye anachita zimenezi chifukwa choti zimene a Mboni amakhulupirira ndi zosiyana ndi zimene a tchalitchi cha Orthodox amakhulupirira. Akuluakulu a boma anatsegulira milandu Titos Manoussakis ndi abale ena atatu a m’deralo. Anawagamula kuti alipire ndalama komanso kuti akakhale kundende kwa miyezi iwiri. Monga nzika zokhulupirika za Ufumu wa Mulungu, a Mboni anaona kuti zimene khoti linagamulazi zikuphwanya ufulu wawo wolambira Mulungu, choncho anapititsa nkhaniyo kumakhoti ena a m’dzikolo ndipo pambuyo pake anapita nayo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

10 Mu 1996, khotili linagamula nkhaniyi m’njira imene anthu otsutsa sankayembekezera. Khotilo linanena kuti “a Mboni za Yehova ali m’gulu la ‘zipembedzo zodziwika’ potengera malamulo a ku Greece” komanso kuti zimene makhoti enawo anagamula “zinasokoneza ufulu wawo wa kulambira.” Linapezanso kuti boma la Greece linalibe mphamvu “younika ngati zikhulupiriro za chipembedzo chinachake kapena zimene anthu a m’chipembedzocho amachita potsatira chikhulupiriro chawo zili zoyenera.” Chigamulo cha makhoti ena aja chinasinthidwa ndipo Mboni zinapatsidwanso ufulu wolambira momasuka.

11 Kodi kuwina mlandu umenewu kunathetsa mavuto amene abale ndi alongo ankakumana nawo ku Greece? Ayi. Mu 2012, khoti la ku Kassandreia, ku Greece, linagamulanso nkhani ina yofanana ndi yomweyi imene inatenga zaka pafupifupi 12 kuti ithe. Amene anasumira Mboni za Yehova pa mlandu umenewu anali bishopu wa tchalitchi cha Orthodox. Khoti lalikulu la m’dzikolo linagamula mlanduwo mokomera anthu a Mulungu. Pogamula mlanduwu  anafotokoza za malamulo a dzikolo omwe amanena kuti chipembedzo chilichonse chiyenera kupatsidwa ufulu wolambira ndipo anatsutsa zimene anthu ankakonda kunena zoti Mboni za Yehova si chipembedzo chodziwika. Khotilo linanena kuti: “A Mboni za Yehova samabisa zimene amaphunzitsa ndipo zimene amachitazo zimasonyeza kuti ndi chipembedzo chodziwika.” Panopa abale ndi alongo a mumpingo waung’ono wa Kassandreia amasangalala kuti ali ndi ufulu wosonkhana mu Nyumba ya Ufumu yawo.

12, 13. Kodi anthu otsutsa a ku France anayesa bwanji ‘kuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo,’ nanga zinatha bwanji?

12 France. Anthu ena odana ndi anthu a Mulungu ‘amayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ (Werengani Salimo 94:20.) Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1990, akuluakulu oona za misonkho m’dziko la France anayamba kuwerengetsera ndalama zonse zimene bungwe la Mboni za Yehova la m’dzikolo lakhala likugwiritsa ntchito. Zimene nduna yoona za chuma cha boma inafotokoza zinasonyeza cholinga chawo pochita zimenezi. Iye anati: “Kuwerengetsera kumeneku kungachititse kuti a khoti athetse bungwe limeneli kapena alizenge milandu . . . , yomwe ingachititse kuti bungweli lisayende bwino kapena lisiye kugwira ntchito m’dziko lathuli.” Ngakhale kuti atawerengetsera sanapeze chilichonse chokayikitsa, akuluakulu oona za misonkho anatchaja bungwe la Mboni za Yehova msonkho wokwera kwambiri. Msonkho umenewu ukanati uperekedwedi wonse, ukanachititsa kuti abale atseke ofesi ya nthambi n’kugulitsa nyumba zonse kuti ndalama zikwanire. Zimenezi zinali zopweteka kwambiri kwa anthu a Mulungu, komabe sanagonje. Iwo sanagwirizane ndi zimene boma linachitazi ndipo m’chaka cha 2005 anakasuma ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

13 Khotili linapereka chigamulo chake pa June 30, 2011. Linafotokoza kuti kulemekeza ufulu wa chipembedzo kuyenera kuchititsa boma kuti lisiye kumaunika ngati zimene anthu a chipembedzo chinachake amakhulupirira zili zoona kapena ngati zimene anthu amachita chifukwa cha chikhulupiriro chawo zili zoyenera. Boma lingachite zimenezi pokhapokha ngati zinthu zafika povuta kwambiri. Khotili linanenanso kuti: “Msonkhowo . . . ukanachititsa kuti bungwe la Mboni za Yehova ligulitse zinthu zake zofunikira, zomwe zikanachititsa kuti anthu a m’chipembedzochi asakhalenso ndi mwayi wolambira Mulungu wawo pamalo oyenerera.” Oweruza onse a m’khotili anagamula nkhaniyi mokomera Mboni za Yehova. Anthu a Yehova anasangalala pamene boma la France linabweza msonkho wonse limodzi ndi chiwongoladzanja chake. Potsatira zimene a khoti analamula, bomali linabweza katundu yense wa bungweli yemwe analanda ngati chikole.

Mukhoza kupempherera mobwerezabwereza abale ndi alongo omwe akuzunzika chifukwa cha malamulo amene ali m’dziko lawo

14. Kodi inuyo mungathandize nawo bwanji pa nkhondo imeneyi yomenyera ufulu wolambira Mulungu?

14 Mofanana ndi mmene anachitira Esitere ndi Moredekai, anthu a Yehova a masiku ano amamenyera ufulu wolambira Yehova m’njira imene mwiniwake anatilamula. (Esitere 4:13-16) Kodi nanunso mungathandize nawo pomenyera ufuluwu? Inde. Mukhoza kupempherera mobwerezabwereza abale ndi alongo omwe akuzunzika chifukwa cha malamulo amene ali m’dziko lawo. Mapemphero ngati amenewo angathandize kwambiri abale ndi alongo omwe akuzunzidwa. (Werengani Yakobo 5:16.) Koma kodi  Yehova amayankha mapemphero otero? Milandu imene takhala tikuwina ikusonyeza kuti Yehova amayankhadi mapemphero amenewa.Aheb. 13:18, 19.

Ufulu Wosankha Chithandizo cha Mankhwala Chogwirizana ndi Zimene Timakhulupirira

15. Pa nkhani yogwiritsa ntchito magazi, kodi anthu a Mulungu amaganizira mfundo ziti?

15 Malinga ndi zomwe tinafotokoza Mutu 11, nzika za Ufumu wa Mulungu zinapatsidwa malangizo omveka bwino a m’Malemba owaletsa kugwiritsa ntchito magazi molakwika ngati mmene anthu ambiri akuchitira masiku ano. (Gen. 9:5, 6; Lev. 17:11; werengani Machitidwe 15:28, 29.) Ngakhale kuti sitimalola kuthiridwa magazi, timafuna kuti ifeyo komanso abale athu tipatsidwe chithandizo cha mankhwala choyenerera chomwe sichikutsutsana ndi malamulo a Mulungu. Makhoti akuluakulu a m’mayiko ambiri aona kuti anthu ali ndi ufulu wolandira kapena kukana chithandizo cha mankhwala potsatira chikumbumtima chawo komanso zimene amakhulupirira. Koma anthu a Mulungu a m’mayiko ena akumana ndi mavuto aakulu pa nkhani imeneyi. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

16, 17. Kodi ndi chithandizo chotani chakuchipatala chimene mlongo wina wa ku Japan anakhumudwa nacho, nanga mapemphero ake anayankhidwa bwanji?

16 Japan. Mlongo wina wa ku Japan wazaka 63, dzina lake Misae Takeda, ankafunika kuchitidwa opaleshoni yaikulu. Monga nzika yokhulupirika ya Ufumu wa Mulungu, anafotokozera madokotala momveka bwino kuti akufuna chithandizo chosagwiritsa ntchito magazi. Koma patapita miyezi ingapo anakhumudwa kumva kuti anamuthira magazi pa nthawi imene ankamuchita opaleshoniyo. Poona kuti amulakwira, mu June 1993, Mlongo Takeda anakasumira madokotala komanso chipatala chimene anapitacho kukhoti. Mlongoyu anali wofatsa ndiponso wosakonda kulankhulalankhula koma anali ndi chikhulupiriro cholimba. Anafotokoza mbali yake molimba mtima m’khoti mutadzaza anthu ndipo anaimirira malo amodzi kwa nthawi yoposa ola limodzi ngakhale kuti anali akudwala. Anaonekera m’khotilo komaliza kutangotsala mwezi umodzi kuti amwalire. Kodi nafenso sitikulakalaka kukhala olimba mtima komanso kukhala ndi chikhulupiriro ngati chimenechi? Mlongo Takeda ananena kuti nthawi zonse ankapempha Yehova kuti amuthandize pa nthawi ya mlanduwu ndipo sankakayikira kuti mapemphero ake ayankhidwa. Koma kodi anayankhidwadi?

17 Patapita zaka zitatu kuchokera pamene Mlongo Takeda anamwalira, Khoti Lalikulu la ku Japan linagamula nkhaniyi mokomera iyeyo. Khotili linavomereza kuti kunali kulakwa kumuthira magazi mwiniwakeyo atanena momveka bwino kuti sakufuna. Chigamulochi chinaperekedwa pa February 29, 2000, ndipo a khoti ananena kuti “ufulu wosankha” pa nkhani zimenezi “uyenera kulemekezedwa ngati mmene zimakhalira ndi ufulu wina wonse.” Kulimba mtima kwa Mlongo Takeda pomenyera ufulu wake wosankha yekha chithandizo cha mankhwala chogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo, kwathandiza kuti Mboni za ku Japan zizithandizidwa bwinobwino kuchipatala popanda kukhala ndi nkhawa yoti athiridwa magazi asakufuna.

Pablo Albarracini (Onani ndime 18 mpaka 20)

18-20. (a) Kodi khoti la apilo ku Argentina linatetezera bwanji ufulu wokana kuthiridwa magazi wa munthu yemwe anali ndi chikalata chosonyeza thandizo lomwe tingalandire? (b) Pa nkhani yogwiritsa ntchito magazi molakwika, kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika ku ulamuliro wa Khristu?

 18 Argentina. Kodi nzika za Ufumu zimachita chiyani kuti zinthu zisadzavute ngati pakufunika kusankha chithandizo cha mankhwala koma atakomoka? Timayenda ndi chikalata chovomerezeka ndi boma chomwe chimasonyeza thandizo lomwe tingalandire, ngati mmene anachitira M’bale Pablo Albarracini. M’mwezi wa May 2012, zigawenga zokhala ndi mfuti zinamuwombera kangapo pamene zinkafuna kumubera. Anagonekedwa m’chipatala ali chikomokere ndipo zinali zosatheka kuti afotokozere madokotala zoti sangalole kuthiridwa magazi. Koma anali ndi chikalata cholembedwa bwino chofotokoza maganizo ake chomwe analemba komanso kuchisainira kudakali zaka zoposa 4 zimenezi zisanachitike. Ngakhale kuti sanali bwino ndipo madokotala ankaona kuti akufunika kuthiridwa magazi kuti asafe, madokotalawo anali okonzeka kutsatira zomwe mwiniwakeyo anasankha. Koma bambo ake a Pablo, omwe sanali a Mboni za Yehova, anakatenga chikalata kukhoti chopatsa mphamvu madokotalawo kuti asatsatire zimene mwana wawoyo anasankha.

19 Nthawi yomweyo loya woimira mkazi wa Pablo anakachita apilo nkhaniyi kukhoti la apilo. Patangopita maola ochepa, khotilo linagamula nkhaniyi ndipo linasintha chigamulo cha khoti laling’ono lija. Khotili linauza madokotala kuti atsatire zimene wodwalayo analemba m’chikalata chake. Bambo ake a Pablo anachitanso apilo chigamulo chimenechi ku Khoti Lalikulu la m’dziko la Argentina. Koma khotili linapeza kuti “panalibe chifukwa chokayikirira kuti [zimene Pablo analemba m’chikalata chija kuti sakufuna kuthiridwa magazi] anazilemba akuganiza bwinobwino, akudziwa zimene akuchita komanso mogwirizana ndi ufulu wake.” Khotili linanena kuti: “Munthu aliyense wamkulu komanso yemwe akuganiza bwinobwino akhoza kusankhiratu chithandizo cha mankhwala chimene angakonde, ndipo angalandire kapena kukana zinthu zina . . . Dokotala amene akuthandiza munthuyo ayenera kutsatira zimene wodwalayo anasankha.”

Kodi inuyo munalemba zonse zofunikira pachikalata chanu chakuchipatala?

20 Panopa M’bale Albarracini anachira bwinobwino. Iye ndi mkazi wake amaona kuti anachita bwino kulemberatu chikalata chija. Kulemba chikalatachi kungaoneke ngati nkhani yaing’ono koma ndi yofunika kwambiri chifukwa kunasonyeza kuti m’baleyu ndi wokhulupirika ku Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Khristu. Kodi inuyo ndi banja lanu munalemberatu chikalata chanu?

April Cadoreth (Onani ndime 21 mpaka 24)

21-24. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Canada lipereke chigamulo chosangalatsa pa nkhani ya ana omwe sakufuna kuthiridwa magazi? (b) Kodi chigamulo chimenechi chingalimbikitse bwanji ana omwe amatumikira Yehova?

21 Canada. M’mayiko ambiri, makhoti amaona kuti makolo ali ndi ufulu wosankhira ana awo chithandizo choyenera cha mankhwala. Nthawi zina makhoti amavomereza kuti ana omwe angathe kusankha okha zinthu, ayenera kupatsidwa mwayi wosankha chithandizo chomwe angakonde. Izi ndi zomwe zinachitikira April Cadoreth. Ali ndi zaka 14, April anagonekedwa m’chipatala chifukwa cha vuto lomwe limachititsa kuti magazi azingotsikira m’mimba. Miyezi ingapo izi zisanachitike, iye anali atalemberatu chikalata chosonyeza kuti sakufuna kuthiridwa magazi ngakhale atachita ngozi. Dokotala amene ankamusamalira ananyalanyaza malangizo omveka bwino amene April analemba m’chikalatachi ndipo anapita kukhoti kukatenga chilolezo choti amuthirebe magazi.  Anamuthira magazi okwana madiripi atatu mokakamiza. Pambuyo pake April ananena kuti zimene zinamuchitikirazi n’chimodzimodzi ndi kugwiriridwa.

22 April limodzi ndi makolo ake anapita ndi nkhaniyi kukhoti. Patapita zaka ziwiri, mlanduwu unapititsidwa ku Khoti Lalikulu la m’dziko la Canada. Poyamba zinaoneka ngati kuti April waluza mlanduwu, koma zoona zake n’zakuti anawina chifukwa khotili linabweza ndalama zomwe anawononga pa mlanduwu ndiponso linagamula nkhaniyi mokomera iyeyo limodzi ndi ana ena omwe ankafuna kuti boma lizilemekeza ufulu wawo wosankha okha chithandizo cha mankhwala chimene angakonde. Khotilo linati: “Pa nkhani ya thandizo la mankhwala, ana amene sanakwanitse zaka 16 azipatsidwa mwayi wosonyeza ngati asankha okha thandizolo mwa kufuna kwawo komanso akudziwa chimene akuchita.”

23 Mlandu umenewu unali wapadera chifukwa unachititsa kuti Khoti Lalikulu lifotokoze momveka bwino ufulu umene ana amene angathe kusankha okha zinthu ali nawo. Chigamulo chimenechi chisanaperekedwe, makhoti a ku Canada anali ndi mphamvu yosankhira chithandizo ana omwe sanakwanitse zaka 16 ngati  akuona kuti chithandizocho n’choyeneradi kwa mwanayo. Koma pambuyo pa chigamulochi, khoti lililonse linalibe mphamvu yosankhira ana omwe sanakwanitse zaka 16 chithandizo chilichonse asanawapatse kaye mwayi wosonyeza ngati angathe kusankha okha chithandizo chimene akufuna.

“Ndimasangalala kuona kuti ndinathandizako pang’ono polemekeza dzina la Mulungu ndiponso kusonyeza kuti Satana ndi wabodza”

24 Kodi tingati mlandu umenewu, womwe unatenga zaka zitatu, unatha bwino? April amaona kuti unatha bwino. Panopa anachira bwinobwino ndipo ndi mpainiya wokhazikika. Iye anati: “Ndimasangalala kuona kuti ndinathandizako pang’ono polemekeza dzina la Mulungu ndiponso kusonyeza kuti Satana ndi wabodza.” Nkhani ya April ikusonyeza kuti ana akhoza kulimba mtima posonyeza kuti ndi nzika zodalirika za Ufumu wa Mulungu.Mat. 21:16.

Ufulu Wolera Ana Mogwirizana Ndi Mfundo za Yehova

25, 26. Kodi nthawi zina pamakhala mavuto otani banja likatha?

25 Yehova anapatsa makolo udindo wolera ana awo mogwirizana ndi mfundo zake. (Deut. 6:6-8; Aef. 6:4) Udindo umenewu ndi wovuta koma umakhala wovuta kwambiri ngati banja latha chifukwa makolo amasiyana maganizo pa nkhani ya njira yoyenera yolerera ana awo. Mwachitsanzo, kholo lomwe ndi Mboni limaona kuti choyenera ndi kulera anawo motsatira mfundo zachikhristu, pomwe kholo linalo, lomwe si Mboni, silingafune zimenezo. Komabe, kholo lomwe ndi Mbonilo liyenera kuzindikira kuti kutha kwa banja sikuthetsa udindo womwe kholo lililonse lili nawo wolera ana awo.

26 Nthawi zina kholo lomwe si Mboni likhoza kukasuma kukhoti kuti alipatse mphamvu yosunga anawo n’cholinga choti azipita nawo kutchalitchi kwake. Ena amanena kuti sibwino kuphunzitsa ana zinthu zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira. Amanena kuti kuchita zimenezi kungapangitse kuti anawo asakhale ndi mwayi wokondwerera tsiku lobadwa ndiponso maholide ena. Amanenanso kuti ngati patachitika ngozi, anawo sangapatsidwe magazi kuti apulumutse moyo wawo. Mwamwayi, makhoti ambiri amagamula nkhaniyi potengera zimene zingakhale zothandiza kwambiri kwa mwanayo, mosatengera chipembedzo cha makolo. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

27, 28. Kodi Khoti Lalikulu ku Ohio linagamula bwanji mlandu wonena kuti sibwino kuphunzitsa mwana kuti adzakhale wa Mboni za Yehova?

27 United States. Mu 1992, Khoti Lalikulu ku Ohio, linaweruza mlandu umene bambo wina yemwe si Mboni anakadandaula kuti sibwino kuti mwana wake wamng’ono aleredwe ndi mayi ake omwe ndi a Mboni chifukwa zimenezi zingachititse kuti nayenso adzakhale wa Mboni. Khoti laling’ono linagwirizana ndi maganizo amenewa ndipo linagamula kuti ndi bwino kuti mwanayo aleredwe ndi bamboyo. Khotilo linanena kuti mayi wa mwanayo, Jennifer Pater, akhoza kumapita kukaona mwanayo, koma anamulamula kuti “asamaphunzitse kapena kusonyeza mwanayo chinthu chilichonse chokhudzana ndi zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira.” Zimene a khoti laling’ono analamulazi zinali ndi mphamvu kwambiri chifukwa zinkatanthauza kuti Mlongo Pater sangafotokozere mwana wawo, Bobby, chilichonse chokhudza Baibulo kapena mfundo za makhalidwe abwino zimene limanena. Kodi mukuganiza kuti mlongoyu anamva bwanji ndi chigamulo chimenechi? Anakhumudwa  kwambiri koma anafotokoza kuti anaphunzira kukhala wodekha ndiponso kuyembekezera kuti Yehova ndi amene athetse nkhaniyo. Iye anati: “Pa nthawi yonseyi, Yehova sanandisiye ndekha.” Loya wake, mothandizidwa ndi gulu la Yehova, anachita apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu ku Ohio.

28 Khotili silinagwirizane ndi zimene khoti laling’ono lija linagamula, ndipo linanena kuti, “makolo ali ndi ufulu wophunzitsa ana awo, kuphatikizapo kuwaphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino kapena za chipembedzo zomwe iwowo amakhulupirira.” Khotilo linanena kuti khoti lilibe mphamvu yoletsa kholo kusunga mwana wake chifukwa cha chipembedzo chake, pokhapokha ngati pali umboni woti zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira zikhoza kusokoneza moyo kapena maganizo a mwanayo. A khoti anapeza kuti palibe umboni wosonyeza kuti zimene a Mboni amakhulupirira zikhoza kusokoneza moyo kapena maganizo a mwanayo.

Makhoti ambiri amagamula kuti ana aleredwe ndi kholo lomwe ndi Mkhristu

29-31. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti mlongo wina wa ku Denmark alandidwe mwana, nanga Khoti Lalikulu linagamula bwanji nkhaniyi?

29 Denmark. Anita Hansen anakumananso ndi vuto lofanana ndi limeneli pamene mwamuna wake woyamba anakadandaula kukhoti kuti apatsidwe chilolezo cholera mwana wawo wazaka 7, dzina lake Amanda. M’chaka cha 2000, khoti laling’ono linagamula kuti Mlongo Hansen ndi amene alere mwanayo, koma bambo ake a Amanda anachita apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu lomwe linagamula kuti khoti laling’ono lija linalakwitsa ndipo linagamula kuti bamboyo ndi amene alere mwanayo. Khotili linapereka chigamulo  chimenechi chifukwa chakuti makolowo anali ndi maganizo osiyana pa nkhani ya zimene amakhulupirira, choncho bamboyo ndi amene akhoza kuthetsa bwino nkhaniyi chifukwa ndiye mutu wa banja. Zimenezi zinachititsa kuti Mlongo Hansen alandidwe mwanayo chifukwa chakuti anali wa Mboni za Yehova.

30 Pa nthawi yonse ya mlanduwu, Mlongo Hansen ankavutika maganizo kwambiri moti nthawi zina sankadziwa zoti anene popemphera. Mlongoyu ananena kuti: “Mfundo za pa Aroma 8:26, 27 zinandilimbikitsa kwambiri. Nthawi zonse ndinkaona kuti Yehova ankamvetsa bwino zimene ndinkanena ndikamapemphera. Ndinkaona kuti Yehova ankandiyang’anira komanso anali nane pa nthawi yonseyo.”Werengani Salimo 32:8; Yesaya 41:10.

31 Mlongo Hansen anakapanga apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu ku Denmark. Pogamula mlanduwu Khotili linati: “Kuti tigamule bwinobwino nkhaniyi pangafunike kuchita kafukufuku wotithandiza kudziwa kholo limene lingalere bwino mwanayu.” Khotilo linanenanso kuti posankha kholo limene liyenera kulera mwanayo liyenera kuonanso zimene kholo lililonse limachita pakakhala kusemphana maganizo mosatengera zimene a Mboni za Yehova “amaphunzitsa komanso zimene amaganiza.” Zimene Khotili linagamula zinali zolimbikitsa kwambiri kwa Mlongo Hansen chifukwa Khotili linagamula kuti mwanayo aleredwe ndi mlongoyu. Khotili litafufuza, linapeza kuti mlongoyu ndi amene akhoza kulera bwino mwanayo.

32. Kodi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya latetezera bwanji makolo omwe ndi Mboni kuti asamasalidwe?

32 Mayiko osiyanasiyana a ku Europe. Nthawi zina milandu yokhudza amene ayenera kulera ana imavuta kwambiri mpaka imakafika ku makhoti akuluakulu. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya laweruzapo milandu ngati imeneyi. Pa milandu ina iwiri, khotili linanena kuti makhoti ang’onoang’ono amene anaweruza milanduyi poyamba, anagamula milanduyi potengera kuti munthuyo ndi wa Mboni kapena si wa Mboni. Linanenanso kuti kuweruza milandu mwa njira imeneyi n’kuchita zinthu mwatsankho ndipo linagamula kuti “n’kulakwa kugamula milandu pongotengera kusiyana kwa zipembedzo.” Mayi wina wa Mboni, yemwe nkhani yake inayenda bwino chifukwa cha zimene Khotili linagamula, ananena kuti: “Zinandipweteka kwambiri kuimbidwa mlandu woti ndinkasokoneza ana anga chifukwa ineyo ndinkaona kuti ndikuwathandiza kukhala ndi moyo wabwino komanso kuti azitsatira mfundo zachikhristu.”

33. Kodi makolo omwe ndi Mboni angatsatire bwanji mfundo ya pa Afilipi 4:5?

33 Makolo a Mboni amene akumenyera ufulu wolera ana awo kuti aziwaphunzitsa mfundo za m’Baibulo amayesetsa kukhala ololera. (Werengani Afilipi 4:5.) Makolo a Mboniwa amasangalala akapatsidwa ufulu wolera mwanayo potsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu, koma amadziwanso kuti kholo linalo lomwe si la Mboni, limakhalanso ndi udindo wolera mwanayo ngati likufuna. Kodi kholo lomwe ndi la Mboni limaona bwanji udindo wolera mwana?

34. Kodi makolo achikhristu angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Ayuda a m’nthawi ya Nehemiya?

34 Zimene zinkachitika m’nthawi ya Nehemiya zikhoza kutithandiza kuyankha funsoli. Ayuda ankagwira ntchito yokonza ndi kumanganso mpanda wa Yerusalemu mwakhama. Ankadziwa kuti  akamanga mpanda akhala otetezeka komanso ateteza mabanja awo kwa adani omwe anawazungulira. Pa chifukwa chimenechi, Nehemiya anawalimbikitsa kuti: “Menyerani nkhondo abale anu, ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” (Neh. 4:14) Pamenepatu Ayudawo anafunika kudzipereka kwambiri pa nkhondoyo. N’chimodzimodzinso masiku ano, makolo omwe ndi a Mboni za Yehova amadzipereka kuti alere ana awo potsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. Iwo amadziwa kuti ana awo amakumana ndi anthu amene amawanyengerera kuti achite zinthu zoipa akakhala kusukulu kapena m’dera limene akukhala. Nthawi zina anawa akhoza kuyamba makhalidwe oipa potengera zimene amawerenga, kumvetsera kapena zimene amaonera pa TV. Choncho makolo, muzichita zonse zomwe mungathe kuti mumenyere nkhondo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kuti akhale otetezeka. Zimenezi zingawathandize kuti akhale olimba mwauzimu.

Muzikhulupirira Kuti Yehova Apitiriza Kutsogolera Kulambira Koona

35, 36. Kodi kumenyera ufulu kumene Mboni za Yehova zachita kwathandiza bwanji, nanga inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

35 Yehova wakhala akudalitsa zimene gulu lake likuchita pomenyera ufulu wawo woti azilambira momasuka. Pomenyera ufulu wawo wa kulambira, anthu a Yehova akhala akuchitira umboni m’makhoti komanso kwa anthu ambiri. (Aroma 1:8) Milandu imene akhala akuwinayi yathandizanso anthu ambiri omwe si Mboni kuti akhale ndi ufulu. Komabe, monga anthu a Mulungu cholinga chathu si kumenyera ufulu wa anthu kapena kudzitchukitsa. Cholinga chachikulu cha Mboni za Yehova pochita zimenezi ndi kukhazikitsa ndiponso kupititsa patsogolo kulambira koona.Werengani Afilipi 1:7.

36 Tikhoza kuphunzira zambiri pa chikhulupiriro cha anthu amenewa omwe anamenyera ufulu wolambira Yehova. Nafenso tiyenera kupitiriza kukhala okhulupirika podziwa kuti Yehova akutithandiza pa ntchito yathu ndipo amatipatsa mphamvu kuti tizichita chifuniro chake.Yes. 54:17.