Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ufumu wa Mulungu Ukulamulira

 MUTU 8

Zinthu Zogwiritsa Ntchito Polalikira—Kukonza Mabuku Ogwiritsa Ntchito Polalikira Padziko Lonse

Zinthu Zogwiritsa Ntchito Polalikira—Kukonza Mabuku Ogwiritsa Ntchito Polalikira Padziko Lonse

CHOLINGA CHA MUTUWU

Yehova akupitirizabe kutipatsa zinthu zoti tizigwiritsa ntchito pophunzitsa anthu amitundu, mafuko ndi zinenero zosiyanasiyana

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire mu ufumu wonse wa Roma m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi tili ndi umboni wotani wosonyeza kuti Yehova akutithandiza masiku ano? (Onani bokosi lakuti, “ Uthenga Wabwino Ukufalitsidwa M’zinenero 670.”)

ANTHU amene anapita ku Yerusalemu sanakhulupirire zimene zinkachitika. Agalileya ankalankhula bwinobwino zinenero za mayiko ena ndipo anthu anachita chidwi kwambiri ndi zimene ankalankhulazo. Zimenezi zinachitika pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Pa nthawi imeneyi, ophunzira anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana modabwitsa ndipo umenewu unali umboni wakuti Mulungu akuwathandiza. (Werengani Machitidwe 2:1-8, 12, 15-17.) Anthu azikhalidwe komanso ochokera m’madera osiyanasiyana anamva uthenga wabwino umene atumwi analalikira pa nthawi imeneyi ndipo unafalikira m’madera onse a ufumu wa Roma.Akol. 1:23.

2 Masiku ano, atumiki a Mulungu salankhula zinenero zachilendo ngati mmene anachitira atumwi. Komabe, atumikiwa amamasulira uthenga wonena za Ufumu m’zinenero zoposa 670, zomwe ndi zochuluka kwambiri poyerekezera ndi zinenero zimene atumwi aja analankhula. (Mac. 2:9-11) Anthu a Mulungu afalitsa mabuku ambiri m’zinenero zochuluka moti uthenga wa Ufumu wafalikira padziko lonse. * Umenewu ndi umboni wosatsutsika wakuti Yehova akugwiritsa ntchito Mfumu Yesu Khristu kutsogolera ntchito yathu yolalikira. (Mat. 28:19, 20) Pamene tikukambirana zinthu zimene takhala tikugwiritsa ntchito pa zaka 100 zapitazi, onani mmene Mfumu yakhala ikutiphunzitsira kuti tizichita chidwi kwambiri ndi munthu aliyense payekha. Onaninso mmene Mfumuyi yakhala ikutilimbikitsira kuti tikhale aphunzitsi a Mawu a Mulungu.2 Tim. 2:2.

Mfumu Inathandiza Anthu Ake Kuti Abzale Mbewu za Choonadi

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene takhala tikugwiritsa ntchito, nanga zatithandiza bwanji?

3 Yesu anayerekeza “mawu a ufumu” ndi mbewu ndipo mtima wa munthu anauyerekezera ndi nthaka. (Mat. 13:18, 19) Mofanana ndi mlimi amene amagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana kuti akonze nthaka asanabzale mbewu zake, anthu a Yehova akhala akugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana pokonzekeretsa mitima ya anthu mamiliyoni ambiri kuti aphunzire za Ufumu. Zina mwa zinthu zimenezi zinagwira ntchito kwa nthawi yochepa pomwe zina, ngati mabuku ndiponso magazini, zikupitirizabe kugwira ntchito. Zinthu zonse zimene tikambirane m’mutu uno zathandiza anthu  amene amalengeza za Ufumuwu kulalikira kwa anthu pamasom’pamaso ndipo zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi njira zolalikira zimene takambirana m’mutu wapitawu.Mac. 5:42; 17:2, 3.

Abale akukonza magalamafoni ndi zokuzira mawu ku Toronto, m’dziko la Canada

4, 5. Kodi magalamafoni ankagwiritsidwa ntchito bwanji, nanga anali ndi mavuto otani?

4 Nkhani zojambulidwa. M’zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940, abale ankagwiritsa ntchito nkhani zofotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zinkajambulidwa pazimbale, kapena kuti malekodi. Kuti anthu amvetsere nkhanizi ankagwiritsa ntchito galamafoni. Nkhani iliyonse siinkapitirira mphindi 5 ndipo nkhani zina zinali ndi mitu ifupiifupi ngati “Utatu,” “Puligatoliyo” ndi “Ufumu.” Kodi ankagwiritsa ntchito bwanji galamafoni? M’bale Clayton Woodworth, Jr., amene anabatizidwa mu 1930 ku America ananena kuti: “Ndinkanyamula galamafoni yooneka ngati kasutikesi kakang’ono. Galamafoni inkakhala ndi malo oikapo chimbale ndipo kuti mawu ayambe kumveka ndinkaika kawilo pamalo oyenerera kumapeto kwa chimbalecho. Ndikafika pakhomo ndinkatsegula kasutikesiko n’kuika kawilo kaja pamalo ake kenako ndinkagogoda pachitseko. Ndiyeno mwininyumba akatsegula chitseko ndinkanena kuti, ‘Ndili ndi uthenga wofunika kwambiri umene ndikufuna kuti mumvetsere.’” Kodi anthu ankamvetsera? M’bale Woodworth ananena kuti: “Nthawi zambiri anthu ankamvetsera. Koma nthawi zina ankangotseka chitseko ndipo ena ankaganiza kuti ndikugulitsa magalamafoni.”

Pofika m’chaka cha 1940, panali nkhani zosiyanasiyana zojambulidwa zoposa 90 ndipo anali atapanga zimbale zoposa 1 miliyoni

5 Pofika m’chaka cha 1940, panali nkhani zosiyanasiyana zojambulidwa zoposa 90 ndipo anali atapanga zimbale zoposa 1 miliyoni. Pa nthawi imeneyo, M’bale John E. Barr amene ankachita upainiya ku Britain, yemwe patapita nthawi anatumikira m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti: “Pakati pa zaka za 1936 ndi 1945, sindinkalowa muutumiki popanda galamafoni moti ndinkasowa chochita ndikakhala kuti sindinayende ndi galamafoni. Zinkakhala zolimbikitsa kwambiri ukamamva mawu a M’bale Rutherford ndipo  ndinkamva ngati ndikuyenda naye. Komabe ukamagwiritsa ntchito galamafoni zinali zovuta kufika anthu pamtima chifukwa zinali zosatheka kusintha ulaliki kuti ugwirizane ndi munthu amene ukumulalikirayo.”

6, 7. (a) Kodi kugwiritsa ntchito timakadi kunali ndi ubwino komanso mavuto otani? (b) Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake kuti azilankhula muutumiki?

6 Timakadi tolalikirira. Kuyambira m’chaka cha 1933, ofalitsa anayamba kulimbikitsidwa kuti azigwiritsa ntchito timakadi akamalalikira khomo ndi khomo. Timakaditi tinkakhala tamasentimita 7.6 m’lifupi ndi masentimita 12.7 m’litali. Tinkakhala ndi uthenga wachidule wochokera m’Baibulo komanso buku limene munthuyo angaitanitse. Wofalitsa akafika pakhomo ankangopereka kakhadiko kwa mwininyumba n’kumupempha kuti awerenge. Lilian Kammerud, yemwe patapita nthawi anatumikira monga m’mishonale ku Puerto Rico ndi ku Argentina, ananena kuti: “Ndinkasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito timakadi polalikira.” Kodi n’chifukwa chiyani mlongoyu ankasangalala ndi timakaditi? Iye ananena kuti: “Ndikafika pakhomo ndinkasowa chonena koma timakaditi tinandithandiza kuti ndizolowere kulankhula ndi anthu.”

Timakadi tolalikirira (Chitaliyana)

7 M’bale David Reusch, yemwe anabatizidwa m’chaka cha 1918, ananena kuti: “Timakadi tolalikirira tinathandiza kwambiri abale chifukwa ambiri sankadziwa zoyenera kunena.” Komabe timakaditi tinali ndi mavuto ake. M’bale Reusch ananenanso kuti: “Zimene tinkachita polalikira zinkachititsa kuti anthu ena aziganiza kuti sititha kulankhula. Kunena zoona ambirife sitinkadziwadi kulankhula. Koma Yehova ankatikonzekeretsa kuti tiyambe kulankhula ndi anthu muutumiki. Pasanapite nthawi yaitali anatiphunzitsa kugwiritsa ntchito Malemba tikafika pakhomo la munthu. Zimenezi zinatheka chifukwa cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene inakhazikitsidwa m’zaka za m’ma 1940.”Werengani Yeremiya 1:6-9.

8. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukulola Khristu kukuphunzitsani?

8 Mabuku. Kuyambira m’chaka cha 1914, anthu a Yehova atulutsa mabuku oposa 100 ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Ena mwa mabuku amenewa anakonzedwa n’cholinga chothandiza atumiki a Mulungu kuti azilalikira mwaluso. Mlongo wina dzina lake Anna Larsen wa ku Denmark, yemwe wakhala akugwira ntchito yolalikira kwa zaka pafupifupi 70, ananena kuti: “Yehova anatithandiza kuti tikhale ndi luso pogwira ntchito yolalikirayi kudzera mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso kudzera m’mabuku amene tinalandira. Ndikukumbukira kuti buku loyamba linali ndi mutu wakuti, Theocratic Aid to Kingdom Publishers, ndipo linatuluka mu 1945. Kenako m’chaka cha 1946 panatulukanso buku lakuti, “Wokonzeka Mokwanira Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino.” Panopo tikugwiritsa ntchito buku lakuti, Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, lomwe linatuluka m’chaka cha 2001.” Kunena zoona, “ndife oyenera kukhala atumiki” chifukwa cha zimene Yehova watiphunzitsa kudzera mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso mabuku amene timagwiritsa ntchito m’sukuluyi. (2 Akor. 3:5, 6) Kodi inuyo munalembetsa mu Sukulu ya Utumiki? Kodi mumabweretsa buku lanu la Sukulu ya Utumiki mlungu uliwonse n’kumatsatira pamene woyang’anira sukulu akuwerenga mfundo zina m’bukuli?  Ngati mumachita zimenezi, ndiye kuti mukulola Khristu kukuphunzitsani kuti mukhale mphunzitsi wabwino.2 Akor. 9:6; 2 Tim. 2:15.

9, 10. (a) Kodi mabuku athandiza bwanji pa ntchito yobzala komanso kuthirira mbewu za choonadi? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mabukuwa akhaladi othandiza?

9 Kudzera m’gulu lake, Yehova watithandizanso potipatsa mabuku amene amafotokoza mosavuta zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo buku lakuti, Choonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wosatha, linatuluka m’chaka cha 1968 ndipo linathandiza anthu ambiri kumvetsa choonadi. Utumiki wa Ufumu wa November 1968, unanena kuti: “Anthu ambiri akufuna buku la Choonadi moti m’mwezi wa September fakitale yathu ya ku Brooklyn inawonjezera gulu la anthu kuti azigwira ntchito yosindikiza mabukuwa usiku.” Utumiki wa Ufumu womwewu unanenanso kuti: “Pa nthawi ina m’mwezi wa August anthu ofuna buku la Choonadi anali ambiri moti tinafunika kusindikiza mabuku oposa 1.5 miliyoni kuwonjezera pa mabuku amene tinali titasindikiza kale.” Pofika chaka cha 1982 mabuku oposa 100 miliyoni anali atasindikizidwa m’zinenero 116. Kuyambira m’chaka cha 1968 kufika chaka cha 1982, zomwe ndi zaka 14, buku la Choonadi linali litathandiza anthu oposa 1 miliyoni kuti akhale olengeza Ufumu. *

10 M’chaka cha 2005, munatuluka buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwe lathandiza anthu ambiri kuphunzira Baibulo. Mabuku pafupifupi 200 miliyoni asindikizidwa m’zinenero 256. Koma kodi bukuli lakhaladi lothandiza? Kuyambira m’chaka cha 2005 mpaka m’chaka cha 2012, zomwe ndi zaka 7 zokha, anthu pafupifupi 1.2 miliyoni ayamba kugwira ntchito yolengeza uthenga wabwino. Pa nthawi imeneyinso, chiwerengero cha anthu amene ankaphunzira Baibulo chinakwera kuchoka pa 6 miliyoni n’kuposa 8.7 miliyoni. Kunena zoona, Yehova akudalitsa khama lathu lobzala ndiponso kuthirira mbewu za choonadi cha Ufumu.Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.

11, 12. Pogwiritsa ntchito malemba amene ali m’ndimezi, fotokozani magulu a anthu amene amawalembera magazini athu.

11 Magazini. Poyambirira penipeni, Nsanja ya Olonda inkalembedwera anthu a “kagulu ka nkhosa” omwe ndi “oitanidwa kumwamba.” (Luka 12:32; Aheb. 3:1) Pa October 1, 1919, gulu la Yehova linatulutsanso magazini ina yomwe inkalembedwera anthu ena onse. Magaziniyi inayamba kukondedwa kwambiri ndi Ophunzira Baibulo komanso anthu ena onse moti kwa zaka zambiri magaziniwa ankasindikizidwa ochuluka kuposa magazini a Nsanja ya Olonda. Poyamba magaziniyi inkadziwika kuti The Golden Age. Mu 1937, inasintha n’kumadziwika kuti Consolation. Kenako m’chaka cha 1946 inayamba kudziwika kuti Galamukani!

12 Pa zaka zimene zapitazi, kaonekedwe ka magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kakhala kakusintha koma cholinga chake sichinasinthe. Cholinga cha magazini onsewa ndi kulengeza za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuthandiza anthu kuti azikhulupirira Baibulo. Masiku ano, tili ndi Nsanja ya Olonda yophunzira ndi yogawira. Magazini yophunzira imakonzedwera “antchito apakhomo” omwe ndi “kagulu kankhosa” komanso a “nkhosa zina.” * (Mat. 24:45; Yoh. 10:16) Magazini yogawira imakonzedwera anthu amene sakudziwa choonadi koma amalemekeza Mulungu komanso Baibulo. (Mac. 13:16) Ndipo magazini ya Galamukani! imakonzedwa  n’cholinga chofuna kuthandiza anthu amene amadziwa zinthu zochepa zonena za Mulungu woona, yemwe ndi Yehova, ndiponso Baibulo.Mac. 17:22, 23.

13. N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi magazini athu? (Kambiranani tchati chakuti “ Chiwerengero cha Mabuku Amene Afalitsidwa Padziko Lonse Lapansi.”)

13 Pamene chaka cha 2014 chimayamba, tinkasindikiza magazini a Galamukani! oposa 44 miliyoni ndiponso magazini a Nsanja ya Olonda pafupifupi 46 miliyoni mwezi uliwonse. Magazini a Galamukani! ankamasuliridwa m’zinenero pafupifupi 100 ndipo a Nsanja ya Olonda ankamasuliridwa m’zinenero zoposa 200. Zimenezi zikutanthauza kuti magaziniwa ankamasuliridwa ndiponso kufalitsidwa kwambiri kuposa magazini ena alionse padziko lonse. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa m’magaziniwa mumapezeka uthenga umene Yesu ananena kuti udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.Mat. 24:14.

14. Kodi takhala tikugwira mwakhama ntchito yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Baibulo. M’chaka cha 1896, M’bale Russell ndi anzake anasintha dzina la bungwe limene ankagwiritsa ntchito posindikiza mabuku n’cholinga choti likhale ndi mawu oti Baibulo. Bungweli linayamba kudziwika kuti Watch Tower Bible and Tract Society. Dzina limeneli ndi loyenera chifukwa timagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 24:27) Atumiki a Mulungu akhala akugwira mwakhama ntchito yofalitsa ndiponso kulimbikitsa anthu kuti aziwerenga Baibulo ndipo zimenezi n’zogwirizana kwambiri ndi cholinga cha bungwe lawo. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1926 tinasindikiza Baibulo la The Emphatic Diaglott, lomwe ndi la Malemba Achigiriki Achikhristu okha ndipo linkafalitsidwa ndi Benjamin Wilson. Kuyambira m’chaka cha 1942, tinasindikiza komanso kufalitsa mabaibulo pafupifupi 700,000 a King James Version. Patangopita zaka ziwiri zokha tinayamba kusindikiza Baibulo la American Standard Version, lomwe lili ndi dzina lakuti Yehova m’malo 6,823. Pofika chaka cha 1950, tinali titafalitsa mabaibulo oposa 250,000.

15, 16. (a) N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi Baibulo la Dziko Latsopano? (Kambiranani bokosi lakuti, “ Ntchito Yomasulira Baibulo Ikuchitika Mofulumira Kwambiri.”) (b) Kodi mungatani kuti Mawu a Mulungu azikufikani pamtima?

15 M’chaka cha 1950 tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu koma Baibulo lonse lathunthu linatuluka m’chaka cha 1961. Baibulo la Dziko Latsopano limalemekeza dzina la Yehova chifukwa tinabwezeretsa dzinali m’malo onse amene limapezeka m’Baibulo lachiheberi loyambirira. Dzina la Mulungu limapezeka maulendo okwana 237 m’Malemba enieni Achigiriki Achikhristu a Baibulo la Dziko Latsopano. Baibuloli lakonzedwapo maulendo angapo ndipo mu 2013 linakonzedwanso n’cholinga chofuna kutsimikizira kuti likumveka bwino komanso kuti n’losavuta kuwerenga. Pofika m’chaka cha 2013 Baibulo la Dziko Latsopano, lonse lathunthu kapena mbali yake, linali litafalitsidwa makope oposa 201 miliyoni m’zinenero 121.

16 Kodi anthu ena ananena chiyani atawerenga Baibulo la Dziko Latsopano m’chinenero chawo? Munthu wina wa ku Nepal ananena kuti: “Baibulo la chinepolizi limene tinali nalo linali lovuta kumva chifukwa anagwiritsa ntchito chinenero chakale kwambiri. Koma Baibulo ili ndi losavuta kumva chifukwa anagwiritsa ntchito mawu amene timalankhula tsiku lililonse.” Mzimayi wina wa ku Central African Republic atawerenga Baibulo la Chisango anayamba kulira ndipo ananena kuti: “Mawuwa ayamba kundifika pamtima.”  Mofanana ndi mzimayi ameneyu, ifenso tikamawerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, mawuwo adzatifika pamtima.Sal. 1:2; Mat. 22:36, 37.

Tiziyamikira Zinthu Zimene Timalandira

17. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira maphunziro komanso zinthu zina zimene mumalandira, nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?

17 Kodi mumayamikira maphunziro komanso zinthu zina zimene Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu, akutipatsa? Kodi mumapeza nthawi yowerenga mabuku amene gulu la Mulungu latulutsa komanso kugwiritsa ntchito zimene mwawerengazo pothandizira anthu ena? Ngati mumatero mungavomereze zimene Mlongo Opal Betler, yemwe anabatizidwa pa October 4, 1914 ananena. Mlongoyu anati: “Kwa zaka zambiri, ine ndi mwamuna wanga [Edward] tinkagwiritsa ntchito galamafoni komanso timakadi polalikira. Polalikira khomo ndi khomo tinkagawira mabuku, timabuku komanso magazini. Tinkagwira nawo ntchito yogawira zinthu zapadera komanso tinkalalikira pogwiritsa ntchito zikwangwani. Patapita nthawi tinaphunzitsidwa kuchita maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu amene asonyeza chidwi. Takhala ndi moyo wotanganidwa koma wosangalala kwambiri.” Yesu ananena kuti otsatira ake adzakhala akugwira ntchito yofesa komanso yokolola ndipo onse azidzasangalala pogwira ntchito imeneyi. Anthu mamiliyoni ambiri amene akhala ndi moyo ngati wa Mlongo Opal angavomereze zimene Yesu ananenazi.Werengani Yohane 4:35, 36.

18. Kodi ndi mwayi waukulu uti womwe tili nawo?

18 Anthu ambiri amene sanayambe kutumikira Mfumu akhoza kumaona anthu a Mulungu ngati anthu “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Koma taganizirani izi. Mfumuyo yasankha anthu wamba kuti agwire ntchito yofalitsa mabuku amene akumasuliridwa m’zinenero zambiri komanso akufalitsidwa kwambiri kuposa mabuku ena alionse. Kuwonjezera pamenepo, Mfumuyi yatiphunzitsa ndiponso kutilimbikitsa kuti polalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse tizigwiritsa ntchito zinthu zimene gulu lake limafalitsa. Kunenatu zoona, tili ndi mwayi waukulu wogwira ntchito yobzala mbewu za choonadi ndiponso kugwira ntchito yokolola limodzi ndi Khristu.

^ ndime 2 Zaka 10 zapitazi, anthu a Yehova afalitsa mabuku oposa 20 biliyoni ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Komanso anthu oposa 2.7 biliyoni padziko lonse akhoza kugwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org.

^ ndime 9 Mabuku ena amene athandiza atumiki a Mulungu pophunzitsa anthu ena choonadi cha m’Baibulo ndi Zeze wa Mulungu (linafalitsidwa mu 1921), “Mulungu Akhale Woona” (linafalitsidwa mu 1946), Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (linafalitsidwa mu 1982) ndi lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha (linafalitsidwa mu 1995).

^ ndime 12 Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 23 ndime 13, yomwe ikufotokoza momveka bwino kuti “antchito apakhomo” ndi ndani.