CHOLINGA CHA MUTUWU

Anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira kuti alalikire anthu ambiri

1, 2. (a) Kodi Yesu anachita chiyani pofuna kuti anthu ambiri amene ankawalalikira azimumva bwinobwino? (b) Kodi ophunzira okhulupirika a Khristu atsatira bwanji chitsanzo chake ndipo chifukwa chiyani?

TSIKU lina Yesu akuphunzitsa m’mphepete mwa nyanja, gulu la anthu linakhala momuzungulira. Kenako iye anakwera ngalawa n’kusunthira m’madzi pang’ono. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti madzi amene anali pakati pa ngalawayo ndi anthuwo athandiza kuti mawu ake azimveka bwino komanso kuti azimveka patali.​—Werengani Maliko 4:1, 2.

2 Ufumu usanabadwe komanso pambuyo poti wabadwa, ophunzira a Khristu okhulupirika anatsatira chitsanzo chake pofuna kuthandiza anthu kuti amve za Ufumu. Ophunzirawa anagwiritsa ntchito njira zatsopano komanso zosiyanasiyana polengeza uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu ambiri. Chifukwa cha kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga, Mfumu ikutsogolera anthu a Mulungu kupeza njira zatsopano zolalikirira. Tikufunitsitsa kulalikira kwa anthu ambiri mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Tiyeni tione njira zina zimene takhala tikugwiritsa ntchito kuti tilalikire anthu padziko lonse lapansi. Pamene tikuona njirazi, ganizirani zimene mungachite potsanzira chikhulupiriro cha anthu amene anagwira ntchito yolalikira uthenga wabwinowu.

Kulalikira Kwa Anthu Ambiri

3. Fotokozani mmene anthu odana ndi choonadi anakhumudwira titayamba kugwiritsa ntchito manyuzipepala.

3 Manyuzipepala: M’bale Russell ndi anzake ankafalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda kuyambira m’chaka cha 1879, ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wa Ufumu. Koma zikuoneka kuti chaka cha 1914 chitatsala pang’ono kukwana m’pamene Khristu anayendetsa zinthu kuti uthenga wabwino ulalikidwe kwa anthu ambiri. Zinthu zinayamba kusintha kuyambira m’chaka cha 1903. M’chaka chimenechi, Dr. E. L. Eaton yemwe anali mneneri wa matchalitchi achipulotesitanti ku Pennsylvania, anauza Charles Taze Russell kuti azichita mtsutso wa ziphunzitso za m’Baibulo. M’kalata imene Eaton analembera Russell, munali mawu akuti: “Ndikuona kuti anthu ambiri angachite chidwi kwambiri ndi mfundo zimene iweyo ndi ine timasiyana maganizo. . . . Choncho, ndikuona kuti zingakhale bwino kuchita mtsutso pa mfundo zimenezi pamaso pa anthu ambiri.” Poganizira kuti anthu ambiri angachitedi chidwi ndi zimenezi, M’bale Russell ndi anzake anakonza zoti zimene azikambirana pa mtsutsowo zizisindikizidwa m’nyuzipepala yodziwika bwino ya  The Pittsburgh Gazette. Nkhanizi zinadziwika kwambiri ndipo chifukwa chakuti M’bale Russell ankafotokoza mfundo momveka bwino komanso mogwira mtima, amene ankafalitsa nyuzipepalayi anakonza zoti mlungu uliwonse azisindikiza zimene M’bale Russell wafotokoza. Apa n’zoonekeratu kuti anthu amene ankadana ndi choonadi anakhumudwa kwambiri.

Pofika m’chaka cha 1914, manyuzipepala oposa 2,000 ankafalitsa maulaliki a M’bale Russell

4, 5. Kodi M’bale Russell anasonyeza khalidwe lotani, nanga abale amene ali ndi udindo angatsatire bwanji chitsanzo chake?

4 Pasanapite nthawi, manyuzipepala ambiri ankafuna kufalitsa nkhani za M’bale Russell. Pofika m’chaka cha 1908, mu Nsanja ya Olonda munali lipoti lakuti ulaliki wa M’bale Russell unkafalitsidwa “m’manyuzipepala okwana 11.” Pa nthawi imeneyi, abale amene ankadziwa bwino ntchito yofalitsa nkhani m’manyuzipepala, analangiza M’bale Russell kuti ngati atasamutsa maofesi a sosaite kuchoka ku Pittsburgh n’kupita ku mzinda umene unali wodziwika bwino ndiye kuti manyuzipepala ambiri akanayamba kufalitsa nkhani zake. Ataganizira mfundo zimenezi komanso mfundo zina, M’bale Russell anasamutsa maofesi n’kupita ku Brooklyn, ku New York, m’chaka cha 1909. Patangopita miyezi yochepa atasamuka, manyuzipepala okwana 400 anayamba kufalitsa nkhani zimene M’bale Russell ankakamba ndipo chiwerengerochi chinapitirizabe kukwera. Pa nthawi imene Ufumu unkakhazikitsidwa mu 1914, manyuzipepala oposa 2,000 ankafalitsa maulaliki komanso nkhani zimene M’bale Russell ankalemba ndipo ankazisindikiza m’zinenero 4.

5 Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova masiku ano angachite bwino kutengera chitsanzo cha M’bale Russell cha kudzichepetsa. Kodi angachite bwanji zimenezi? Popanga zosankha zikuluzikulu angachite bwino kuganizira malangizo a anthu ena.​—Werengani Miyambo 15:22.

6. Kodi nkhani zofotokoza choonadi zimene zinkatuluka m’manyuzipepala zinathandiza bwanji munthu wina?

6 Nkhani zimene zinkatuluka m’manyuzipepala amenewa zinasintha moyo wa anthu ambiri. (Aheb. 4:12) Mwachitsanzo, Ora Hetzel amene anabatizidwa m’chaka cha 1917, ndi munthu mmodzi mwa anthu ambiri amene anaphunzira choonadi chifukwa chowerenga nkhani zimenezi. Ora ananena kuti: “Nditakwatiwa ndinapita kukaona amayi anga ku Rochester, Minnesota. Nditafika ndinapeza mayi anga akudula nkhani za munyuzipepala zokambidwa ndi M’bale Russell ndipo anandifotokozera zimene anaphunzira m’nkhanizi.” Ora anaphunzira choonadi ndipo anagwira ntchito yolengeza za Ufumu wa Mulungu kwa zaka pafupifupi 60.

7. N’chiyani chinachititsa abale amene ankatsogolera gulu kuganiza zosiya kugwiritsa ntchito manyuzipepala polalikira?

7 Koma m’chaka cha 1916, panachitika zinthu ziwiri zimene zinachititsa abale kuganiza zosiya kugwiritsa ntchito manyuzipepala polalikira. Choyamba, kupeza zinthu zogwiritsa ntchito posindikiza kunali kovuta chifukwa cha nkhondo yaikulu imene inkachitika. Mu 1916, dipatimenti yoona za manyuzipepala ya ku nthambi ya Britain inafotokoza kuti: “Panopa pali manyuzipepala oposa 30 okha amene akufalitsabe maulaliki athu. Sitikukayikira kuti chiwerengerochi chitsika chifukwa cha kukwera mtengo kwa mapepala.” Chachiwiri chinali imfa ya M’bale Russell pa October 31, 1916. Mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1916,  munali chilengezo chakuti: “Tsopano popeza M’bale Russell wamwalira, tasiya kufalitsa maulaliki m’manyuzipepala.” Ngakhale kuti anasiya kugwiritsa ntchito manyuzipepala polalikira, anapitiriza kugwiritsa ntchito njira zina. Mwachitsanzo, ankaonetsa “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” ndipo ntchito yolalikira inapitiriza kuyenda bwino.

8. Fotokozani mmene zinalili pokonza “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.”

8 Kuonetsa zithunzi. M’bale Russell ndi anzake anagwira ntchito yokonza “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” kwa zaka pafupifupi zitatu ndipo anatulutsa seweroli m’chaka cha 1914. (Miy. 21:5) Seweroli linali lokonzedwa mwaluso kwambiri chifukwa ankaonetsa zithunzi za zinthu zoti zikuyenda komanso zithunzi zina zosiyanasiyana ndipo pankamveka mawu. Anagwiritsa ntchito anthu ambiri komanso zinyama popanga zigawo zosiyanasiyana zofotokoza nkhani za m’Baibulo. Lipoti lina lomwe linalembedwa mu 1913 linanena kuti: “Popanga chigawo chofotokoza za Nowa, chomwe chinali ndi mawu komanso zithunzi zomwe  zinkayenda, anagwiritsa ntchito nyama zambiri komanso anthu ndipo ankawajambula akuyerekezera mmene zinthu zinalili nthawi ya Nowa.” Abale ndi alongo aluso ochokera ku London, ku New York, ku Paris, ndiponso ku Philadelphia ankajambula ndi kuchekenira pamanja zithunzi zimene zinkaonetsedwa mu seweroli.

9. N’chifukwa chiyani anatenga nthawi yaitali komanso kugwiritsa ntchito ndalama zambiri popanga “Sewero la Pakanema”?

9 Koma kodi n’chifukwa chiyani anatenga nthawi yaitali komanso kugwiritsa ntchito ndalama zambiri popanga seweroli? Pa misonkhano imene inachitika mu 1913 panawerengedwa chigamulo chakuti: “Tikaona mmene anthu ku America akukondera mafilimu, makatuni, zithunzi zimene zimajambulidwa m’manyuzipepala ndi m’magazini, tikukhulupirira ndipo tili ndi zifukwa zomveka, kuti ifeyo pokhala alaliki amene tikupita patsogolo komanso amene tikuphunzitsa anthu Baibulo, tiyenera kugwiritsa ntchito mafilimu ndiponso zithunzi kuti tithe kuwafika anthu pamtima.”

Pamwamba: Makina amene ankaonetsera “Sewero la Pakanema”; Pansi Zithunzi zojambula pamanja zimene ankazionetsa mu “Sewero la Pakanema”

10. Kodi “Sewero la Pakanema” linaonetsedwa m’mayiko ati?

10 M’chaka cha 1914, seweroli ankalionetsa m’mizinda 80 tsiku lililonse. Anthu pafupifupi 8 miliyoni a ku America ndi ku Canada anaonera seweroli. M’chaka chomwechi, anthu a ku Australia, Britain, Denmark, Finland, Germany, New Zealand, Norway, Sweden, ndi Switzerland anaoneranso seweroli. Ndiyeno anakonzanso sewero lofanana ndi lomweli lomwe linkatchedwa “Eureka Drama” koma munalibe zithunzi zosonyeza anthu akuyenda. Seweroli linali losawonongetsa ndalama zambiri komanso zinthu zofunika pa seweroli zinali zosavuta kunyamula. Mmene chimafika chaka cha 1916, n’kuti masewerowa atamasuliridwa m’zinenero zingapo. “Sewero la Pakanema” kapena la “Eureka Drama” linamasuliridwa mu Chiameniya, Chidano cha ku Norway, Chifalansa, Chigiriki, Chijeremani, Chipolishi, Chisipanishi, Chiswidishi ndi Chitaliyana.

Mu 1914, ankaonetsa “Sewero la Pakanema” m’maholo akuluakulu omwe ankadzaza kwambiri ndi anthu

11, 12. Kodi mnyamata wina anachita chiyani ataonera “Sewero la Pakanema,” ndipo anapereka chitsanzo chotani?

11 “Sewero la Pakanema” lomwe linamasuliridwa m’Chifalansa linafika pamtima mnyamata wina wazaka 18, dzina lake Charles Rohner. Iye ananena kuti: “Ndinaonera seweroli m’tawuni yakwathu ku Colmar, m’chigawo cha Alsace, m’dziko la France. Seweroli litangoyamba ndinachita chidwi ndi mmene mfundo za choonadi cha m’Baibulo zinafotokozedwera momveka bwino.”

12 Kenako Charles anabatizidwa ndipo mu 1922 anayamba utumiki wa nthawi zonse. Imodzi mwa ntchito zimene ankagwira inali yothandiza kuonetsa nawo “Sewero la Pakanema” ku France. Pofotokoza zimene ankachita, Charles ananena kuti: “Ndinali ndi ntchito zambiri. Ndinkaimba vayolini, ndinali mtumiki woona za ndalama komanso ndinali mtumiki wa mabuku. Komanso ankandipempha kuti ndiziuza anthu kukhala chete sewero lisanayambe. Pa nthawi yopuma, tinkagawira mabuku ndipo m’bale ndi mlongo aliyense ankakhala ndi mabuku okwanira oti agawe m’kachigawo kamene wapatsidwa. Pakhomo la holo yomwe tikuonetsera kanemayo pankakhalanso matebulo omwe tinkaikapo mabuku ambiri.” Mu 1925, Charles anaitanidwa kukatumikira ku Beteli ya ku Brooklyn, New York. Ali kumeneko anapatsidwa ntchito yotsogolera oimba omwe ankamveka pa wailesi ya WBBR yomwe inali itangotsegulidwa kumene. Tikaganizira za zimene Charles anachita, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka  kuchita utumiki wina uliwonse umene ndapatsidwa pothandiza nawo ntchito yolengeza uthenga wa Ufumu?’​—Werengani Yesaya 6:8.

13, 14. Fotokozani mmene anagwiritsira ntchito wailesi pofalitsa uthenga wabwino? (Onaninso bokosi lakuti, “ Mapulogalamu Amene Ankaulitsidwa pa Wailesi ya WBBR” ndiponso lakuti “ Msonkhano Wosaiwalika.”)

13 Wailesi. M’zaka za m’ma 1920, abale anayamba kusiya pang’onopang’ono kugwiritsa ntchito “Sewero la Pakanema” polalikira. Pa nthawiyi wailesi inayamba kuoneka kuti ndi njira yothandiza kwambiri pofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Pa April 16, 1922, M’bale Rutherford analankhula pa wailesi kuchokera muholo yotchedwa Metropolitan Opera House ku Philadel-phia, ku Pennsylvania. Iye anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa,” ndipo anthu pafupifupi 50,000 anamvetsera nkhaniyi. Ndiyeno mu 1923, anaulutsa koyamba nkhani zimene zinakambidwa pa msonkhano. Poyamba abale ankalipira ku mawailesi a anthu ena kuti aulutse nkhani zawo, koma kenako anaona kuti angachite bwino kukhalanso ndi siteshoni yawoyawo. Siteshoniyi inamangidwa ku Staten Island, ku New York ndipo inkadziwika kuti WBBR. Siteshoniyi inayamba kugwira ntchito pa February 24, 1924.

Mu 1922 anthu pafupifupi 50,000 anamvetsera nkhani pa wailesi ya mutu wakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa”

14 Pofotokoza cholinga cha wailesi ya WBBR, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1924, inanena kuti: “Tikukhulupirira kuti wailesiyi itithandiza kuti tisamawononge ndalama zambiri komanso njira imeneyi itithandiza kufalitsa uthenga wa choonadi kwa anthu ambiri kuposa njira zimene takhala tikugwiritsa ntchito m’mbuyomu.” Magaziniyi inanenanso kuti: “Ngati Ambuye angaone kuti n’koyenera kuti timangenso masiteshoni ena n’cholinga choti uthenga wa choonadi ufalikire, ndiye kuti adzaperekanso ndalama zogwirira ntchitoyo.” (Sal. 127:1) Mmene chimafika chaka cha 1926, anthu a Yehova anali ndi masiteshoni okwana 6 ndipo awiri anali ku America. Yoyamba inali ku New York ndipo inkadziwika ndi dzina lakuti WBBR, pamene yachiwiri inali kufupi ndi ku Chicago ndipo inkadziwika ndi dzina lakuti WORD. Masiteshoni ena 4 anali ku Alberta, British Columbia, Ontario ndi ku Saskatchewan m’dziko la Canada.

15, 16. (a) Kodi atsogoleri amatchalitchi amene amati ndi achikhristu a ku Canada anachita chiyani posonyeza kuti sakusangalala ndi maulaliki athu a pa wailesi? (b) Kodi kulalikira pa wailesi komanso khomo ndi khomo kunathandiza bwanji?

15 Atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu sanasangalale kuona kuti anthu ambiri akumvetsera mawailesi amenewa. Albert Hoffman, amene ankadziwa bwino ntchito imene inkachitika ku Saskatchewan, ku Canada, ananena kuti: “Anthu ambiri anayamba kudziwa za Ophunzira Baibulo [lomwe linali dzina la Mboni za Yehova pa nthawiyo]. Anthu ambiri ankamvetsera bwinobwino uthenga wathu mpaka m’chaka cha 1928 pamene atsogoleri a zipembedzo anakakamiza akuluakulu a boma kuti atseke mawailesi onse a ku Canada amene ankayendetsedwa ndi Ophunzira Baibulo. Zimenezi zinachitikadi chifukwa boma linalanda zikalata zonse zowalola kuti aziulutsa mawu.”

16 Ngakhale kuti masiteshoni athu anatsekedwa m’dziko la Canada, uthenga wa m’Baibulo unapitirizabe kuulutsidwa chifukwa abale ankalipira mawailesi a anthu ena kuti aziulutsirapo uthengawo. (Mat. 10:23) Pofuna kuthandiza anthu ambiri kuti azimvera maulaliki a pa wailesi, anakonza zoti m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndi The Golden Age muzikhala mayina a mawailesi  amene ankaulutsa uthengawu. Zimenezi zinkathandiza ofalitsa akamalalikira khomo ndi khomo kuti azilimbikitsa anthu kumvetsera maulaliki amene ankaulutsidwa pa mawailesiwo. Kodi zimenezi zinathandiza? Mu The Bulletin ya mwezi wa January 1931, munali mawu akuti: “Maulaliki a pa wailesi alimbikitsa kwambiri abale pamene akugwira ntchito yolalikira khomo ndi khomo. Talandira malipoti osonyeza kuti anthu ambiri akhala akumvetsera maulalikiwa ndipo ayamba kulandira mabuku athu chifukwa chomvetsera maulaliki a M’bale Rutherford.” Munalinso mawu akuti kugwiritsa ntchito wailesi komanso kulalikira khomo ndi khomo ndi “njira ziwiri zikuluzikulu zimene gulu la Ambuye likugwiritsa ntchito polalikira.”

17, 18. Fotokozani ubwino wogwiritsa ntchito wailesi ngakhale kuti tinasiya kugwiritsa ntchito njira imeneyi.

17 M’zaka za m’ma 1930, anthu otsutsa anayamba kuchita zinthu zosonyeza kuti sankagwirizana ndi zoti tizigwiritsa ntchito masiteshoni a anthu ena. Choncho chakumapeto kwa chaka cha 1937, anthu a Yehova anachepetsa zogwiritsa ntchito wailesi ndipo anayamba kulimbikitsa kwambiri zolalikira khomo ndi khomo. * Komabe, ulaliki wa pa wailesi unkathandizabe kwambiri pofalitsa uthenga wa Ufumu kwa anthu okhala kumadera akutali kapena komwe kunali kovuta kulalikira chifukwa cha mavuto a zandale. Mwachitsanzo, kuyambira mu 1951 mpaka mu 1991 siteshoni inayake yomwe inali ku West Berlin, ku Germany, nthawi zambiri inkaulutsa nkhani za m’Baibulo n’cholinga choti anthu amene ankakhala m’dera limene pa nthawi imeneyo linali East Germany, azimvetsera uthenga wa Ufumu. Kuyambira m’chaka cha 1961 wailesi ya boma ku Suriname, m’dziko la South America inali ndi pulogalamu ya mphindi 15 yomwe ankaulutsapo nkhani za m’Baibulo. Wailesiyi inachita zimenezi kwa zaka zoposa 30. Kuyambira m’chaka cha 1969 kufika m’chaka cha 1977, gulu lathu linajambula nkhani zokwana 350 zokhala ndi mutu wakuti “Malemba Onse ndi Opindulitsa,” zomwe ankaziulutsa pa wailesi. Masiteshoni okwana 291 ankaulutsa nkhanizi m’madera okwana 48 a ku America. Mu 1996, siteshoni ya mumzinda wa Apia, womwe ndi likulu la dziko la Samoa ku South Pacific, inkaulutsa pulogalamu ya mutu wakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” mlungu uliwonse.

18 Pamene timayandikira zaka za m’ma 2000, tinasiya kugwiritsa ntchito wailesi pofalitsa uthenga wabwino. Komabe, tinapeza njira ina yomwe ikuthandiza kuti tizilalikira uthenga wabwino kwa anthu ambiri.

19, 20. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova anayamba kugwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org, ndipo yathandiza bwanji kufalitsa uthenga wabwino? (Onaninso bokosi lakuti “ JW.ORG.”)

19 Intaneti. Pofika m’chaka cha 2013, n’kuti anthu oposa 2.7 biliyoni padziko lonse lapansi akugwiritsa ntchito intaneti. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu 40 pa 100 alionse padziko lapansi amagwiritsa ntchito intaneti. Malinga ndi kafukufuku wina, pafupifupi anthu 2 biliyoni amatsegula intaneti pafoni kapena pa zipangizo zina za m’manja. Chiwerengero chimenechi chikuwonjezeka padziko lonse koma ku Africa n’kumene anthu ogwiritsa ntchito intaneti akuwonjezeka kwambiri. Panopa anthu oposa 90 miliyoni amagwiritsa ntchito intaneti pafoni kapena pa zipangizo  za manja. Kubwera kwa intaneti kwachititsa kuti anthu ambiri azitha kufufuza, kuwerenga ndiponso kutumizirana zinthu mosavuta.

20 Kuyambira m’chaka cha 1997, atumiki a Yehova anayamba kugwiritsa ntchito intaneti. M’chaka cha 2013, zinenero zoposa 300 zinayamba kugwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org. Pa webusaitiyi pali mabuku komanso zinthu zina zofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero zoposa 520. Tsiku lililonse, webusaitiyi imatsegulidwa ndi anthu pafupifupi maulendo 750,000. Mwezi uliwonse anthu amakopera mabuku oposa 3 miliyoni, magazini 4 miliyoni komanso zinthu zomvetsera zokwana 22 miliyoni.

21. Kodi mwaphunzira chiyani poona mmene Sina anaphunzirira choonadi?

21 Webusaitiyi yathandizanso kwambiri pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ngakhale m’madera amene ntchito yolalikira ndi yoletsedwa. Mwachitsanzo, chakumayambiriro kwa chaka cha 2013, munthu wina dzina lake Sina atadziwa kuti pali webusaiti ya jw.org anaimba foni kulikulu lathu ku America ndipo anayamba kufunsa mafunso ambiri okhudza nkhani za m’Baibulo. Zimenezi zinali zochititsa chidwi chifukwa Sina anakulira m’banja lachisilamu ndipo amakhala m’mudzi winawake wakutali m’dziko limene ntchito ya Mboni za Yehova ndi yoletsedwa. Kenako wa Mboni wina wa ku America anakonza zoti aziphunzira Baibulo ndi Sina kawiri pa mlungu. Iwo amachita phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito intaneti.

Kuphunzira Ndi Munthu Payekha

22, 23. (a) Kodi njira zolalikira kwa anthu ambiri zinalowa m’malo mwa njira yolalikira khomo ndi khomo? (b) Kodi Mfumu yadalitsa bwanji khama lathu?

22 Pa njira zonse zimene takhala tikugwiritsa ntchito kuti tilalikire anthu ambiri, monga manyuzipepala, Sewero la Pakanema, mapulogalamu a pa wailesi, ndiponso webusaiti, palibe njira imene inalowa m’malo mwa ulaliki wa khomo ndi khomo. Tikutero  chifukwa chakuti anthu a Yehova amatsatira chitsanzo cha Yesu. N’zoona kuti Yesu ankalalikira kwa anthu ambiri koma cholinga chake chinali kuthandiza munthu aliyense payekha. (Luka 19:1-5) Yesu anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azilalikira kwa munthu aliyense payekha ndipo anawauza uthenga woti azikalalikira. (Werengani Luka 10:1, 8-11.) Mmene taonera m’Mutu 6, abale amene ali ndi udindo mumpingo nthawi zonse amalimbikitsa mtumiki wa Yehova aliyense kuti azilalikira kwa anthu pamasom’pamaso.​—Mac. 5:42; 20:20.

23 Tsopano papita zaka 100 kuchokera pamene Ufumu unabadwa ndipo anthu oposa 7.9 miliyoni akugwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu ena zimene Mulungu amafuna. Kunena zoona, Mfumu yadalitsa njira zimene takhala tikugwiritsa ntchito polengeza za Ufumu. M’mutu wotsatira tidzaona kuti Mulungu watipatsa zinthu zomwe zatithandiza pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino kwa anthu a mitundu, mafuko ndiponso zinenero zosiyanasiyana.​—Chiv. 14:6.

^ ndime 17 Mu 1957 abale amene ankatsogolera gulu anakonza zotseka siteshoni youlutsira mawu yomaliza ya WBBR ku New York.