TAYEREKEZERANI kuti mwakonzekera kuti mulowe muutumiki tsiku limene simupita kuntchito. Mukukayikira pang’ono chifukwa mukumva kutopa ndipo mukungofuna kupumula. Ndiyeno mukupemphera kuti Mulungu akupatseni mphamvu kenako mukunyamuka. Mukulowa muutumiki ndi mlongo wokhulupirika wachikulire yemwe ndi wokoma mtima komanso akupirira mavuto ambiri. Zimenezi zikukukhudzani mtima kwambiri. Pamene mukulalikira kunyumba ndi nyumba, mukukumbukira kuti abale ndi alongo anu padziko lonse lapansi akugwiranso ntchito yomweyi. Abale ndi alongowa akugawira mabuku ofanana ndi amene inuyo mukugawira komanso akugwiritsa ntchito malangizo amene inunso mumalandira. Pamene mukubwerera kunyumba mukuona kuti mwalimbikitsidwa kwambiri ndipo mukusangalala kuti munasankha kulowa muutumiki.

Panopa ntchito yaikulu ya Ufumu wa Mulungu ndi kulalikira. Yesu analosera kuti m’masiku otsiriza ntchito yolalikira izidzachitika padziko lonse. (Mat. 24:14) Kodi ulosi umenewu wakwaniritsidwa bwanji? M’gawo limeneli tikambirana zimene anthu akhala akuchita, njira zimene akhala akutsatira komanso zipangizo zimene zathandiza kuti anthu ambiri padziko lonse aone kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni.