Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ufumu wa Mulungu Ukulamulira

 MUTU 3

Yehova Anathandiza Anthu Kudziwa Cholinga Chake

Yehova Anathandiza Anthu Kudziwa Cholinga Chake

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kudziwa zimene Yehova wakhala akuchita pothandiza anthu amene amamuopa kumvetsa pang’onopang’ono cholinga chake

1, 2. Kodi Yehova wakhala akuthandiza bwanji anthu kudziwa cholinga chake?

MAKOLO achikondi amauza ana awo nkhani zokhudza banja lawo. Koma sikuti amangowauza chilichonse. Amawauza nkhani zokhazo zimene akudziwa kuti anawo angakwanitse kuzimvetsa.

2 N’zimenenso Yehova amachita. Iye wakhala akuthandiza anthu kudziwa cholinga chake pang’onopang’ono ndipo wakhala akuchita zimenezi pa nthawi imene iye waona kuti ndi yoyenera. Tiyeni tikambirane mwachidule mmene Yehova wakhala akuthandizira anthu ake kudziwa za Ufumu wake.

N’chifukwa Chiyani Tikufunikira Ufumu wa Mulungu?

3, 4. Kodi Yehova analemberatu mmene moyo wa munthu aliyense udzakhalire? Fotokozani.

3 Pamene Yehova ankalenga anthu, sanakonze zoti padzakhale Ufumu wa Mesiya. Izi zili choncho chifukwa Yehova analenga anthu ndi ufulu wosankha zochita ndipo sanalemberetu mmene moyo wa munthu aliyense udzakhalire. Iye anauza Adamu ndi Hava cholinga chake cholengera anthu kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Gen. 1:28) Yehova ankayembekezeranso kuti anthu amenewa azimvera malamulo ake. (Gen. 2:16, 17) Adamu ndi Hava akanatha kusankha kuti akhale okhulupirika kwa Yehova. Iwo ndi ana awo akanakhala kuti anamvera Mulungu, sipakanafunikiranso Ufumu wa Khristu kuti ukwaniritse cholinga cha Mulungu. Bwenzi panopa dziko lonse litadzaza ndi anthu angwiro okhaokha omwe amatumikira Yehova.

4 Kupanduka kwa Satana komanso Adamu ndi Hava sikunapangitse kuti Yehova asinthe cholinga chake choti dziko lapansili lidzaze ndi anthu angwiro. M’malomwake, Yehova anangosintha njira yokwaniritsira cholinga chakecho. Cholinga chake sichili ngati sitima yomwe imangotsatira njanji kuti ikafike komwe ikupita ndipo ikhoza kusokonekera ngati wina atasokoneza njanjiyo. Yehova akanena zomwe akufuna, palibe aliyense amene angazilepheretse. (Werengani Yesaya 55:11.) Ngati mavuto ena asokoneza njira imene amafuna kutsatira pokwaniritsa cholinga chake, Yehova amagwiritsa ntchito njira ina. * (Eks. 3:14, 15) Akaona kuti n’zofunikira, iye amadziwitsa atumiki ake okhulupirika za njira yatsopano yomwe agwiritse ntchito pokwaniritsa cholingacho.

5. Kodi Yehova anatani Adamu ndi Hava atapanduka?

 5 Adamu ndi Hava atapanduka m’munda wa Edeni, Yehova anakonza zokhazikitsa Ufumu. (Mat. 25:34) Kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunachititsa kuti moyo wa anthu usokonekere koma Yehova anayamba kufotokoza za Ufumuwu monga njira imene adzagwiritse ntchito pothandiza anthu kuti adzakhalenso ndi moyo wabwino ndiponso pothetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa cha mapulani a Satana ofuna kulamulira dzikoli. (Gen. 3:14-19) Komabe, Yehova sanafotokoze kamodzin’kamodzi zonse zokhudza Ufumuwu.

Yehova Anayamba Kuulula za Ufumuwo

6. Kodi Yehova analonjeza chiyani, nanga pa nthawiyi sanafotokoze chiyani?

6 Mu ulosi wake woyamba, Yehova analonjeza kuti kudzabwera “mbewu” imene idzaphwanye njoka. (Werengani Genesis 3:15.) Komabe pa nthawiyi sanafotokoze kuti mbewuyi ndi ndani, nanga mbewu ya njoka ndi ndani. Ndipo Yehova sanafotokoze zimenezi mpaka patadutsa zaka zoposa 2,000. *

7. N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha Abulahamu kuti adzakhale kholo la mbewu yolonjezedwa, nanga tikuphunzirapo chiyani?

7 Kenako, Yehova anasankha Abulahamu kuti ndi amene adzakhale kholo la mbewuyo. Abulahamu anasankhidwa chifukwa chakuti ‘ankamvera mawu a Yehova.’ (Gen. 22:18) Nkhani imeneyi ikutiphunzitsa kuti Yehova amaulula cholinga chake kwa anthu okhawo amene amamuopa.Werengani Salimo 25:14.

8, 9. Kodi Yehova anaulula chiyani kwa Abulahamu ndi Yakobo?

8 Kudzera mwa mngelo, Yehova anaulula koyamba kwa Abulahamu, yemwe anali bwenzi lake, mfundo yofunika kwambiri yakuti mbewu imeneyi idzakhala munthu. (Gen. 22:15-17; Yak. 2:23) Koma kodi munthu ameneyu adzaphwanya bwanji mutu wa njoka? Kodi njokayo inali ndani? Zimene Yehova anaulula pambuyo pake zinayankha mafunso amenewa.

9 Yehova anakonza zoti mbewu imeneyi idzabadwe kudzera mwa Yakobo, yemwe anali chidzukulu cha Abulahamu. Yakobo ankakhulupirira kwambiri Mulungu. (Gen. 28:13-22) Kudzera mwa Yakobo, Yehova anaulula kuti Mbewu Yolonjezedwayo idzakhala chidzukulu cha Yuda, mwana wa Yakobo. Yakobo analosera kuti chidzukulu cha Yuda chimenechi chidzalandira “ndodo yachifumu,” yomwe ndi ndodo yosonyeza kuti wapatsidwa ulamuliro, komanso analosera kuti “mitundu ya anthu idzamumvera.” (Gen. 49:1, 10) Pamenepa, Yehova anasonyeza kuti Mbewu Yolonjezedwayo idzakhala wolamulira, kapena kuti mfumu.

10, 11. N’chifukwa chiyani Yehova anaulula cholinga chake kwa Davide ndi Danieli?

10 Patadutsa zaka 650 kuchokera pamene Yuda anamwalira, Yehova anaululanso zinthu zina zokhudza cholinga chake kwa Mfumu Davide, yemwe anali chidzukulu cha Yuda. Yehova anafotokoza kuti Davide anali “munthu wapamtima pake.” (1 Sam. 13:14; 17:12; Mac. 13:22) Davide ankaopa Mulungu, n’chifukwa chake Yehova anasankha kuchita naye pangano ndipo anamulonjeza kuti mmodzi mwa zidzukulu zake adzakhala wolamulira mpaka kalekale.2 Sam. 7:8, 12-16.

 11 Patadutsa zaka pafupifupi 500, Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Danieli kuulula chaka chenicheni chimene Wodzozedwayo, kapena kuti Mesiya, adzaonekere padziko lapansi. (Dan. 9:25) Yehova ankaona kuti Danieli anali “munthu wokondedwa kwambiri,” chifukwa chakuti Danieliyo ankamutumikira mosalekeza komanso ankamulemekeza kuchokera pansi pa mtima.Dan. 6:16; 9:22, 23.

12. Kodi Danieli anauzidwa kuti achite chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anauzidwa zimenezi?

12 Ngakhale kuti Yehova anagwiritsa ntchito aneneri okhulupirika ngati Danieli kuti alembe zinthu zosiyanasiyana zokhudza mbewu yolonjezedwayo, yomwe ndi Mesiya, nthawi yoti Yehova athandize atumiki ake kumvetsa kufunika kwa zimene anawauzira kuti alembezo inali isanakwane. Mwachitsanzo, Danieli ataona masomphenya a kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, Yehova anamuuza kuti amate buku laulosilo kufikira nthawi imene Yehova angaone kuti ndi yoyenera. Pa nthawi imeneyi anthu adzadziwa “zinthu zambiri” zoona.Dan. 12:4.

Yehova anagwiritsa ntchito anthu okhulupirika ngati Danieli kuti alembe zinthu zosiyanasiyana zokhudza Ufumu wa Mesiya

Yesu Anafotokoza Cholinga Cha Mulungu

13. (a) Kodi mbewu yolonjezedwa inali ndani? (b) Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kumvetsa ulosi wopezeka pa Genesis 3:15?

13 Yehova ananena momveka bwino kuti Yesu ndi mbewu yolonjezedwayo, chidzukulu cha Davide amene adzalamulire monga Mfumu. (Luka 1:30-33; 3:21, 22) Yesu atayamba utumiki wake zinali ngati dzuwa lawalira anthu moti anayamba kudziwa zinthu zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu. (Mat. 4:13-17) Mwachitsanzo, Yesu ananena mosakayikira kuti “njoka” imene inatchulidwa pa Genesis 3:14, 15, inali Mdyerekezi yemwe ndi “wopha anthu” komanso “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) M’masomphenya amene Yohane anaona, Yesu anafotokoza kuti “njoka yakale” imeneyi ndi “iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” * (Werengani Chivumbulutso 1:1; 12:9.) Masomphenyawo anasonyezanso mmene Yesu, monga mbewu yolonjezedwa, adzakwaniritsire ulosi womwe unaperekedwa mu Edeni, woti Yesuyo adzawononga Satana.Chiv. 20:7-10.

14-16. Kodi nthawi zonse ophunzira a Yesu ankamvetsetsa mfundo za choonadi zimene iye ankaphunzitsa? Fotokozani.

14 Monga taonera m’mutu woyamba wa bukuli, Yesu ananena zambiri zokhudza Ufumu. Komabe, iye sanafotokoze zinthu zonse zimene ophunzira ake ankafuna kudziwa. Ngakhale pamene Yesu anafotokoza zinthu mwatsatanetsatane, zinkatenga nthawi ndipo nthawi zina zaka zambiri kuti otsatira ake amvetse tanthauzo la zimene Mbuye wawo anawaululira. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

15 Mu 33 C.E., Yesu anafotokozera anthu momveka bwino kuti anthu amene adzalamulire pamodzi ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu adzatengedwa padziko lapansi n’kupita kumwamba monga zolengedwa zauzimu. Koma pa nthawiyo ophunzira ake sanamvetse zimenezi. (Dan. 7:18; Yoh. 14:2-5) M’chaka chomwecho, Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza kuti Ufumuwo sudzakhazikitsidwa mpaka patadutsa zaka zambiri iye atabwerera kumwamba. (Mat. 25:14, 19; Luka 19:11, 12) Ophunzirawo sanamvetse mfundo yofunika imeneyi moti Yesu  ataukitsidwa anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Koma Yesu anasankha kuti asawauze zambiri pa nthawi imeneyi. (Mac. 1:6, 7) Yesu anaphunzitsanso anthu kuti padzakhala “nkhosa zina,” zomwe sizidzakhala mbali ya “kagulu ka nkhosa” komwe kadzalamulire naye limodzi. (Yoh. 10:16; Luka 12:32) Otsatira a Khristu sankatha kusiyanitsa bwinobwino magulu awiriwa mpaka pamene Ufumuwo unakhazikitsidwa mu 1914.

16 Yesu akanatha kuuza ophunzira ake zinthu zambiri ali padziko lapansi koma ankadziwa kuti sakanatha kuzimvetsa pa nthawiyo. (Yoh. 16:12) Mfundo zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu zinaululidwa m’nthawi ya atumwi. Komabe, imeneyi sinali nthawi imene mfundo zimenezi zinayenera kudziwika kwa anthu ambiri.

Anthu Akudziwa Zinthu Zambiri Zoona ‘M’nthawi Yamapeto’

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizimvetsa mfundo za choonadi zokhudza Ufumu, nanga n’chiyaninso china chimene chimafunika?

17 Yehova analonjeza Danieli kuti ‘m’nthawi yamapeto’ anthu ambiri “adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona” zokhudza cholinga cha Mulungu. (Dan. 12:4) Anthu amene akufuna kudziwa zinthu zimenezi ayenera kuchita khama. Buku lina limanena kuti mawu achiheberi akuti ‘kuyenda uku ndi uku’ amafotokoza zimene munthu amachita akamawerenga buku mofatsa komanso mosamala kwambiri. Komabe, ngakhale titayesetsa kuwerenga Baibulo mofatsa, sitingathe kumvetsa bwinobwino mfundo za choonadi zokhudza Ufumu pokhapokha ngati Yehova atatithandiza kuti tizimvetse.Werengani Mateyu 13:11.

18. Kodi anthu amene amaopa Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi odzichepetsa komanso kuti ali ndi chikhulupiriro?

18 Yehova ankaulula pang’onopang’ono mfundo za choonadi zokhudza Ufumuwu chaka cha 1914 chisanafike ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi m’nthawi yamapeto ino. Mutu 4 ndi 5 usonyeza kuti m’zaka 100 zapitazi, anthu a Mulungu asintha  maulendo angapo mmene ankamvera mfundo zina. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova sakuwathandiza kumvetsa mfundozi? Ayi, amawathandiza. Tikutero chifukwa chakuti, anthu amene amaopa Yehova ali ndi makhalidwe awiri amene Yehovayo amawakonda. Makhalidwe amenewa ndi chikhulupiriro ndi kudzichepetsa. (Aheb. 11:6; Yak. 4:6) Atumiki a Yehova amakhulupirira kuti malonjezo onse amene ali m’Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa. Amasonyezanso kudzichepetsa chifukwa amavomereza kuti sanamvetse bwinobwino mmene Yehova adzakwaniritsire malonjezowo. Kudzichepetsa kumeneku kunaonekera mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925, yomwe inanena kuti: “Tikudziwa kuti Ambuye amatanthauzira yekha Mawu ake ndipo adzatanthauzira mawuwo moyenera kwa anthu ake pa nthawi imene iyeyo akuona kuti ndi yoyenera.”

“Ambuye . . . adzatanthauzira [Mawu Ake] moyenera kwa anthu ake pa nthawi imene iyeyo akuona kuti ndi yoyenera”

19. Kodi panopa Yehova watithandiza kumvetsa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

19 Pamene Ufumuwo unkakhazikitsidwa mu 1914, anthu a Mulungu ankangodziwa zinthu zochepa zokhudza mmene maulosi onena za Ufumuwo adzakwaniritsidwire. (1 Akor. 13:9, 10, 12) Chifukwa chofunitsitsa kuti malonjezo a Mulungu akwaniritsidwe mwamsanga, nthawi zina tinkaona zinthu molakwika. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925, ija inanenanso mfundo ina yomwe ikugwirizana ndi zimene zakhala zikuchitika m’zaka zapitazi. Mfundo yake ndi yakuti: “Ndi nzeru kukhulupirira kuti ulosi sitingaumvetse mpaka utayamba kukwaniritsidwa kapena pambuyo poti wakwaniritsidwa kale.” Popeza tili m’katikati mwa nthawi yamapeto, maulosi ambiri onena za Ufumu akwaniritsidwa ndipo ena akukwaniritsidwa. Chifukwa chakuti anthu a Mulungu ndi odzichepetsa komanso ndi okonzeka kuthandizidwa ngati sanamvetse mfundo inayake, Yehova watithandiza kuti tiyambe kumvetsa bwinobwino cholinga chake. Apa n’zoonekeratu kuti anthu ayamba kudziwa zinthu zambiri zoona.

 Kusintha Kwa Zinthu Kumayesa Chikhulupiriro cha Anthu a Mulungu

20, 21. Kodi kusintha kwa mmene ankamvera mfundo za choonadi kunakhudza bwanji Akhristu a m’nthawi ya atumwi?

20 Yehova akatithandiza kumvetsa mfundo inayake ya choonadi, mtima wathu umayesedwa. Kodi kudzichepetsa komanso chikhulupiriro chathu zimatithandiza kuti tisinthe n’kuyamba kutsatira mfundo zatsopanozo? Nawonso Akhristu amene anakhala ndi moyo m’nthawi ya atumwi anayesedwa zinthu zitasintha. Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti ndinu Mkhristu Wachiyuda amene amalemekeza kwambiri Chilamulo cha Mose komanso kusangalala ndi mwayi wokhala mu mtundu wapadera. Kenako mukulandira makalata ouziridwa olembedwa ndi mtumwi Paulo okudziwitsani kuti Chilamulo chasiya kugwira ntchito komanso kuti Yehova wakana mtundu wa Aisiraeli ndipo wasankha Isiraeli wauzimu, yemwe wapangidwa ndi Ayuda komanso anthu a mitundu ina. (Aroma 10:12; 11:17-24; Agal. 6:15, 16; Akol. 2:13, 14) Kodi mukanakhala kuti munalipo nthawi imeneyo mukanatani?

21 Akhristu amene anali odzichepetsa anamvera zimene Paulo analemba ndipo Yehova anawadalitsa. (Mac. 13:48) Koma ena sankafuna kusintha ndipo ankangokakamirabe mfundo zoyambirirazo. (Agal. 5:7-12) Akhristuwo akanakhala kuti sanasinthe maganizo awo, akanataya mwayi wokalamulira kumwamba ndi Khristu.2 Pet. 2:1.

22. Kodi inuyo mumatani kamvedwe ka mfundo za choonadi kakasintha?

22 M’zaka zapitazi, Yehova wakhala akutithandiza kumvetsa bwino mfundo zokhudza Ufumu. Mwachitsanzo, watithandiza kudziwa nthawi imene anthu amene adzakhale nzika za Ufumuwo adzasiyanitsidwe ndi anthu osamvera. Zimenezi zili ngati kusiyanitsa nkhosa ndi mbuzi. Watiphunzitsanso nthawi imene chiwerengero cha 144,000 chidzakwane, tanthauzo la mafanizo onena za Ufumu amene Yesu ananena komanso kudziwa nthawi imene wodzozedwa womaliza adzatengedwe kupita kumwamba. * Kodi inuyo mumatani kamvedwe ka mfundo za choonadi kakasintha? Kodi zimakuthandizani kuti chikhulupiriro chanu chilimbe? Kodi mumaona kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova akupitirizabe kuphunzitsa anthu ake odzichepetsa? Mfundo zimene zili m’bukuli zikuthandizani kutsimikizira kuti Yehova akuulula cholinga chake pang’onopang’ono kwa anthu amene amamuopa.

^ ndime 4 Dzina la Mulungu likuchokera ku mawu achiheberi amene amatanthauza “kukhala.” Dzina lakuti Yehova limasonyeza kuti iye amachititsa kuti malonjezo ake akwaniritsidwe. Onani bokosi lakuti, “Tanthauzo la Dzina la Mulungu,” patsamba 43.

^ ndime 6 Ngakhale kuti masiku ano nthawi imeneyi ingaoneke ngati yaitali kwambiri, tiyenera kukumbukira kuti anthu akale ankakhala ndi moyo wautali moti panali mibadwo 4 yokha kuchokera pa Adamu kufika pa Abulahamu. Pamene Lameki, bambo ake a Nowa amabadwa n’kuti Adamu adakali ndi moyo. Pamene Semu, mwana wa Nowa amabadwa, n’kuti Lameki adakali ndi moyo. Pamene Abulahamu amabadwa n’kuti Semu adakali ndi moyo.Gen. 5:5, 31; 9:29; 11:10, 11; 25:7.

^ ndime 13 Dzina lakuti “Satana” limagwiritsidwa ntchito ponena za munthu maulendo 18 m’Malemba Achiheberi. Koma m’Malemba Achigiriki mawu akuti “Satana” amapezeka maulendo oposa 30. Zimenezi zinali zoyenera chifukwa Malemba Achiheberi sankafunikira kufotokoza kwambiri za Satana koma kufotokoza mfundo zomwe zingathandize anthu kuzindikira Mesiya. Mesiya atabwera anathandiza anthu kumudziwa Satana ndipo zimenezi zinalembedwa m’Malemba Achigiriki.

^ ndime 22 Kuti mumvetse mfundo zina zimene zinasinthidwa, werengani nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda otsatirawa: October 15, 1995, tsamba 23-28; January 15, 2008, tsamba 20-24; July 15, 2008, tsamba 17-21; July 15, 2013, tsamba 9-14.