Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ufumu wa Mulungu Ukulamulira

Anthu ambiri amakhala mosangalala chifukwa anasankha kuti azilamuliridwa ndi boma labwino kwambiri la Mulungu. Kodi nanunso mungakonde kukhala nzika za Ufumu umenewu?

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

N’chiyani chikusonyeza kuti zimene M’bale C. T. Russell analengeza pa 2 October, 1914 n’zoona?

MUTU 1

“Ufumu Wanu Ubwere”

Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kodi Ufumuwu udzabwera liti ndipo udzabwera bwanji?

MUTU 2

Ufumu Wakhazikitsidwa Kumwamba

Kodi otsatira Yesu okhulupirika anathandizidwa ndi ndani kukonzekera kubwera kwa Ufumu padziko lapansi? Fotokozani zinthu zimene Akhristu oona anachita pokonzekera kubwera kwa Ufumu wa Mulungu

MUTU 3

Yehova Anathandiza Anthu Kudziwa Cholinga Chake

Kodi mmene Yehova ankalenga anthu anali ndi cholinga choti kudzakhale Ufumu wa Mesiya? Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kudziwa za Ufumuwo?

MUTU 4

Yehova Analemekeza Dzina Lake

Kodi Ufumu wa Mulungu wakwanitsa kuchita zotani zokhudza dzina la Mulungu? Kodi inuyo mumachita zotani poyeretsa nawo dzina lakuti Yehova?

MUTU 5

Mfumu Inathandiza Anthu Kudziwa Bwino za Ufumu

Dziwani zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu, olamulira ake ndiponso anthu amene adzalamuliridwe komanso kufunika kokhala wokhulupirika.

MUTU 6

Anthu Amene Akulalikira—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa

N’chiyani chinachititsa Yesu kukhulupirira kuti m’masiku otsiriza adzakhala ndi gulu la anthu amene adzadzipereka kugwira ntchito yolalikira? Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mukufuna Ufumu choyamba?

MUTU 7

Njira Zolalikirira—Ankagwiritsa Ntchito Njira Zosiyanasiyana Kuti Anthu Amve Uthenga

Dziwani njira zina zimene atumiki a Yehova akhala akugwiritsa ntchito kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu ambiri mapeto asanafike.

MUTU 8

Zinthu Zogwiritsa Ntchito Polalikira—Kukonza Mabuku Ogwiritsa Ntchito Polalikira Padziko Lonse

Kodi ntchito yomasulira magazini ndi mabuku athu imasonyeza bwanji kuti Mfumu ikutsogolera pogwira ntchitoyi? Fotokozani mfundo zonena za mabuku athu zimene zikukutsimikizirani kuti Ufumuwu ndi weniweni.

MUTU 9

Zotsatira za Ntchito Yolalikira—“M’mindamo Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

Yesu anathandiza ophunzira kudziwa mfundo ziwiri zofunika kwambiri pa ntchito yaikulu yokolola. Kodi mfundo ziwirizi zikutikhudza bwanji masiku ano?

MUTU 10

Mfumu Inayenga Anthu Ake Mwauzimu

Kodi Khirisimasi ndi mtanda zimafanana bwanji?

MUTU 11

Anawayenga Kuti Akhale Ndi Makhalidwe Abwino Potsanzira Mulungu Woyera

Zipinda za alonda komanso zipata za pakachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya zakhala ndi zothandiza kwambiri kwa anthu a Mulungu polambira kuyambira mu 1914.

MUTU 12

Gulu Limene Likutumikira “Mulungu Wamtendere”

Baibulo limasiyanitsa chisokonezo ndi mtendere osati ndi kuchita zinthu mwadongosolo mtendere. N’chifukwa chiyani? Kodi yankho la funso limeneli limathandiza bwanji Akhristu masiku ano?

MUTU 13

Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti

Masiku ano oweruza a makhoti ena amachita zinthu ngati mmene anachitira mphunzitsi wakale wa Chilamulo, dzina lake Gamaliyeli.

MUTU 14

Timakhala Okhulupirika ku Boma la Mulungu Lokha Basi

Mavuto, omwe anali ngati “mtsinje,” amene a Mboni za Yehova anakumana nawo chifukwa chosalowerera ndale, anathetsedwa ndi anthu omwe sankayembekezera kuti angawathandize.

MUTU 15

Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka

Anthu a Mulungu amenyera ufulu woti azitsatira malamulo a Ufumu wa Mulungu.

MUTU 16

Kusonkhana Kuti Tilambire Mulungu

Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi misonkhano imene timalambirako Yehova?

MUTU 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Kodi masukulu a gulu athandiza bwanji atumiki a Ufumu kuti azisamalira bwino maudindo awo?

MUTU 18

Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu

Kodi ndalama zimene amagwiritsa ntchito zimachokera kuti? Kodi ndalamazo zimagwira ntchito yanji?

MUTU 19

Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova

Malo olambirira amalemekeza Mulungu, koma pali chinthu china chomwe Mulungu amachiona kuti n’chamtengo wapatali kwambiri.

MUTU 20

Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto

Kodi timadziwa bwanji ntchito yothandiza anthu ndi mbali ya utumiki wopatulika kwa Yehova?

MUTU 21

Ufumu wa Mulungu Udzachotsa Adani Ake

Mukhoza kukonzekera nkhondo ya Aramagedo.

MUTU 22

Ufumu Udzakwaniritsa Zimene Mulungu Amafuna Padziko Lapansi

N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu udzabweradi?