Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Pulogalamu ya Msonkhano Wachigawo wa 2017

Mawu kwa Osonkhana

Mawu kwa Osonkhana

KUKUMANA NDI OFUNA

UTUMIKI WA PA BETELI Ofalitsa obatizidwa osapitirira zaka 35 omwe akufuna kukatumikira pa Beteli adzakhale nawo pamsonkhano wa ofuna utumiki wa pa Beteli Lachisanu masana pa nthawi yopuma. Ngati msonkhano umenewo ukhalepo, alengeza malo ndi nthawi yake yeniyeni.

SUKULU YA AKHRISTU OLALIKIRA ZA UFUMU Apainiya azaka zapakati pa 23 ndi 65 amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo, akuitanidwa kukakhala nawo pamsonkhano wa anthu ofuna kupita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, Lamlungu masana pa nthawi yopuma. Malo ndi nthawi yake yeniyeni zilengezedwa pasadakhale.

 MAWU KWA OSONKHANA

OLANDIRA ALENDO Amene akulandira alendo ntchito yawo n’kukuthandizani. Choncho, tsatirani malangizo amene angakupatseni okhudza koimika galimoto ndi njinga, njira zoyenera kuyendamo polowa ndi potuluka pamalo a msonkhano, kusunga malo okhala ndi zinthu zina.

UBATIZO Anthu amene akonzekera kubatizidwa ayenera kukhala m’mipando yakutsogolo imene awakonzera, nkhani ya ubatizo isanayambe Loweruka m’mawa. Ngati pali malangizo ena osiyana ndi amenewa, adzalengezedwa pasadakhale. Aliyense ayenera kubweretsa thaulo ndi zovala zoyenera zolowera m’madzi.

ZOPEREKA Kupeza malo okwanira ochitirapo msonkhano, zokuzira mawu, zipangizo zoonetsera mavidiyo ndi zinthu zina zothandiza kuti msonkhanowu ukhale wosangalatsa, kumafuna ndalama zambiri. Zonsezi n’zothandiza kuti tiyandikire kwa Yehova. Ndalama zimene mungapereke mwakufuna kwanu pamsonkhanowu, zitithandiza kulipirira zinthu zimenezi komanso zithandiza pa ntchito ya padziko lonse. Mabokosi olembedwa bwino amene mungaponyemo zopereka zanu, aikidwa m’malo osiyanasiyana pamsonkhanowu. Timayamikira kwambiri zopereka zanu zonse, ndipo Bungwe Lolamulira likukuyamikirani chifukwa chothandiza ndi mtima wonse pa ntchito ya Ufumu.

DIPATIMENTI YOTHANDIZA PANGOZI Kumbukirani kuti dipatimenti imeneyi imathandiza pa ZAKUGWA MWADZIDZIDZI ZOKHA.

ZOTAYIKA NDI ZOPEZEKA Mukatola chinthu chilichonse, kachiperekeni ku Dipatimenti ya Zotayika Komanso Yosunga Zinthu. Ngati mwataya chilichonse, kafunseni kudipatimentiyi. Mukapeza mwana amene wasochera, kamuperekeni kudipatimenti imeneyi. Komabe dipatimentiyi siyosungirako ana, choncho samalani ana anu ndipo nthawi zonse muzikhala nawo pamodzi.

MALO OKHALA Yesetsani kuganizira ena. Kumbukirani kuti mungasungire malo a m’banja lanu, aliyense amene mwayenda naye galimoto imodzi kapena munthu amene mukuphunzira naye Baibulo. Musaike zinthu pamalo okhala omwe ali pafupi nanu. Zimenezi zithandiza ena kuona kuti pamalopo palibe anthu.

ANTCHITO ONGODZIPEREKA Ngati mukufuna kuthandiza nawo ntchito pamsonkhanowu, pitani ku Dipatimenti Yothandiza Anthu Ndiponso Yoyang’anira Antchito Ongodzipereka.

Wokonzedwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova