Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Pulogalamu ya Msonkhano Wachigawo wa 2017

Onani nkhani zimene zidzakambidwe tsiku lililonse la msonkhanowu zomwe zingakuthandizeni kuti mupitirizebe kuchita zabwino komanso kuti mupitirizebe kupirira.

Lachisanu

Kodi n’chiyani chingathandize Akhristu kukhala ndi makhalidwe amene angawathandize kupirira?

Loweruka

Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji, nanga amatithandiza bwanji kuti tipirire?

Lamlungu

Yesu anati: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” Kodi mungatani kuti muzitsatira mawu amenewa?

Mawu kwa Osonkhana

Mwina mungakonde kudzachita nawo misonkhano yapadera yomwe idzachitike pamsonkhanowu. Mungaonenso pano ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza olandira alendo, ubatizo, zopereka, dipatimenti yothandiza pangozi, zotayika ndi zopezeka komanso za antchito ongodzipereka.

Onaninso

KODI NDANI AKUCHITA CHIFUNIRO CHA YEHOVA MASIKU ANO?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakhala ndi Misonkhano Ikuluikulu?

Chaka chilichonse, timachita misonkhano ikuluikulu. Kodi kupezeka pamisonkhano imeneyi kungakuthandizeni bwanji?