Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzitsani Ana Anu

 PHUNZIRO 10

Yesu Anali Womvera

Yesu Anali Womvera

Kodi umaona kuti kumvera makolo n’kophweka?— Nthawi zina zimakhala zovuta. Kodi ukudziwa kuti Yesu ankamvera makolo ake komanso Yehova?— Zimene iye ankachita zingakuthandize kuti nawenso uzimvera makolo ako ngakhale kuti nthawi zina zimakhala zovuta. Tiye tikambirane zambiri pa nkhani imeneyi.

Yesu asanabwere padziko lapansi ankakhala kumwamba ndi Atate ake, Yehova. Koma atabwera padziko lapansi anali ndi makolo ena. Mayina awo anali Yosefe ndi Mariya. Kodi ukudziwa kuti zinatheka bwanji kuti Yosefe ndi Mariya akhale makolo a Yesu?—

Yehova anatenga moyo wa Yesu n’kuuika m’mimba mwa Mariya kuti Yesu abadwe padziko lapansi. Zimenezi zinali zodabwitsa kwambiri. Yesu anakula m’mimba mwa Mariya ngati mmene ana onse amakulira. Patapita miyezi 9, Yesu anabadwa. Zimenezi ndi zimene zinachitika kuti Mariya ndi mwamuna wake Yosefe akhale makolo a Yesu.

Yesu ali ndi zaka 12 zokha anachita zinthu zosonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake, Yehova. Zimenezi zinachitika pa nthawi imene Yesu ndi makolo ake anayenda ulendo wautali wopita ku chikondwerero cha Pasika ku Yerusalemu. Pobwerera, Yosefe ndi Mariya anazindikira kuti Yesu wasowa. Kodi ukudziwa kuti anali kuti?—

N’chifukwa chiyani Yesu anapita kukachisi?

Yosefe ndi Mariya anabwerera msangamsanga ku Yerusalemu ndipo anamufufuza Yesu pena paliponse. Atalephera kumupeza, anadandaula kwambiri. Koma patadutsa masiku atatu, anamupeza ali m’kachisi. Kodi ukudziwa chifukwa chimene Yesu anapitira kukachisi?— Chifukwa ankadziwa kuti kukachisiko ndi kumene angaphunzire za Atate wake, Yehova. Yesu ankakonda kwambiri Yehova ndipo ankafuna kudziwa zimene angachite kuti azimusangalatsa. Atakula, Yesu anapitirizabe kumvera Yehova. Ankamveranso Yehova ngakhale pamene zinali zovuta moti ankalolera kuvutika. Kodi Yesu ankamveranso Yosefe ndi Mariya?— Inde, chifukwa Baibulo limanena kuti ankawamvera.

Kodi waphuzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?— Iwenso uyenera kumvera makolo ngakhale pamene kuchita zimenezi kuli kovuta. Kodi iweyo uzichita zimenezi?—