Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzitsani Ana Anu

 PHUNZIRO 14

Ufumu Umene Udzalamulira Dziko Lonse

Ufumu Umene Udzalamulira Dziko Lonse

Kodi ukuganiza kuti ufumu umenewu ndi uti?— Inde, ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu udzasintha dzikoli kuti likhale Paradaiso. Kodi ungakonde kudziwa zambiri za Ufumuwu?—

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu. Ndipo mfumuyo imalamulira anthu omwe ali m’dziko lake. Kodi ukudziwa amene ali Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?— Ndi Yesu Khristu. Panopa Yesu ali kumwamba koma posachedwapa iye adzalamulira aliyense padziko lapansi. Kodi ukuganiza kuti tidzakhala osangalala Yesu akadzakhala Mfumu padziko lapansi?—

Kodi iweyo ukufuna kudzaona chiyani m’Paradaiso?

Tonse tidzakhala osangalala kwambiri. M’Paradaiso palibe amene azidzamenyana kapena kupita ku nkhondo. Anthu onse azidzakondana. Palibe amene azidzadwala kapena kumwalira. Anthu osaona adzayamba kuona, osamva adzayamba kumva ndipo anthu amene satha kuyenda adzayamba kuyenda bwinobwino komanso kudumpha. Aliyense adzakhala ndi chakudya chambiri. Zinyama sizizidzapwetekana komanso kupweteka anthu. Anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Anthu onse amene atchulidwa m’bukuli monga Rabeka, Rahabi, Davide ndi Eliya adzakhalanso ndi moyo.  Kodi ukufuna kudzakumana nawo?—

Yehova amakukonda kwambiri ndipo amafuna kuti uzisangalala. Ngati utapitiriza kuphunzira za Yehova komanso kumumvera, udzakhala ndi moyo m’paradaiso mpaka kalekale. Kodi iweyo ukufuna kudzakhala ndi moyo m’paradaiso?—