Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzitsani Ana Anu

 PHUNZIRO 3

Rahabi Ankakhulupirira Yehova

Rahabi Ankakhulupirira Yehova

Tiye tiyerekeze kuti tili mumzinda wa Yeriko womwe uli m’dziko la Kanani. Anthu a m’dziko limeneli sakhulupirira Yehova. Mumzinda umenewu mumakhala mkazi wina dzina lake Rahabi.

Rahabi ali kamtsikana anamva zimene zinachitika pamene Mose anatulutsa Aisiraeli ku Iguputo ndiponso pamene anachititsa kuti madzi a m’Nyanja Yofiira agawanike. Anamvanso mmene Yehova anawathandizira kuti apambane pankhondo zomenyana ndi adani awo. Kenako akumva kuti Aisiraeliwo ali pafupi ndi mzinda wa Yeriko.

Rahabi anabisa Aisiraeli amene anabwera kunyumba kwake chifukwa ankakhulupirira Yehova

Tsiku lina madzulo, Aisiraeli awiri akulowa mumzinda wa Yeriko kuti aone ngati zili zotheka kulanda mzindawo. Anthuwa akufika kunyumba ya Rahabi ndipo iye akuwalola kuti akhale kunyumba kwakeko. Usiku, mfumu ya mzinda wa Yeriko yazindikira kuti kwabwera anthu ofuna kulanda mzindawo ndipo ali kunyumba kwa Rahabi. Ndiyeno mfumu ikutumiza anthu kuti akawagwire. Rahabi akubisa Aisiraeli aja padenga la nyumba yake n’kuuza anthu otumidwa ndi mfumuwo kuti: ‘Anthuwo anabweradi, koma atuluka kale mumzinda muno. Ngati mutawathamangira muwapeza.’ Kodi ukudziwa kuti n’chifukwa chiyani Rahabi akuteteza anthuwa?— N’chifukwa chakuti amakhulupirira Yehova komanso akudziwa kuti Yehova apereka dziko la Kanani kwa Aisiraeli.

Koma Aisiraeli awiriwo asanachoke akulonjeza Rahabi kuti iyeyo ndi abale ake adzapulumuka mzinda wa Yeriko ukamadzawonongedwa. Kodi ukudziwa zimene akumuuza kuti achite?— Akumuuza kuti: ‘Tenga chingwe chofiirachi ndipo uchimangirire pawindo. Ukachita zimenezi, aliyense amene adzakhale m’nyumbamu sadzaphedwa.’ Rahabi akuchita zonse zimene amuuza. Kodi ukudziwa zimene zikuchitika kenako?—

Yehova anapulumutsa Rahabi ndi abale ake

Patapita masiku angapo, Aisiraeli anayenda ngati asilikali mozungulira mzindawo popanda kuchita phokoso lililonse. Kwa masiku 6, iwo ankazungulira mzindawo kamodzi tsiku lililonse. Koma patsiku la 7, anazungulira mzindawo maulendo 7. Kenako onse anakuwa kwambiri ndipo Yehova anachititsa kuti mpanda wonse wa mzindawo ugwe pansi. Koma nyumba imene pawindo pake panali chingwe chofiira siinagwe. Kodi ukuiona pachithunzipo?— Rahabi ndi abale ake anapulumuka.

 Kodi waphunzirapo chiyani kwa Rahabi?— Rahabi ankakhulupirira Yehova chifukwa chomva kuti Yehova anachita zinthu zambiri zabwino. Nawenso waphunzira zinthu zambiri zimene Yehova wachita. Kodi umakhulupirira Mulungu ngati mmene Rahabi anachitira?— Tikudziwa kuti umamukhulupirira.

WERENGANI MAVESI AWA