Rabeka ankakonda Yehova. Mwamuna wake anali Isaki ndipo nayenso ankakonda Yehova. Kodi ukudziwa kuti Rabeka anakumana bwanji ndi Isaki? Nanga Rabeka anasonyeza bwanji kuti ankafuna kusangalatsa Yehova? Tiye tione zimene zinachitika.

Makolo ake a Isaki anali Abulahamu ndi Sara. Iwo ankakhala m’dziko la Kanani ndipo anthu a kumeneko sankalambira Yehova. Koma Abulahamu ankafuna kuti mwana wake adzakwatire mkazi wolambira Yehova. Choncho anatuma wantchito wake Eliezere kuti apite ku Harana kuti akapezere Isaki mkazi. Ku Harana n’kumene kunkakhala abale ake a Abulahamu.

Rabeka anapita ndi Eliezere kuti akakwatiwe ndi Isaki

Eliezere anayenda ulendowu ndi antchito ena a Abulahamu. Ulendowu unali wautali kwambiri. Anatenga ngamila 10 zomwe zinanyamula zakudya ndi mphatso. Koma kodi Eliezere akanasankha bwanji mtsikana woti akakhale mkazi wa Isaki? Atafika ku Harana, Eliezere ndi antchito ena aja anaima pachitsime chifukwa ankadziwa kuti sipapita nthawi yaitali anthu asanabwere kudzatunga madzi. Ndiyeno anapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti, ‘Ndikapempha mtsikana kuti andipatseko madzi oti ndimwe, iye n’kundipatsa komanso n’kumwetsa ngamilazi, ndidziwa kuti mtsikana ameneyo ndi amene mwamusankha.’

Kenako Rabeka anafika pachitsimepo. Baibulo limanena kuti Rabeka anali wokongola kwambiri. Eliezere anamupempha madzi ndipo anayankha kuti: ‘Eni imwani. Nditungiranso  madzi ngamila zanu.’ Tangoganiza, kutungira madzi ngamila zimene zinali ndi ludzu kwambiri. Pamenepatu Rabeka anafunika kuyenda maulendo ambirimbiri kuti atunge madzi okwanira ngamila zonsezo. Kodi ukuona zimene akuchita pachithunzipo?— Eliezere anadabwa kwambiri ndi mmene Yehova anayankhira pemphero lake.

Eliezere anam’patsa Rabeka mphatso zambirimbiri. Rabeka anaitanira Eliezere ndi antchito ena aja kunyumba kwawo. Atafika, Eliezere anafotokoza chifukwa chimene Abulahamu anamutumira kumeneko komanso mmene Yehova anayankhira pemphero lake. Abale ake a Rabeka anagwirizana ndi zoti Rabeka akakhale mkazi wa Isaki.

Rabeka anayenda maulendo ambirimbiri kuti atunge madzi okwanira ngamila zonse

Kodi ukuganiza kuti Rabeka ankafunadi kukwatiwa ndi Isaki?— Rabeka ankadziwa kuti Yehova ndi amene analondolera Eliezere kuti afike kwawo. Ndiyeno abale ake a Rabeka atamufunsa ngati akufuna kupita ku Kanani kuti akakhale mkazi wa Isaki, iye anayankha kuti: “Inde ndipita.” Nthawi yomweyo ananyamuka limodzi ndi Eliezere. Atafika ku Kanani, anakwatiwa ndi Isaki.

Yehova anadalitsa Rabeka chifukwa chakuti anachita zimene Yehovayo ankafuna. Moti patapita zaka zambiri, zidzukulu za Rabeka zinabereka Yesu. Iwenso Yehova akhoza kukudalitsa ngati utamachita zinthu zomusangalatsa ngati mmene Rabeka anachitira.

WERENGANI MAVESI AWA