Tiye tikambirane za mnyamata wina yemwe anapulumutsa moyo wa ankolo ake. Ankolo ake a mnyamatayu anali mtumwi Paulo. Sitimadziwa dzina la mnyamatayu koma timadziwa kuti anachita zinthu molimba mtima. Kodi ukufuna kudziwa zimene anachita?—

Pa nthawi ina Paulo anamangidwa ndipo anali m’ndende ku Yerusalemu chifukwa ankalalikira za Yesu. Mkulu wa asilikali anaganiza zotumiza Paulo ku mzinda wina, dzina lake Kaisareya. Anthu ena oipa ankadana ndi Paulo ndipo anakonza chiwembu n’cholinga choti amuphe. Iwo anagwirizana kuti: ‘Tiyeni tipemphe mkulu wa asilikali kuti atumize Paulo ku khoti. Ndiyeno ifeyo tim’bisalira panjira kuti akamadutsa, timuphe.’

Mwana wa mchemwali wake wa Paulo anauza Paulo ndi mkulu wa asilikali za chiwembu

Mwana wa mchemwali wake anamva za chiwembucho. Atamva zimenezi, anapita kundende kukamuuza Paulo. Nthawi yomweyo, Paulo anauza mnyamatayo kuti akanene nkhaniyi kwa mkulu wa asilikali. Kodi ukuganiza kuti zinali zophweka kuti mnyamatayu alankhule ndi mkulu wa asilikali?— Ayi, chifukwa mkulu wa asilikali ankapatsidwa ulemu kwambiri. Komabe mnyamatayu analimba mtima ndipo anakalankhula naye.

Nthawi yomweyo mkulu wa asilikaliyo anadziwa zoyenera kuchita. Anasankha asilikali pafupifupi 500 kuti ateteze Paulo. Anawauza kuti amuperekeze ku Kaisareya usiku wa tsiku lomwelo. Kodi Paulo anapulumuka?— Inde, ndipo anthu oipa aja sanamuchite chilichonse. Chiwembu chawo chija chinalephereka.

Kodi waphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi?— Iwenso ukhoza kuchita zinthu molimba mtima ngati mwana wa mchemwali wake wa Paulo. Timafunika kulimba mtima kuti tiziuza ena za Yehova. Kodi iweyo uzilimba mtima n’kumauzabe anthu za Yehova?— Ngati utamachita zimenezi, ukhoza kupulumutsa moyo wa anthu ena.