Takaona kamnyamata komwe kali pachithunzichi. Kakuoneka kuti kali kokhakokha ndipo kakuchita mantha. Kodi zimenezi zinakuchitikirapo?— Munthu aliyense amamva choncho nthawi zina. Baibulo limafotokoza za anthu amene ankakonda Yehova omwe nthawi ina ankaona kuti atsala okha ndipo ankachita mantha. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Eliya. Tiye tione zimene zinamuchitikira.

Yezebeli ankafuna kupha Eliya

Eliya ankakhala ku Isiraeli kalekale Yesu asanabadwe. Pa nthawiyo Ahabu anali mfumu ya ku Isiraeli ndipo sankatumikira Mulungu woona, Yehova. Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli ankalambira mulungu wonama, yemwe dzina lake linali Baala. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri a ku Isiraeli ayambenso kulambira Baala. Yezebeli anali munthu woipa kwambiri ndipo ankafuna kupha anthu onse amene ankalambira Yehova, kuphatikizapo Eliya. Kodi ukudziwa kuti Eliya anatani?—

 Eliya anathawira kutali kwambiri. Anapita kuchipululu n’kukabisala kuphanga. Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Eliya anachita zimenezi?— Iye ankachita mantha. Koma Eliya sankafunika kuchita mantha chifukwa ankadziwa kuti Yehova akhoza kumuthandiza. Yehova anali atamusonyeza kale Eliya kuti ndi wamphamvu. Nthawi ina, Yehova anayankha pemphero la Eliya potumiza moto wochokera kumwamba. Ndiye kuti Yehova ankanathadi kumuthandiza Eliya.

Kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya?

Eliya atabisala kuphanga, Yehova analankhula naye n’kumufunsa kuti: ‘Kodi ukufuna chiyani kuno?’ Eliya anayankha kuti: ‘Pa atumiki anu onse ndatsala ndine ndekha. Ndatsala ndekhandekha ndipo ndikuopa kuti andipha.’ Eliya ankaganiza kuti atumiki onse a Yehova anali ataphedwa. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Ayi, zimenezo si zoona. Pali anthu ena okwana 7,000 amene akunditumikirabe. Limba mtima. Padakali ntchito yoti ugwire.’ Kodi ukuganiza kuti Eliya anasangalala atamva zimenezi?—

Kodi ukuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikira Eliya?— Usamaone ngati watsala wekhawekha komanso usamachite mantha. Pali anthu ambiri amene amakonda Yehova komanso amene amakukonda iweyo. Komanso Yehova ali ndi mphamvu zambiri ndipo adzakuthandiza nthawi zonse. Kodi wasangalala kudziwa kuti suli wekha?—