Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzitsani Ana Anu

 PHUNZIRO 6

Davide Sankachita Mantha

Davide Sankachita Mantha

Kodi iweyo umatani chinachake chikakuchititsa mantha?— Mwina umathamangira kwa mayi kapena bambo ako kuti akuthandize. Koma pali winanso amene akhoza kukuthandiza. Iye ndi wamphamvu kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Kodi ukudziwa kuti ndi ndani?— Inde, ndi Yehova Mulungu. Tiye tikambirane za mnyamata wina wotchulidwa m’Baibulo, dzina lake Davide. Iye ankadziwa kuti Yehova akhoza kumuthandiza nthawi zonse ndipo sankachita mantha.

Kuyambira ali mwana, makolo ake ankamuphunzitsa kuti azikonda Yehova. Zimenezi zinathandiza Davide kuti asamachite mantha akakumana ndi zinthu zoopsa. Ankadziwa kuti Yehova ndi mnzake ndipo amuthandiza. Tsiku lina Davide akuweta nkhosa, kunatulukira chimkango ndipo chinagwira nkhosa imodzi. Kodi ukudziwa zimene Davide anachita? Anathamangitsa mkangowo ndipo anaupha ndi manja ake. Kenako chimbalangondo chinagwira nkhosa ndipo Davide anachiphanso. Kodi ukuganiza kuti ndani anamuthandiza kuti aphe zilombo zimenezi?— Inde, anali Yehova.

Nthawi inanso Davide anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Aisiraeli ankamenyana ndi gulu lina la anthu lotchedwa Afilisiti. Msilikali mmodzi wa Afilisitiwo anali wamtali, wamkulu komanso wamphamvu kwambiri. Dzina lake linali Goliyati. Goliyati ankanyoza Yehova komanso Aisiraeli. Ankaputa dala asilikali a ku Isiraeli kuti akamenyane naye. Koma Aisiraeli onse ankaopa kukamenyana naye. Davide atamva zimenezi anamuuza Goliyati kuti: ‘Umenyana ndi ine. Yehova andithandiza ndipo ndikugonjetsa.’ Kodi ukuganiza kuti Davide anali wolimba mtima?— Inde, anali wolimba mtima kwambiri. Kodi ukufuna kudziwa kuti kenako chinachitika n’chiyani?

Davide anatenga gulaye ndi miyala 5 yosalala bwino n’kupita kukamenyana ndi Goliyati. Goliyati ataona kuti Davide ndi mwana anayamba kumunyoza. Koma Davide anamuuza kuti: ‘Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova.’ Kenako anatenga mwala n’kuika pagulayepo, n’kuyamba kuthamangira kumene kunali Goliyati. Atatero anagenda Goliyati ndi mwalawo. Mwalawo unamenya Goliyati pakati pa maso ake ndipo anagwa pansi n’kuferatu. Afilisiti ataona zimenezi anachita mantha kwambiri ndipo onse anathawa. Kodi zinatheka bwanji kuti kamnyamata ngati Davide  kagonjetse Goliyati yemwe anali munthu wamphamvu?— Yehova ndi amene anamuthandiza chifukwa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Goliyati.

Davide sankachita mantha chifukwa ankadziwa kuti Yehova amuthandiza

Kodi waphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi?— Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Ndipotu ndi mnzako. Ndiyeno nthawi ina chinachake chikadzakuchititsa mantha, udzakumbukire kuti Yehova angakuthandize kuti ulimbe mtima.

WERENGANI MAVESI AWA