Kodi ukuwaona anthu omwe ali pachithunzipa?— Anthu amenewa ndi Mateyu, Maliko, Luka, Yohane, Petulo, Yakobo ndi Paulo. Anthuwa anakhala ndi moyo pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi ndipo analemba za Yesu. Tiye tikambirane zambiri za anthu amenewa.

Kodi ukudziwa chiyani za anthu awa?

Atatu mwa anthu amenewa anali atumwi amene ankalalikira ndi Yesu. Kodi ukudziwa kuti anthu ake ndi ati?— Ndi Mateyu, Yohane ndi Petulo. Mateyu ndi Yohane ankamudziwa  Yesu kwambiri moti aliyense analemba buku lofotokoza za moyo wa Yesu. Mtumwi Yohane analemba buku la Chivumbulutso ndiponso makalata atatu omwe amadziwika kuti 1 Yohane, 2 Yohane ndi 3 Yohane. Mtumwi Petulo analemba makalata awiri omwe amadziwika kuti 1 Petulo ndi 2 Petulo. M’kalata yake yachiwiri, Petulo analemba kuti nthawi ina Yehova analankhula ali kumwamba za Yesu kuti: ‘Uyu ndi mwana wanga. Ndimamukonda kwambiri.’

Anthu enanso amene ali pachithunzipa analemba mabuku amene amatiphunzitsa za Yesu. Mmodzi mwa anthuwa ndi Maliko. Iye ayenera kuti analipo pamene Yesu ankamangidwa ndipo anaona zonse zimene zinachitika. Munthu wina ndi Luka. Iye anali dokotala ndipo n’kutheka kuti pamene ankakhala Mkhristu n’kuti Yesu atamwalira kale.

Anthu ena awiri amene ali pachithunzichi anali azichimwene ake a Yesu. Kodi ukuwadziwa mayina awo?— Mayina awo anali Yakobo ndi Yuda. Poyamba sankamukhulupirira Yesu moti ankaganiza kuti wayamba misala. Koma kenako anayamba kumukhulupirira ndipo anakhala Akhristu.

Munthu womaliza pachithunzipo ndi Paulo. Asanakhale Mkhristu dzina lake linali Saulo. Ankadana ndi Akhristu ndipo ankawachitira nkhanza. Kodi ukudziwa chimene chinamuchititsa Paulo kuti akhale Mkhristu?— Tsiku lina Paulo akuyenda mumsewu anangomva munthu winawake akumulankhula kuchokera kumwamba. Amene ankamulankhulayo anali Yesu. Anamufunsa Paulo kuti: ‘N’chifukwa chiyani ukuzunza anthu amene amandikhulupirira?’ Zitangochitika zimenezi, Paulo anasintha n’kukhala Mkhristu. Paulo analemba mabuku 14 a m’Baibulo, kuyambira buku la Aroma mpaka la Aheberi.

Paja timawerenga Baibulo tsiku lililonse eti?—Tikamawerenga Baibulo timaphunzira zinthu zambiri zonena za Yesu. Kodi iweyo ukufuna kudziwa zambiri zonena za Yesu?—