MAKOLO onse amachita ntchito imene anthu satha kuimvetsetsa. Kholo lililonse limapereka mbali inayake ya thupi lake. Ndiyeno munthu wamoyo amayamba kukula m’mimba mwa amayi ake. Ndiye mwana akabadwa, titha kumvetsa chifukwa chake anthu amati “kubadwa kwa munthu ndi nkhani yozizwitsa.”

N’zoona kuti kubereka ana ndi chiyambi chabe cha udindo wa makolo. Poyamba, makanda amadalira makolo awo kuwachitira chilichonse, koma akamakula amafunika zoposa pamenepo. Amafunika kuwathandiza kuti akhwime maganizo, kuti akule ndi mtima wabwino, makhalidwe abwino, komanso kuti alimbe mwauzimu.

Kuti ana akule bwino, makolo amafunika kuwasonyeza chikondi. Ngakhale kuti n’kofunika kulankhula mawu osonyeza kuti ana anu mumawakonda, zochita zanu zifunika kutsimikizira mawu anuwo. Inde, pamafunika kuti makolo azikhala chitsanzo chabwino kwa ana awo. Amafunika kuwalangiza makhalidwe abwino, kuwapatsa mwambo woti azitsatira pamoyo wawo. Ana amafunika zimenezi kuyambira ali aang’ono. Ngati ana ayamba kuthandizidwa atakula kale, pangachitike zinthu zopweteketsa mtima, ndipotu ena zoterezi zimawachitikira.

Kulikonse kumene mungakhale, mwambo wabwino mungaupeze m’Baibulo. Malango ochokera m’Baibulo ndi opindulitsa kwambiri. Ana akamapatsidwa malango oterowo amayamba kuzindikira kuti akuuzidwa zimene Mlengi wawo, Atate wawo wakumwamba, amanena, osati zimene amanena munthu winawake. Motero uphunguwo umakhala ndi mphamvu kuposa wina uliwonse.

Baibulo limalimbikitsa makolo kuchita khama kukhomereza mwambo wabwino m’maganizo mwa ana awo. Komabe nthaŵi zambiri pamene ana akukula kumakhala kovuta kuti makolo azikambirana nawo nkhani zofunika kwambiri.  Buku lino, lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lalembedwa kuti likuthandizeni kupeŵa zimenezo. Lidzakupatsani inuyo makolo limodzi ndi ana anu nkhani zauzimu zoti muziŵerengera limodzi. Komanso, lidzathandiza kuti ana aang’ono azilankhulana mosavuta ndi amene akuŵerenga nawo limodzi bukuli.

Mudzaona kuti bukuli likufuna kuti ana azilankhulapo. M’nkhani zake muli mafunso oyalidwa bwino ambiri. Mukafika pa mafunsoŵa, mudzaona kamzere (—). Kamzereka ndi kokukumbutsani kuti muime ndi kulimbikitsa mwanayo kuyankha funsolo. Ana amafuna kuti azilankhulapo. Ngati mwana simumulola kulankhulapo sachedwa kuona kuti sizikumukhudza.

Komabe, chofunika kwambiri n’chakuti mafunso ameneŵa adzakuthandizani kudziŵa zimene mwana wanu akuganiza. Inde, mwana angapereke mayankho olakwika. Koma zimene zikunenedwa pambuyo pa funso lililonse ndi zoti zithandize mwanayo kuyamba kuganiza zolondola pa nkhaniyo.

Mbali ina yapadera ya bukuli ndi yakuti lili ndi zithunzi zoposa 230. Zambiri mwa zithunzizi zili ndi mafunso amene amafuna kuti mwana ayankhe kuchokera pa zimene akuona ndi zimene waŵerenga. Choncho muzipenda zithunzizi ndi mwana wanu. Ndi zabwino kwambiri pophunzitsa, moti zingakuthandizeni kutsindika bwino mfundo imene mukuiphunzitsa.

Mwana akadziŵa kuŵerenga, mulimbikitseni kuti azikuŵerengerani bukuli komanso kuti aziliŵerenga payekha. Akamaŵerenga bukuli kwambiri, malangizo ake abwino adzakhomerezekanso kwambiri m’maganizo ndi mumtima mwake. Koma kuti mukulitse chikondi chanu ndi mwana wanu, ndiponso kuti muzilemekezana kwambiri, yesetsani kuŵerengera limodzi bukuli, ndipo chitani zimenezi nthaŵi zonse.

Masiku ano ana akuona anthu akuchita zachiwerewere, kukhulupirira mizimu, ndiponso kuchita makhalidwe ena onyansa m’njira zimene zaka zochepa m’mbuyomo zinali zosaganizirika. Choncho afunika kutetezedwa, ndipo buku lino likupereka chitetezo chimenecho m’njira yolemekezeka koma mosapita m’mbali. Komatu, ana afunika makamaka kuwatsogolera kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, yemwe ndi Gwero la nzeru zonse. Izi n’zimene Mphunzitsi Waluso, Yesu, anali kuchita nthaŵi zonse. Tili otsimikiza kuti buku lino lidzakuthandizani inuyo ndi banja lanu kukonza moyo wanu kuti uzikondweretsa Yehova, ndipo motero mudzapeza madalitso osatha.