Kodi Yesu umamuona ngati ndani—ngati Mfumu yamphamvu kapena ngati mwana wopanda mphamvu?

YESU atakula, anadziŵa kuti anatetezedwa ali mwana. Kodi ukuganiza kuti iye anapemphera kwa Yehova ndi kumuyamika chifukwa chomuteteza?— Kodi ukuganiza kuti Yesu atakula anauza Mariya ndi Yosefe zotani atadziŵa kuti iwo anapulumutsa moyo wake mwa kupita naye ku Igupto?—

Koma Yesu tsopano si mwananso. Sakukhalanso padziko lapansi ngati kale lija. Kodi umaona masiku ano kuti anthu ena akamaganiza za Yesu amaona ngati kuti iye ndi mwana amene ali m’chodyeramo ziŵeto?— Zimenezi zimachitika makamaka pa Khirisimasi pamene m’madera ambiri timaona zithunzi zimene zimasonyeza Yesu ngati mwana.

Ngakhale kuti Yesu sakukhalanso padziko lapansi pano, kodi ukukhulupirira kuti ali moyo?— Inde, anaukitsidwa kwa akufa, ndipo tsopano ndi Mfumu yamphamvu kumwamba. Kodi ukuganiza kuti iye angachite chiyani kuti ateteze anthu amene amamutumikira?— Eya, pamene Yesu anali padziko lapansi pano, anasonyeza mmene akanatetezera aja amene anali kumukonda. Tiye tione mmene anachitira zimenezo tsiku lina pamene anali mu boti ndi ophunzira ake.

 Inali nthaŵi ya kumadzulo. Tsiku lonselo Yesu anali kuphunzitsa anthu m’mphepete mwa nyanja ya Galileya, imene kutalika kwake ndi pafupifupi makilomita 20 ndipo kufupika kwake makilomita 12. Ndiye anauza ophunzira ake kuti: “Tiwolokere kutsidya lija la nyanja.” Atatero, iwo anakwera boti ndipo anayamba ulendo wawo kudutsa nyanjayo. Yesu anali wotopa kwambiri, choncho anapita kumbuyo kwa boti ndi kukagona pa pilo. Posapita nthaŵi, tulo tinamupeza.

Kodi Yesu akunena chiyani ku chimphepo ndi mafundeŵa?

Koma ophunzirawo anakhalabe maso kuti aziyendetsa botilo. Poyamba zonse zinali bwino. Koma kenako panyanjapo panauka chimphepo. Chinali kuwomba kwambiri, ndipo mafunde anali kukula. Mafundewo anayamba kuloŵa mu boti, ndipo linayamba kudzala madzi.

Ophunzirawo anaopa kuti amira. Koma Yesu sanaope. Pajatu anali m’tulo kumbuyo kwa boti. Ndiye ophunzira ake anamuutsa, ndipo anati kwa iye: ‘Mphunzitsi, Mphunzitsi, tipulumutseni; tifa ndi chimphepo.’ Pamenepo, Yesu anauka ndipo analamula mphepoyo ndi mafundewo kuti: “Tonthola, khala bata”!

Nthaŵi yomweyo mphepo ija inasiya, ndipo nyanjayo inakhala bata. Ophunzira aja anadabwa kwambiri. Sanaonepo zinthu ngati  zimenezo chibadwire. Ndiye anayamba kufunsana kuti: “Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye.”—Luka 8:22-25; Marko 4:35-41.

Kodi ukudziŵa kuti Yesu ndani?— Kodi ukudziŵa kumene iye amapeza mphamvu zake zazikuluzo?— Ophunzira sanafunikire kuopa pamene anali limodzi ndi Yesu, chifukwa Yesu sanali munthu ŵamba. Iye anali kuchita zinthu zodabwitsa zimene munthu wina aliyense sakanachita. Taleka ndikuuze zina zimene anachita tsiku lina panyanja patakhala chimphepo.

Zimene ndikuuze zinachitika nthaŵi ina patapita masiku kuchoka pa ulendo woyamba uja. Madzulo, Yesu anauza ophunzira ake kukwera boti ndi kutsogola kupita tsidya lina la nyanja. Koma iye anakwera paphiri yekha. Malo amenewo anali abata ndiponso abwino kuti iye akapemphere kwa Atate ake, Yehova Mulungu.

Ophunzira aja anakwera boti ndi kuyamba ulendo wawo kudutsa  nyanja. Koma sipanatenge nthaŵi ndipo mphepo inayamba kuwomba. Inawomba kwambiri. Apa tsopano unali usiku. Iwo anatsitsa nsalu zimene zimathandiza kuti boti liziyenda ndi mphepo ndipo anayamba kupalasa. Koma sanapite patali chifukwa cha chimphepo chimene anali kulimbana nacho. Botilo linali kugwedezeka kupita kumbuyo kenako kutsogolo chifukwa cha mafunde aakulu, ndipo madzi anali kuloŵa mu botilo. Amunawo analimbikira kuti afike kumtunda, koma anali kulephera.

Yesu anali kuphiri kuja yekha. Apa n’kuti atakhala kumeneko nthaŵi yaitali. Ndiye anaona kuti ophunzira ake ali pangozi chifukwa cha mafunde aakulu aja. Choncho anatsika paphiri paja kufika m’mphepete mwa nyanja. Yesu anali kufuna kuti athandize ophunzira ake, ndipo anayamba kuyenda pa madzi panyanjapo kupita kwa iwo, chimphepo chija chikuwomba!

Kodi iwe utayesa kuyenda pa madzi chingachitike ndi chiyani?— Ukhoza kumira ndi kufa. Koma Yesu amasiyana ndi ife. Ali ndi mphamvu zapadera. Ndiye Yesu uja anayenda mtunda wautali kuti apeze boti. Pamene ophunzira ake anaona Yesu akubwera pamadzi, kunali mbandakucha. Koma iwo sanathe kukhulupirira zimene anali kuonazo. M’malo mwake anaopa kwambiri, ndipo anafuula ndi mantha. Kenako Yesu anati kwa iwo: “Limbani mtima; ndine; musaope.”

Chifukwa chiyani Yesu anachita zodabwitsa?

Yesu atangokwera boti lija, mphepo ija inasiya. Ophunzira anadabwanso kwambiri. Iwo anagwadira Yesu, ndipo anati: “Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.”—Mateyu 14:22-33; Yohane 6:16-21.

Kodi sizikanakhala zosangalatsa ngati tinaliko panthaŵiyo ndi kuona Yesu akuchita zinthu ngati zimenezi?— Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yesu anachita zinthu zodabwitsa zimenezo?— Anachita zimenezo chifukwa chakuti anakonda ophunzira ake ndipo anafuna kuwathandiza. Komanso anachita zinthuzo kuti asonyeze mphamvu yaikulu imene anali nayo imenenso akagwiritsa ntchito m’tsogolo atakhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu.

Kodi Yesu amawateteza bwanji otsatira ake masiku ano?

 Ngakhale masiku ano Yesu nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza otsatira ake kwa Satana amene akuyesetsa kuwaletsa kuti asauze anzawo za Ufumu wa Mulungu. Koma mphamvu zakezo Yesu sazigwiritsa ntchito kuteteza ophunzira ake kuti asadwale kapena kuwachiritsa akadwala. Ngakhale atumwi a Yesu anafa onse. Yakobo mbale wake wa Yohane anaphedwa, ndipo Yohaneyo anaikidwa m’ndende.—Machitidwe 12:2; Chivumbulutso 1:9.

Ndi mmenenso zilili masiku ano. Kaya anthu amatumikira Yehova kapena samutumikira, onse angadwale ndi kufa. Koma posachedwapa, Yesu akayamba kulamulira monga Mfumu m’boma la Mulungu, zinthu zidzasintha. Panthaŵiyo palibe munthu amene adzachita mantha, chifukwa chakuti Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kudalitsa anthu onse amene amamvera iye.—Yesaya 9:6, 7.

Malemba ena amene amasonyeza mphamvu zazikulu za Yesu, amene Mulungu wamusankha kukhala Wolamulira mu Ufumu wa Mulungu, ndi Danieli 7:13, 14; Mateyu 28:18; ndi Aefeso 1:20-22.