MULUNGU anaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edene. Ngakhale kuti Adamu ndi Havayo anafa chifukwa cha kusamvera, Mulungu wakonza kuti ana awo, kuphatikizapo ifeyo lerolino tidzakhale ndi moyo wosatha mu Paradaiso. Baibulo limalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

Ndipo Baibulo limanenanso za “miyamba yatsopano” ndi “dziko latsopano.” (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13) “Miyamba” imene ilipoyi ndi ya maboma a anthu, koma Yesu Kristu ndi awo amene adzalamulira naye pamodzi kumwamba adzapanga “miyamba yatsopano.” Kudzakhalatu kosangalatsa kwambiri pamene miyamba yatsopano imeneyi, yomwe ndi boma lolungama la Mulungu lamtendere, idzalamulira dziko lonse lapansi!

Komano, kodi “dziko latsopano” ndi chiyani?— Dziko latsopano adzakhala anthu abwino okonda Yehova. Ukuonatu eti, kuti Baibulo likamanena za “dziko,” nthaŵi zina limatanthauza anthu okhala m’dzikolo osati dziko lenileni lapansili. (Genesis 11:1; Salmo 66:4; 96:1) Choncho, anthu opanga dziko latsopano adzakhala padziko lapansi pompano.

Dziko lamakono la anthu oipali silidzakhalakonso lidzachoka. Kumbukira kuti ndi dziko la anthu oipa okha limene linawonongedwa pa Chigumula masiku a Nowa. Ndiyeno monga momwe taphunzirira kumbuyoku, dziko lamakono loipali lidzawonongedwa pa Armagedo. Tsopano tiye tione kuti moyo udzakhala wotani m’dziko latsopano la Mulungu itadutsa Armagedo.

 Kodi iweyo ukufuna kudzakhala ndi moyo wosatha mu Paradaiso m’dziko latsopano la Mulungu lamtendere?— Palibe dokotala aliyense amene angatipatse moyo wosatha. Ndipo palibe mankhwala amene angatiteteze kuti tisafe. Njira yokha imene tingakhalire ndi moyo wosatha ndiyo kuyandikira kwa Mulungu basi. Ndipotu Mphunzitsi Waluso amatiuza mmene tingakhalire pafupi kwambiri ndi Mulungu.

Tiye titsegule Baibulo lathu tsopano pa Yohane chaputala 17, vesi 3. Pamenepa tipezapo mawu awa a Mphunzitsi Waluso akuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamutuma.”

Ndiyeno, paja Yesu anati tichite chiyani kuti tikhale ndi moyo wosatha?— Choyamba anati, tidziŵe Atate wathu wakumwamba, Yehova ndi Mwana wake, amene anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kuphunzira Baibulo. Moti buku ili la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso likutithandiza kuchita zimenezo.

Komabe kodi kuphunzira za Yehova kungatithandize bwanji kuti tikhale ndi moyo wosatha?— Eya, monga momwe timafunira chakudya tsiku ndi tsiku, tifunikanso kuphunzira za Yehova tsiku lililonse. Baibulo limanena kuti: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse otuluka m’kamwa mwa Mulungu.’—Mateyu 4:4.

Tifunikanso kudziŵa Yesu Kristu chifukwa Mulungu anatumiza Mwana wakeyo kuti adzachotse machimo athu. Baibulo limati: “Palibe chipulumutso mwa wina yense,” ndipo limanenanso kuti “iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Machitidwe 4:12; Yohane 3:36) Ndiyeno, kodi kumatanthauza chiyani ‘kukhulupirira’ Yesu?— Kumatanthauza kuti timakhulupiriradi Yesuyo ndi kudziŵanso kuti sitingakhale ndi moyo wosatha popanda iye. Kodi ifeyo timakhulupiriradi zimenezo?— Ngati timatero, ndiye kuti tidzapitiriza kuphunzira kwa Mphunzitsi Waluso tsiku lililonse, ndiponso tidzachita zimene amanena.

Njira imodzi yabwino imene tingaphunzirire kwa Mphunzitsi  Waluso ndiyo kuŵerenga buku limeneli mobwerezabwereza ndi kuyang’ana zithunzi zonse ndi kuziganizira bwino. Uziyesa kuyankha mafunso amene ali pa zithunzizo. Ungathenso kuŵerenga buku limeneli ndi amayi ako kapena atate ako. Ngati makolo ako palibe, ungaŵerenge ndi anthu ena aakulu komanso ngakhale ndi ana anzako. Kodi sizingakhale bwino utathandiza anthu ena kuphunzira kwa Mphunzitsi Waluso zimene anthuwo ayenera kuchita kuti nawonso akapeze moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu?—

Baibulo limatiuza kuti: “Dziko lapansi lipita,” ndiyeno limafotokozanso mmene tingapezere moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Ilo limati: ‘Iye amene achita zimene Mulungu amafuna adzakhala ku nthaŵi yonse.’ (1 Yohane 2:17) Ndiyeno kodi ndi motani mmene tingapezere moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu limeneli?— Eya, mwa kudziŵa Yehova ndi Mwana wake wokondedwayo, Yesu. Komanso tifunika kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzira. Kuphunzira kwako buku limeneli kukuthandize kuchita zimenezi.