KODI winawake anayamba wakuuzapo kuti uchite chinthu choipa?— Kodi anachita kukukakamiza kuti uchite zimenezo? Kapena kodi ananena kuti ndi zosangalatsa ndipo si zoipa?— Munthu akanena zimenezi ndiye kuti akutiyesa.

Kodi tiyenera kuchita chiyani pamene munthu wina akutiyesa? Kodi ukuganiza kuti tiyenera kumumvera ndi kuchita zoipa zimene akutiuza?— Yehova Mulungu sangasangalale nazo zimenezo. Koma kodi ukudziŵa amene angasangalale nazo?— Ee, ndi Satana Mdyerekezi.

Satana ndi mdani wa Mulungu, ndipo ndi mdani wathunso. Sitingamuone chifukwa iye ndi mzimu. Koma iye amationa. Nthaŵi ina Mdyerekezi analankhula ndi Yesu, Mphunzitsi Waluso, ndipo anamuyesa. Tiye tione zimene anachita Yesu. Tikatero tidzadziŵa zoyenera kuchita munthu wina akatiyesa.

Kodi Yesu ayenera kuti anayamba kukumbukira chiyani pamene anabatizidwa?

Nthaŵi zonse Yesu anafuna kuchita zimene Mulungu amafuna. Anasonyeza zimenezi kwa anthu mwa kubatizidwa mu mtsinje wa Yordano. Yesu atangobatizidwa Satana anamuyesa. Baibulo limati ‘kumwamba kunatsegukira’ Yesu. (Mateyu 3:16) Izi zingatanthauze kuti pamenepa Yesu anayamba kukumbukira zonse zimene anali kuchita pamoyo wake woyambirira ali ndi Mulungu kumwamba.

Atabatizidwa Yesu anapita ku chipululu kuti akaganize za zinthu zimene anayamba kukumbukirazo.  Panatha masiku 40 usana ndi usiku ali komweko. Nthaŵi yonseyi Yesu sanadye kalikonse, ndipo anamva njala kwambiri. Ndi panthaŵi imeneyi pamene Satana anayesa Yesu.

Kodi Mdyerekezi anagwiritsa ntchito miyala motani kuti ayese Yesu?

Mdyerekezi anati: ‘Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi isanduke buledi.’ Komatu ndiye buledi akanakoma kwambiri panthaŵiyi! Ndiye kodi Yesu akanatha kusandutsa miyala kukhala buledi?— Inde akanatha. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yesu, Mwana wa Mulungu, anali ndi mphamvu zapadera.

Kodi iwe ukanasandutsa mwala kukhala buledi Mdyerekezi akanakuuza kuti utero?— Yesu anali ndi njala. Ndiye mmene iweyo ukuonera, kodi sikukanakhala bwino kuchita zimenezi kamodzi kokha basi?— Yesu anadziŵa kuti ndi kulakwa kugwiritsa ntchito mphamvu zake mwa njira imeneyo. Yehova anamupatsa mphamvuzo kuti akokere anthu kwa Mulungu, osati kuti azipezera zimene akufuna.

Motero Yesu anauza Satana zimene zinalembedwa m’Baibulo kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” Yesu anadziŵa kuti kuchita zokondweretsa Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi chakudya.

Koma Mdyerekezi anayesanso Yesu kachiŵiri. Anapita naye ku Yerusalemu ndi kumukweza pamwamba pa kachisi. Kenako Satana anati: ‘Ngati ndinu Mwana wa Mulungu,  mudziponye pansi kuchokera pamwamba pano. Pakuti kunalembedwa kuti angelo a Mulungu adzakutetezani kuti musavulale.’

N’chifukwa chiyani Satana ananena zimenezi?— Ananena zimenezi kuti ayese Yesu kuchita mwadala zinthu zimene zikanamupweteka. Koma apanso Yesu sanamvere Satana. Anauza Satana kuti: “Kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.” Yesu anadziŵa kuti ndi kulakwa kuyesa Yehova mwa kuika dala moyo wake pachiswe.

Komabe Satana sanaleke. Kenako anatenga Yesu ndi kupita naye paphiri lalitali zedi. Kumeneko anamuonetsa maufumu, kapena kuti maboma, onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. Ndiyeno Satana anauza Yesu kuti: ‘Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundilambira.’

Taganizira mawu a Mdyerekeziwo. Kodi maufumu, kapena kuti maboma a anthu, onsewo analidi ake Satana?— Yesu sanakane kuti anali a Satana. Akanakhala kuti sanali a Satana, Yesu akanamutsutsa. Inde, Satana ndiye amene amalamulira mayiko onse padziko lapansi pano. Moti Baibulo limanena kuti iye ndiye “mkulu wa dziko ili lapansi.”—Yohane 12:31.

N’chifukwa chiyani Satana anati apatsa Yesu maufumu onseŵa?

Kodi iwe ungachite chiyani ngati Mdyerekezi walonjeza kuti akupatsa chinachake ukamulambira?— Yesu anadziŵa kuti kulambira Mdyerekezi ndi kulakwa ngakhale akanapatsidwa chinthu chabwino bwanji. Motero Yesu anati: ‘Choka Satana! Baibulo limati uyenera kulambira Yehova Mulungu wako ndi kutumikira iye yekha basi.’—Mateyu 4:1-10; Luka 4:1-13.

Kodi n’chiyani chimene iwe udzachita ngati wayesedwa?

Nafenso timayesedwa. Kodi ndi ziyeso ziti zimene ukuzidziŵa?— Taona chitsanzo ichi. Amayi ako akhoza kuphika mandasi kapena chikondamoyo. Angakuuze kuti usadye mudyera limodzi panthaŵi inayake. Koma iwe uli ndi njala, ndiyetu ungafune kutenga ndi kudya. Kodi udzamvera amayi ako?— Satana amafuna kuti usawamvere.

Kumbukira Yesu. Nayenso anali ndi njala kwambiri. Koma iye anadziŵa  kuti kukondweretsa Mulungu ndi kofunika kwambiri kuposa kudya. Ngati iwe umvera zimene amayi ako amanena, udzakhala ngati Yesu.

Mwina ana ena angakuuze kuti umwe mapilitsi enaake. Angakuuze kuti ukamwa umva bwino kwambiri ndipo usangalala. Koma mapilitsi ameneŵa akhoza kukhala mankhwala osokoneza bongo. Angakudwalitse kwambiri ndipo ukhoza kufa. Kapena munthu wina angakupatse fodya,  yemwenso amasokoneza bongo, ndi kukukakamiza kuti usute. Kodi iwe udzachita chiyani?—

Kumbukira Yesu. Satana anauza Yesu kuika dala moyo wake pachiswe mwa kumuuza kuti alumphe kuchokera pamwamba pa kachisi. Komatu Yesu sanachite zimenezo. Kodi iwe udzachita chiyani ngati munthu wina akukuuza kuchita chinthu choopsa?— Yesu sanamvere Satana. Iwenso suyenera kumvera aliyense amene akukuuza kuchita zinthu zoipa.

N’chifukwa

chiyani si bwino kugwiritsa ntchito mafano polambira?

Nthaŵi ina ukhoza kuuzidwa kuti ulambire fano, zimene Baibulo limatiuza kuti sitiyenera kuchita. (Eksodo 20:4, 5) Mwina ungakhale mwambo winawake kusukulu kwanu. Akhoza kukuuza kuti usadzapitenso kusukuluko ngati ukana kuchita zimenezo. Kodi iwe udzachita chiyani?—

Kuchita zinthu zabwino sikuvuta ngati wina aliyense akuchita zomwezo. Komabe, kuchita zinthu zabwino kungakhale kovuta kwambiri pamene anthu ena akutikakamiza kuchita zoipa. Akhoza kunena kuti zimene akuchita si zoipa kwenikweni. Koma funso lofunika kwambiri ndi lakuti, Kodi Mulungu amanena chiyani za nkhani imeneyo? Iye ndiye amadziŵa bwino kwambiri.

Choncho zilizonse zimene anthu angatiuze kuchita, ifeyo sitiyenera kuchita zinthu zimene Mulungu amati ndi zoipa. Tikatero nthaŵi zonse tidzakondweretsa Mulungu, ndipo sitidzayesa ngakhale pang’ono kusangalatsa Mdyerekezi.

Mungapeze mfundo zina za mmene mungakanire ziyeso za kuchita zinthu zoipa pa Salmo 1:1, 2; Miyambo 1:10, 11; Mateyu 26:41; ndi 2 Timoteo 2:22.