Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 30

Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha

Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha

KODI umaona kuti kutumikira Yehova ndi kosavuta?— Mphunzitsi Waluso ananena kuti kudzakhala kovuta. Usiku woti aphedwa maŵa lake, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.”—Yohane 15:18.

Petro anadzitama kuti sangalekane naye Yesu, koma Yesu ananena kuti usiku womwewo Petro amukana maulendo atatu kuti samudziŵa. Ndipotu ndi zimene Petro anachitadi! (Mateyu 26:31-35, 69-75) Kodi ukuganiza kuti zinatheka bwanji kuti amukane?— Zinatheka chifukwa chakuti Petro anachita mantha, ndipo nawonso atumwi ena anachita manthanso.

Kodi ukudziŵa chifukwa chake atumwiwo anachita mantha?— Ndi chifukwa chakuti iwo sanachite chinachake chofunika kwambiri. Kudziŵa zimenezi kungatithandize kutumikira Yehova, ngakhale munthu wina anene mawu anji kaya atichitire zinthu zotani. Koma tiye tiyambe taona zimene zinachitika usiku womaliza umene Yesu anali ndi atumwi ake.

Choyamba, onse pamodzi anachita phwando la Paskha. Paskha chinali chakudya chapadera chimene anthu a Mulungu anali kudya chaka chilichonse kuti azikumbukira kuti analanditsidwa ku ukapolo ku Igupto. Kenako Yesu anayambitsanso kudya chakudya china chapadera ndi atumwi akewo. M’mutu wina kutsogoloku tidzafotokoza za chakudyachi ndiponso mmene chimatithandizira kukumbukira Yesu. Atadya chakudya chimenecho komanso atalimbikitsa atumwi ake, Yesu anapita ku munda wa Getsemane ndi atumwi akewo. Anali kukonda kupita kumalo ameneŵa nthaŵi zambiri.

 Yesu anapita kukapemphera payekha pa malo ena mu mundamo. Anauzanso Petro, Yakobo, ndi Yohane kuti azipemphera. Koma iwo anagona tulo. Kwa maulendo atatu Yesu anapita kukapemphera payekha, ndipo kwa maulendo atatu anabwera ndi kupeza Petro ndi anzakewo akugona! (Mateyu 26:36-47) Kodi ukudziŵa chifukwa chake iwo anafunika kukhalabe maso ndi kumapemphera?— Tiye tikambirane zimenezi.

Ndi chifukwa chiyani Petro, Yakobo, ndi Yohane sanafunike kugona?

Madzulo a usiku umenewo, Yudasi Isikariote anali limodzi ndi Yesu ndi atumwi ena pa Paskha uja. Mwina ukukumbukira kuti Yudasi anali atasanduka wakuba. Apa tsopano iye anakhala wopereka Yesu kwa adani ake. Anali kudziŵa malo amene nthaŵi zambiri Yesu anali kukumanako ndi atumwi ake mu munda wa Getsemane. Ndiye Yudasi anapita komweko ndi asilikali kuti akagwire Yesu. Atafika Yesu anawafunsa kuti: “Mufuna yani?”

Asilikaliwo anayankha kuti: “Yesu.” Yesu sanachite mantha, ndipo anayankha kuti: “Ndine.” Asilikaliwo anadabwa kwambiri ndi kulimba mtima kwa Yesu moti anabwerera m’mbuyo ndi kugwa pansi. Ndiyeno Yesu ananena kuti: ‘Ngati mukufuna ine, alekeni atumwi anga azipita.’—Yohane 18:1-9.

Asilikaliwo atagwira Yesu ndi kumumanga, atumwi anachita mantha ndi kuthaŵa. Koma Petro ndi Yohane anafuna kuona zimene zichitike, motero iwo anali kutsatira gululo chapatali ndithu. Yesu anapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe. Popeza kuti Yohane anali wodziŵika kwa mkulu wa ansembeyo, munthu wodikira pakhomo analola Yohaneyo ndi Petro kuloŵa kumpanda.

Ansembe anali atasonkhana kale kunyumba ya Kayafa kuja kuti aweruze Yesu. Iwo anali kufuna kuti Yesu aphedwe. Ndiye anabweretsa mboni zimene zinali kunena zabodza zokhudza iye. Anthuwo anamenya nkhonya Yesu ndi kumumenya mbama. Pamene zonsezi zinali kuchitika ndi kuti Petro ali chapafupi pomwepo.

Mtsikana wantchito, yemwe ndi wodikira pakhomo uja amene analoŵetsa  Petro ndi Yohane mu mpanda, anazindikira Petro. “Iwenso unali ndi Yesu,” iye anatero. Koma Petro anakana kuti Yesu samudziŵa. Patapita kanthaŵi mtsikana winanso anazindikira Petro ndipo anauza anthu amene anali pamenepo kuti: “Uyonso anali ndi Yesu.” Apanso Petro ananena kuti samudziŵa Yesu. Panthaŵi inanso anthu ena anaona Petro ndi kumuuza kuti: ‘Ndithudi iwenso ndiwe wa gulu lomweli.’ Kwa nthaŵi yachitatu Petro anakana, ndipo ananena kuti: ‘Munthu ameneyu ine sindimudziŵa.’ Petro anachita kulumbira kuti akunena zoona, ndipo Yesu anatembenuka ndi kumuyang’ana.—Mateyu 26:57-75; Luka 22:54-62; Yohane 18:15-27.

Ndi chifukwa chiyani Petro anachita mantha kwambiri mpaka kunama kuti Yesu samudziŵa?

Kodi ukudziŵa chifukwa chake Petro ananena zabodza?— Inde, ndi chifukwa chakuti anachita mantha. Koma kodi anachita mantha chifukwa chiyani? Kodi iye sanachite chiyani kuti akhale wolimba mtima? Taganizira. Kodi Yesu anachita chiyani kuti akhale wolimba mtima?— Anapemphera kwa Mulungu, ndipo Mulungu anamuthandiza kuti alimbe mtima. Ndipo ungakumbukire kuti Yesu anauza Petro maulendo atatu kuti apemphere, kuti asagone ndi kuti akhale akudikira. Koma kodi chinachitika ndi chiyani?—

 Ulendo uliwonse Petro anagona. Iye sanapemphere, ndipo sanadikire. Tsono chifukwa chosachita zimenezi kugwidwa kwa Yesu kunamudzidzimutsa. Kenako pamene Yesu anali kumuweruza, Petro anaopa kwambiri kuona anthu akumenya Yesu ndi kupangana kuti amuphe. Komatu, maola angapo chabe izi zisanachitike, kodi Yesu anauza atumwi ake kuyembekezera chiyani?— Yesu anawauza kuti monga dziko linada iye, nawonso likawada.

Kodi zingatheke bwanji kuti iweyo zikuchitikire zofanana ndi zimene zinachitikira Petro?

Tsopano tiye tione zimene zingachitikire ifeyo zomwe zingafanane ndi zimene zinachitikira Petro. Tayerekeza kuti uli m’kalasi ndiye ena ayamba kunyoza anthu amene sachitira sailuti mbendera  kapena amene sakondwerera Khirisimasi. Bwanji ngati kenako wina akufunsa iweyo kuti: “Eti ndi zoona kuti iweyo suchitira sailuti mbendera?” Mwina enanso akunena kuti: “Akuti suchita Khirisimasi eti!” Kodi ungaope kunena zoona?— Kodi ungaganize zonena bodza monga anachitira Petro?—

Pambuyo pake Petro anamva chisoni kwambiri kuti anakana Yesu. Atazindikira zimene anachita, anatuluka panja ndi kukalira. Ee, iye analapa ndi kuyambanso kutsatira Yesu. (Luka 22:32) Ndiyeno taganizira nkhaniyi. Kodi ndi chiyani chimene chingatithandize kuti tisachite mantha kwambiri ndi kunena zofanana ndi zimene ananena Petro?— Kumbukira kuti Petro sanapemphere ndiponso sanadikire. Tsono pamenepa iwe unganene kuti tifunika kuchita chiyani kuti tikhale wophunzira wa Mphunzitsi Waluso?—

Ndithudi tifunika kupemphera kwa Yehova kuti atithandize. Kodi ukudziŵa zimene Mulungu anamuchitira Yesu atapemphera?— Anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse. (Luka 22:43) Kodi ukuganiza kuti ifeyo angelo a Mulungu angatithandize?— Baibulo limanena kuti: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Salmo 34:7) Koma kuti Mulungu atithandize, tifunika kuchita zinthu zinanso kuwonjezera pa kupemphera. Kodi unganene kuti ndi chiyani china chimene tifunika kuchita?— Yesu anauza ophunzira ake kuti asagone koma apitirize kudikira. Kodi uganiza tingachite zimenezi motani?—

Tifunika kumvetsera kwambiri zimene zimanenedwa pa misonkhano yathu yachikristu ndi kumatsatira zimene timaŵerenga m’Baibulo. Koma tifunikanso kumapemphera kwa Yehova nthaŵi zonse ndi kumupempha kuti atithandize kumutumikira. Tikachita zimenezi, adzatithandiza kuthetsa mantha amene timakhala nawo. Tikatero tidzasangalala pamene tikhala ndi mwayi wouza ena za Mphunzitsi Waluso ndi Atate ake.

Malemba aŵa angatithandize kuti tisamaope anthu, zimene zingatilepheretse kuchita zinthu zabwino: Miyambo 29:25; Yeremiya 26:12-15, 20-24; ndi Yohane 12:42, 43.