KODI umadziŵa kuti tsankho ndi chiyani?— Tsankho ndi kusafuna kapena kusakonda munthu wina chifukwa chakuti iye amaoneka mosiyana ndi iweyo kapena chifukwa chakuti amalankhula chinenero china. Chotero munthu watsankho ndi munthu amene amaganizira munthu wina zoipa asanamudziŵe n’komwe.

Kodi ukuganiza kuti ndi bwino kudana ndi munthu wina usanamudziŵe bwinobwino kapena chifukwa chakuti iye ndi wosiyana ndi iweyo?— Ayi, tsankhotu si labwino, ndipo ndi kuipa mtima. Ngati munthu wina ali wosiyana ndi ife, si chifukwa chimenecho chakuti timuchitire zoipa.

Kodi umadziŵapo munthu wina aliyense amene khungu lake ndi losiyana ndi lako kapena amene amalankhula chinenero china osati chimene iwe umalankhula?— Mwinanso ukudziŵa anthu ena amene amaoneka mosiyana ndi iwe chifukwa chakuti anavulala kapena akudwala. Kodi anthu otero amene safanana ndi iweyo umawakonda ndi kuwakomera mtima?—

Kodi anthu amene ndi osiyana ndi ifeyo tiyenera kuwachitira zotani?

Ngati timvera Mphunzitsi Waluso, Yesu Kristu, tidzakhala okoma mtima kwa aliyense. Ife sitiyenera kusiyanitsa kuti munthu akuchokera dziko liti kapena ndi wakhungu lotani. Tiyenera kukhala okoma mtima. Ngakhale kuti si zimene anthu onse amakhulupirira, imeneyi ndi mfundo imene Yesu anaphunzitsa. Tiye tikambirane nkhani imeneyi.

Myuda watsankho anakafunsa Yesu kuti, ‘Kodi ndiyenera kuchita chiyani kuti ndikhale ndi moyo kosatha?’ Yesu anadziŵa kuti munthuyu anali kufuna kuti Yesuyo anene kuti tiyenera kuchitira zabwino anthu a mtundu wathu kapena a dziko lathu okha. Ndiye m’malo moti Yesu  ayankhe funsolo, anafunsa munthuyo kuti: ‘Kodi Chilamulo cha Mulungu chimanena kuti tizichita chiyani?’

Munthuyo anayankha kuti: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndiponso uzikonda mnansi wako monga udzikondera iwe mwini.’ Yesu anati: ‘Wayankha bwino. Pitiriza kuchita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo wosatha.’

Komabe munthuyu sanafune kumakomera mtima anthu osiyana naye kapenanso kumawakonda. Choncho anayesa kupeza pothaŵira. Anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi mnansi wanga ndani?’ Iye mwina anafuna kuti Yesu anene kuti: “Anansi ako ndi anzako” kapena kuti, “Anansi ako ndi anthu amene amaoneka mofanana ndi iweyo.” Koma Yesu poyankha funso lakelo anafotokoza nkhani inayake yonena za Myuda ndi Msamariya. Nkhaniyo inali motere.

Munthu wina anali kuyenda panjira yochokera ku mudzi wa Yerusalemu kupita ku Yeriko. Munthuyu anali Myuda. Akuyenda m’njiramo anakumana ndi achifwamba. Anamugwetsa pansi ndi kumulanda ndalama ndi zovala. Achifwambawo anamumenya kwambiri moti anamusiya atatsala pang’ono kufa m’mbali mwa njira.

Pasanathe nthaŵi yaitali, wansembe wina anali kuyenda m’njira  yomweyo. Anaona munthu anapwetekedwa kwambiri uja. Kodi ukanakhala iweyo ukanachita chiyani?— Eya, wansembeyo anangodutsa mbali ina ya njirayo ndi kumapitirira ndi ulendo wake. Sanaime n’komwe. Palibe chilichonse chimene anachitapo kuti athandize munthuyo.

Kenako panjirapo panafika munthu wina wokondanso kupembedza kwambiri. Iye anali Mlevi ndipo amatumikira pa kachisi ku Yerusalemu. Kodi iye anaima kuti amuthandize?— Ayi. Anachita zomwe anachita wansembe zija.

Patapita nthaŵi panafika Msamariya. Kodi ukumuona uyo akubwera pakonayo mumsewumo?— Anaona Myudayo ali gone atapwetekeka kwambiri. Tsonotu Asamariya ndi Ayuda ambiri sanali kugwirizana. (Yohane 4:9) Ndiye kodi Msamariya uyu anangodutsa, munthu wopwetekayu  wosamuthandiza? Kodi iye anaganiza kuti: ‘Ndithandize Myuda chifukwa chiyani? Iye sakanandithandiza ndikanakhala kuti ndapweteka’?

N’chifukwa chiyani Msamariyayu anali mnansi wabwino?

Msamariyayo anayang’ana munthu anali m’mbali mwa njirayo, ndipo anamumvera chisoni. Iye anaganiza kuti si bwino kumusiya pomwepo kuti afe. Choncho anatsika pa bulu wake ndi kupita panali munthuyo kukamukonza mabala ake. Anamuthira mafuta ndi vinyo pa mabalawo kuti apole msanga. Kenako pa mabalapo anamangapo nsalu.

Msamariyayo ananyamula munthu wopweteka uja bwinobwino ndi kumuika pa bulu wake. Ndiyeno anayenda naye pang’onopang’ono mpaka anafika pa nyumba yogonamo alendo. Msamariya uja anapeza malo pamenepo oti munthuyo akhale kaye, ndipo anamusamalira bwino.

Ndiyeno Yesu anafunsa munthu anali kulankhula naye uja kuti: ‘Kodi ndi uti wa anthu atatu ameneŵa amene ukuganiza kuti anali mnansi wabwino?’ Kodi iweyo unganene kuti ndi uti? Wansembe, Mlevi, kapena Msamariya?—

Munthu amene anali kulankhula ndi Yesu anayankha kuti: ‘Munthu amene anaima ndi kusamalira munthu wopwetekayo ndiye anali mnansi wabwino.’ Yesu anati: ‘Wayankha bwino. Pita nawenso uzichita zomwezo.’—Luka 10:25-37.

 Imeneyi ndi nkhani yabwino zedi, eti? Imafotokoza bwino amene ali anansi athu. Anansi athu si anthu okhawo amene ndi anzathu zedi. Ndiponso si anthu okhawo amene timafanana nawo khungu kapena amene timalankhula chinenero chimodzi. Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenera kukhala okoma mtima kwa anthu ochokera kwina kulikonse, ooneka mulimonsemo, ndiponso olankhula chinenero chilichonsecho.

Ndi mmene Yehova Mulungu alili. Alibe tsankho. Yesu anati: ‘Atate wanu wakumwamba amawalitsira dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino. Ndipo amagwetsa mvula pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe.’ Ukuonatu, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, monga mmene Mulungu amachitira.—Mateyu 5:44-48.

Kodi iweyo ungakhale mnansi wabwino motani?

Ndiyeno iwe utaona munthu wina wapweteka, kodi ungachite chiyani?— Nanga bwanji munthuyo atakhala kuti ndi wochokera dziko lina kapena khungu lake ndi losiyana ndi lako? Iye ndi mnansi wako ndithu, ndipo uyenera kumuthandiza. Ngati ukuona kuti ndiwe wamng’ono moti sungathe kumuthandiza, ukhoza kuuza munthu wina wamkulu. Mwinanso ukhoza kuitana aphunzitsi kusukulu. Ukatero udzakhala wokoma mtima monga Msamariya uja.

Mphunzitsi Waluso amafuna kuti ife tikhale okoma mtima. Amafuna kuti tizithandiza ena mosaganizira kuti ndi ndani. Ndicho chifukwa chake anafotokoza nkhani imeneyi ya Msamariya wokoma mtima.

Pa nkhani imeneyi ya kukhala okoma mtima kwa anthu ena ngakhale a mtundu wina kapena dziko lina, ŵerengani Miyambo 19:22; Machitidwe 10:34, 35; ndi Machitidwe 17:26.