Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 24

Usakhale Wakuba

Usakhale Wakuba

KODI winawake anayamba wakuberapo chinthu chako?— Kodi unamva bwanji?— Aliyenseyo amene anakubera anali mbala, ndipo palibe amene amakonda munthu wakuba. Kodi ukuganiza kuti zimayamba bwanji kuti munthu akhale wakuba? Kodi amabadwa wakuba?—

Taphunzira posachedwapa kuti anthu amabadwa ndi uchimo. Motero tonsefe ndife opanda ungwiro. Komatu palibe amene amabadwa ali wakuba. Kumene amachokera munthu wakuba kungakhale anthu abwino okhaokha. Makolo ake, akulu ake kapena ang’ono ake, ndiponso alongo ake onse angakhale anthu oona mtima. Koma mtima wake munthuyo wofuna ndalama ndiponso zinthu zimene angagule ndiwo ungamuchititse kuyamba kuba.

Kodi iwe unganene kuti ndani anali woyamba kuba?— Tiye tiganizirepo. Pamene Mphunzitsi Waluso anali kumwamba anali kumudziŵa wakuba ameneyu. Wakubayo anali mngelo. Koma popeza kuti angelo onse amene Mulungu anapanga anali angwiro, kodi mngelo ameneyo anakhala wakuba motani?— Eya, monga tinaphunzirira m’Mutu 8 wa buku lino, iye anafuna chinthu chimene sichinali chake. Kodi ukuchikumbukira?—

Mulungu atalenga munthu wamwamuna ndi munthu wamkazi oyamba, mngelo ameneyo anafuna kuti iwo azimulambira. Komatu iye analibe ufulu woti iwo azimulambira. Iwo anayenera kulambira Mulungu. Tsonotu iye anaba kulambira kumeneko! Mwa kuchititsa Adamu ndi Hava kumulambira, mngelo ameneyu anakhala wakuba. Anakhala Satana Mdyerekezi.

Kodi chimachititsa munthu kukhala wakuba ndi chiyani?— Ndi mtima wake wofuna chinthu chimene si chake. Mtima woterewu ukhoza  kukula kwambiri mpaka ungachititse anthu abwino kuchita zoipa. Nthaŵi zina anthu akuba amangopitirizabe kuba osasiya kuti azichita zabwino. Mmodzi wa anthu oterowo anali mtumwi wa Yesu. Dzina lake anali Yudasi Isikariote.

Yudasi anali kudziŵa kuti kuba ndi kulakwa chifukwa anaphunzira Chilamulo cha Mulungu kuyambira ali wamng’ono. Anali kudziŵa kuti panthaŵi ina Mulungu analankhula kuchokera kumwamba ndi kuuza anthu ake kuti: ‘Musamabe.’ (Eksodo 20:15) Yudasi atakula, anakumana ndi Mphunzitsi Waluso ndipo anakhala wophunzira wake. Kenako Yesu anasankha Yudasi kukhala mmodzi wa atumwi ake 12.

Yesu ndi atumwi ake anali kuyendera limodzi, ndiponso anali kudyera limodzi. Ndipo ndalama zonse zimene gulu lawo linali nazo anali kuziika m’bokosi. Yesu anapatsa Yudasi bokosi limenelo kuti azisunga. Zoona, ndalamazo sizinali zake Yudasi. Koma kodi ukudziŵa zimene Yudasi anachita patapita nthaŵi?—

Ndi chifukwa chiyani Yudasi anali kuba?

Yudasi anayamba kutengamo ndalama m’bokosi lija pomwe sanafunike kuchita zimenezo. Anali kutengamo pamene ena sanali kumuona, ndipo anali kuyesetsa kupeza njira zoti azipezera ndalama zambiri. Anayamba kuganiza za ndalama nthaŵi zonse. Tiye tione zimene anachita chifukwa cha mtima wake wolakwika umenewu kutatsala masiku ochepa kuti Mphunzitsi Waluso aphedwe.

Mariya, yemwe anali mlongo wake wa Lazaro mnzake wa Yesu, anatenga mafuta abwino kwambiri ndi kuwathira pa mapazi a Yesu. Koma Yudasi anadandaula. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Iye ananena kuti anadandaula chifukwa chakuti zikanakhala bwino mafutawo akanagulitsa ndiye ndalama zakezo ndi kupatsa anthu osauka. Koma zoona zake ndi zakuti iye anafuna kuti m’bokosi muja mukhale ndalama zambiri kuti aziba bwino.—Yohane 12:1-6.

Yesu anauza Yudasi kuti asavutitse Mariya yemwe anali atamukomera mtima chonchi. Yudasi sanagwirizane nazo zimene Yesu anamuuza, choncho anapita kwa akulu ansembe omwe anali kudana ndi Yesu. Iwo  anali kufuna kugwira Yesu, koma anali kufuna kumugwira usiku kuti anthu asawaone.

Yudasi anauza ansembewo kuti: ‘Mutandipatsa ndalama ndingakuuzeni mmene mungagwirire Yesu. Mundipatsa zingati?’

Ansembewo anayankha kuti: ‘Tikupatsa ndalama 30 zasiliva.’—Mateyu 26:14-16.

Yudasi anatenga ndalamazo. Zinangokhala ngati kuti anali kugulitsa Mphunzitsi Waluso kwa anthuwo! Kodi ukuganiza munthu angachite zinthu zoipa chonchi?— Komatu ndi zimene zimachitika munthu akakhala wakuba ndalama. Amakonda kwambiri ndalama kuposa mmene amakondera anthu ena ngakhalenso Mulungu amene.

Mwina iwe unganene kuti, ‘Ine sizidzatheka kukonda kwambiri chinthu china kuposa mmene ndimakondera Yehova Mulungu.’ Maganizo amenewo ndi abwino. Pamene Yesu anasankha Yudasi kukhala mtumwi, mwinamwake nayenso Yudasi anaganiza chomwecho. Enanso amene anakhala akuba mwina analinso kuganiza choncho. Tiye tikambirane za ena a iwo.

Kodi Akani ndi Davide akuganiza zinthu zoipa zotani?

Mmodzi wa iwo anali mtumiki wa Mulungu wotchedwa Akani, amene analipo kalekale Mphunzitsi Waluso asanabadwe. Akani anaona  chovala chokongola, golide, ndi siliva. Sizinali zake. Baibulo limanena kuti zinali za Yehova chifukwa zinatengedwa kwa adani a anthu a Mulungu. Koma Akani anazikhumbira kwambiri mpaka kuziba.—Yoswa 6:19; 7:11, 20-22.

Nachi chitsanzo china. Kalekalelo, Yehova anasankha Davide kukhala mfumu ya Aisrayeli. Tsiku lina, Davide anayamba kuyang’ana mkazi wokongola dzina lake Bateseba. Anali kumangoyang’ana Bateseba ndi kumaganiza zomutenga kukakhala naye kunyumba kwake. Komatu iye anali mkazi wa Uriya. Kodi uganiza kuti Davide anafunika kuchita chiyani?—

Davide anafunika kuleka kuganiza zokhala ndi Bateseba. Koma sanatero. Motero Davide anatenga Bateseba ndi kupita naye kunyumba kwake. Ndipo kenako anakonza  zoti Uriya aphedwe. Ndi chifukwa chiyani Davide anachita zinthu zoipa zimenezi?— Ndi chifukwa chakuti anapitiriza kufuna mkazi wa mwini wake.—2 Samueli 11:2-27.

Kodi Abisalomu anali wakuba m’njira yotani?

Chifukwa chakuti Davide anamva chisoni ndi zimene anachita, Yehova anamulola kukhalabe ndi moyo. Koma kuchokera pamenepo Davide anakumana ndi mavuto ambiri. Mwana wake Abisalomu anafuna kumulanda ufumu. Abisalomu amati anthu akabwera kudzaonana ndi Davide, iye anali kuwakupatira ndi kuwampsompsona. Baibulo limanena kuti: ‘Abisalomu anali kukopa mitima ya anthu a Israyeli.’ Anachititsa anthuwo kufuna kuti iye akhale mfumu m’malo mwa Davide.—2 Samueli 15:1-12.

Kodi nthaŵi ina unayamba wafunapo kwambiri chinthu china, ngati mmene anachitira Akani, Davide, ndi Abisalomu?— Ngati chinthucho ndi cha winawake, kutenga popanda kukuloleza ndi kuba. Kodi ukukumbukira chimene wakuba woyambirira, Satana, anafuna?— Anafuna kuti anthu azilambira iye m’malo molambira Mulungu. Motero Satana anaba pamene anachititsa Adamu ndi Hava kumvera iye.

Munthu akakhala ndi chinthu ali ndi ufulu wonena amene angachigwiritse ntchito. Mwachitsanzo, ungapite kukaseŵera ndi ana ena kunyumba kwawo. Kodi ndi bwino kutenga chinthu cha kumeneko ndi kupita nacho kwanu?— Ngati atate awo a anzakowo kapena amayi awo sanakuuze kuti utenge, si bwino kutenga. Ngati utenga chinthu mosapempha ndi kubwera nacho kuno, ndi kuba kumeneko.

Kodi ndi chifukwa chiyani iwe ungaganize kuti ube?— Ungaganize zimenezo chifukwa chakuti ukufuna chinthu chimene si chako. Ngakhale kuti palibe munthu amene akuone ukutenga, kodi ndani amene amakuona?— Yehova Mulungu. Ndipo tizikumbukira kuti Mulungu amadana ndi kuba. Ndiyetu kukonda Mulungu ndi anansi ako kudzakuthandiza kuti usakhale wakuba.

Baibulo limanena momveka bwino kuti kuba ndi kulakwa. Ŵerengani Marko 10:17-19; Aroma 13:9; ndi Aefeso 4:28.