NDIKHULUPIRIRA ungavomereze kuti pali winawake wamkulu ndiponso wamphamvu kuposa tonsefe. Kodi ukuganiza kuti ameneyo ndani?— Ndi Yehova Mulungu. Nanga bwanji Mwana wake, Mphunzitsi Waluso uja? Kodi ndi wamkulu kuposa ife?— Inde, nayenso ndi wamkulu kuposa ife.

Yesu anali kukhala ndi Mulungu kumwamba. Mwana ameneyu anali mzimu, kapena kuti mngelo. Kodi Mulungu anapanganso mizimu ina, kapena kuti angelo, kukhala ana ake?— Inde, anapanga mamiliyoni ambirimbiri. Angelo ameneŵa nawonso ndi aakulu ndiponso amphamvu kuposa ifeyo.—Danieli 7:10; Ahebri 1:7.

Kodi ukukumbukira dzina la mngelo amene analankhula ndi Mariya?— Anali Gabrieli. Gabrieli anauza Mariya kuti mwana wake adzakhala Mwana wa Mulungu. Mulungu anaika m’mimba mwa Mariya moyo wa Mwana wake yemwe anali mzimu kuti Yesu abadwe monga khanda padziko lapansi.—Luka 1:26, 27.

Kodi Mariya ndi Yosefe ayenera kuti anali kumuuza zotani Yesu?

Kodi iweyo umakhulupirira zodabwitsa zimenezi? Kodi umakhulupirira kuti Yesu anayamba wakhalapo ndi Mulungu kumwamba?— Yesu anati iye anakhalapo ndi Mulungu. Kodi Yesu anadziŵa bwanji zimenezi? Eya, pamene anali mwana, Mariya ayenera kuti anamuuza zimene Gabrieli ananena. Ndiponso, Yosefe ayenera kuti anamuuza Yesu kuti Atate ake enieni anali Mulungu.

Pamene Yesu anabatizidwa, Mulungu analankhula ali kumwamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga.”  (Mateyu 3:17) Ndipo usiku woti akufa maŵa lake, Yesu anapemphera kuti: ‘Atate Inu, mundilemekeze pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu lisanalengedwe dziko lapansi.’ (Yohane 17:5) Inde, Yesu anapempha Mulungu kuti amutenge akakhalenso naye kumwamba. Kodi zinatheka bwanji kuti akakhalenso kumwamba?— Zinatheka chifukwa Yehova Mulungu anamupanga kukhalanso mzimu wosaoneka, kapena kuti mngelo.

Tsopano ndikufunse funso lofunika zedi. Kodi angelo onse ndi abwino? Ukuganiza bwanji?— Ee, panthaŵi ina onse anali abwino. Zinali choncho chifukwa Yehova ndiye anawapanga, ndipo zonse zimene iye amapanga ndi zabwino. Pambuyo pake mngelo mmodzi anakhala woipa. Kodi zimenezi zinachitika bwanji?

Kuti tipeze yankho, tiye tionenso zimene zinachitika panthaŵi imene Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi oyamba, Adamu ndi Hava. Anthu ena amati nkhani ya anthu ameneŵa ndi yabodza. Koma Mphunzitsi Waluso ananena kuti inali yoona.

Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola womwe unali kutchedwa kuti Edene. Anali malo okongola, paradaiso. Iwo akanatha kukhala ndi ana ambirimbiri, banja lawo likanakhala lalikulu, ndipo akanakhala mu Paradaiso mpaka kalekale. Koma iwo anafunika kuphunzira mfundo yofunika kwambiri. Mfundo imeneyi tinakambiranapo kale. Tiye tione ngati tingaikumbukire.

Kodi zikanatheka bwanji kuti Adamu ndi Hava akhale ndi moyo wosatha mu Paradaiso?

 Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti akhoza kudya zipatso zonse zimene anafuna m’mitengo ya m’mundawo. Koma panali mtengo umodzi umene sanayenere kudya zipatso zake. Mulungu anawauza zimene zikanachitika ngati akanadya zipatso za mtengo umenewo. Anati: ‘Mudzafa ndithu.’ (Genesis 2:17) Ndiye ndi mfundo yotani imene Adamu ndi Hava anafunika kuphunzira?—

Inali kumvera. Inde, kukhala ndi moyo kumadalira kumvera Yehova Mulungu! Sikunali kokwanira kuti Adamu ndi Hava angonena kuti adzamvera Mulungu. Anafunika kusonyeza kuti ndi omvera mwa zimene anali kuchita. Akanamvera Mulungu, akanasonyeza kuti anamukonda ndipo anafuna kuti iye akhale Wolamulira wawo. Ndiponso akanakhala ndi moyo wosatha mu Paradaiso. Koma ngati iwo akanadya zipatso za mtengo umenewo, kodi zikanasonyeza chiyani?—

Zikanasonyeza kuti iwo sanali kuyamikira kwenikweni zimene Mulungu anawapatsa. Kodi iwe ukanamvera Yehova ukanakhalapo panthaŵiyo?— Poyamba Adamu ndi Hava anamvera. Koma panabwera wina wamkulu kuposa iwo amene ananyengerera Hava. Chifukwa cha ameneyo Hava sanamvere Yehova. Kodi ameneyo ndani?—

Kodi ndani anachititsa njoka

kulankhula ndi Hava?

Baibulo limati njoka inalankhula ndi Hava. Koma  iwe ukudziŵa kuti njoka silankhula. Nanga zinatheka bwanji kuti ilankhule?— Mngelo anachititsa njokayo kuoneka ngati ikulankhula. Komatu anali mngeloyo amene anali kulankhula. Mngeloyo anayamba kuganiza zinthu zoipa. Anafuna kuti Adamu ndi Hava amulambire. Anafuna kuti iwo achite zinthu zimene iye ananena. Anafuna kulanda malo a Mulungu.

Kuti achite zimenezo mngelo woipa ameneyo anaika maganizo oipa mumtima mwa Hava. Iye anauza Hava kudzera mwa njoka kuti: ‘Mulungu sanakuuze zoona. Sudzafa ukadya zipatso za mtengowu. Udzakhala wanzeru ngati Mulungu.’ Kodi iwe ukanakhulupirira mawu amenewo?—

Hava anayamba kufuna chimene Mulungu sanamupatse. Anadya zipatso za mtengo umene anamuletsa uja. Kenako anapatsa Adamu zipatso zina. Adamu sanakhulupirire zimene njoka inanena. Koma iye anakonda kwambiri kukhala ndi Hava kuposa mmene anakondera Mulungu. Choncho nayenso anadya zipatso za mtengowo.—Genesis 3:1-6; 1 Timoteo 2:14.

Ndiye chinachitika ndi chiyani?— Adamu ndi Hava anakhala opanda ungwiro, moti anayamba kukalamba, ndipo anafa. Ndipo chifukwa chakuti  iwo anali opanda ungwiro, ana awo onse analinso opanda ungwiro ndipo m’kupita kwa nthaŵi anakalamba ndi kufa. Waona kuti Mulungu sananame! Ndithudi kukhala ndi moyo kumadalira kumvera iye. (Aroma 5:12) Baibulo limatiuza kuti mngelo amene ananamiza Hava amatchedwa Satana Mdyerekezi, ndipo angelo ena amene anakhala oipa amatchedwa ziwanda.—Yakobo 2:19; Chivumbulutso 12:9.

Kodi n’chiyani chinachitikira Adamu ndi Hava pamene sanamvere Mulungu?

Kodi tsopano ukumvetsa chifukwa chake mngelo wabwino amene Mulungu anapanga anakhala woipa?— Chinali chifukwa chakuti anayamba kuganiza zinthu zoipa. Anafuna kukhala Nambala Wani. Anali kudziŵa kuti Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti akhale ndi ana, ndiye iye anafuna kuti onsewo azimulambira. Mdyerekezi amafuna kuti aliyense asamvere Yehova. Ndiye chifukwa chake amayesa kuika maganizo oipa mumtima mwathu.—Yakobo 1:13-15.

Mdyerekezi amanena kuti palibe munthu amene amakondadi Yehova. Amati iweyo ndi ineyo sitimukonda Mulungu ndi kuti pansi pa mtima wathu sitifuna kuchita zimene Mulungu amanena. Amanena kuti timamvera Yehova ngati zinthu zonse zikuchitika mmene ifeyo timafunira. Kodi Mdyerekezi amanena zoona? Kodi ndi mmene ife tilili?

Mphunzitsi Waluso anati Mdyerekezi ndi wabodza! Mwa kukhala womvera, Yesu anasonyeza kuti anakonda Yehova. Ndipo Yesu sanamvere Mulungu panthaŵi yokha imene zinthu zinali bwino. Anali womvera nthaŵi zonse, ngakhale pamene anthu ena anachititsa kumverako kukhala kovuta. Anali wokhulupirika kwa Yehova mpaka kufa kwake. Ndicho chifukwa chake Mulungu anamupatsanso moyo kuti akhale kosatha.

Tsono kodi iwe unganene kuti mdani wathu wamkulu ndani?— Inde, ndi Satana Mdyerekezi. Kodi ukhoza kumuona?— Ayi sungamuone! Koma timadziŵa kuti alipo ndi kuti ndi wamkulu ndiponso wamphamvu kuposa ifeyo. Komabe, kodi ndani amene ali wamkulu kuposa Mdyerekezi?— Ndi Yehova Mulungu. Choncho tikudziŵa kuti Mulungu akhoza kutiteteza.

Ŵerengani za Amene tiyenera kumulambira: Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:14, 15; Miyambo 27:11; ndi Mateyu 4:10.