Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 39

Mulungu Anakumbukira Mwana Wake

Mulungu Anakumbukira Mwana Wake

YESU analira bwenzi lake Lazaro atamwalira. Kodi ukuganiza kuti Yehova zinamupweteka pamene Yesu anavutika ndi kufa?— Baibulo limanena kuti Mulungu ‘amamva chisoni’ ndi zinthu zimene zimachitika ndipo zimamupweteka mumtima.—Salmo 78:40, 41; Yohane 11:35.

Kodi ukuganiza kuti Yehova zinamupweteka kwambiri kuona Mwana wake wokondedwayo akufa?— Yesu analitu wotsimikiza kuti Mulungu sadzamuiwala. Ndi chifukwa chake mawu ake omaliza asanafe anali akuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka [moyo] wanga.”—Luka 23:46.

Yesu anali wotsimikiza kuti adzaukitsidwa, kuti sadzamusiya “mu Hade,” kapena kuti m’manda. Yesu ataukitsidwa, mtumwi Petro ananena mawu omwe analembedwa m’Baibulo okhudza Yesu akuti: ‘Sanasiyidwe mu Hade, ndipo thupi lake silinavunde.’ (Machitidwe 2:31; Salmo 16:10) Thupi la Yesu silinakhale  ndi nthaŵi yoti livunde m’manda, kutanthauza kuwola ndi kuyamba kununkha.

Yesu ali padziko lapansi anauza ophunzira ake kuti sadzakhala wakufa kwa nthaŵi yaitali. Anawafotokozera kuti ‘adzaphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.’ (Luka 9:22) Motero ophunzirawo sanafunike kudabwa Yesu ataukitsidwa. Kodi anadabwa?— Tiye tione mmene zinalili.

Nthaŵi inali pafupifupi fili koloko Lachisanu masana pamene Mphunzitsi Waluso anafa pamtengo wozunzirapo. Yosefe, yemwe anali wolemera komanso membala wa Sanihedirini, anali kukhulupirira Yesu mosaonetsera kwa anthu. Atamva kuti Yesu wafa, anapita kwa Pilato yemwe anali nduna ya Roma. Anakapempha kuti akachotse mtembo wa Yesu pamtengo paja kuti akauike m’manda. Kenako Yosefe anatenga mtembo wa Yesu ndi kupita nawo kumunda kumene kunali mandawo.

Ataika mtembowo m’manda, anakankhira mwala waukulu pakhomo a mandawo. Umu ndi mmene anatsekera mandawo. Tsiku lachitatu linakwana, lomwe linali Lamlungu. Dzuŵa linali lisanatuluke, ndiye kunali kudakali kamdima. Kumanda kuja kunali anthu aamuna amene anali kulondera mandawo. Ansembe aakulu ndiwo anawauza kukalondera. Nanga chifukwa chake ukuchidziŵa?—

Ansembewo anamva kuti Yesu ananena kuti adzauka. Ndiye anaika alonda kumanda kuja poopa kuti ophunzira ake angabe mtembowo kenako ndi kumanena kuti Yesu anaukitsidwa. Koma mwadzidzidzi pansi panayamba kugwedezeka. Mumdimawo munawala. Anali mngelo wa Yehova! Asilikaliwo anachita mantha kwambiri moti sanayende. Mngeloyo anafika pamandapo ndi kuchotsa chimwala chija. M’mandamo munadzakhala mopanda kanthu eti!

Ndi chifukwa chiyani m’mandamu mulibe kanthu? Kodi chachitika ndi chiyani?

Inde, “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa,” anatero mtumwi Petro pambuyo pake. (Machitidwe 2:32) Mulungu anaukitsa Yesu ndi  kumupatsa thupi lofanana ndi lomwe Yesuyo anali nalo asanabwere padziko lapansi. Anamupatsa thupi lauzimu lofanana ndi la angelo. (1 Petro 3:18) Ndiye kuti anthu athe kumuona, Yesu anayenera kuvala thupi ngati lathuli. Kodi ndi zimene anachita?— Tiye tione.

Dzuŵa linali kutuluka tsopano. Asilikali aja anali atapita. Mariya Magadalene ndi akazi ena amene anali ophunzira a Yesu anali kupita kumanda kuja. Anali kukambirana kuti: ‘Akatichotsera ndani mwala wolemera uja?’ (Marko 16:3) Koma atafika pamandapo anapeza mwalawo utachotsedwa kale. M’mandanso munalibe kanthu! Mtembo wa Yesu munalibe! Mariya Magadalene sanachedwenso ayi, anathamanga kukauza atumwi ena a Yesu.

Akazi enawo anakhalabe pamanda pomwepo. Anali kuganiza kuti: ‘Kodi mtembo wa Yesu wapita kuti?’ Mwadzidzidzi anangoona anthu aamuna aŵiri ovala zonyezimira afika. Amunaŵa anali angelo! Anauza akaziwo kuti: ‘Ndi chifukwa chiyani mukuyang’ana Yesu kunoko? Iye anaukitsidwa. Fulumirani kauzeni ophunzira ake.’ Ndiye taganizira liŵiro limene anathamanga akaziŵa! Ali m’njira anakumana ndi munthu wina wamwamuna. Kodi ukumudziŵa?—

Anali Yesu, ndipo apa anavala thupi ngati lathuli! Anauzanso akaziwo kuti: ‘Pitani mukauze ophunzira anga.’ Akaziwo anasangalala kwambiri. Anapeza ophunzirawo ndi kuwauza kuti: ‘Yesu ali moyo! Ife tamuona!’ Mariya anali atauza kale Petro ndi Yohane kuti m’manda mulibe kanthu. Tsono iwo anapita kumanda komweko, monga ukuonera apamu. Anayang’ana nsalu zimene anafundika Yesu, koma anasoŵa chonena. Anafuna kukhulupirira kuti Yesu anali moyo, koma zinali kuoneka zokayikitsa kwambiri.

Kodi Petro ndi Yohane mwina akuganiza chiyani?

Panthaŵi ina Lamlungu lomwelo, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake aŵiri amene anali kupita ku mudzi wa Emau. Yesu anali kuyenda nawo limodzi ndi kumacheza nawo, koma iwo sanamuzindikire chifukwa chakuti thupi lake silinali lofanana ndi limene anali nalo kale.  Iye atadya nawo limodzi chakudya ndi kupereka pemphero ndi pamene iwo anamuzindikira. Ophunzirawo anasangalala kwambiri mpaka anayenda mofulumira mtunda wa makilomita ambirimbiri kubwerera ku Yerusalemu! Mwinamwake izi zitangochitika kumene ndi pamene Yesu anaonekera kwa Petro kuti amusonyeze kuti Iye ali moyo.

Kenako madzulo Lamlungu lomwelo, ophunzira ambiri anali m’chipinda chimodzi. Zitseko zinali zotseka. Mwadzidzidzi anangoona kuti Yesu ali nawo limodzi m’chipindacho! Apa iwo anatsimikiza kuti Mphunzitsi Waluso analidi moyo. Ndiye taganizira mmene iwo anasangalalira!—Mateyu 28:1-15; Luka 24:1-49; Yohane 19:38–20:21.

Kwa masiku 40 Yesu anali kuoneka ndi matupi osiyanasiyana kuti  asonyeze ophunzira ake kuti anali moyo. Ndiyeno anachoka padziko lapansi ndi kubwerera kwa Atate ake kumwamba. (Machitidwe 1:9-11) Sipanatenge nthaŵi, ophunzirawo anayamba kuuza aliyense kuti Mulungu anaukitsa Yesu kwa akufa. Iwo anali kulalikirabe ngakhale pamene ansembe anawamenya ndi kupha ena a iwo. Anali kudziŵa kuti ngati afa, Mulungu adzawakumbukira monga mmene anakumbukirira Mwana wake.

Ikafika nthaŵi imene Yesu anaukitsidwa, kodi anthu ambiri amaganiza za chiyani? Koma kodi iwe umaganiza za chiyani?

Otsatira a Yesu oyambirirawo analitu osiyana kwambiri ndi mmene anthu ambiri alili masiku ano! M’madera ena a dzikoli, ikafika nthaŵi imene Yesu anaukitsidwa anthu amangoganizira za akalulu a Isitala ndi mazira a Isitala amaŵangamaŵanga basi. Komatu Baibulo silinenapo za akalulu ndi mazira a Isitala. Limanena za kutumikira Mulungu.

Ife tingakhale ngati ophunzira a Yesu mwa kuuza anthu kuti Mulungu anachita chinthu chabwino kwambiri poukitsa Mwana wake. Sitifunika kuchita mantha, ngakhale anthu anene kuti atipha. Ngati tingafe, Yehova adzatikumbukira ndi kutiukitsa monga mmene anachitira ndi Yesu.

Kodi si zosangalatsa kudziŵa kuti Mulungu amakumbukira anthu amene amamutumikira ndiponso kuti iye adzawaukitsa kwa akufa?— Kudziŵa zimenezi kuyenera kutilimbikitsa kufuna kudziŵa mmene tingasangalatsire Mulungu. Kodi ukudziŵa kuti tikhoza kumusangalatsa?— Tiye tikambiranenso nkhani imeneyi.

Kukhulupirira kuti Yesu anauka kuyenera kulimbitsa chiyembekezo chathu ndi kukulitsa chikhulupiriro chathu. Tiŵerenge Machitidwe 2:22-36; 4:18-20; ndi 1 Akorinto 15:3-8, 20-23.