KODI unamvapo munthu wina akulankhula za kutha kwa dziko?— Masiku ano anthu ochuluka akulankhulapo kwambiri. Anthu ena amaganiza kuti dziko lidzatha pamene anthu adzachita nkhondo kugwiritsa ntchito mabomba a nyukiliya. Kodi ukuganiza kuti Mulungu adzaloladi kuti anthu awonongedziko lapansi lokongolali?—

Monga taphunzirira kale, Baibulo limanena za kutha kwa dziko. “Dziko lapansi lipita,” limatero Baibulo. (1 Yohane 2:17) Kodi ukuganiza kuti kutha kwa dziko kukutanthauza kutha  kwa dziko lapansi limene tikukhalamo?— Ayi. Baibulo limanena kuti Mulungu anapanga dziko lapansi ili kuti ‘anthu akhalemo,’ inde, kuti anthu akhalemo ndi kusangalala. (Yesaya 45:18) Salmo 37:29 limanena kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Ndi chifukwa chake Baibulo limanenanso kuti dziko lapansi ndi lachikhalire.—Salmo 104:5; Mlaliki 1:4.

Ndiye ngati kutha kwa dziko sikutanthauza kutha kwa dziko lapansi limene tikukhalamo, kumatanthauza chiyani?— Yankho lake tingalipeze ngati taona bwinobwino zimene zinachitika masiku a Nowa. Baibulo limafotokoza kuti: ‘Dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, linawonongeka.’—2 Petro 3:6.

Kodi pamene dziko linali kutha pa Chigumula masiku a Nowa alipo amene anapulumuka?— Baibulo limanena kuti Mulungu ‘anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake seveni pakulitengera dziko la [anthu] osapembedza chigumula.’—2 Petro 2:5.

Kodi dziko limene linawonongeka masiku a Nowa ndi chiyani?

Ndiye, pamenepa tinganene kuti dziko limene linatha ndi chiyani? Kodi linali dziko lapansi limene tikukhalamo, kapena anali anthu oipa?— Baibulo likunena kuti linali ‘dziko la anthu osapembedza.’ Ndipo taona, Nowa akutchedwa “mlaliki.” Kodi ukuganiza kuti anali kulalikira za chiyani?— Nowa anali kuchenjeza anthu za kutha kwa ‘dziko lapansi la masiku aja.’

Pamene Yesu analankhula za Chigumula, anauza ophunzira ake zimene anthu anali kuchita kalelo mapeto atatsala pang’ono kufika. Iye anawauza kuti: ‘M’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziŵe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.’ Kenako Yesu ananena kuti anthu adzachitanso zomwezo dziko ili lisanathe.—Mateyu 24:37-39.

Zimene Yesu ananena zikusonyeza kuti tingaphunzirepo zinazake  pa zimene anthu anali kuchita chisanafike Chigumula. Poganiza zimene tinaŵerenga mu Mutu 10 wa buku lino, kodi ungakumbukire zimene anthu aja anali kuchita?— Ena anali ankhanza ndipo anali kuchita zachiwawa. Koma Yesu ananena kuti ena ambiri sanafune kumvera pamene Mulungu anatuma Nowa kuti awalalikire.

Ndiye tsiku linafika pamene Yehova anauza Nowa kuti Iye adzawononga anthu oipa ndi chigumula. Madzi adzamiza dziko lonse lapansi, ngakhale mapiri. Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa chachikulu. Chingalawacho chinali ngati chibokosi chachikulu komanso chachitali ngati chimene ukuchiona utabwerera pa chithunzi chili patsamba 238.

Mulungu anauza Nowa kumanga chingalawa chachikulu chokwana iyeyo ndi banja lake ndi nyama zambiri kuti iwo akakhalemo bwinobwino otetezeka. Nowa ndi banja lake anagwira ntchito kwambiri. Anadula mitengo yaikulu, ndipo matabwa ake anayamba kupangira chingalawa pamodzi. Zimenezi zinatenga zaka zambirimbiri chifukwa chakuti chingalawacho chinali chachikulu kwambiri.

Kodi ukukumbukira kuti ndi chiyani china chimene Nowa anali kuchita zaka zonse zimene anali kumanga chingalawa?— Anali kulalikira, kuwachenjeza anthu za Chigumula chimene chinali kubwera. Kodi alipo amene anamvera? Panalibe, kupatulapo banja la Nowa basi. Anthu ena onse analibe nthaŵi chifukwa chakuti anali kuchita zinthu zina. Kodi ukukumbukira zimene Yesu ananena kuti iwo anali kuchita?— Iwo anali kutaya nthaŵi yonse kudya ndi kumwa ndi kukwatirana. Iwo sanaganize kuti anali anthu oipa, ndipo analibe nthaŵi yomvetsera kwa Nowa. Tsono tiye tione zimene zinawachitikira.

Nowa ndi banja lake ataloŵa m’chingalawa, Yehova anatseka pakhomo. Anthu amene anali kunja sanakhulupirirebe kuti Chigumula chinali kubwera. Ndiyeno mwadzidzidzi, madzi anayamba kugwa kuchokera kumwamba! Imeneyi sinali mvula ŵamba. Inali chimvula  choopsa! Sipanatenge nthaŵi madziwo anakhala ngati mitsinje yaikulu, ndipo panali kumveka chiphokoso. Anagwetsa mitengo yaikulu ndi kukokolola miyala yaikulu ngati timiyala tating’ono. Nanga ndi chiyani chinachitikira anthu amene anali kunja kwa chingalawa?— Yesu ananena kuti: “Chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” Inde, anthu onse amene anali kunja kwa chingalawa chija anafa. Ukudziŵa chifukwa chake?— Yesu ananena kuti, ‘sanadziŵe kanthu.’ Iwo sanamvere!—Mateyu 24:39; Genesis 6:5-7.

Ndi chifukwa chiyani sitifunika kungoganiza za kuseŵera basi?

Tsopano ukakumbukira, Yesu ananena kuti zimene zinachitikira anthu amene aja zili ndi phunziro kwa ife masiku ano. Kodi tikuphunzirapo chiyani?— Eya, chimene anthu amenewo anawonongekera si chifukwa chabe chakuti anali anthu oipa ayi. Komanso ndi chifukwa chakuti ambiri anali ndi zambiri zochita, ndipo analibe nthaŵi yophunzira za Mulungu ndi zimene iye anati adzachita. Tifunika kusamala kuti tisakhale ngati iwo, si choncho?—

Kodi ukuganiza kuti Mulungu adzawononganso dziko ndi chigumula?— Ayi. Mulungu analonjeza kuti sadzatero. Iye anati: ‘Utawaleza wanga umene uli mu mtambomo, udzakhala chizindikiro.’ Yehova ananena kuti utawaleza udzakhala chizindikiro chakuti ‘zamoyo zonse sizidzawonongeka konse ndi madzi a chigumula.’—Genesis 9:11-17.

Choncho tikutsimikiza kuti Mulungu sadzawononganso dziko ndi chigumula. Koma, monga taonera kale, Baibulo limanenadi kuti dziko  lidzatha. Pamene Mulungu adzawononga dzikoli, kodi adzapulumutsa ndani?— Kodi adzapulumutsa anthu aja amene anali kukonda zinthu zina moti sanafune kuphunzira za Mulungu? Kapena kodi adzapulumutsa aja amene analibe nthaŵi yophunzira Baibulo? Ukuganiza bwanji?—

Ife tikufuna kukhala anthu amene Mulungu adzapulumutsa, si choncho?— Kodi sizingakhale bwino ngati banja lathu lingakhale ngati la Nowa kuti Mulungu akatipulumutse ife tonse?— Ngati tikufuna kupulumuka pamene dziko lidzatha, tifunika kumvetsa mmene Mulungu adzaliwonongera ndi mmene adzabweretsera dziko latsopano lolungama. Tiye tione mmene adzachitira zimenezi.

Baibulo likuyankha pa Danieli chaputala 2, vesi 44. Lembali likufotokoza za masiku ano. Likuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kapena kuti, boma] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”

Kodi ukumvetsa zimenezi?— Baibulo likunena kuti boma la Mulungu lidzawononga maboma onse a padziko lapansi. Ukudziŵa chifukwa chake?— Chifukwa chakuti iwo samvera Iye amene Mulungu wamusankha kukhala Mfumu. Ndipo kodi anasankha ndani?— Eya, anasankha Yesu Kristu!

Yesu Kristu, Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, adzawononga dzikoli pa Armagedo

Yehova Mulungu ali ndi ufulu wosankha boma limene liyenera kulamulira, ndipo wasankha Mwana wake, Yesu, kukhala Mfumu. Posachedwapa Wolamulira amene Mulungu wasankhayu, Yesu Kristu, adzatsogolera kuwononga maboma onse a dzikoli. Baibulo, pa Chivumbulutso chaputala 19, vesi 11 mpaka 16, limamufotokoza akuchita zimenezi, ngati zimene ukuona pa chithunzichi. M’Baibulo, nkhondo ya Mulungu yowononga maboma onse a dzikoli imatchedwa Harmagedo, kapena kuti Armagedo.

 Pajatu, Mulungu amanena kuti Ufumu wake udzawononga maboma a anthu. Koma kodi iye amatiuza ife kuchita zimenezo?— Ayi. Baibulo limati Armagedo ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Inde, Armagedo ndi nkhondo ya Mulungu, ndipo adzagwiritsa ntchito Yesu Kristu kutsogolera magulu a nkhondo akumwamba pomenya nkhondo imeneyi. Koma kodi nkhondo ya Armagedo imeneyi ili pafupi? Tiye tione mmene tingadziŵire zimenezi.

Tiye tiŵerengere limodzi za nthaŵi pamene Mulungu adzachotsa oipa onse ndi kupulumutsa amene akumutumikira, pa Miyambo 2:21, 22; Yesaya 26:20, 21; Yeremiya 25:31-33; ndi Mateyu 24:21, 22.