TIYEREKEZE kuti mtsikana akuuza amayi ake kuti: “Ee, ndikangoweruka kusukulu sindichedwa kubwera.” Komano ataweruka akutsalira kaye ndi kuyamba kuseŵera ndi anzake ndiye pamene wafika kunyumba akuuza amayi ake kuti: “Aphunzitsi anati nditsalire.” Kodi ndi bwino kunena zoterezi?—

Kodi mnyamata uyu walakwa chiyani?

Kapena mwinamwake mnyamata akuuza atate ake kuti: “Ayi, sindine ndinaponyera mpira m’nyumba.” Koma bwanji ngati iye ndiye anaponyeramo mpirawo? Kodi ndi kulakwa kunena kuti sanaponyeremo?—

Mphunzitsi Waluso anatisonyeza chomwe chili chabwino kuchita. Ananena kuti: ‘Mukanena kuti Inde, azikhaladi Inde, ndipo mukanena kuti Iyayi, azikhaladi Iyayi; chifukwa mawu ena oposera apa ndi ochokera kwa woipayo.’ (Mateyu 5:37) Kodi ukuganiza kuti Yesu anatanthauza chiyani?— Anatanthauza kuti tizichita zimene timanena.

M’Baibulo muli nkhani ina imene imasonyeza kuti kunena  zoona ndi kofunika kwambiri. Nkhaniyi imanena za anthu ena aŵiri amene anali kunena kuti ndi ophunzira a Yesu. Tiye tione zimene zinachitika.

Miyezi iŵiri isanathe Yesu atafa, anthu ambirimbiri ochokera kumadera akutali anabwera ku Yerusalemu kudzachita phwando lofunika la Ayuda lotchedwa Pentekoste. Mtumwi Petro anakamba nkhani yabwino kwambiri; anafotokozera anthuwo za Yesu yemwe Yehova anamuukitsa kwa akufa. Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuti ambiri mwa anthu omwe anabwera ku Yerusalemuwo amve za Yesu. Tsono iwo anafuna kudziŵa zambiri. Kodi akanatani?

Iwo anawonjezera masiku okhala kumeneko. Koma patapita nthaŵi ena ndalama zinawathera, ndipo panafunika kuwathandiza kuti azigula chakudya. Ophunzira a ku Yerusalemu anafuna kuthandiza alendowo. Motero ambiri anagulitsa zinthu zawo ndi kupereka ndalamazo kwa atumwi a Yesu. Kenako atumwiwo anali kugaŵa ndalamazo kwa anthu omwe analibe ndalama aja.

Hananiya ndi mkazi wake, Safira, omwe anali Akristu mu mpingo wa ku Yerusalemu, anagulitsa munda wawo. Palibe yemwe anawauza  kuti agulitse. Anasankha okha. Koma iwo anachita zimenezi osati chifukwa chokonda ophunzira a Yesu atsopanowo ayi. Zimene Hananiya ndi Safira anafuna ndi zakuti anthu aziganiza kuti iwo anali abwino kuposa mmene iwo analili. Choncho anaganiza zokanena kuti akupereka ndalama zonse kuti zithandize ena. Komatu zenizeni ndi zakuti iwo sanafune kupereka zonse koma kungonena chabe kuti apereka zonse. Kodi ukuganiza kuti anachita bwino?—

Eya, Hananiya anapita kwa atumwi, ndipo anawapatsa ndalama zija. Koma Mulungu anadziŵa kuti sanapereke ndalama zonse. Motero Mulungu anadziŵitsa mtumwi Petro kuti Hananiya anali kunama.

Kodi Hananiya akuuza Petro bodza lotani?

Ndiyeno Petro anati: ‘Hananiya, ndi chifukwa chiyani walola Satana kukuchititsa zimenezi? Munda unali wako. Panalibe chifukwa chakuti uugulitse. Ndipo ngakhale pamene unaugulitsa, zinali ndi iwe kusankha kuti ndalamazo uchita nazo chiyani. Nanga ndi chifukwa chiyani ukuyerekeza kupereka ndalama zonse pamene ukupereka zochepa chabe? Iwetu suli kunamiza ife tokha, ukunamizanso Mulungu.’

Waona, sinalitu nkhani yamaseŵera. Hananiya anali kunena bodza! Zimene anali kunena si zimene anali kuchita. Anangoyerekeza kuti ndi zimene akuchita. Baibulo limatiuza zimene zinachitika kenako. Limanena kuti: ‘Hananiya atamva mawu a Petro, anagwa pansi ndi kufa.’ Mulungu anapha Hananiya! Kenako mtembo wake anautulutsa ndi kukauika m’manda.

Kodi chinachitikira Hananiya ndi chiyani chifukwa chonama?

 Patatha pafupifupi fili awazi, Safira anafikanso. Iye sanadziŵe zimene zinachitikira mwamuna wake. Ndiye Petro anamufunsa kuti: ‘Kodi iwe ndi mwamuna wako munagulitsa munda pa mtengo wa ndalama zimene mwatipatsa?’

Safira anayankha kuti: ‘Inde, mundawo tagulitsadi pa mtengo umenewo.’ Komatu linali bodza! Iwo anasunga ndalama zina za mundawo. Motero Mulungu anaphanso Safira.—Machitidwe 5:1-11.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikira Hananiya ndi Safira?— Tikuphunzira kuti Mulungu amadana ndi anthu abodza. Nthaŵi zonse amafuna kuti tizinena zoona. Koma anthu ambiri amanena kuti kunena zabodza si kulakwa. Kodi iwe ukuganiza kuti iwo amalondola?— Kodi umadziŵa kuti kudwala, kumva kuŵaŵa, ndiponso kufa kumene kuli pa dziko lapansi pano kunayamba chifukwa cha bodza?—

Kodi Yesu ananena kuti ndani anayambitsa bodza, nanga chinatsatirapo ndi chiyani?

Ndiganiza ukukumbukira kuti Mdyerekezi ananamiza munthu wamkazi woyambirira, Hava. Mdyerekezi anauza Hava kuti sadzafa ngati atati asamvere Mulungu ndi kudya chipatso chimene Mulungu ananena kuti sayenera kudya. Hava anakhulupirira mawu a Mdyerekezi ndipo anadya chipatsocho. Anakakamiza Adamu kuti nayenso adye. Atachita zimenezi anakhala ochimwa, ndipo ana awo onse anabadwa ochimwa. Ndipo chifukwa chakuti ana a Adamu anali ochimwa, onse anavutika komanso anafa. Kodi mavuto onseŵa anayamba bwanji?— Anayamba chifukwa cha bodza.

Ndi pake kuti Yesu ananena kuti Mdyerekezi ‘ndi wabodza ndiponso ndi atate wake wa bodza’! Iye ndiye anali woyamba kunena zabodza. Munthu wina aliyense akamanena zabodza amachita zimene Mdyerekezi anayambitsa kuchita. Tiyenera  kuganizira zimenezi nthaŵi zonse tikakhala ndi maganizo onena zabodza.—Yohane 8:44.

Kodi ndi nthaŵi iti pamene ungaganize zonena bodza?— Ndi pamene wachita chinachake cholakwika, si choncho?— Mwina ukhoza kuswa chinachake mwangozi. Ndiye ngati wafunsidwa, kodi uyenera kunena kuti waswa ndi mkulu wako kapena mng’ono wako kapena mlongo wako? Kapena kodi uyenera kuyerekeza kuti sukudziŵa kuti chasweka bwanji?—

Kodi ndi nthaŵi iti pamene ungaganize zonena bodza?

Bwanji ngati unafunika kuchita homuweki koma sunamalize? Kodi uyenera kunena kuti wamaliza, ngakhale kuti sunamalize?— Tizikumbukira Hananiya ndi Safira. Iwo sananene zoona. Ndipo Mulungu anasonyeza kuti zimenezo zinali zoipa kwambiri mwa kuwapha.

Ndiye kaya tachita zotani, nthaŵi zonse kunena bodza kumaipitsa zinthu kwambiri. Ndipo sitiyenera kubisa chilichonse. Baibulo limanena kuti: “Lankhulani zoona.” Limanenanso kuti: “Musamanamizana wina ndi mnzake.” Nthaŵi zonse Yehova amalankhula zoona, ndipo amayembekeza kuti ifenso tizilankhula zoona.—Aefeso 4:25; Akolose 3:9.

Nthaŵi zonse tiyenera kunena zoona. Imeneyi ndiyo mfundo yomwe ili pa Eksodo 20:16; Miyambo 6:16-19; 12:19; 14:5; 16:6; ndi Ahebri 4:13.