Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 7

Kumvera Kudzakuteteza

Kumvera Kudzakuteteza

KODI ungakonde kuti uzichita chilichonse chimene ukufuna? Kodi nthaŵi ina umalakalaka kuti munthu wina asakuuze zochita? Tandiuza zoona zimene umaganiza.—

N’chifukwa chiyani uyenera kumvera anthu akuluakulu?

Koma ukuganiza kuti chabwino ndi chiyani? Kodi ndi chinthudi chanzeru kuti uzichita chilichonse chimene ukufuna? Kapena kodi zinthu zimakukhalira bwino ukamamvera atate ako ndi amayi ako?— Mulungu amati uzimvera makolo ako, ndiye kuti payenera kukhala chifukwa chabwino chochitira zimenezi. Tiye tione ngati tingamvetse bwino zimenezi.

Kodi uli ndi zaka zingati?— Kodi umadziŵa kuti atate ako ali ndi zaka zingati?— Nanga amayi ako kapena agogo ako ali ndi zaka zingati?— Iwo akhala ndi moyo zaka zambiri kuposa iweyo. Ndipo munthu akakhala ndi moyo nthaŵi yaitali, amakhalanso ndi nthaŵi yambiri yophunzira zinthu. Chaka chilichonse amamva zinthu zambiri, amaona zinthu zambiri, ndiponso amachita zinthu zambiri. Motero ana angaphunzire kwa anthu akuluakulu.

Kodi ukudziŵapo munthu wina aliyense amene ndi wamng’ono kwa iweyo?— Kodi iweyo umadziŵa zinthu zambiri kuposa iyeyo?— N’chifukwa chiyani iweyo umadziŵa zambiri?— N’chifukwa chakuti iweyo wakhala ndi moyo nthaŵi yaitali. Wakhala ndi nthaŵi yambiri yophunzira zinthu kusiyana ndi munthu amene ndi wamng’ono kwa iweyo.

 Kodi ndani amene wakhala ndi moyo nthaŵi yaitali kuposa iweyo kapena ineyo kapenanso munthu wina aliyense?— Yehova Mulungu. Iye amadziŵa zambiri kuposa zimene iweyo umadziŵa, ndiponso kuposa zimene ineyo ndimadziŵa. Akatiuza kuti tichite chilichonse, timadziŵa kuti chimene akutiuzacho ndi chinthu choyenera kuchita, ngakhale kuti chingavute kuchita kwake. Kodi umadziŵa kuti ngakhalenso Mphunzitsi Waluso panthaŵi ina anavutika pofuna kumvera zinazake?—

Nthaŵi ina Mulungu anauza Yesu kuchita chinthu chovuta kwambiri. Yesu anapemphera za nkhaniyo, monga tikuonera pachithunzichi. Anapemphera kuti: ‘Mukafuna Inu, chotsani chinthu chovuta ichi pa Ine.’ Mwa kupemphera chomwechi, Yesu anasonyeza kuti nthaŵi zina kunali kovuta kuchita chifuno cha Mulungu. Koma kodi Yesu anamaliza motani pemphero lake? Kodi ukudziŵa?—

Kodi pemphero la Yesu likutiphunzitsa chiyani?

Yesu anamaliza mwa kunena kuti: ‘Si kufuna kwanga ayi, komatu kufuna kwanu kuchitike.’ (Luka 22:41, 42) Inde, anafuna kuti zofuna za Mulungu ndizo zichitike, osati zofuna zake ayi. Ndipo iye anachita zimene Mulungu anafuna m’malo mochita zimene iye anaganiza kuti ndizo zabwino.

N’chiyani chimene tikuphunzira pamenepa?— Tikuphunzira kuti nthaŵi zonse ndi bwino kuchita zimene Mulungu amanena, ngakhale zikhale zovuta kuchita. Koma tikuphunziraponso kanthu kena. Kodi wakadziŵa?— Tikuphunzira kuti Mulungu ndi Yesu si munthu mmodzi, monga amanenera anthu ena. Yehova Mulungu ndi wamkulu ndipo amadziŵa zinthu kuposa Mwana wake Yesu.

Tikamamvera Mulungu timasonyeza kuti timamukonda. Baibulo limati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.”  (1 Yohane 5:3) Tsono ungaone kuti tonse tifunika kumvera Mulungu. Iwe ukufuna kuti uzimumvera, si choncho?—

Tatenga Baibulo ndipo tione zimene Mulungu amauza ana kuti azichita. Tiŵerenga zimene Baibulo limanena pa Aefeso chaputala 6, mavesi 1, 2, ndi 3. Limati: ‘Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezo), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.’

Waonatu nanga, Yehova Mulungu mwiniyo ndiye amene akukuuza kuti uzimvera atate ako ndi amayi ako. Kodi ‘kuwalemekeza’ kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kuti uziwapatsa ulemu. Ndipo Mulungu akulonjeza kuti ngati umvera makolo ako, ‘iweyo zidzakukhalira bwino’ zinthu.

Tsopano ndikuuze nkhani ya anthu enaake amene anapulumuka chifukwa chomvera. Anthu ameneŵa anali kukhala m’mudzi waukulu wa Yerusalemu kalekalelo. Anthu ambiri m’mudzi umenewo sanamvere Mulungu, ndiye Yesu anawachenjeza kuti Mulungu akawononga mudzi wawowo. Yesu anawauzanso mmene akanapulumukira ngati akanakonda kuchita zabwino. Iye anati: ‘Pamene mudzaona magulu a ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziŵe kuti watsala pang’ono kuwonongedwa. Pamenepo mukachoke mu Yerusalemu ndi kuthaŵira kumapiri.’—Luka 21:20-22.

Kodi kumvera lamulo la Yesu kunawapulumutsa motani anthu aŵa?

Ndiye monga ananenera Yesu, asilikali anabwera kudzamenyana ndi Yerusalemu. Asilikali a Roma anazungulira mudzi wonsewo. Kenako pa zifukwa zinazake asilikaliwo anachokako ku mudziwo. Anthu ambiri anaganiza kuti tsopano panalibenso choopsa. Ndipo anapitiriza kukhala m’mudzimo. Koma kodi paja Yesu anati anayenera kuchita chiyani?— Kodi n’chiyani chimene iweyo ukanachita ukanakhala kuti unali kukhala ku Yerusalemu?— Amene anakhulupiriradi Yesu anasiya nyumba zawo ndi kuthaŵira kumapiri kutali ndi Yerusalemu.

 Chaka chathunthu chinatha popanda kuchitika chilichonse ku Yerusalemu. Chaka chachiŵiri, palibe chinachitika. Chaka chachitatu, palibe chinachitika. Anthu ena ayenera anaganiza kuti amene anathaŵa m’mudzimo anali opusa. Komano m’chaka chachinayi, asilikali a Roma aja anabweranso. Nthaŵi inonso anazungulira mudzi wonse wa Yerusalemu. Tsopano panalibe nthaŵi yoti munthu angathe kuthaŵa. Ulendo uno asilikaliwo anawononga mudziwo. Anthu ambiri amene anali m’mudzimo anaphedwa, ndipo ena onse anawagwira kukhala akapolo.

Koma n’chiyani chinachitikira aja amene anamvera Yesu?— Iwo anapulumuka. Anali kutali ndi ku Yerusalemu. N’chifukwa chake anali bwinobwino. Kumvera kunawateteza.

Ngati iwe ukhala womvera, ndiye kuti nawenso udzatetezeka?— Makolo ako angakuuze kuti osamaseŵera mu msewu. N’chifukwa chiyani  amatero?— N’chifukwa chakuti galimoto ikhoza kukugunda. Koma tsiku lina ungaganize kuti: ‘Panopa mumsewu simukudutsa magalimoto. Sandigunda. Ana ena amaseŵera mumsewu, koma sindinawaone atagundidwa.’

N’chifukwa chiyani uyenera kumverabe ngakhale sukuona choopsa chilichonse?

Ndi mmene anali kuganizira anthu ambiri ku Yerusalemu. Asilikali a Roma atachoka, kunaoneka kuti kunalibe choopsa. Anthu ena anali kukhala m’mudzimo. Choncho iwonso anakhala momwemo. Anachenjezedwa, koma sanamvere. Mapeto ake anaphedwa.

Tiye tione chitsanzo china. Kodi unayamba waseŵerapo ndi macheso?— Zimasangalatsa kuona moto ukuyaka ukayatsa machesowo. Koma kuseŵera ndi macheso ndi ngozi yaikulu. Nyumba yonse ikhoza kupsa ndipo iwe ungafere pomwepo!

Kumbukira kuti kumvera panthaŵi zina chabe si kokwanira. Koma ngati umamvera nthaŵi zonse, ndiye kuti udzatetezedwadi. Ndipo ndani amene akukuuza kuti, “Ananu, mverani akukubalani”?— Mulungu. Ndipo kumbukira kuti iye amanena zimenezi chifukwa amakukonda.

Tsopano ŵerengani malemba aŵa amene amasonyeza kuti kumvera ndi kofunika: Miyambo 23:22; Mlaliki 12:13; Yesaya 48:17, 18; ndi Akolose 3:20.