Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 40

Kukondweretsa Mulungu

Kukondweretsa Mulungu

KODI tingachite chiyani kuti tikondweretse Mulungu? Kodi tingamupatse chinachake?— Yehova amanena kuti: “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga.” Ndiponso amanena kuti: “Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga.” (Salmo 24:1; 50:10; Hagai 2:8) Ngakhale zili choncho, pali chimene tingapatse Mulungu. Kodi chimenecho ndi chiyani?—

Yehova amatilola kusankha kumutumikira kapena kusamutumikira. Satikakamiza kuchita zimene iye akufuna kuti tichite. Tiye tione ngati tingapeze chifukwa chimene Mulungu anatipangira m’njira yakuti tizitha kusankha kumutumikira kapena kusamutumikira.

Ndiganiza ukudziŵa kuti pali makina amene amapangidwa kuti azichita ntchito zina zimene anthu amachita. Makina ameneŵa amapangidwa m’njira yakuti azichita zilizonse zimene munthu amene anawapanga akufuna kuti achite. Makina amenewo satha kusankha zochita. Yehova akanatha kutipanga ife tonse mofanana ndi makina ameneŵa. Akanatha kutipanga m’njira yakuti tizichita zokhazo zimene akanafuna kuti tizichita. Koma Mulungu sanatero. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Eya, pali zoseŵeretsa zina zimene zili ngati makina amene tatchulaŵa. Ukadinikiza batani, zoseŵeretsazo  zimachita zokhazo zimene munthu amene anazipanga anafuna kuti zizichita. Kodi unaonapo choseŵeretsa ngati chimenecho?— Nthaŵi zambiri anthu amatopa kuseŵeretsa chinthu chimene chimangochita zinthu zimodzimodzi zokhazo zimene anachipangira. Mulungu safuna kuti ife tizimumvera popanda kuganiza ngati kuti ndife makina amene anawapanga kuti amutumikire. Yehova amafuna kuti ife tizimutumikira chifukwa chakuti timamukonda ndipo chifukwa chakuti tikufuna kumvera iye.

Ndi chifukwa chiyani Mulungu sanatipange ngati kamakina koseŵeretsa aka?

Kodi ukuganiza kuti Atate wathu wakumwamba amamva bwanji pamene timvera iye chifukwa chakuti tikufuna kumumvera?— Eya, tandiuza, kodi makolo ako amamva bwanji ndi zimene umachita?— Baibulo limanena kuti mwana wanzeru “akondweretsa atate [ake]” koma mwana wopusa “amvetsa amake chisoni.” (Miyambo 10:1) Kodi umaona kuti amayi ako ndi atate ako amasangalala ukachita zimene iwo akuuza kuchita?— Koma kodi iwo amamva bwanji ngati suwamvera?—

Kodi ungachite chiyani kuti ukondweretse Yehova ndi makolo ako?

Tsono tiye tiganize za Atate wathu wa kumwamba, Yehova. Iye amatiuza zimene tingachite kuti timukondweretse. Tenga Baibulo lako utsegule pa Miyambo 27:11. Pamenepo Mulungu akutiuza kuti: ‘Mwananga, khala wanzeru, ukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.’ Kodi ukudziŵa kuti kutonza munthu wina kumatanthauza chiyani?— Chabwino, munthu amakutonza mwa kukuseka ndi kukunena kuti sungachite zimene iwe wanena kuti ungathe kuchita. Kodi Satana amachita chiyani potonza Yehova?— Tiye tione.

 Ngati ukukumbukira, tinaphunzira mu Mutu 8 wa buku lino kuti Satana amafuna kukhala Nambala Wani ndipo amafuna kuti aliyense amvere iye. Satana amanena kuti anthu amalambira Yehova chabe chifukwa chakuti Yehovayo adzawapatsa moyo wosatha. Atachititsa Adamu ndi Hava kuti asamvere Yehova, Satana anayamba kutsutsa Mulungu. Anauza Mulungu kuti: ‘Anthu amakutumikirani chabe chifukwa cha zimene mumawapatsa. Mutangondipatsa mpata wowayesa, palibe amene angamverenso inu.’

Adamu ndi Hava atachimwa, kodi Satana anachita chiyani potsutsa Yehova?

Inde, ndi zoona kuti mawu amenewo sapezeka m’Baibulo. Koma tikaŵerenga nkhani ya Yobu, zimaonekeratu kuti Satana ananena zinthu ngati zimenezo kwa Mulungu. Kukhulupirika kapena kusakhulupirika kwa Yobu inalidi nkhani yaikulu kwa Satana ndi kwa Yehova. Tiye titsegule Baibulo pa Yobu chaputala 1 ndi chaputala 2 kuti tione zimene zinachitika.

Waona mu Yobu chaputala 1 kuti Satana analinso kumwamba pamene angelo anafika kudzaona Yehova. Ndiye Yehova  anafunsa Satana kuti: ‘Ukuchokera kuti?’ Satana anayankha kuti anali kuyendayenda kuyang’ana m’dziko. Choncho Yehova anafunsa kuti: ‘Kodi waona Yobu, kuti iye amanditumikira ndipo sachita choipa chilichonse?’—Yobu 1:6-8.

Pamenepo Satana anatsutsa. Iye anati: ‘Yobu amakulambirani chabe chifukwa chakuti alibe mavuto ngakhale pang’ono. Mukasiya kumuteteza ndi kumudalitsa, adzakuchiritani mwano pamaso panu.’ Atatero, Yehova anayankha kuti: ‘Chabwino, iwe Satana, ungachite chilichonse chimene ukufuna, koma Yobu yekha usamupweteke.’—Yobu 1:9-12.

Kodi Satana anachita chiyani?— Anakonza zoti anthu abe ng’ombe ndi abulu a Yobu ndi kupha amene anali kuzisamalira. Kenako mphezi inawomba ndi kuwononga nkhosa ndi abusa omwe. Pambuyo pake, anthu anabwera ndi kuba ngamila ndi kupha amene anali kuzisamalira. Pomaliza, Satana anautsa chimphepo chimene chinagwetsa nyumba imene munali ana teni a Yobu, ndipo onse anafa. Ngakhale kuti zonsezi zinachitika, Yobu sanasiye kutumikira Yehova.—Yobu 1:13-22.

Yehova ataonanso Satana, ananena kuti Yobu akali wokhulupirika. Koma Satana anatsutsa. Iye anati: ‘Mutangondilola kuti ndimupweteke, iye adzakuchitirani mwano  pamaso panu.’ Choncho Yehova analola Satana kuti apweteke Yobu koma anamuchenjeza kuti asamuphe.

Kodi Yobu anapirira chiyani, ndipo ndi chifukwa chiyani Mulungu anakondwera?

Satana anadwalitsa Yobu kwambiri mpaka thupi lake lonse linakhala zilonda zokhazokha. Zilondazi zinali kununkha kwambiri moti palibe amene anafuna kuyandikana naye. Ngakhale mkazi wa Yobu anauza Yobuyo kuti: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Aja amene anali kuyerekeza kukhala mabwenzi ake anafika kudzamuona. Koma iwo anawonjezera chisoni chakecho mwa kunena kuti Yobu anachita zinazake zoipa kwambiri kuti iye akumane ndi mavuto amenewo. Komabe, ngakhale kuti Satana anadzetsa mavuto onseŵa ndi zopweteka pa Yobu, iye anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.—Yobu 2:1-13; 7:5; 19:13-20.

Kodi ukuganiza kuti Yehova anamva bwanji ndi kukhulupirika kwa Yobu?— Yehova anakondwera chifukwa chakuti tsopano akanatha kuuza Satana kuti: ‘Wamuona Yobu! Iye amanditumikira chifukwa chakuti amafuna kutero.’ Kodi iwe udzakhala ngati Yobu? Kodi udzakhala munthu amene Yehova angakuloze monga chitsanzo chotsimikizira kuti Satana ndi wabodza?— Pajatu ndi mwayi kupereka yankho pa zimene Satana amanena kuti angachititse aliyense kusiya kutumikira Yehova. Inde, Yesu naye anaona kuti ndi mwayi.

Mphunzitsi Waluso sanalole Satana kumuchitisa zinthu zoipa. Taganiza mmene chitsanzo chake chinakondweretsera Atate ake! Yehova anatha kuloza Yesu ndi kuyankha Satana kuti: ‘Wamuona Mwana wanga! Wakhala wokhulupirika kwa ine kotheratu chifukwa chakuti amandikonda!’ Taganizanso chimwemwe chimene Yesu ali nacho pokondweretsa mtima wa Atate ake. Chifukwa cha chimwemwe chimenecho, Yesu anapirira ngakhale imfa pamtengo wozunzirapo.—Ahebri 12:2.

Kodi ukufuna kukhala ngati Mphunzitsi wathu Waluso ndi kukondweretsa Yehova?— Ndiye upitirize kuphunzira zimene Yehova akufuna kuti iwe uzichita, ndipo uzimukondweretsa mwa kuchita zimenezo!

Tiŵerenge zimene Yesu anachita kuti akondweretse Mulungu ndi zimene ifenso tifunikira kuchita, pa Miyambo 23:22-25; Yohane 5:30; 6:38; 8:28; ndi 2 Yohane 4.