Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 21

Kodi Tiyenera Kudzitama Tikachita Zabwino?

Kodi Tiyenera Kudzitama Tikachita Zabwino?

KODI kudzitama ndi kutani? Umadziŵa?— Nachi chitsanzo. Kodi unayamba wayesapo kuchita chinachake chimene suchidziŵa bwino kachitidwe kake? Mwinamwake unali kuyesa kuseŵera mpira. Kapena unali kuyesa kuseŵera maseŵera aja amene wina amagwira chingwe mbali ina winanso mbali ina ndi kumazunguza chingwecho ndiye wina ndi kumadumpha. Kodi wina anayamba wakusekapo, ndi kunena kuti, “Ine ndikhoza kukuposa”?— Munthu ameneyotu anali kudzitama.

Kodi iwe umamva bwanji ena akamachita zimenezi? Kodi umasangalala?— Ndiyeno, kodi ukuganiza kuti ena amamva bwanji iweyo ukamadzitama?— Kodi ndi kukoma mtima kuuza munthu wina kuti, “Ine ndimachita bwino kuposa iwe”?— Kodi Yehova amasangalala ndi anthu amene amachita zimenezi?—

Mphunzitsi Waluso anali kudziŵa anthu amene anali kuganiza kuti anali kuchita bwino kuposa anthu ena. Anthuwo anali kudzitama, kapena kuti kudzionetsera, ndipo wina aliyense anali kumuona ngati wosafunika. Ndiye tsiku lina Yesu anawauza nkhani inayake pofuna kuwasonyeza kuti kudzitama si kwabwino. Tamvetsera nkhani yake.

Nkhaniyi imanena za Mfarisi ndi munthu wokhometsa msonkho. Tsono Afarisi anali aphunzitsi achipembedzo, amene nthaŵi zambiri anali kudzionetsa kuti anali olungama kwambiri kuposa anthu ena. Mfarisi yemwe Yesu anali kumunena anapita kukapemphera ku kachisi wa Mulungu ku Yerusalemu.

Ndi chifukwa chiyani Mulungu anasangalala ndi wokhometsa msonkho koma osati Mfarisi?

Yesu ananena kuti wokhometsa msonkho nayenso anapita kukapemphera kukachisiko. Anthu ambiri sanali kugwirizana ndi okhometsa msonkho. Anali kunena kuti anthu okhometsa msonkho anali kubera  anthu. Ndipo ndi zoona kuti nthaŵi zambiri okhometsa msonkho ochuluka sanali kuchita chilungamo.

Kukachisiko, Mfarisi uja anayamba kupemphera kwa Mulungu kuti: ‘Mulungu, ndikuyamikani kuti sindine wochimwa monga anthu ena onse. Sindibera anthu kapena kuchita zinthu zina zoipa. Sindili ngati wamsonkho ali apoyo. Ine ndine munthu wolungama. Ndimakhala wosadya kaŵiri pa mlungu kuti ndithe kukhala ndi nthaŵi yokwanira yoganizira za inu. Ndipo ndimapereka ku kachisi gawo limodzi la magawo teni a zonse zimene ndimapeza.’ Mfarisi uyu anaganiza kuti analidi kuchita bwino kuposa anthu ena, eti?— Ndipo anauza Mulungu zimenezo.

Koma wokhometsa msonkho uja sanali wotero. Iye popemphera sanayang’ane ndi kumwamba komwe. Anaima patali ndi kuŵerama mutu pansi. Wokhometsa msonkhoyu anali wachisoni kwambiri kuti anali wochimwa, ndipo anadzimenya pachifuwa chifukwa cha chisonicho. Sanayese n’komwe kuuza Mulungu kuti anali wabwino. Koma iye anapemphera kuti: “Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.”

Kodi iwe ukuganiza kuti mwa aŵiriŵa ndani anasangalatsa Mulungu? Kodi anali Mfarisi, amene anaganiza kuti anali wabwino kwambiri? Kapena kodi anali wamsonkho, amene anamva chisoni chifukwa chakuti anali wochimwa?—

Yesu ananena kuti Mulungu anasangalala ndi wamsonkho. Chifukwa chiyani? Yesu analongosola kuti: ‘Pakuti aliyense amene amafuna kuoneka monga wochita bwino kusiyana ndi anthu ena  adzamuchepetsa. Koma amene amadziona monga wamng’ono adzamukweza.’—Luka 18:9-14.

Kodi mu nkhani imeneyi Yesu anali kuphunzitsa mfundo yanji?— Anali kuphunzitsa kuti ndi kulakwa kuganiza kuti timachita bwino kuposa anthu ena. Mwina sitinganene kuti timaganiza zimenezo, koma mwa zimene timachita tikhoza kusonyeza kuti timaganiza kuti ndife abwino kuposa ena. Kodi iwe unachitapo zinthu mwa njira imeneyo?— Taganizira mtumwi Petro.

Panthaŵi ina Yesu anauza atumwi ake kuti onse adzamuthaŵa pamene iye wagwidwa. Koma Petro anadzitama kuti: ‘Ngakhale onse atakuthaŵani, ine sindidzakuthaŵani!’ Koma Petro ananama. Anadzidalira kwambiri. Iye anamuthaŵadi Yesu. Komabe anabweranso, monga mmene tidzaonera m’Mutu 30 wa buku lino.—Mateyu 26:31-33.

Tiye tione chitsanzo cha masiku ano. Tinene kuti iweyo ndi winawake m’kalasi mwanu aphunzitsi akukufunsani mafunso kusukulu. Kodi ungachite chiyani ngati iweyo ukhoza kuyankha mafunsowo mofulumira, koma winayo sangathe? Ndi zoona kuti zimasangalatsa ukakhala kuti mayankho ake ukuwadziŵa. Koma kodi kungakhale kukoma mtima kudziyerekeza iweyo ndi amene amayankha mochedwayo?— Kodi ndi bwino kuchititsa munthu wina kuoneka woipa kuti iwe uoneke wabwino?—

Zimenezi ndi zimene anachita Mfarisi uja. Iye anadzitama kuti anali kuchita bwino kuposa wokhometsa msonkho uja. Koma Mphunzitsi Waluso ananena kuti Mfarisiyo analakwa kuganiza zimenezo. Ndi zoona kuti munthu wina akhoza kuchita chinthu china bwino kusiyana ndi wina. Koma zimenezi sizitanthauza kuti iye ndi wabwino kuposa winayo.

Ngati iwe ukudziŵa zinthu zambiri kuposa wina, kodi umakhala wabwino kuposa iyeyo?

Ndiye ngati ife timadziŵa zambiri kuposa munthu wina, kodi chimenechi ndi chifukwa chokwanira kuti tizidzitama?— Taganizira izi. Kodi tinapanga tokha ubongo wathu?— Ayi, Mulungu ndiye anapatsa ubongo munthu aliyense. Ndipo zinthu zambiri zimene timazidziŵa tinaziphunzira kwa anthu ena. Mwina tinaziŵerenga m’buku. Kapena munthu wina ndiye anatiuza. Ngakhale ngati tinadziŵa mwa ife tokha mmene tingachitire zinazake, kodi tinazidziŵa bwanji?— Ee, tinagwiritsa  ntchito ubongo umene Mulungu anatipatsa.

Pamene wina akuyesetsa kuchita chinachake, ndi bwino kumulimbikitsa. Muuze kuti ukusangalala ndi zimene wachita. Mwina ungamuthandize kuchita bwino kuposa pamenepo. Ndi zimene iwe umafuna kuti anthu ena azikuchitira, si choncho?—

Ndi chifukwa chiyani ndi kulakwa kudzitama kuti tili ndi mphamvu kuposa munthu wina?

Anthu ena ndi amphamvu kuposa ena. Bwanji ngati iweyo uli ndi mphamvu kuposa mng’ono wako kaya mkulu wako kapenanso mlongo wako? Kodi chimenechi ndi chifukwa choti uzidzitama?— Ayi. Chakudya chimene timadya ndicho chimatipatsa mphamvu. Ndipo Mulungu ndiye amapereka dzuŵa ndi mvula ndiponso chilichonse chofunika kuti zomera zikule kuti tikhale ndi chakudya, kodi si choncho?— Motero tiyenera kuyamika Mulungu kuti tili ndi mphamvu.—Machitidwe 14:16, 17.

Palibe amafuna kumva wina akudzitama, kapena ukuganiza alipo?— Ndiyetu tizikumbukira mawu a Yesu akuti: ‘Zimene inu mufuna kuti anthu ena akuchitireni, muwachitirenso zomwezo.’ Ngati tichita zimenezi, sitidzakhala ngati Mfarisi anadzitama uja m’nkhani imene Mphunzitsi Waluso anafotokoza.—Luka 6:31.

 Nthaŵi ina munthu wina ananena Yesu kuti ndi wabwino. Kodi Mphunzitsi Waluso ananena kuti, ‘Inde, ndine wabwino’?— Ayi sanatero. Koma ananena kuti: ‘Palibe wabwino koma Mulungu yekha.’ (Marko 10:18) Ngakhale kuti Mphunzitsi Waluso anali wangwiro, iye sanadzitame. M’malo mwake iye analemekeza Atate ake, Yehova.

Ndiye kodi pali amene tikhoza kumutama?— Inde alipo. Tingatame Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Tikaona kukongola kwa dzuŵa pamene likuloŵa kapena cholengedwa china chilichonse chochititsa kaso, tikhoza kuuza munthu wina kuti, ‘Mulungu wathu wabwino, Yehova, ndiye anapanga zimenezi!’ Nthaŵi zonse tizikhala okonzeka kulankhula za zinthu zazikulu zimene Yehova wachita kale ndiponso zimene adzachita m’tsogolo.

Kodi mnyamata uyu akutama yani?

Tiŵerenge zimene Malemba amanena zokhudza kudzitama, kapena kuti kudzionetsera, ndipo tione mmene ifeyo tingapewere kudzitama: Miyambo 16:5, 18; Yeremiya 9:23, 24; 1 Akorinto 4:7; ndi 1 Akorinto 13:4.