Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 27

Kodi Mulungu Wako Ndani?

Kodi Mulungu Wako Ndani?

NDI chifukwa chiyani funso lakuti, Kodi Mulungu Wako Ndani? lili lofunika kwambiri?— Ndi chifukwa chakuti anthu amalambira milungu yambiri. (1 Akorinto 8:5) Pamene mtumwi Paulo analandira mphamvu kwa Yehova ndi kuchiritsa munthu amene sanayendepo kuyambira kubadwa kwake, anthu anafuula kuti: “Milungu yatsikira kwa ife monga anthu”! Anthu amenewo anafuna kulambira Paulo ndi mnzake Barnaba. Iwo anapatsa Paulo dzina lakuti Herme, ndipo Barnaba anamupatsa dzina lakuti Zeu. Mayina ameneŵa anali mayina a milungu yonama.

Koma Paulo ndi Barnaba sanalole anthuwo kuti awalambire. Choncho iwo analumphira mu khamulo ndipo ananena kuti: ‘Siyani zinthu zachabe izi, mutembenukire kwa Mulungu wamoyo.’ (Machitidwe 14:8-15) Kodi “Mulungu wamoyo” ameneyu, amene analenga zinthu zonse, ndani?— Inde, ndi Yehova, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Yesu anati Yehova ndi “Mulungu woona yekha.” Ndiye ukaganiza, ndani yekha amene tiyenera kumulambira?— Ndi Yehova yekha basi!—Salmo 83:18; Yohane 17:3; Chivumbulutso 4:11.

Kodi ndi chifukwa chiyani Paulo ndi Barnaba sanalole anthuŵa kuwagwadira?

Anthu ambiri amalambira milungu ina m’malo mwa “Mulungu woona yekha.” Nthaŵi zambiri amalambira zinthu zimene amapanga ndi mitengo, miyala, kapena zitsulo. (Eksodo 32:4-7; Levitiko 26:1; Yesaya 44:14-17) Nthaŵi zina ngakhale amuna ndi akazi otchuka amatchedwa milungu, ngwazi, kapena amaonedwa ngati oyenera kuwagwadira. Kodi ndi bwino kupatsa anthuwo ulemerero?—

Saulo atakhala mtumwi Paulo, analemba kuti: ‘Mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.’ (2 Akorinto 4:4) Kodi mulungu ameneyu ndani?— Inde, ndi Satana Mdyerekezi! Satana wachititsa anthu kulambira anthu anzawo ndi zinthu zina zambiri.

 Pamene Satana anauza Yesu kuti agwade ndi kumulambira, kodi Yesu ananena chiyani kwa Satanayo?— Ananena kuti, ‘Yehova Mulungu wako ndiye amene uyenera kumugwadira, ndipo iye yekhayekha ndiye amene uyenera kumulambira.’ (Mateyu 4:10) Apa tikuona kuti Yesu anamveketsa bwino kuti amene tiyenera kumulambira ndi Yehova yekha basi. Tiye tiŵerenge za anyamata ena amene anachita zimenezi. Mayina awo ndi Sadrake, Mesake, ndi Abedinego.

Ahebri achinyamata ameneŵa anali a mtundu wa Israyeli umene unali mtundu wa Mulungu, ndipo anatengedwa ukapolo kupita ku dziko la Babulo. Ali kumeneko, mfumu ina dzina lake Nebukadinezara inapanga fano lalikulu lagolidi. Ndiye tsiku lina mfumuyo inalamula kuti akayamba kuimba nyimbo, aliyense agwadire fanolo. ‘Aliyense wosagwadira ndi kulambira fanolo, adzaponyedwa mu ng’anjo yotentha  yamoto,’ inachenjeza motero mfumuyo. Ukanakhala iwe ukanachita chiyani?—

Ndi chifukwa chiyani amuna aŵa akana kugwadira fanolo?

Sadrake, Mesake, ndi Abedinego nthaŵi zambiri anali kuchita zonse zimene mfumu inalamula. Koma apa iwo anakana kugwadira fano. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Chinali chifukwa chakuti lamulo la Mulungu linanena kuti: ‘Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema ndi kuligwadira.’ (Eksodo 20:3-5) Choncho Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anamvera lamulo la Yehova m’malo mwa lamulo la mfumu.

Mfumuyo inakwiya kwambiri moti nthaŵi yomweyo inaitana Ahebri achinyamata atatu ameneŵa. Inawafunsa kuti: ‘Kodi ndi zoona kuti mukukana kutumikira milungu yanga? Ndikupatsani mpata wina. Mukamva nyimbo zikuimbidwa, mugwade ndi kulambira fano limene ndapanga. Ngati simudzatero, mudzaponyedwa mu ng’anjo yotentha yamoto. Ndipo mulungu amene adzakulanditsani m’manja mwanga ndani?’

Kodi anyamata ameneŵa akanachita chiyani? Nanga ukanakhala iwe ukanachita chiyani?— Iwo anati kwa mfumu: ‘Mulungu wathu amene timutumikira akhoza kutilanditsa. Koma akapanda kutero, sitidzatumikira milungu yanu. Sitidzagwadira fano lanu lagolidi.’

Kodi Yehova anawapulumutsa bwanji atumiki ake mu ng’anjo yamoto?

Mfumuyo inakalipa kwambiri ndipo inalamula kuti: ‘Sonkhezani  ng’anjo yamoto ka seveni kuposa masiku onse!’ Kenako inalamula anyamata ake amphamvu kumanga Sadrake, Mesake, ndi Abedinego ndi kuwaponya mu ng’anjo yamoto ija! Ng’anjoyo inatentha kwambiri moti malaŵi ake anapha anyamata a mfumu aja! Nanga ndi chiyani chimene chinachitikira Ahebri atatu aja?

Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anagwera pakati penipeni pa moto. Kenako anaimirira! Iwo sanapweteke kapenanso kupsa. Ndipo sanalinso omangidwa. Kodi zimenezo zinatheka bwanji?— Mfumu itayang’ana mu ng’anjo muja, inachita mantha ndi zimene inaona. ‘Kodi sitinaponye amuna atatu m’moto?’ inafunsa choncho. Atumiki a mfumu anayankha kuti: “Inde, mfumu.”

Ndiyeno mfumuyo inati: ‘Taonani, ndikuona amuna anayi omasuka, alikuyenda m’kati mwa moto; ndipo moto sukuwaotcha.’ Kodi ukudziŵa kuti munthu wachinayiyo anali ndani?— Anali mngelo wa Yehova. Iye anateteza Ahebri atatuwo kuti moto usawaotche.

Itaona zimenezi, mfumu ija inafika pakhomo la ng’anjoyo ndi kufuula kuti: “Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, inu  atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba, tulukani, idzani kuno”! Iwo atatuluka, munthu aliyense anaona kuti moto uja sunawaotche. Ngakhale fungo la moto silinamveke pa iwo. Pamenepo, mfumu inati: ‘Alemekezeke Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mngelo wake, ndi kupulumutsa atumiki ake chifukwa anakana kulambira mulungu wina aliyense, koma Mulungu wawowawo.’—Danieli, chaputala 3.

Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu masiku ano amazilemekeza ngati mafano?

Tingaphunzirepo kanthu pa zimene zinachitika kalelo. Ngakhale masiku ano anthu amapanga zinthu, kapena kuti mafano, kuti azilambira. Buku lakuti The Encyclopedia Americana limati: “Mbendera ndi yopatulika ngati mtanda.” Mafanowo angapangidwe ndi mtengo, mwala, chitsulo, kapena nsalu. Ophunzira oyambirira a Yesu anali kukana kulambira mfumu ya Roma. Ndipo malinga ndi wolemba mbiri, Daniel P. Mannix, kukana kulambira mfumu kuli ngati “kukana kuchitira sailuti mbendera kapena kulumbira kukhala wokhulupirika ku boma.”

Ndiye kodi ukuganiza kuti kwa Mulungu zimasiyana ngati fano logwiritsa ntchito polambira alipanga ndi nsalu, mtengo, mwala, kapena chitsulo?— Kodi ndi bwino kuti mtumiki wa Yehova azilambirira pa mafano ngati ameneŵa?— Sadrake, Mesake, ndi Abedinego sanachite zimenezo, ndipo Yehova anakondwera nawo. Kodi iwe ungachite chiyani potengera chitsanzo chawo?—

Anthu amene amalambira Yehova sangalambire munthu wina aliyense kapena chinthu china. Taŵerengani zimene zanenedwa pa nkhaniyi pa Yoswa 24:14, 15, 19-22; Yesaya 42:8; 1 Yohane 5:21; ndi Chivumbulutso 19:10.