Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

 Mutu 43

Kodi Abale Athu ndi Alongo Athu Ndani?

Kodi Abale Athu ndi Alongo Athu Ndani?

TSIKU lina Mphunzitsi Waluso anafunsa funso lodabwitsa. Funsolo linali lakuti: ‘Amayi anga ndani, ndipo abale anga ndani?’ (Mateyu 12:48) Kodi iwe ukanayankha bwanji funso limenelo?— Ndikhulupirira kuti ukudziŵa kuti amayi ake a Yesu dzina lawo linali Mariya. Koma kodi mayina a abale ake ukuwadziŵa?— Kodi Yesu analinso ndi alongo ake?—

Baibulo limanena kuti abale ake a Yesu mayina awo anali “Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda.” Ndipo Yesu anali ndi alongo ake amene anali moyo panthaŵi imene iye anali kulalikira. Popeza kuti Yesu anali woyamba kubadwa, onseŵa anali aang’ono kwa iye.—Mateyu 13:55, 56; Luka 1:34, 35.

Kodi abale a Yesu analinso ophunzira ake?— Baibulo limanena kuti poyamba iwo ‘sanakhulupirire Iye.’ (Yohane 7:5) Koma pambuyo pake, Yakobo ndi Yuda anakhala ophunzira ake, ndipo mpaka analemba mabuku a m’Baibulo. Kodi mabuku amene iwo analemba ukuwadziŵa?— Inde, buku la Yakobo ndi la Yuda.

Ngakhale kuti Baibulo silitchula mayina a alongo ake a Yesu, tikudziŵa kuti anali ndi alongo ake osachepera aŵiri. Koma pangakhale panalinso ena. Kodi alongo ake ameneŵa anakhala otsatira ake?— Baibulo silinena, choncho sitikudziŵa. Koma kodi ukudziŵa chifukwa chake Yesu anafunsa funso lakuti, ‘Amayi anga ndani, ndipo abale anga ndani?’— Tiye tipeze yankho.

Pamene Yesu anali kuphunzitsa ophunzira ake, munthu wina analankhula kuti: ‘Amayi anu ndi abale anu aima pabwalo, ndipo akufuna kulankhula nanu.’ Ndiye Yesu anagwiritsa ntchito mpata  umenewu kuti awaphunzitse mfundo yofunika kwambiri mwa kufunsa funso lodabwitsalo lakuti: ‘Amayi anga ndani, ndipo abale anga ndani?’ Kenako anatambasula dzanja lake kuloza ophunzira ake ndipo anayankha kuti: “Penyani amayi anga ndi abale anga!”

Yesu atatero, anafotokoza zimene anatanthauza. Iye anati: ‘Aliyense amene adzachita zimene Atate anga a Kumwamba amafuna, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi anga.’ (Mateyu 12:47-50) Zimenezi zikusonyeza mmene Yesu anakondera ophunzira ake. Pamenepa Yesu anali kutiphunzitsa kuti kwa iye ophunzira ake anali ngati abale ake, alongo ake, ndi amayi ake enieni.

Kodi Yesu anafotokoza kuti abale ake ndi alongo ake anali ndani?

Panthaŵi imeneyo abale ake enieni a Yesu—Yakobo, Yosefe, Simoni, ndi Yuda—sanali kukhulupirira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu. Ayenera kuti sanakhulupirire zimene mngelo Gabrieli anauza amayi awo. (Luka 1:30-33) Choncho mwina iwo anali kuvutitsa Yesu. Munthu aliyense akamachita zofanana ndi zimene iwo anachita ndiye kuti si mbale kapena mlongo weniweni. Kodi ukudziŵapo  munthu aliyense amene wakhala akuvutitsa mbale wake kapena mlongo wake?—

Baibulo limasimba za Esau ndi Yakobo ndi mmene Esauyo anakwiyira mpaka kunena kuti: ‘Ndidzamupha mbale wanga Yakobo.’ Rebeka, amene anali amayi awo, anaopa kwambiri mpaka anauza Yakobo kuthaŵa kuti Esau asamuphe. (Genesis 27:41-46) Koma patapita zaka zambiri, Esau anasintha maganizo ake, ndipo anakumbatira ndi kupsompsona Yakobo.—Genesis 33:4.

Ndiye patapita nthaŵi, Yakobo uja anakhala ndi ana 12. Koma ana aakulu a Yakobo sanakonde Yosefe mng’ono wawo. Iwo anamuchitira nsanje chifukwa chakuti atate awo anamukonda kwambiri. Choncho anamugulitsa kwa anthu ogula ndi kugulitsa akapolo, amene anali kupita ku Igupto. Kenako anauza atate awo kuti Yosefe waphedwa ndi chilombo. (Genesis 37:23-36) Kodi zimenezo sizinali zoipa?—

Pambuyo pake abale a Yosefe anamva chisoni ndi zimene iwo anachita. Ndiye Yosefe anawakhululukira. Kodi ukuona kufanana kwa Yosefe ndi Yesu?— Nthaŵi imene Yesu anali pamavuto, atumwi ake anathaŵa kumusiya, ndipo  mpaka Petro anachita kukana kuti sadziŵa Yesuyo. Koma Yesu, mofanana ndi Yosefe, anawakhululukira iwo onse.

Kodi tiyenera kuphunzirapo chiyani pa zimene Kaini anachita kwa Abele?

Ndiye pali abale aŵiri omwe mayina awo ndi Kaini ndi Abele. Iwonso angatiphunzitse mfundo yofunika kwambiri. Mulungu atayang’ana mu mtima wa Kaini, anaona kuti Kainiyo sanali kumukondadi mbale wake. Chotero Mulungu anauza Kaini kuti asinthe khalidwe lake. Kaini akanakhala kuti anali kukondadi Mulungu, akanamvera. Koma iye sanakonde Mulungu. Ndiye tsiku lina Kaini anauza Abele kuti: ‘Tiye kumunda.’ Abele anapita ndi Kainiyo. Ali kumundako, Kaini anamenya mbale wake kwambiri mpaka kumupha.—Genesis 4:2-8.

Baibulo limatiuza kuti pali mfundo yapadera imene tingaphunzirepo pamenepa. Kodi ukuidziŵa?— Baibulo limati: ‘Uwu ndi uthenga umene munaumva kuyambira pachiyambi kuti: Tikondane wina ndi mnzake; osati monga Kaini amene anali wochokera kwa woipayo.’ Choncho abale ndi alongo ayenera kukondana wina ndi mnzake. Asamakhale ngati Kaini.—1 Yohane 3:11, 12.

Kodi ndi chifukwa chiyani si bwino kukhala ngati Kaini?— Chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti iye ‘anali wochokera kwa woipayo,’ Satana Mdyerekezi. Popeza kuti Kaini anachita ngati Mdyerekezi, zinakhala ngati kuti Mdyerekeziyo ndiye anali atate ake.

Kodi ukuona chifukwa chake ufunika kukonda abale ako ndi alongo ako?— Ngati suwakonda, kodi udzakhala ukutsanzira ana a ndani?— Udzakhala ukutsanzira ana a Mdyerekezi. Iwe sukufuna kukhala mwana wake, kapena ukufuna?— Ndiye ungasonyeze bwanji kuti ukufuna kukhala mwana wa Mulungu?— Mwa kuwakondadi abale ako ndi alongo ako.

Nanga kodi chikondi ndi chiyani?— Chikondi ndi mtima umene timakhala nawo wofuna kuchitira anthu ena zinthu zabwino. Timasonyeza kuti timakonda ena ngati mumtimamu timawaganizira zabwino ndiponso ngati timawachitira zinthu zabwino. Ndipo kodi abale athu ndi alongo athu amene tiyenera kuwakonda ndani?— Ngati  ukukumbukira, Yesu anaphunzitsa kuti ndi Akristu anzathu a mumpingo amene tonse pamodzi timapanga banja lalikulu.

Kodi ungasonyeze bwanji kuti umakonda mbale wako?

Kodi ndi chifukwa chiyani tifunika kukonda abale athu ndi alongo athu achikristu ameneŵa?— Baibulo limanena kuti: “Iye wosakonda mbale wake [kapena mlongo wake] amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:20) Choncho sitingangokonda anthu ochepa chabe m’banja lachikristu limeneli. Tiyenera kukonda onse. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Kodi iwe umakonda abale ndi alongo onse?— Uzikumbukira kuti ngati suwakonda, ndiye kuti sukondadi Mulungu wachikondi.

Nanga tingasonyeze bwanji kuti timakondadi abale athu ndi alongo athu?— Chabwino, ngati timawakonda, sitidzawapewa chifukwa chosafuna kulankhula nawo. Tidzakhala waubwenzi kwa onse. Nthaŵi zonse tidzafuna kuwachitira zabwino ndi kugaŵana nawo zinthu. Ndipo akakumana ndi mavuto, tidzawathandiza chifukwa chakuti ndifedi banja limodzi lalikulu.

Kodi timasonyeza chiyani ngati tikukondadi abale athu ndi alongo athu onse?— Timasonyeza kuti ndife ophunzira a Yesu, Mphunzitsi Walusoyo. Ndipo kodi zimenezi si zimene ife tikufuna?—

Nkhani yokonda abale athu ndi alongo athu ikufotokozedwanso pa Agalatiya 6:10 ndi 1 Yohane 4:8, 21. Bwanji osatsegula Baibulo lako uŵerenge malemba ameneŵa?