PAMENE Saulo anali kuchita zinthu zoipa, kodi ukuganiza kuti ndani anasangalala?— Amene anasangalala ndi Satana Mdyerekezi. Atsogoleri achipembedzo cha Ayuda anasangalalanso. Ndiye pamene Saulo anakhala wophunzira wa Mphunzitsi Waluso ndipo dzina lake ndi kukhala Paulo, atsogoleri achipembedzo aja anamuda iye. Kodi ukuona chifukwa chake zimavuta kuti wophunzira wa Yesu achite zinthu zabwino?—

Kodi Paulo anakumana ndi mavuto otani pamene anachita zinthu zabwino?

Mkulu wa ansembe dzina lake Hananiya anauza anthu tsiku lina kuti amenye Paulo kumaso. Hananiya anayesa ngakhale kuika Paulo mu ndende. Paulo anavutika kwambiri atakhala wophunzira wa Yesu. Mwachitsanzo, anthu oipa anamenya Paulo ndipo anayesa kumupha ndi miyala ikuluikulu.—Machitidwe 23:1, 2; 2 Akorinto 11:24, 25.

Anthu ambiri adzatiumiriza kuchita zinthu zimene Mulungu sakondwera nazo. Choncho taganizira izi: Kodi umakonda kwambiri kuchita zinthu zabwino? Kodi umazikonda kwambiri mpaka poti  udzachitabe zabwino ngakhale pamene ena akukuda chifukwa chochita zabwinozo? Kuchita zimenezi kumafuna kulimba mtima, kodi si choncho?—

Mwina iwe ungadabwe kuti, ‘Kodi anthu angatide bwanji pamene tikuchita zinthu zabwino? Ndimaganiza afunika kusangalala?’ Zikuyeneradi kukhala choncho. Anthu nthaŵi zambiri anakonda Yesu chifukwa cha zinthu zabwino zimene iye anali kuchita. Tsiku lina, anthu onse a pamudzi wina anasonkhana pakhomo la nyumba imene iye anali kukhala. Iwo anafika pakhomopo chifukwa chakuti Yesu anali kuchiritsa anthu odwala.—Marko 1:33.

Komabe nthaŵi zina anthu sanakonde zimene Yesu anawaphunzitsa. Ngakhale kuti iye anali kuphunzitsa zabwino nthaŵi zonse, anthu ena  anadana naye kwambiri chifukwa anali kulankhula zoona. Izi ndi zimene zinachitika tsiku lina ku Nazarete, mudzi umene Yesu anakulira. Kumeneko iye analoŵa mu sunagoge, nyumba imene Ayuda anali kulambiriramo Mulungu.

Mu sunagogemo, Yesu anakamba nkhani yabwino kwambiri yochokera m’Malemba. Poyamba, anthu anaikonda. Iwo anadabwa kumva zinthu zabwino zimene iye anali kulankhula. Sanakhulupirire kuti munthu ameneyu ndi uja amene anamuona akukula mu mudzi wawo womwewo.

Kenako Yesu anatchula mfundo ina. Ananena kuti panali nthaŵi zina pamene Mulungu anakonda kwambiri anthu amene sanali Ayuda. Yesu atanena zimenezi, anthu mu sunagogemo anakwiya. Ukudziŵa chifukwa chake?— Ayudawo anaganiza kuti Mulungu anali kukonda mtundu wawo wokha osati wina ayi. Anaganiza kuti mtundu wawo unali kuposa mitundu ina. Ndiye chifukwa chake anada Yesu pa zimene ananena. Nanga kodi ukudziŵa zimene iwo anayesa kuchita kwa Yesu?—

Baibulo limanena kuti: ‘Iwo anagwira Yesu ndi kumutulutsira kunja kwa mudziwo. Anapita naye pamwamba pa phiri kuti amuponye kuphedi afe! Koma Yesu anawapulumuka ndi kuthaŵa.’—Luka 4:16-30.

Ndi chifukwa chiyani anthu aŵa akufuna kupha Yesu?

Ngati zoterezi zitachitikira iwe, kodi ungapitenso kukalankhula ndi anthu amenewo za Mulungu?— Ungafunike kulimba mtima kuti uchite zimenezo, eti?— Koma patapita chaka, Yesu anapitanso ku Nazarete. Baibulo limanena kuti: ‘Anaphunzitsa iwo mu sunagoge mwawo.’ Yesu sanasiye kulankhula choonadi chifukwa choopa anthu amene sanali kukonda Mulungu.—Mateyu 13:54.

Tsiku lina pa sabata, Yesu anali pamalo pamenenso panali munthu wolemala dzanja. Yesu anali ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu yochiritsira munthuyo. Koma anthu ena pamenepo anayesa kuvutitsa Yesu. Kodi Mphunzitsi Waluso anachita chiyani?— Choyamba iye anawafunsa kuti: ‘Ngati muli ndi nkhosa, ndipo nkhosayo yagwera mu chidzenje pa tsiku la Sabata, kodi mungaitulutse?’

 Inde, iwo akanaitulutsadi nkhosayo, ngakhale pa tsiku la Sabata, limene iwo anafunikira kupuma. Chotero Yesu anati: ‘Ndiye ndi bwino kuthandiza munthu pa Sabata, chifukwa chakuti munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa!’ Apatu zinaonekeratu kuti Yesu afunika kuthandiza munthuyo mwa kumuchiritsa!

Atatero, Yesu anauza munthuyo kutambasula dzanja lake. Nthaŵi yomweyo dzanja lake linachira ndipo munthuyo anakondwera kwambiri! Nanga anthu ena aja anatani? Kodi anasangalala?— Ayi. M’malo mwake, anada Yesu kwambiri. Iwo anatuluka kukapangana kuti amuphe!—Mateyu 12:9-14.

Ndi mmenenso zilili masiku ano. Ngakhale tichite zotani, sitingasangalatse anthu onse. Choncho tiyenera kusankha kuti tikufuna kusangalatsa ndani. Ngati tikufuna kusangalatsa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndiye kuti nthaŵi zonse tiyenera kuchita zimene iwo akutiphunzitsa. Koma tikachita zimenezo, ndani amene adzatida? Ndani adzavutitsa zinthu pamene ife tikufuna kuchita zinthu zabwino?—

Ndi Satana Mdyerekezi. Nanga enanso ndani?— Anthu amene Mdyerekezi wawapusitsa kuti akhulupirire zinthu zolakwika. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo masiku akewo kuti: ‘Inu muchokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mufuna kuchita zolakalaka za atate wanu.’—Yohane 8:44.

Pali anthu ambiri amene Mdyerekezi amawakonda. Yesu anati amenewo ndi “dziko.” Kodi ukuganiza kuti “dziko” limene Yesu anali kunena ndi chiyani?— Eya, tiye tiŵerenge Yohane chaputala 15, vesi 19, tione. Pamenepo tikupezapo mawu aŵa a Yesu: “Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”

Chotero dziko limene limada ophunzira a Yesu lapangidwa ndi anthu onse amene sali otsatira ake. Ndi chifukwa chiyani dzikoli limada  ophunzira a Yesu?— Taganiza kaye. Kodi amene akulamulira dzikoli ndani?— Baibulo limanena kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Woipayo ndi Satana Mdyerekezi.—1 Yohane 5:19.

Kodi ukuona tsopano chifukwa chake kuchita zinthu zabwino kumavuta?— Satana ndi dziko lake amavutitsa zinthu. Koma palinso chifukwa china. Kodi ukuchikumbukira?— M’Mutu 23 wa buku lino, tinaphunzira kuti ife tonse timabadwa ndi uchimo. Ndiye zidzakhala zosangalatsa pamene uchimo, Mdyerekezi, ndi dziko lake zidzachokeratu, si choncho?—

Dzikoli likachoka, kodi chidzachitika ndi chiyani kwa anthu amene amachita zinthu zabwino?

Baibulo limalonjeza kuti: “Dziko lapansi lipita.” Zimenezi zikutanthauza kuti anthu onse amene satsatira Mphunzitsi Waluso sadzakhalakonso. Sadzaloledwa kukhala ndi moyo wosatha. Kodi ukuwadziŵa amene adzakhala ndi moyo wosatha?— Baibulo likupitiriza kunena kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Inde, amene amachita zinthu zabwino, amene amachita “chifuniro cha Mulungu,” ndi okhawo amene adzakhala ndi moyo wosatha mu dziko latsopano la Mulungu. Choncho, ngakhale kuti zimavuta, tiyenerabe kuchita zinthu zabwino, eti?—

Tiye tiŵerenge limodzi malemba aŵa amene akusonyeza chifukwa chake kuchita zinthu zabwino kumavuta: Mateyu 7:13, 14; Luka 13:23, 24; ndi Machitidwe 14:21, 22.